ZOCHITIKA PADZIKOLI
Nkhani za ku Middle East
Ku Middle East n’kumene kale kunali maufumu ambiri. Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zinthu zambiri zakale kudera limeneli.
Anthu a ku Kanani Ankapanga Vinyo
Mu 2013, akatswiri ofukula zinthu zakale anatulukira chipinda cha pansi pa nthaka ku Kanani. Chipindachi chinali chosungiramo vinyo zaka 3,700 zapitazo. M’chipindamo anapezamo mitsuko ikuluikulu ya vinyo yokwana 40 ndipo vinyo yemwe ankasungidwamo ndi wofanana ndi vinyo yemwe angakwane m’mabotolo 3,000 a masiku ano. Akatswiri omwe anafufuza zotsalira zomwe zinali m’mitsukoyi anapeza kuti anthu a ku Kanani anali akatswiri opanga vinyo. Katswiri wina wofukula zinthu zakale anati: “Zimene anthu a ku Kanani ankathira akamapanga vinyo komanso njira zimene ankatsatira popanga vinyoyu, zinkakhala zofanana.”
KODI MUKUDZIWA? Baibulo limanena kuti anthu akale a ku Isiraeli ankapanga “vinyo wabwino kwambiri” komanso kuti ankamusunga m’mitsuko ikuluikulu.—Nyimbo ya Solomo 7:9; Yeremiya 13:12.
Kukwera kwa Chiwerengero cha Anthu
Nyuzipepala ina inanena kuti chiwerengero cha ana omwe anabadwa ku Egypt mu 2012 chinawonjezeka ndi 560,000 kuposa ana omwe anabadwa mu 2010. (Guardian) Magued Osman yemwe ali m’bungwe lina la kafukufuku ku Egypt anati: “Kuyambira kale, zimenezi sizinachitikepo.” Akatswiri ena akunena kuti ngati chiwerengero cha ana obadwa chitapitiriza kukwera chonchi, dziko la Egypt likhoza kudzakumana ndi mavuto monga kusowa kwa madzi, chakudya komanso magetsi.
KODI MUKUDZIWA? Baibulo limanena kuti Mulungu ankafuna kuti anthu ‘adzaze dziko lapansi,’ koma osati achite kuchulukana n’kufika pomasowa zinthu zofunika pa moyo.—Genesis 1:28; Salimo 72:16.
Anapeza Ndalama Zomwe Zinabisidwa
Ndalama zamkuwa zoposa 100 zomwe zinalembedwa kuti, “Chaka cha 4,” zinapezeka pafupi ndi msewu wina ku Israel. Akatswiri anapeza kuti ndalamazi ziyenera kuti zinabisidwa m’chaka cha 4, Ayuda ataukira ufumu wa Roma, zomwe zinachititsa kuti Yerusalemu awonongedwe. Mkulu wina yemwe ankayang’anira ntchito yokumba pamene panali ndalamazi, dzina lake Pablo Betzer anati: “N’kutheka kuti munthu wina ataona kuti asilikali a Roma akufuna kuwononga mzinda wa Yerusalemu, anabisa ndalamazi poganiza kuti adzabweranso kudzazitenga.”
KODI MUKUDZIWA? M’chaka cha 33 C.E., Yesu ananeneratu kuti asilikali a Roma adzazungulira mzinda wa Yerusalemu. Ananena kuti Akhristu ayenera kuthawira kumapiri kuti adzapulumuke.—Luka 21:20-24.