Zimene Mungachite Kuti Musamasungulumwe Kwambiri
Zimene Mungachite Kuti Musamasungulumwe Kwambiri
NGATI nthawi zambiri mumakhala osungulumwa, mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi pali zinthu zimene ndingachite kuti ndisamasungulumwe kwambiri? Kodi ndikufunika kusintha zinthu zina pa moyo wanga? Ngati ndi choncho, kodi ndingasinthe chiyani?’ Mafunso otsatirawa akhoza kukuthandizani kudziunika bwinobwino n’kupeza njira zomwe zingakuthandizeni kuti musamasungulumwe kwambiri.
Kodi Ndikufunika Kusintha Mmene Ndimaonera Zinthu?
Aliyense amasungulumwa, koma ngati nthawi zonse mumakhala osungulumwa ndiye kuti pali vuto. Nthawi zambiri vutolo limakhudza mmene mumaonera zinthu. Mwina vuto lagona pa zimene mumachita mukakhala ndi anthu ena. Anthu ena amakhala ngati adzimangira mpanda umene umalepheretsa ena kucheza nawo. Kuti vutoli lithe, nthawi zambiri mungangofunika kusintha mmene mumaonera zinthu.
Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Sabine atasamukira ku England, anati: “Zinanditengera nthawi yaitali kuti anzanga atsopano ayambe kundikhulupirira. Choncho sindinkamasukirana nawo ndipo ndikakhala nawo ndinkachita zinthu mokayikira. Ndinazindikira kuti kufunsa anzako kuti akufotokozere mmene anakulira n’kothandiza kwambiri. Munthu wina anandiuza kuti: ‘Palibe chikhalidwe chapamwamba kwambiri kuposa china. Chofunika n’kungophunzira zimene anthu azikhalidwe zosiyanasiyana amakonda.’” Choncho, monga mmene Sabine anauzidwira, tifunika kufufuza zinthu zabwino zimene anthu azikhalidwe zina amachita, n’kutengera zimenezo.
Kodi Sindikonda Kukhala Ndi Anthu Ena?
Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi sindikonda kukhala ndi anthu ena? Kodi mwina anthu
samasuka nane chifukwa chakuti inenso sindimasuka nawo?’ Ngati zili choncho, muziyesetsa kumasukirana ndi anthu. Mayi wina wa zaka 30 dzina lake Roselise, yemwe anasamukira ku England kuchokera ku Guadeloupe, anati: “Nthawi zambiri anthu amene amasungulumwa amakonda kudzipatula.” Choncho iye anapereka malangizo akuti: “Muzifufuza anthu amene akuoneka kuti nawonso ndi osungulumwa. Muziyamba ndi inuyo kulankhula nawo. Nthawi zina kungofunsa funso limodzi lokha kungathandize kuti muyambe kucheza ndi munthu amene angadzakhale mnzanu wapamtima mpaka kalekale.”Koma kuti munthu apeze mnzake wapamtima, pamafunika nthawi ndiponso khama. Choyamba, mufunika kuphunzira kumvetsera anthu ena akamalankhula. Kumvetsera mwatcheru kungakuthandizeni kuti muthe kukamba nkhani zimene munthu winayo angasangalale nazo. Kumbukirani kuti kuganizira ena kumathandiza kuti mupange ubwenzi wolimba.
Kodi Ndimadziona Bwanji?
Kudziona kuti ndinu munthu wosafunika kungakulepheretseni kucheza ndi anthu ena. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nthawi zambiri ndimadziona kuti ndine munthu wosafunika?’ Abigaïl, yemwe ali ndi zaka 15 ndipo anachokera ku Ghana, anati: “Nthawi zina ndinkadziona molakwika ndipo zimenezi zinkachititsa kuti ndizisungulumwa. Ndinkaona kuti ndine wachabechabe komanso anthu sandikonda.” Dziwani kuti ngati mutayamba ndi inuyo kucheza ndi ena komanso kuwathandiza, enawo sangaone kuti ndinu munthu wosafunika. Ndipo mwa njira imeneyi iwo akhoza kukhala anzanu apamtima. Choncho, bwanji osayamba ndi inuyo kucheza nawo?
