Zochitika Padzikoli
Israel
Lipoti la pa webusaiti ina linanena kuti “ana amene anabadwa ndi chilema chomwe madokotala akanatha kuchitulukira anawo asanabadwe,” sakuloledwanso kutengera kukhoti madokotalawo chifukwa cholola makolo awo kuwabereka m’malo mongochotsa mimbayo. Komabe makolo a anawo akhoza kupempha boma kuti liwapatse chipukutamisozi chowathandiza kusamalira ana awo kwa moyo wawo wonse.
Australia
Ku Australia, mabanja 8 pa 10 alionse anayamba kukhalira limodzi asanakwatirane.
Greece
Lipoti lina limene unduna wa zaumoyo wa ku Greece unatulutsa, linasonyeza kuti chiwerengero cha anthu amene anadzipha m’dzikolo chinawonjezeka ndi 40 peresenti kuyambira m’mwezi wa January mpaka May, 2011. Chiwerengero chimenechi n’chokwera poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu omwe anadzipha m’miyezi yomweyi, chaka cha 2010. Chiwerengerochi chinakwera kwambiri panthawi imenenso m’dzikolo munali mavuto azachuma.
United States
Nthambi yaboma yosamalira zachilengedwe ku United States inanena kuti 40 peresenti ya chakudya cha m’dzikolo chimawonongeka. Mwachitsanzo 7 peresenti ya chakudya chimangosiyidwa m’munda osakololedwa, 17 peresenti ya chakudya cha m’malesitanti chimatsala komanso 25 peresenti ya chakudya m’mabanja ambiri chimatayidwa.
Madagascar
Chaposachedwapa, anthu apeza mtundu winawake wa tianamzikambe tating’ono kwambiri ku Madagascar. Tianamzikambeti timakhala tatitali mainchesi 1.1, moti timakwana pachikhadabo cha munthu. Anthu ena akuona kuti tianamzikambe timeneti tili m’gulu la nyama zimene zatsala pang’ono kutheratu.