Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mungatani Ngati Mukuvutika Maganizo?

Kodi Mungatani Ngati Mukuvutika Maganizo?

“Ndinkagwira ntchito maola 16 pa tsiku ndipo nthawi zambiri ndinkagwiranso Loweruka ndi Lamlungu lomwe. Chifukwa cha zimenezi, sindinkakhala ndi nthawi yocheza ndi mwana wanga chifukwa ndinkamusiya asanadzuke n’kudzamupezanso atagona. Zimenezi zinkandikhumudwitsa kwambiri ndipo zinkachititsa kuti ndizivutika maganizo. Ndinkangoona ngati ndikuthamangitsa mphepo.”Kari, Finland.

ZIMENE zinkachitikira Kari, zimachitikiranso anthu ambiri. Mwachitsanzo, bungwe lina la ku United Kingdom linanena kuti, munthu mmodzi pa anthu 5 alionse, anadwalapo chifukwa cha kuvutika maganizo pa nthawi yomwe anali pa ntchito. Ndipo munthu mmodzi pa anthu 4 alionse ankalira kuntchito chifukwa chopanikizika. Bungweli linanenanso kuti m’chaka china posachedwapa, pamene mavuto azachuma anakula m’dzikoli, panali anthu ambiri amene ankavutika maganizo.

Kodi n’chiyani chikukuvutitsani maganizo?

  • Mukuona kuti ndinu wosatetezeka pa nkhani zachuma kapena zinthu zina?

  • Mumafunika kuchita zomwezomwezo nthawi zonse, zomwenso n’zotopetsa?

  • Kusagwirizana ndi anthu ena?

  • Zinthu zoipa zomwe zachitika pa moyo wanu?

Kodi zimenezi zakukhudzani bwanji?

  • Mukumadwaladwala?

  • Mukumakhala wotopa nthawi zonse?

  • Mukumasowa tulo?

  • Mwayamba kudwala matenda ovutika maganizo?

  • Simukugwirizana ndi anthu ena?

 Munthu akamavutika maganizo ndi zinazake, m’thupi mwake mumachitika zambiri. Thupi limayamba kutulutsa mahomoni enaake amene amapangitsa kuti azipuma mofulumira, mtima uzigunda mofulumira komanso kuti magazi azithamanga. Izi zimachititsanso kuti magazi ndi zinthu zina zofunika m’thupi zifalikire m’mitsempha yonse. Zimenezi zimachititsa kuti thupi lithe kulimbana ndi chimene chayambitsa kuti munthu azivutika maganizo. Izi zikatheka, thupi limayambanso kugwira ntchito bwinobwino. Koma ngati zalephereka, vutoli limakula ndipo limakhala matenda. Choncho kudziwa zimene mungachite mukayamba kuvutika maganizo kungakuthandizeni kuti mukhale ndi thanzi labwino komanso kuti muzisangalala.

Zimene Mungachite

Kuvutika maganizo pakokha si koipa. Bungwe lina la ku United States loona za matenda a maganizo linati: “Kuvutika maganizo kwambiri kukhoza kupha munthu. Komabe si bwinonso kuti munthu asamade nkhawa ngakhale pang’ono. Kuda nkhawa moyenera kungathandize munthu kuti akonze zinazake n’kukhala wosangalala. Zili ngati mmene chida chinachake choimbira chokhala ngati gitala, chimagwirira ntchito. Woimba akakoka kwambiri zingwe za chidachi, nyimbo zake sizimveka bwino ndipo zingwezo zikhoza kuduka. Komanso akangokoka pang’ono chabe, nyimbo zake sizingamvekenso bwino. Choncho munthu ayenera kukoka zingwezo moyenera kuti nyimbo zake zikhale zokoma.”

Komanso, anthu amaona zinthu mosiyanasiyana. Choncho zimene zingam’pangitse munthu wina kuvutika maganizo, sizingavutitse maganizo munthu wina. Mwachitsanzo, munthu wina akhoza kuyamba kuvutika maganizo ngati ntchito imene amagwira imachititsa kuti asamakhale ndi nthawi yopuma kapena yochita zinthu zinanso zofunika kwambiri. Koma zinthu ngati zomwezi sizingapangitse munthu wina kuyamba kuvutika maganizo.

