Zimene Anthu Amaganiza Zokhudza Kutha kwa Dziko
KODI mumachita mantha mukaganizira za m’tsogolo? Dziwani kuti pali anthu ambiri amene amachitanso mantha ndi zimenezi. Kuyambira kale, anthu akhala akunena zinthu zosiyanasiyana zokhudza zimene zidzachitike m’tsogolo, ndipo ena amaganiza kuti anthu adzakumana ndi zoopsa. Komanso kwa zaka zambiri anthu akhala akuchita chidwi ndi nkhani zokhudza kutha kwa dziko.
Mwachitsanzo, anthu akhala akulemba mabuku, kujambula makatuni, kupanga mafilimu ndi mapulogalamu a pa TV osonyeza kuti nthawi ina maloboti, zinyama zoopsa, mizukwa, njoka zikuluzikulu, anyani, mbalame, makoswe ndi mavu akuluakulu zidzapha anthu onse padzikoli. Koma n’zovuta kuti munthu akhulupirire kuti zimenezi zingadzachitikedi.
Komabe pali nkhani zina zokhudza kutha kwa dziko zimene anthu amachita nazo mantha kwambiri. Mwachitsanzo, asayansi ena amanena kuti dzikoli lidzagwedezeka kwambiri zimene zidzachititse kuti pachitike tsunami, zivomezi komanso kuti mapiri aphulike. Asayansi ena amati mapulaneti onse adzaima pamzera umodzi zomwe zidzachititse kuti chimphepo chotentha chochokera kudzuwa chiwononge dziko lapansili. Ena amanena kuti pulaneti lathuli lidzasuntha mwadzidzidzi zomwe zidzachititse kuti anthu onse afe chifukwa cha kutentha kwa dzuwa. Koma palibe chifukwa chochitira mantha chifukwa zimenezi sizidzachitika. Komabe anthu ambiri amachita chidwi ndi nkhani ngati zimenezi.
Intaneti komanso mabuku ena akusonyeza kuti dziko litha pa December 21
chaka chino. Mwachitsanzo, amanena kuti pulaneti linalake lotchedwa Nibiru (kapena Pulaneti X) lidzawombana ndi dziko lapansi mu December chaka chino. Anthu ambiri anayamba kukhulupirira zimenezi potengera kalendala yakale ya anthu amtundu wa Maya, yomwe ena amakhulupirira kuti imasonyeza kuti dziko litha cha mu December 2012.Chifukwa chokhulupirira zimenezi, anthu ena amanga malo pafupi ndi nyumba zawo ndipo ena awononga ndalama zambiri kumanga nyumba za pansi pa nthaka zoti adzabisalemo dziko likamadzatha. Enanso asamukira kumapiri kopanda madzi ndi magetsi, n’cholinga choti azolowere moyo wovutika kuti dziko likamadzatha asadzaone zachilendo.
Koma pali anthu ena amene sakhulupirira kuti dziko lidzatha. Mwachitsanzo, asayansi a bungwe la NASA, ananena kuti: “Palibe choopsa chilichonse chimene chichitikire dziko lapansi mu 2012. Pulaneti lathuli latha zaka zoposa 4 biliyoni lilipo, ndipo wasayansi aliyense wanzeru amadziwa kuti dziko silitha mu 2012.”
Komabe si nzeru kuganiza kuti palibe choopsa chilichonse chimene chidzachitikire anthu kutsogoloku ndiponso kuganiza kuti ndi anthu otengeka okha amene amakhulupirira kuti dziko lidzatha. Koma kodi dziko lidzathadi? Ngati lidzathe, lidzatha liti komanso lidzatha bwanji?