Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Indonesia

Dziko la Indonesia

DZIKO la Indonesia linapangidwa ndi zilumba zokwana 17,000. Anthu ake amadziwika kuti ndi okonda kulandira alendo, ochezeka, aulemu, komanso ofatsa.

Anthu a ku Indonesia amakonda kudya mpunga ndi ndiwo zothira zokometsera komanso amakonda zipatso. M’madera ena, anthu amadya atakhala pamphasa ndipo amadya ndi manja. Anthu ambiri a ku Indonesia amanena kuti chakudya chimakoma kwambiri akamadya ndi manja komanso atakhala pansi.

Ku Indonesia kumapezeka zipatso zotchedwa njale, ndipo anthu amazikonda kwambiri ngakhale kuti zimanunkha

Anthu a ku Indonesia amakonda zojambulajambula, kuvina komanso kuimba. Chipangizo chotchuka kwambiri ndi anklong, chomwe amachipanga pogwiritsa ntchito nsungwi zokhala ndi mphako. Nsungwizo amazimangirira kuchithabwa ndipo amazichuna kuti ziziimba mosiyanasiyana akamazigwedeza. Akafuna kuimba nyimbo, nthawi zambiri pamakhala anthu angapo ndipo aliyense amakhala ndi chipangizo chake chomwe amachigwedeza mogwirizana ndi anzakewo kuti nyimboyo imveke bwino.

Anyani otchedwa orangutan, omwe amapezeka kunkhalango ya Sumatra ndi Borneo, ndi mtundu wa nyama zazikulu kwambiri padziko lonse zomwe zimakhala m’mitengo. Nyani wamkulu amatha kulemera makilogalamu 90 ndipo amakhala ndi manja aatali pafupifupi mamita awiri ndi hafu

M’zaka za m’ma 1400 C.E., zipembedzo zotchuka kwambiri ku Indonesia zinali Chihindu ndi Chibuda. Koma pofika m’ma 1500, Chisilamu chinali chitafalikira m’madera ambiri. Kenako pasanapite nthawi, azungu anabwera kudzafunafuna  zokometsera ndiwo ndipo anayambitsa Chikhristu.

A Mboni za Yehova, omwe amadziwika ndi ntchito yophunzitsa Baibulo padziko lonse, akhala akugwira ntchito imeneyi ku Indonesia kuyambira mu 1931. Panopa m’dzikoli muli Mboni za Yehova zokwana 22,000, ndipo akuyesetsa kulalikira uthenga wabwino ngakhale kwa anthu ogontha. Mwachitsanzo, chaka chatha anthu oposa 500, anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Yesu womwe unachitika m’chinenero cha manja.

Magazini ya Galamukani! imafalitsidwa m’zinenero 98, kuphatikizapo Chiindonesia (chomwe chimatchedwanso Chiindonesia cha Chibahasa)