Anthu ena amayamba kumwa mowa, kusuta fodya kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, n’cholinga choti asiye kuvutika maganizo. Enanso amayamba kudya kwambiri, kumangokhalira kuonera TV kapena kugwiritsa ntchito kompyuta. Koma zimenezi zimangochititsa kuti vutoli likule. Ndiye kodi njira yabwino yothetsera kuvutika maganizo ndi iti?

Anthu ambiri amatsatira malangizo a nzeru a m’Baibulo ndipo zimenezi zawathandiza kwambiri. Kodi nanunso malangizo a m’Baibulo angakuthandizeni? Tiyeni tikambirane yankho la funsoli ndi kuona mmene Baibulo lingathandizire kuthana ndi zinthu zimene nthawi zambiri zimayambitsa kuvutika maganizo.

 1 KUONA KUTI NDINU WOSATETEZEKA

Palibe munthu amene ndi wotetezeka pa chilichonse. Monga Baibulo limanenera, “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera [tonsefe].” (Mlaliki 9:11) Ndiye kodi mungatani ngati mumada nkhawa chifukwa choona kuti ndinu wosatetezeka? Tayesani kuchita izi.

  • Fotokozerani mnzanu kapena munthu wa m’banja lanu za vuto lanulo. Kafukufuku wina anasonyeza kuti nthawi zonse kufotokozera wina vuto, kumathandiza kuti munthu achepetse nkhawa. Ndipotu Baibulo limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

  • Musamangoganizira kuti mudzatani m’tsogolo zinthu zinazake zikadzachitika. Maganizo amenewa angangochititsa kuti muzikhala wankhawa ndiponso wosasangalala. Komanso mwina zimene mukudera nkhawazo sizidzachitika n’komwe. N’chifukwa chaketu Baibulo limati: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34.

  • Pempheronso lingakuthandizeni. Lemba la 1 Petulo 5:7 limati: ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse [Mulungu], pakuti amakuderani nkhawa.” Mulungu amasonyeza kuti amatidera nkhawa potithandiza kukhala ndi mtendere wa mumtima. Komanso iye amatitsimikizira kuti ‘sadzasiya’ anthu amene, akakhala ndi mavuto amadalira iyeyo kuti awathandize komanso kuwalimbikitsa.—Aheberi 13:5; Afilipi 4:6, 7.

2 KUCHITA ZOMWEZOMWEZO NTHAWI ZONSE

Zinthu monga kupita kuntchito tsiku ndi tsiku, kuphunzira zinazake komanso kusamalira ana kapena makolo okalamba, zingapangitse kuti munthu azivutika maganizo, makamaka ngati amafunika kuchita zomwezomwezo nthawi zonse. Koma nthawi zambiri zinthu zoterezi zimakhala zofunika kwambiri moti sungazisiye. (1 Timoteyo 5:8) Ndiye kodi mungatani ngati zimenezi zikuchititsa kuti muzivutika maganizo?

  • Muzipeza nthawi yopuma komanso muzigona mokwanira. Baibulo limati: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”—Mlaliki 4:6.

  • Mukakhala ndi zochita zambiri, muzichita kaye zofunika kwambiri ndipo muzikhala moyo wosalira zambiri. (Afilipi 1:10) Yesani kusintha zinthu zina pa moyo wanu, monga kuchepetsa kugula zinthu komanso nthawi imene mumagwira ntchito.—Luka 21:34, 35.

