Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | MASSIMO TISTARELLI

Katswiri Wopanga Maloboti Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Katswiri Wopanga Maloboti Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Pulofesa Massimo Tistarelli ndi katswiri wasayansi wa pa yunivesite ya Sassari ku Italy. Iye ndi mmodzi mwa anthu amene amalemba nkhani m’magazini ina yasayansi ndipo walemba nawonso nkhani zoposa 100 zokhudza sayansi. Iye amafufuza zimene zimathandiza kuti anthufe tizitha kuzindikira nkhope za anthu ena komanso zomwe zimatithandiza kupanga zinthu ngati kuwakha mpira. Kenako amagwiritsa ntchito zimene wapezazo popanga maso a maloboti ogwira ntchito ngati anthu. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe za chikhulupiriro chake komanso za ntchito yake yasayansi.

Poyamba munali m’chipembedzo chiti?

Makolo anga anali Akatolika koma sankapita kutchalitchi. Ndili wamng’ono ndinayamba kukhulupirira kuti kulibe Mulungu. Ndinaphunzira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina ndipo ndinkaona kuti zimenezo ndi zoona. Komabe ngakhale kuti sindinkakhulupirira kuti kuli Mlengi, ndinkaona kuti payenera kukhala winawake amene ndi wamphamvu kuposa anthufe. Choncho kuti ndidziwe zoona zake, ndinayamba kufufuza m’zipembedzo za Chibuda, Chihindu ndi Chitao koma zimene ankaphunzitsa sizinkandigwira mtima.

N’chifukwa chiyani munayamba kukonda za sayansi?

Kuyambira ndili mwana ndinkachita chidwi kwambiri ndi makina osiyanasiyana. Nthawi zina ndinkaphwasula zidole zanga zoyendera magetsi, n’kuzilumikizanso. Komanso bambo anga ankagwira ntchito yokonza makina pakampani ya matelefoni. Choncho nthawi zambiri ndinkawapanikiza kwambiri ndi mafunso kuti andiuze mmene mawailesi komanso matelefoni amagwirira ntchito.

Ndiye munaphunzira zotani?

Ndinaphunzira luso lopanga zipangizo zamagetsi pa yunivesite ya Genoa, kenako ndinapeza digirii ya kapangidwe ka maloboti kapena kuti zipangizo zotha kugwira ntchito ngati anthu. Ndinaphunzira za mmene maso a munthu amagwirira ntchito komanso mmene tingapangire maloboti otha kuona ngati mmene munthu amachitira.

N’chifukwa chiyani munachita chidwi ndi kufufuza mmene maso athu amagwirira ntchito?

N’zovuta kumvetsa mmene maso athu amaonera zinthu. Mwachitsanzo,  taganizirani zimene zimachitika munthu wina akakuponyerani mpira. Mukamauthamangira, maso anu amatha kuona mwaluso kwambiri pamalo penipeni pomwe mpirawo uli musanaugwire. Maso anu amatha kusungabe chithunzi champirawo ngakhale mutayang’ana kumbali komanso ngakhale mpirawo utasuntha. Zimenezi zimathandiza kuti muuwakhe.

Zimenezi zikamachitika, maso amatha kudziwa mmene mpirawo ukuthamangira komanso kumene ukulowera. Ndipo chochititsa chidwi n’chakuti maso amatha kudziwa mmene mpira ukuthamangira poona kumene ukulowera. Minyewa ya maso imatumiza chithunzicho kuubongo womwe umakudziwitsani mmene mungatambasulire manja anu kuti muuwakhe. Zimenezi n’zovuta kumvetsa komanso zochititsa chidwi kwambiri.

N’chiyani chinakuthandizani kuti muyambe kukhulupirira kuti kuli Mlengi?

