Ndikungoona Kuchedwa Kuti Ndidzawauze Kuti, “Tonse Tilipo”
Ndikungoona Kuchedwa Kuti Ndidzawauze Kuti, “Tonse Tilipo”
Yosimbidwa ndi Abigail Austin
Tsiku lina mu April 1995, anthu a mu mpingo wathu wa Mboni za Yehova ananyamuka pa magalimoto osiyanasiyana kuti akasangalale kumalo enaake okongola m’dera lakumudzi, ku England konkuno. Ineyo, mkulu wanga Sarah, mnzathu wina dzina lake Deborah ndiponso mayi ndi bambo anga tinakwera galimoto imodzi. Koma mwadzidzidzi galimoto ina yomwe inkathamanga kwambiri inasiya msewu n’kudzatiwomba. Anthu onse amene anali m’galimoto yathu anafera pomwepo kupatulapo ineyo. Pa nthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 9.
ANANDITENGERA kuchipatala ndili chikomokere ndipo ndinadzidzimuka patapita milungu iwiri. Ndinavulala kwambiri m’mutu moti madokotala anachita kumangirira mutu wanga ndi zitsulo kuti ugwirane. Komabe, ndinachira pasanapite nthawi yaitali. Kenako achibale anga anandiuza zimene zinachitika, koma sindinakhulupirire. Ndinkaganiza kuti makolo anga ndi mkulu wanga ankabwera kuchipatalako kudzandiona ndipo amandipeza nditagona. Koma nditatuluka m’chipatala n’kubwerera kunyumba, ndinazindikira kuti iwo kulibedi. Ndinali ndi chisoni chachikulu kwambiri.
Kodi n’chiyani chinandithandiza kuti ndipirire mavuto amenewa?
Makolo Anga Anandisiyira Chuma Chauzimu
M’banja mwathu tinalipo ana asanu ndipo ineyo ndinali womaliza. Pa nthawi ya ngoziyi Sarah anali ndi zaka 22, mchimwene wanga Shane anali ndi zaka 20, mkulu wanga Jessica anali ndi zaka 17 ndipo mchimwene wanga Luke anali ndi zaka 15. Makolo athu anali abwino kwambiri. Bambo anga, a Steve, anali mkulu mu mpingo wa Mboni za Yehova wa West Yorkshire ku Shipley, ndipo anthu ambiri ankawakonda chifukwa anali munthu womvetsera mwatcheru komanso wokonda kuthandiza anthu. Mayi anga, a Carol, ankakondedwanso ndi anthu ambiri. Ankasamalira anthu okalamba a mu mpingo mwathu ngati mmene munthu angasamalilire makolo ake. Ankaitana ana ena kuti adzacheze kunyumba kwathu n’cholinga choti ifeyo tipeze anzathu abwino. Panyumba pathu tinkalandira alendo osiyanasiyana. Makolo athu anatiphunzitsanso kukhala okoma mtima ndi oganizira anthu ena, kuphatikizapo amene tinayandikana nawo nyumba.
Lachitatu lililonse madzulo, banja lathu linkaphunzira Baibulo pamodzi. Nthawi zina tinkachita masewero a nkhani za m’Baibulo ndipo tinkavala ngati mmene anthu ankavalira kalelo. Mayi ndi bambo athu anatiphunzitsa kuyambira tili aang’ono kukonzekera misonkhano ya mpingo, komanso kulalikira uthenga wa m’Baibulo kunyumba ndi nyumba. Ngakhale kuti anali ndi ntchito yaikulu yosamalira ana asanu, makolo athu ankayesetsa kupeza nthawi yocheza nafe ndipo anatithandiza kuti tikhale olimba mwauzimu.
Sarah, Shane ndi Jessica atamaliza sukulu, anayamba upainiya, kutanthauza kuti anakhala alaliki a nthawi zonse. Nayenso mnzathu Deborah anayamba upainiya. Ine ndi Sarah tinkagwirizana kwambiri moti ankangokhala ngati mayi wanga. Ndikatsekera sukulu, tinkagwira limodzi ntchito yophunzitsa anthu Baibulo. Tinkasangalala kwambiri masiku amenewo. Ndinkaona kuti apainiyawo anali osangalala ndipo ndinkakonda kwambiri kucheza nawo. Nanenso cholinga changa chinali chakuti ndikamaliza sukulu ndiyambe upainiya ndipo ndizilalikira pamodzi ndi Sarah.
Pa nthawi ya tchuthi, nthawi zambiri banja lathu linkapita kokasangalala limodzi ndi anthu ena a mu mpingo mwathu. Zimenezi zinkathandiza kuti achinyamata komanso achikulire azigwirizana ndi kukondana kwambiri. Koma pa nthawiyo sindinkadziwa kuti mabwenzi amenewa adzandithandiza ndiponso kunditonthoza kwambiri m’tsogolo.
Pambuyo pa Ngozi
Nditatuluka m’chipatala, ndinabwerera kunyumba. Shane ndi Jessica ankayesetsa kugwira maganyu kuti apeze ndalama zosamalira tonsefe, kwinaku akuchita utumiki wa nthawi zonse.