Kari, amene tamutchula poyamba uja, anaganiza zoonanso mmene moyo wake unalili. Iye anati: “Ndinazindikira kuti ndinkachita zinthu modzikonda.” Anagulitsa kampani yake n’kuyamba ntchito imene inkamuthandiza kuti azipezeka pakhomo. Kenako iye ananenanso kuti: “N’zoona kuti panopa sitikukhalanso moyo wawofuwofu ngati poyamba, koma ineyo ndi mkazi wanga sitikukhalanso ndi nkhawa ndipo tikumakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi banja lathu komanso anzathu. Sindingalole kusinthanitsa mtendere wamumtima womwe ndili nawo panopa ndi chilichonse.”

 3 KUSAGWIRIZANA NDI ANTHU ENA

Kusagwirizana ndi ena, makamaka ogwira nawo ntchito, kungachititse kuti munthu azivutika maganizo. Ngati zimenezi n’zimene zikukuchitikirani, pali zinthu zingapo zomwe mungachite.

  • Ngati munthu wina wakulakwirani, yesetsani kuugwira mtima. Musabwezere, chifukwa zimenezi zingangochititsa kuti zinthu ziipe kwambiri. Lemba la Miyambo 15:1 limati: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.”

  • Yesetsani kukambirana nkhaniyo modekha ndi munthuyo muli awiri. Zimenezi zingasonyeze kuti mukulemekeza munthuyo.—Mateyu 5:23-25.

  • Muzimvetsera mwatcheru munthuyo akamalankhula, chifukwa zimenezi zingakuthandizeni kuti mumvetse mmene akumvera komanso mmene akuionera nkhaniyo. Kuchita zimenezi kungathandize kuti musafulumire kukwiya. (Miyambo 19:11) Izi zingakuthandizeninso kudziwa mmene anthu ena amakuonerani.

  • Yesetsani kum’khululukira munthuyo. Kukhululuka kumathandiza kwambiri komanso ndi mankhwala. Kafukufuku wina, yemwe anachitika mu 2001, anasonyeza kuti “kusakhululuka” kumachititsa kuti mtima wa munthu uzigunda mofulumira komanso “kumayambitsa matenda a kuthamanga kwa magazi,” pomwe kukhululuka kumachepetsa nkhawa.—Akolose 3:13.

4 ZINTHU ZOIPA ZOMWE ZACHITIKA PA MOYO WANU

Mayi wina, dzina lake Nieng yemwe amakhala ku Cambodia, anakumana ndi mavuto adzaoneni. Mu 1974 anavulala kwambiri bomba litaphulika pabwalo lina la ndege. M’chaka chotsatira ana ake awiri, mayi ake komanso mwamuna wake anamwalira. M’chaka cha 2000 nyumba ndi katundu wake zinapsa. Patatha zaka zitatu zokha, mwamuna wake wachiwiri anamwaliranso. Chifukwa cha mavuto onsewa, iye anayamba kuganiza zongodzipha.

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama”

Kenako mofanana ndi Kari, Nieng anayamba kuphunzira Baibulo. Zimene ankaphunzirazo zinamuthandiza kwambiri moti anayamba kuuza ena chifukwa anadziwa kuti nawonso zingawathandize. Nkhani yakeyi ikutikumbutsa zotsatira za kafukufuku wina, yemwe anachitika mu 2008 ku Britain. Kafukufukuyu anasonyeza kuti, kukhala ndi “mtima wothandiza ena,” kumathandiza munthu “amene akukumana ndi mavuto kuti asamavutike maganizo kwambiri.” Mfundo imeneyi ndi yogwirizananso ndi zimene Baibulo limanena.—Machitidwe 20:35.

Nieng anaphunziranso kuchokera m’Baibulo kuti mavuto onse amene anthu akukumana nawo adzatha, ndipo padziko lonse padzakhala “mtendere wochuluka.”—Salimo 72:7, 8.

Choncho, Baibulo limatithandiza kudziwa zimene tiyenera kuchita tikamavutika maganizo ndi zinazake. Limatiuzanso za chiyembekezo chosangalatsa choti posachedwapa mavuto onsewa adzatha. Baibulo ndi buku lapadera kwambiri, ndipo malangizo ake athandiza anthu ambiri omwe anali pa mavuto osiyanasiyana. Inunso lingakuthandizeni.