Kudziona moyenerera kukhoza kukuthandizaninso kupeza anzanu amisinkhu yosiyanasiyana. Kucheza ndi munthu wamkulu kapena wamng’ono kwa inu kukhoza kukuthandizani. Kucheza ndi anthu achikulire kunamuthandiza kwambiri Abigaïl kuti asamasungulumwe. Iye anati: “Anthu achikulirewo anandithandiza kwambiri chifukwa akumana ndi zambiri pa moyo wawo.”
Kodi Ndimadzipatula?
Anthu ambiri omwe ali osungulumwa, amakhala nthawi yaitali akuonera TV, kuchita masewera apakompyuta, kapena kuchita zinthu zina pa kompyuta ali okhaokha. Koma amati akamaliza kuchita zimenezi amakhalabe osungulumwa. Mtsikana wina wazaka 21 wa ku Paris, dzina lake Elsa, anati: “TV ndiponso masewera apakompyuta zikhoza kukhala ngati mankhwala amene amachititsa munthu kuti afike poti asamafunenso kucheza ndi anthu ena.”
Koma kuipa koonera TV n’koti poonerapo munthu salankhula, kufotokoza maganizo ake kapena
kudziwana ndi munthu wina. N’chimodzimodzinso ndi masewera apakompyuta. Zimene zimachitika m’masewera amenewa zimakhala zosiyana ndi zimene zimachitikadi pa moyo wa tsiku ndi tsiku. Choncho munthu akamaliza kuchita masewerawa, amayambiranso kumva ngati mmene amamvera poyamba. Kugwiritsa ntchito Intaneti mwachisawawa popanda chinthu chenicheni chimene mukufufuza, kungakuiwalitseniko mavuto anu kwakanthawi. Koma pa nthawi imene muli pa Intanetiyo mukhozanso kuona zinthu zachiwerewere kapena kulankhulana ndi anthu amene amabisa umunthu wawo. Choncho, Intaneti singakuthandizeni kupeza anzanu abwino.Kodi Vuto Langa Lingathe Nditakwatira?
Anthu ena amafuna kukwatira poganiza kuti akatero asiya kukhala osungulumwa. N’zoona kuti ngati mutapeza mwamuna kapena mkazi wabwino, moyo wanu ukhoza kukhala wosangalala kwambiri. Koma samalani kuti musathamangire kukwatira chifukwa ukwati si nkhani yamasewera.
Dziwaninso kuti ngakhale mutakwatira, mukhoza kupitirizabe kukhala osungulumwa. Anthu okwatirana omwe salankhulana bwino, akuti ndi amene “amakhala osungulumwa kwambiri pa anthu onse.” Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu amene amakhala osungulumwa ali m’banja ndi ambiri. Choncho ngati mukuganiza zodzakwatira m’tsogolomu, ndi bwino kuthetseratu vuto lanu losungulumwa musanayambe chibwenzi ndi munthu wina. Mukasintha mmene mumaonera zinthu komanso mukasintha mmene mumachitira zinthu zina pa moyo wanu, n’kuyamba kucheza ndi anthu osiyanasiyana mudakali nokha, m’tsogolo mukhoza kudzakhala ndi banja losangalala.
Mukhoza Kuchepetsa Kusungulumwa
Mwina kusungulumwa kwanu sikungatheretu panopa. Koma kutsatira malangizo amene Yesu ananena pa Mateyo 7:12 kungakuthandizeni kuti musakhale wosungulumwa kwambiri. Lembali limati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” Choncho ngati mukufuna kuti anthu azikumasukirani, inunso muziwamasukira. Komanso ngati mukufuna kuti anthu azicheza nanu, inunso muzicheza nawo. Komabe ngakhale mutayesetsa, ena sangakumasukireni nthawi yomweyo, koma pakapita nthawi ena mwa iwo angayambe kukumasukirani. Ngakhale atapanda kutero, mudzakhalabe osangalala chifukwa munayesetsa kuti akhale anzanu.
Machitidwe 20:35) Potsatira mfundo imeneyi, mwina mukhoza kuthandiza mwana winawake kuti alembe ntchito yake yakusukulu, kapena kuthandiza munthu wachikulire pokamugulira zinthu, ndiponso kumukonzera m’nyumba ndi panja. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti mukhale osangalala ndipo mwina anthuwo akhoza kukhala anzanu apamtima.
