Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kuphunzira Baibulo Kukuthandiza Anthu Osamva”

“Kuphunzira Baibulo Kukuthandiza Anthu Osamva”

“Kuphunzira Baibulo Kukuthandiza Anthu Osamva”

NKHANI ya mutu umenewu inafalitsidwa m’magazini ya anthu osamva m’dziko la Czech Republic. Mlembi wa nkhaniyo, Zdeněk Straka, anayamikira Mboni za Yehova zimene zaphunzira chinenero chamanja kuti zithandize anthu osamva.

Kodi n’chiyani chinachititsa mkuluyu kulemba nkhaniyo? Mu 2006, a Straka anapita ku msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mumzinda wa Prague. Nkhani za pamsonkhano umenewu zinkamasuliridwa m’chinenero chamanja pofuna kuthandiza anthu osamva 70 amene anabwera. Chaka chilichonse, a Mboni za Yehova amakhala ndi misonkhano yachigawo padziko lonse. Pamisonkhano imeneyi, amaphunzira Baibulo ndiponso amasangalala chifukwa chocheza ndi a Mboni anzawo. Nawonso anthu osamva amasangalala ndi misonkhanoyi. M’chaka china posachedwapa, padziko lonse panachitika misonkhano yachigawo yokwana 96 m’chinenero chamanja, ndipo pamisonkhano ina 95, nkhani zinkamasuliridwa m’chinenero chamanja pofuna kuthandiza anthu osamva.

M’chaka chimene msonkhano wachigawo wa ku Prague uja unachitika, anthu amumpingo wachinenero chamanja wa mumzindawo ankaphunzitsa Baibulo anthu 30 osamva. Kuphunzira Baibulo kukuthandiza kwambiri anthu osamva, monga momwe nkhani yotsatirayi ikusonyezera.

Markéta amayenda ulendo wa makilomita oposa 100 mlungu uliwonse kuti akaphunzitse Baibulo mayi wina wosamva wochokera ku Mongolia. Chinenero chamanja chachitcheki n’chosiyana kwambiri ndi chachimongoliya, choncho Markéta amafunika kuganizira njira zosiyanasiyana zothandizira wophunzira wakeyo kuti amvetsetse zimene akunena. Koma khama la Markéta linamupindulira. Pa nthawi imene wophunzira Baibulo wa Markéta anali ndi pakati pa mwana wake wachiwiri, ankaganiza zochotsa mimbayo, koma kenako anasintha maganizo. Markéta anati: “Nditamufunsa chifukwa chimene anasinthira maganizo, iye anandiyankha m’chinenero chamanja kuti, ‘Yehova amadana ndi kuchotsa mimba.’ Ndinasangalala kwambiri kuona kuti akumvetsetsa kuti Mulungu amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali.” *

Padziko lonse, anthu ambiri osamva afika pomudziwa bwino Mulungu chifukwa chophunzira Mawu ake. Baibulo lawathandiza kukhala naye pa ubwenzi, ndipo zimenezi zawachititsa kukhala ndi moyo wosangalala.—Yesaya 48:17, 18.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Kuti mumve zina zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kuchotsa mimba, onani Galamukani! ya June 2009, masamba 3-9.

[Chithunzi pamasamba 26, 27]

KODI MUKUDZIWA?

● Mboni za Yehova zatulutsa ma DVD m’zinenero zamanja zosiyanasiyana zokwana 43. Mukhoza kupeza zinthu zothandiza anthu osamva pa intaneti pa adiresi iyi: www.ps8318.com.

● Pofuna kuthandiza anthu ambiri osamva, Mboni za Yehova zili ndi magulu 59 padziko lonse amene akumasulira mabuku m’zinenero zamanja zosiyanasiyana.

● Padziko lonse, pali mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 1,200 ya zinenero zamanja.

[Chithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

www.ps8318.com.