ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Chiwawa
Kuyambira kale anthu akhala akuchita zachiwawa. Kodi anthu apitirizabe kuchita zimenezi mpaka kalekale?
Kodi Mulungu amagwirizana ndi zoti anthu azichita zachiwawa?
ZIMENE ANTHU AMANENA
Anthu ambiri, ngakhalenso anthu opemphera, amaona kuti kuchita chiwawa sikulakwa ngati ukubwezera munthu amene wakulakwira. Komanso anthu ambiri amaona kuti kuonera mafilimu achiwawa kulibe vuto lililonse.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Pafupi ndi mzinda wa Mosul, womwe uli kumpoto kwa dziko la Iraq, kuli malo omwe panali mzinda wa Nineve. Mzindawu unali likulu la Ufumu wa Asuri. Baibulo linali litaneneratu kuti ‘Nineve adzakhala bwinja’ ngakhale kuti pa nthawiyi n’kuti zinthu zikuyenda bwino mumzindawu. (Zefaniya 2:13) Yehova anati: “Ndidzakuchititsa kukhala chinthu chonyozeka ndiponso choopsa.” N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chifukwa choti mzinda wa Nineve unali “mzinda wokhetsa magazi.” (Nahumu 1:1; 3:1, 6) Lemba la Salimo 5:6 limanena kuti Yehova amadana ndi “munthu wokhetsa magazi.” Choncho, mabwinja a mzinda wa Nineve ndi umboni woti mawu a Yehova anakwaniritsidwa.
Amene anayambitsa chiwawa ndi Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu komanso wa anthufe. Ndipotu Yesu anamutchula kuti “wopha anthu.” (Yohane 8:44) Komanso chifukwa choti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” anthu ambiri amakonda kuchita chiwawa ndiponso kuonera mafilimu achiwawa. (1 Yohane 5:19) Koma kuti Mulungu azitikonda, tiyenera kupewa zachiwawa n’kumachita zimene iye amafuna. * Kodi n’zothekadi kuchita zimenezi?
“Yehova . . . amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”—Salimo 11:5.
Kodi anthu achiwawa angasinthe?
ZIMENE ANTHU AMANENA
Anthu amachita zachiwawa chifukwa ndi mmene alili ndipo zimenezi sizingasinthe.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” Limanenanso kuti: “Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo muvale umunthu watsopano.” (Akolose 3:8-10) Kodi pamenepa Mulungu akufuna kuti tichite zinthu zomwe sitingakwanitse? Ayi. Mulungu amadziwa kuti munthu akhoza kusintha. * Koma kodi zimenezi zingatheke bwanji?
Akolose 3:10) Munthu akaphunzira za Mulungu ndi zimene Mulunguyo amafuna, amayamba kumukonda komanso kupewa zimene amadana nazo.—1 Yohane 5:3.
Choyamba, munthu ayenera kuphunzira Baibulo kuti adziwe Mulungu. (Chachiwiri, munthu ayenera kusankha bwino anthu ocheza nawo. Baibulo limati: “Usamagwirizane ndi munthu aliyense wokonda kukwiya, ndipo usamayende ndi munthu waukali, kuti usazolowere njira zake ndi kuikira moyo wako msampha.”—Miyambo 22:24, 25.
Chachitatu, munthu ayenera kuzindikira kuti amene amachita zachiwawa ndi wolephera, ndipo satha kudziletsa. Koma munthu wokonda mtendere amadziletsa ndipo amaposa munthu wamphamvu. Lemba la Miyambo 16:32 limati: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”
“Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse.”—Aheberi 12:14.
Kodi chiwawa chidzatha?
ZIMENE ANTHU AMANENA
Anthu akhala akuchita chiwawa kuyambira kale ndipo adzachita zimenezi mpaka kalekale.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso . . . koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.” (Salimo 37:10, 11) Choncho, mofanana ndi mmene anachitira ndi mzinda wa Nineve, Mulungu adzawononga anthu achiwawa n’cholinga choti asamadzavutitsenso anthu ofatsa ndi okonda mtendere.—Salimo 72:7.
Kuti Mulungu asadzatiwonongere limodzi ndi anthu amenewa, tiyenera kumachita zimene amafuna komanso kumakhala mwamtendere ndi anthu. Lemba la 2 Petulo 3:9 limati: “Yehova . . . akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”
“Adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.”—Yesaya 2:4.
^ ndime 7 Kale Mulungu ankalola Aisiraeli kumenya nkhondo kuti asalandidwe malo awo. (2 Mbiri 20:15, 17) Koma zimenezi zinatha pamene anathetsa pangano lomwe anachita ndi Aisiraeli n’kukhazikitsa mpingo wachikhristu womwe anthu ake amapezeka padziko lonse.
^ ndime 11 Nkhani zina za anthu omwe anasintha makhalidwe awo oipa, mungazipeze m’magazini a Nsanja ya Olonda. Nkhanizi zimakhala ndi mutu wakuti, “Baibulo Limasintha Anthu.”