Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
Anthu ena ochita kafukufuku anapeza kuti ku Brazil mwamuna mmodzi pa amuna 10 alionse a zaka zapakati pa 15 ndi 64 anagonanapo ndi munthu mmodzi kapena angapo amene anadziwana nawo kudzera pa Intaneti m’miyezi 12 yapitayo.—BRAZILIAN MINISTRY OF HEALTH.
Kwa nthawi yaitali, pamwamba pa madzi a m’nyanja ya Arctic pakhala pali madzi oundana ochuluka kwambiri, mpaka kufika mamita 80 kuchokera pamwamba kupita pansi. Koma tsopano “madziwa, amene anatenga zaka zambiri kuti aundane, angotsala pang’ono kusungunukiratu. Zimenezi zadabwitsa anthu ambiri, koma zithandiza kuti sitima zapamadzi zizitha kukafika kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi.”—REUTERS NEWS SERVICE, CANADA.
Dziko la Russia ndiponso likulu la tchalitchi cha Katolika ku Vatican, akhazikitsa ubale waukazembe.—RIA NOVOSTI, RUSSIA.
Kuyambira chaka cha 2000 mpaka chaka cha 2007, madzi ambiri oundana (26 peresenti) amene anali paphiri la Kilimanjalo, lomwe ndi phiri lalitali kwambiri mu Africa monse, anasungunuka.—DAILY NATION, KENYA.
Ku Britain Kuli Anthu Ambiri Osakonda Kucheza ndi Anthu Komanso Osasangalala
Ochita kafukufuku anapeza kuti ku Britain n’kumene kuli “anthu ambiri padziko lonse osakonda kucheza ndi anthu,” inatero nyuzipepala ya ku London ya Daily Telegraph. Pa kafukufuku wina anapeza kuti anthu a ku Britain ndi amenenso amadwala kwambiri matenda ovutika maganizo komanso amakhala ndi nkhawa kwambiri kuposa anthu a mayiko ena. Akatswiri ena akuganiza kuti moyo wosaganizira ena ndi umene ukuchititsa kuti anthuwa azidwala matenda ovutika maganizo. Ochita kafukufukuwo anayerekezera moyo wa anthu okhala m’mayiko a azungu ndi moyo wa anthu a ku China ndi ku Taiwan. M’mayiko ngati China ndi Taiwan, anthu amalimbikitsidwa kwambiri kuti azikhala bwino ndi anthu ena m’malo mongoganizira zofuna zawo, ndipo zimenezi zimawathandiza kuti asamadwale matenda ovutika maganizo. Nyuzipepala ya Telegraph inanenanso kuti m’mayiko a azungu, “moyo wodzikonda ukuchititsa kuti anthu azidwala matenda ovutika maganizo.”
Ku Sweden Amuna Kapena Akazi Okhaokha Akumakwatirana M’tchalitchi
Mu October 2009, tchalitchi cha Lutheran cha ku Sweden chinavomereza kuti amuna kapena akazi okhaokha azikwatirana m’tchalitchi. Tchalitchichi chinachita izi patangodutsa miyezi yochepa kuchokera pamene nyumba ya malamulo ya m’dzikolo inakhazikitsa lamulo lololeza kuti amuna kapena akazi okhaokha akhoza kumakwatirana. “Zimenezi zikutanthauza kuti tchalitchi cha ku Sweden ndi choyamba pa matchalitchi akuluakulu a padziko lonse kusiya kukhulupirira kuti ukwati uyenera kuchitika pakati pa mwamuna ndi mkazi basi,” inatero nyuzipepala ina ya ku Sweden ya Dagens Nyheter.
Kodi Ana Amalira M’chilankhulo Chanji?
Anthu ena ochita kafukufuku pa yunivesite ya Würzburg ku Germany anapeza kuti ana amalira motsatira chilankhulo cha makolo awo kuyambira ali aang’ono kwambiri, mwina atangotha masiku awiri. Ochita kafukufukuwo anajambula kalilidwe ka ana 30 a ku France ndi ana enanso 30 a ku Germany, ndipo kenako anamvetsera kalilidwe kawo. Iwo anapeza kuti ana a ku France akamalira amayamba motsitsa kenako n’kumakweza, pamene ana a ku Germany amayamba mokweza kenako n’kumatsitsa. Anapezanso kuti kalilidwe ka anaka kanali kofanana ndi mmene makolo awo amalankhulira. Chotero anthu akuganiza kuti mwana amayamba kuphunzira chinenero adakali m’mimba ndipo akamalira amakhala atayamba kale kutengera chinenero cha makolo ake.