Anthu ambiri a mu mpingo mwathu anatithandizanso kwambiri. Ankatibweretsera zakudya, kutikonzera m’nyumba, kukatigulira zinthu zosiyanasiyana ndi kutichapira zovala, mpaka pamene tinafika poti tingathe kuima patokha. Tinkayamikira kwambiri thandizo lawo. Anzathu a Mboni za Yehova ambirimbiri m’mayiko ena komanso m’dziko lathu ankatitumizira mphatso ndi makadi otilimbikitsa. Zimenezi zinatisonyeza kuti gulu la Yehova ndi lachikondi kwambiri.
Patapita chaka chimodzi, azichimwene anga ndi mkulu wanga anaona kuti si bwino kuti ndikulire m’banja la ana okhaokha. Mabanja ambiri a mu mpingo mwathu anadzipereka kuti akhoza kunditenga kuti ndizikakhala nawo. Choncho, abale anga anakhala pansi n’kuganizira zimene mayi ndi bambo athu akanaona kuti ndi zabwino kwa ine, komanso zimene zikanandithandiza mwauzimu. Tinasankha banja la a Billy ndi akazi awo a Dawn, omwe anali ndi mwana mmodzi wamkazi wa zaka zisanu, dzina lake Lois. A Billy anali mkulu mu mpingo ndipo banja lawo linkagwirizana kwambiri ndi banja lathu. A Billy ndi akazi awo anandilandira bwino kwambiri ndipo kuyambira nthawi imeneyo akhala akundisamalira mwachikondi ngati kuti ndine mwana wawo weniweni. Ngakhale kuti makolowo ankafunika kusamalira ineyo komanso mwana wawo, Lois sanandichitirepo nsanje ndipo timagwirizana kwambiri ngati kuti ndi mchemwali wanga weniweni.
Zimene Zandithandiza Kupirira
Poyamba, ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani banja lathu lakumana ndi mavuto amenewa?’ Ndinkadzifunsa funso limeneli makamaka poganizira kuti makolo anga, komanso Sarah ndi Deborah, ankakonda kwambiri Yehova ndiponso anthu ena. Koma kenako ndinakumbukira nkhani ya m’Baibulo ya Yobu, amene anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ana ake atafa. (Yobu 1:19, 22) Mumtima mwanga ndinkati, ‘Satana ndi amene anachititsa kuti anthu azivutika komanso kufa, choncho iye angasangalale ngati ngoziyi itatisiyitsa kutumikira Mulungu.’ (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Ndinkaganiziranso mfundo yakuti Yehova ndi wachikondi ndipo watilonjeza kuti akufa adzauka. (Yohane 5:28, 29) Chifukwa cha lonjezo limeneli, ndikuyembekezera kudzakumananso ndi makolo anga, mkulu wanga komanso Deborah, m’dziko latsopano la paradaiso. Choncho, ndinganene kuti ngoziyi yandithandiza kuti ndizikonda kwambiri Yehova.
Ndikapezana ndi anthu amene akumana ndi mavuto aakulu monga imfa, ndimamva chisoni ngati anthuwo sakudziwa lonjezo labwino kwambiri la Baibulo lakuti akufa adzauka. Ndimafunitsitsa kuuza anthu amenewa za chiyembekezo chimene tili nacho. Ndimaona kuti ifeyo tinakwanitsa kupirira mavuto aakuluwa chifukwa cha Yehova, amene kudzera m’gulu lake, anatithandiza kukhala ndi chiyembekezo.
Mwina zimene zinatichitikirazi zathandizanso anthu ena, ndipo zachititsa makolo ena kudzifunsa kuti, ‘Kodi ana athu tawaphunzitsa mokwanira zinthu zauzimu moti chinachake chitatichitikira akhoza kupitiriza okha kutumikira Yehova?’
Ndakhala ndikuyesetsa kuchita zinthu pa moyo wanga ngati kuti mayi ndi bambo anga alipobe. Ndikudziwa kuti iwo akanafuna kuti ndizichita khama pothandiza anthu ena ngati mmene iwo ankachitira. Ndakhala ndikuchita upainiya kuyambira pamene ndinamaliza sukulu ndipo Lois nayenso akuchita upainiya. Panopa azichimwene anga ndi mkulu wanga anapeza mabanja ndipo akutumikira Yehova mosangalala m’mipingo imene ali.
Ndikulakalaka kuti dziko latsopano limene Mulungu walonjeza lifike mofulumira ndipo ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene anthu adzaukitsidwe. Pa nthawi imeneyo sikudzakhalanso zopweteka kapena imfa. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndimalimba mtima ndikaganizira kuti ndidzaonananso ndi anthu amene anamwalirawo. Ndikungoona kuchedwa kuti ndidzakumbatirane ndi mayi anga, bambo anga, Sarah ndiponso Deborah n’kuwauza kuti, “Tonse tilipo.”
[Chithunzi patsamba 23]
Chithunzi chaposachedwapa cha Abigail (wachiwiri kuchokera kumanzere), pamodzi ndi banja limene lamulera