Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KUCHEZA NDI | FRÉDÉRIC DUMOULIN

Wochita Kafukufuku Wazamankhwala Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Wochita Kafukufuku Wazamankhwala Akufotokoza za Chikhulupiriro Chake

Frédéric Dumoulin wakhala akugwira ntchito m’dipatimenti yofufuza zamankhwala payunivesite ina ku Belgium kwa zaka zoposa 10. Poyamba iye sankakhulupirira kuti kuli Mulungu. Koma kenako anayamba kukhulupirira kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zamoyo. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza ndi Frédéric, yemwe pano ndi wa Mboni za Yehova, kuti adziwe za ntchito yake komanso chikhulupiriro chake.

Kodi munakulira m’banja lachipembedzo?

Ee. Mayi anga anali Mkatolika. Koma nditawerenga zokhudza zinthu zoipa zimene zipembedzo zinachita, monga nkhondo za pakati pa Akhristu ndi Asilamu, ndinayamba kudana ndi chipembedzo moti ndinalibenso nacho ntchito. Ndinawerenganso zokhudza zipembedzo zomwe si zachikhristu, ndipo ndinaona kuti nazonso zimachita zinthu zoipa. Ndili ndi zaka 14 ndinayamba kuganiza kuti zachinyengo zomwe zimachitika m’zipembedzo, ndi umboni woti kulibe Mulungu. Choncho kusukulu nditaphunzira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina, ndinayamba kuona kuti moyo unangoyamba wokha.

N’chiyani chinakuchititsani kuti muzikonda sayansi?

Ndili ndi zaka 7, munthu wina anandipatsa chipangizo choonera tizinthu ting’onoting’ono ndipo ndinkachikonda kwambiri. Ndinkagwiritsa ntchito chipangizochi kuonera mbali zing’onozing’ono za tizilombo touluka, monga agulugufe.

N’chiyani chinakupangitsani kukhala ndi chidwi chofuna kudziwa mmene moyo unayambira?

Ndili ndi zaka 22, ndinakumana ndi mayi wina wasayansi, yemwe anali wa Mboni za Yehova. Iye ankakhulupirira kuti Mulungu ndiye analenga zinthu zamoyo. Zimenezi zinali zachilendo kwambiri kwa ine. Ndinaganiza kuti ndingathe kumusonyeza kuti zimene amakhulupirirazo n’zabodza. Koma ndinadabwa kwambiri kuona kuti anayankha mafunso anga onse mogwira mtima. Ndinayamba kuchita chidwi ndi anthu amene amakhulupirira zoti kuli Mulungu.

Patatha miyezi ingapo, ndinakumananso ndi wa Mboni wina amene ankadziwa zambiri zachipatala. Atandiuza kuti akufuna kundifotokozera zomwe amakhulupirira, ndinavomera chifukwa ndinkafuna kudziwa chifukwa chake anthu ena amakhulupirira zoti kuli Mulungu. Ndinkaganiza kuti ndingathe kumuthandiza kuti asiye kukhulupirira zoti kuli Mulungu chifukwa n’zabodza.

 Ndiye kodi zimenezi zinatheka?

Ayi, chifukwa ndinalephera kupereka umboni woti kulibe Mulungu. Kenako ndinayamba kufufuza mfundo zosiyanasiyana zokhudza mmene moyo unayambira. Ndinadabwa kwambiri nditapeza kuti asayansi ena odziwika bwino amanena kuti selo lililonse ndi logometsa ndipo n’zosatheka kuti zimenezi zingochitika zokha. Asayansi ena amaganiza kuti maselo amenewa anachokera mlengalenga. Choncho asayansi sagwirizana chimodzi pa nkhani ya mmene moyo unayambira.

Nanga kodi pali mfundo ina imene asayansi amagwirizana?