Yesu anatchulanso mfundo ina yofunika kwambiri imene ingakuthandizeni. Iye anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (N’zotheka Kupeza Mabwenzi Abwino Kwambiri
Pali zinthu zambiri zimene mungachite kuti musamakhale osungulumwa. M’malo mongodzitsekera m’nyumba, mungathe kupita kokayenda, mwina kumalo enaake okongola. Ngati muli nokha panyumba, pezani zochita monga kusoka, kugwira ntchito zina ndi zina zapakhomo, kukonza zinthu zowonongeka, kapena kuwerenga. Munthu wina analemba kuti: “Kaya ndikhale ndi nkhawa yaikulu bwanji, ndikangowerenga buku kwa ola limodzi, nkhawa yonseyo imatheratu.” Ambiri amamva bwino kwambiri akawerenga Baibulo, makamaka buku la Masalmo.
Akatswiri ena akuti munthu akamacheza ndi anthu achipembedzo chake, zimamuthandiza kuti asakhale wosungulumwa komanso zingamuthandize kuti asamadwaledwale. Kodi tingawapeze kuti anthu amene amayesetsa kutsatira malangizo a Yesu oti tizichitira ena zomwe timafuna kuti iwo atichitire? Munthu wina yemwe si wa Mboni za Yehova analemba m’buku linalake lonena za zipembedzo, kuti: “Mboni za Yehova zimagwirizana kwambiri komanso zimakhulupirirana ndi kulemekezana m’mipingo yawo.”
Yesu anatchula chizindikiro chachikulu cha Akhristu oona, pamene ananena kuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Chikondi chimenechi n’chimene chimadziwikitsa anthu amene ali m’chipembedzo choona. Iwo amakonda Mulungu komanso amakondana okhaokha.—Mateyo 22:37-39.
Kukhala bwenzi la Mulungu ndiye njira yabwino kwambiri yothandiza kuti munthu asakhale wosungulumwa kwambiri. Choncho, ngati muli pa ubwenzi ndi Mulungu, iye sadzakusiyani kuti muzisungulumwa.—Aroma 8:38, 39; Aheberi 13:5, 6.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]
ZIMENE ANTHU OSIYANASIYANA AMACHITA KUTI ASAMASUNGULUMWE KWAMBIRI
Anny, mkazi wamasiye, anati: “Ndimayesetsa kuti ndisamaganize kwambiri, komanso kuti ndisamangokhalira kudandaula ndi mmene zinthu zilili panopa.”
Carmen, mtsikana wosakwatiwa, anati: “Ndaphunzira kuti si bwino kumangoganizira zakale. Zinthu zikachitika, ndi bwino kuziiwala n’kudziwana ndi anthu ena atsopano.”
Fernande, mkazi wamasiye, anati: “Mukamayesetsa kuthandiza ena, mumaiwala mavuto anu.”
Jean-Pierre, mwamuna wosakwatira, anati: “Nthawi zambiri ndimakonda kuyenda ulendo wautali wapansi, ndipo nthawi imeneyi ndimapemphera kwa Mulungu n’kumuuza zonse zakukhosi kwanga.”
Bernard, mwamuna wamasiye, anati: “Ndimakonda kulankhulana ndi anzanga pa foni, osati n’cholinga choti tizikumbutsana nkhani zomvetsa chisoni, koma kuti ticheze basi.”
David, mwamuna wosakwatira, anati: “Ngakhale kuti mwachibadwa ndimakonda kukhala ndekha, ndimayesetsa kucheza ndi anthu.”
Lorenna, mtsikana wosakwatiwa, anati: “Ndimayamba ndi ineyo kupita pamene pali anthu n’kukacheza nawo.”
Abigaïl, mtsikana wa zaka 15, anati: “Ndimakonda kucheza ndi anthu achikulire chifukwa ndimaphunzira zambiri.”
Cherry, mtsikana wosakwatiwa, anati: “Ndaona kuti ukawauza anthu kuti ukusungulumwa, amayesetsa kucheza nawe.”
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUSAMASUNGULUMWE
● Musamadzione kuti ndinu munthu wosafunika
● Mukafuna kusangalala musamakonde kuchita zinthu nokhanokha, monga kuonera TV muli nokha
● Muzicheza ndi anthu amene amakonda zinthu zofanana ndi zimene inuyo mumakonda, ngakhale ngati si amsinkhu wanu
● Koposa zonse, yesetsani kukhala bwenzi la Mulungu
[Chithunzi patsamba 7]
Muzicheza ndi anthu osiyanasiyana ngakhale amene si amsinkhu wanu