Mu 1990 ndinapita mu mzinda wa Dublin, ku Ireland kukachita maphunziro enaake pa yunivesite ya Trinity. Pa ulendo wanga wobwerera, ndili ndi mkazi wanga Barbara, tinayamba kukambirana za tsogolo la ana athu. Tinagwirizananso zoti tikacheze kwa mchemwali wanga yemwe anali wa Mboni za Yehova. Mchemwali wangayu anandipatsa buku lachingelezi lakuti, Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? lomwe ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndinagoma kwambiri ndi mmene analembera bukuli chifukwa zikuonetsa kuti anafufuza kwambiri. Pamenepa m’pamene ndinazindikira kuti zomwe ndinkakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, zinali zabodza ndipo ndinkangozikhulupirira ndisanafufuze. Mwachitsanzo, ndinkakhulupirira kuti zinthu zakale kwambiri zokwiririka pansi pa nthaka, zimene akatswiri anapeza, zimagwirizana ndi chiphunzitso chimenechi. Koma ndinazindikira kuti zimenezi sizoona. Nditayamba kufufuza bwinobwino za chiphunzitso chimenechi, ndinazindikira kuti anthu amene amakhulupirira zimenezi amangokakamira zinthu zimene sizolondola.

Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi tikamapanga maloboti, timatengera nzeru za ndani?’

Kenako ndinayamba kuganizira za ntchito yanga yopanga maloboti. Ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi tikamapanga maloboti, timatengera nzeru za ndani?’ Komanso ndinazindikira kuti sindingathe kupanga loboti yotha kugwira mpira ndendende ngati mmene anthufe timachitira. Mwachitsanzo, kuti loboti igwire mpira imafunika kuitchera mwanjira inayake. Ngakhale kuti loboti imatha kuchita zinthu zochepa ngati zimenezi, anthu savutika kuvomereza kuti pali winawake amene anaipanga. Anthufe timatha kuphunzira zinthu zovuta kwambiri kuposa mmene maloboti amachitira. Chimenechi ndi chifukwa chimodzi chomwe chinandichititsa kuti ndiyambe kukhulupirira kuti pali winawake amene anatilenga.

N’chifukwa chiyani munakhala wa Mboni za Yehova?

Chifukwa chimodzi n’choti ineyo ndi mkazi wanga Barbara, tinachita chidwi ndi mmene a Mboni za Yehova amafufuzira zinthu. Ineyo ndinachita chidwi ndi mmene amafufuzira asanalembe mabuku awo. Anthu ngati ineyo timakonda kuwerenga kwambiri zinthu zimene tikuona kuti zafufuzidwa bwino. Mwachitsanzo, ndinachita chidwi kwambiri ndi maulosi ambirimbiri a m’Baibulo. Kuphunzira maulosiwo kunandithandiza kudziwa kuti Baibulo ndi lochokeradi kwa Mulungu. Mu 1992 ineyo ndi mkazi wanga tinabatizidwa, n’kukhala a Mboni za Yehova.

Kodi ntchito yanu siisokoneza chikhulupiriro chanu?

Ayi, ngakhale pang’ono. Sayansi yalimbitsa kwambiri chikhulupiriro changa. Ndikaganizira mmene anthufe timazindikirira nkhope ya munthu wina, ndimagoma ndi amene anatilenga. Mwachitsanzo, mwana akangobadwa kumene amatha kuzindikira nkhope ya munthu. Anthu akuluakulu amatha kuzindikira nkhope ya munthu amene akumudziwa ngakhale munthuyo atakhala pachigulu. Tingathenso kudziwa mmene munthuyo akumvera pongoona mmene nkhope yake ikuonekera. Koma anthu ambiri sadziwa kuti diso komanso ubongo wathu umachita zinthu zambirimbiri pa nthawi yochepa kuti zimenezi zitheke.

Panopa sindikayikira kuti Yehova Mulungu ndi amene anatipatsa mphatso imeneyi. Anatipatsanso mphatso ina yomwe ndi Baibulo moti ineyo ndimauza ena za Yehova pofuna kumuyamikira chifukwa cha mphatso imeneyi. Ndimaona kuti Yehova ndi amene ayenera kulandira ulemerero chifukwa cha zimene analenga.