N’zodabwitsa kuti asayansi ambiri amagwirizana pa mfundo yoti pali chinachake chimene chinachititsa kuti moyo uyambe kuchokera ku zinthu zopanda moyo. Ndinayamba kudzifunsa kuti, ‘Ngati asayansi amanena kuti moyo unayamba popanda Mlengi, koma sadziwa chimene chinauyambitsa, ndiye angatsimikize bwanji kuti moyo unayambadi choncho?’ Zimenezi zinandipangitsa kuti ndiyambe kufufuza zomwe Baibulo limanena zokhudza mmene moyo unayambira.

Ndiye munayamba kuliona bwanji Baibulo?

Ndikaphunzira mfundo iliyonse m’Baibulo, inkandipangitsa kukhulupirira kuti Baibulo ndi lolondola. Mwachitsanzo, zaka zaposachedwapa ndi pamene asayansi apeza umboni wosonyeza kuti chilengedwechi chili ndi chiyambi. Koma mawu oyamba a m’Baibulo, omwe analembedwa zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, amati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”1 Ndinapezanso kuti zimene Baibulo limanena zokhudza sayansi, n’zolondola.

Ndinapeza kuti zimene Baibulo limanena zokhudza sayansi, n’zolondola

Kodi zimene munkadziwa zokhudza sayansi zinapangitsa kuti muvutike kuyamba kukhulupirira Mulungu?

Ayi. Pamene ndinkayamba kukhulupirira zoti kuli Mulungu, n’kuti nditaphunzira sayansi payunivesite inayake kwa zaka zitatu. Ndikuona kuti ndikamaphunzira zambiri zokhudza mmene zinthu zamoyo zinayambira, m’pamenenso ndimakhulupirira kwambiri kuti kulidi Mlengi.

Mungatipatse chitsanzo?

Ee. Ndinaphunzira mmene mankhwala ndi poizoni zimakhudzira zinthu zamoyo. Zimene zinandidabwitsa kwambiri, ndi mmene ubongo wathu umadzitetezera ku mabakiteriya ndi zinthu zina. Pali zinthu zina zimene zimalekanitsa magazi ndi maselo a mu ubongo.

Ndiye zimenezi n’zochititsa chidwi chifukwa chiyani?

Zaka 100 zapitazo, akatswiri anapeza kuti zinthu zomwe zafika m’magazi, zimafalikira mbali zonse za thupi lathu kupatulapo mu ubongo ndi m’fupa lakumsana. Mfundo imeneyi inandichititsa chidwi kwambiri chifukwa timitsempha ting’onoting’ono timafikitsa magazi m’maselo onse a mu ubongo. Maselo onse a mu ubongo amayeretsedwa komanso kupeza chakudya ndi mpweya kuchokera ku magazi. Ndiye zimatheka bwanji kuti magazi azisiyanitsidwa ndi maselo a mu ubongo? Kwa zaka zambiri asayansi sankadziwa mmene zimenezi zimachitikira.

Tifotokozereni mmene zimenezi zimachitikira.

Timitsempha ta m’thupi la munthu sitili ngati timachubu tapulasitiki toti zinthu zakunja sizingalowe mkati. Mitsempha imapangidwa ndi maselo. Tizilombo toyambitsa matenda komanso zinthu zina zimatha kudutsa m’maselo amenewa. Koma maselo amene amapanga timitsempha ta mu ubongo wathu, ndi osiyana ndi maselo onse a m’thupi la munthu. Maselowa anakhala mogundana kwambiri ndipo mmene zimenezi zinapangidwira n’zochititsa chidwi kwambiri. Mpweya wabwino ndiponso tizinthu tochokera mu zakudya zimadutsa kuchoka m’mitsempha kupita mu ubongo, koma osati mwachisawawa, ndipo mpweya woipa umadutsa kuchoka mu ubongo kupita m’mitsempha. Koma zinthu monga mapuloteni, maselo akufa ndi zina, sizilowa mu ubongo. Choncho zinthu zimene zimalekanitsa magazi ndi maselo a mu ubongo zimaonetsetsa kuti zinthu zosafunika zisalowe mu ubongo. Zimenezi zimachitika mogometsa kwambiri, ndipo ineyo ndimaona kuti sizingangochitika zokha popanda amene anazilenga kuti zizichita zimenezi.