Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda pa Bwato Ndi Njira Yabwino Yoyendera ku Canada

Kuyenda pa Bwato Ndi Njira Yabwino Yoyendera ku Canada

Kuyenda pa Bwato Ndi Njira Yabwino Yoyendera ku Canada

MUNTHU wina wofufuza malo wa ku France, dzina lake Samuel de Champlain, anawoloka nyanja ya Atlantic n’kukafika mu mtsinje wa St. Lawrence, womwe umapezeka m’dziko la Canada. Atangoyenda pang’ono, anapezana ndi mathithi aakulu kwambiri otchedwa Lachine omwe ali m’dera la Montreal. Mu 1603, iye analemba m’buku lake kuti wayesetsa kuti awoloke mathithiwa pogwiritsa ntchito boti lalikulu koma walephera. Panthawiyo zinali zovuta kuyenda pansi chifukwa m’derali munali nkhalango zikuluzikulu. Kodi Champlain ndi anyamata ake anapitiriza bwanji ulendo wawo?

Champlain anaona kuti anthu okhala m’derali ankagwiritsira ntchito mabwato ang’onoang’ono choncho iye anaganiza zogwiritsanso ntchito mabwato amenewa. Iye analemba kuti: “Bwato linkathandiza munthu kuyenda mofulumira kwambiri m’dziko lonseli chifukwa ankadutsa m’mitsinje ing’onoing’ono komanso ikuluikulu mosavuta.”

Njira Yabwino Kwambiri Yoyendera

Kalelo m’mitsinje komanso m’nyanja za ku Canada munkadzaza mabwato, mofanana ndi mmene magalimoto amadzazira mumsewu masiku ano, ndipo anthu ambiri ankaona kuti mabwato ndi njira yabwino kwambiri yoyendera. Anthu nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito mabwato ponyamulira katundu, kufufuza malo atsopano komanso posaka nyama zam’madzi. Mabwatowa ankapangidwa mosiyanasiyana malinga ndi ntchito yake komanso zipangizo zogwiritsa ntchito powapanga. Mwachitsanzo, anthu omwe ankakhala kumadzulo kwa dziko la Canada ankapanga mabwato pogoba mitengo ikuluikulu. Kenako mkati mwake ankaikamo miyala yotentha ndiponso madzi kuti liwongoke komanso likule mmene akufunira. Mabwato ena otere ankanyamula katundu wolemera matani awiri ndipo ankathamanga kwambiri komanso sankasweka wamba. Ankawagwiritsa ntchito pokasaka nyama zikuluzikulu zam’madzi, monga anangumi.

Mwina bwato lalikulu kwambiri linali lopangidwa kuchokera ku khungwa la mtengo winawake wautali kwambiri. Khungwa la mtengo umenewu sililowa madzi wamba komanso limakhala nthawi yaitali osawonongeka. Chinanso silivuta kulipinda ngakhale kuti ndi lolimba kwambiri. Munthu wina wopanga mabwato dzina lake David Gidmark, ananena kuti: “Bwato lopangidwa kuchokera ku khungwa la mtengo umenewu limatha kudutsa pa mathithi aakulu kwambiri oti mabwato ena sangadutse.”

Mabwatowa ankapangidwa ndi zinthu zosiyanasiyana zochokera ku mitengo, monga mizu, utomoni, makungwa ndi zinthu zina. Ichi n’chifukwa chake mabwatowa sankavuta kuwakonza akawonongeka. Komanso ankakhala osalemera kwambiri, choncho sizinkavuta kudutsa nawo m’mathithi oopsa ndi m’malo ena ovuta kudutsa. Chinanso, mabwatowa sankawononga zachilengedwe chifukwa akatayidwa, m’kupita kwa nthawi ankaola.

Mabwatowa ankapangidwa mwaluso kwambiri. Munthu wina wa m’zaka za m’ma 1800 analemba kuti anthu kalelo “sankagwiritsa ntchito misomali ndipo akafuna kulumikiza zinthu ankazisoka kapena kuzimanga. Mfundo zimene ankamanga ndiponso zingwe zimene ankagwiritsa ntchito zinkakhala zolimba kwambiri komanso zomangidwa mwaluso zedi.”

Kusanabwere sitima zapamtunda, mabwato anali njira yodalirika komanso yachangu yoyendera m’madera ambiri ku Canada. Ndiponso kutabwera sitima zapamtunda, anthu sanasiye msanga kugwiritsa ntchito mabwato.

Mabwato anali ofunika kwambiri pa chikhalidwe komanso zikhulupiriro za anthu a ku North America. Mwachitsanzo, nthano zina zimati mabwato anapulumutsa anthu patachitika chigumula. Koma chigumula chimenechi si chimene chimatchulidwa m’Baibulo.

Kupalasa Bwato Masiku Ano

Masiku ano, anthu ambiri ku Canada amapalasabe bwato koma amachita zimenezi ngati masewera chabe. Koma vuto ndi lakuti mitengo yabwino yopangira mabwatowa ikusowa kwambiri. Komabe, zipangizo zina zomwe amagwiritsa ntchito popanga mabwatowa zikupezeka mosavuta monga aluminiyamu, matabwa ndiponso magalasi.

Munthu wina wotchuka kwambiri pankhani yopalasa bwato, dzina lake Bill Mason, anati: “Kuyenda pabwato m’mitsinje imene kale munkadutsa mabwato ndi njira yabwino kwambiri yothandiza munthu kuphunzira zambiri zimene zinaiwalika zokhudza zinthu zam’chilengedwe komanso Mlengi yemwe anapanga zinthuzo.” Anthu ambiri angavomereze zimenezi mosavuta.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 11]

BWATO LOTCHEDWA KAYAK

Anthu a mtundu wa Inuit amakhala m’dera linalake ku Canada lomwe lilibe mitengo. Koma zimenezi sizinkawalepheretsa kupanga mabwato. Iwo ankagwiritsa ntchito zikopa za nyama monga mphalapala ndi nyama zinazake zikuluzikulu zam’madzi komanso mafupa a nyama ndi mitengo yokokoloka ndi madzi kuchokera kunyanja ya Arctic. Kuti mabwatowa asamalowe madzi, ankawamata ndi mafuta a nyama. Bwato lotereli linkatchedwa kuti kayak.

Kusiyana kwakukulu pakati pa bwato limeneli ndi mabwato ena ndi kwakuti limakhala ndi chophimba pamwamba pake, chomwe chimathandiza kuti lisamalowe madzi komanso lizidutsa m’malo oopsa kwambiri. Mabwato oterewa masiku ano amawapanga pogwiritsa ntchito magalasi ndi mapulasitiki.

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Library of Congress