Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani za ku Europe

Nkhani za ku Europe

Poyamba anthu a m’mayiko a ku Europe ankakonda zopemphera koma panopa zinthu zinasintha moti ambiri sapemphera. Koma mungadabwe kuti zotsatira za kafukufuku amene wachitika posachedwapa m’mayikowa, zikugwirizana kwambiri ndi zimene Baibulo limanena.

Njira Yothandizira Ana Obadwa Masiku Asanakwane

Pa kafukufuku wina yemwe anachitika mumzinda wa Milan m’dziko la Italy, anapeza kuti ana amene amabadwa masiku asanakwane, amakula bwino ngati mayi awo amawayankhula. Anawa anawaika kachipangizo kenakake pamkono kamene kankawathandiza kumva mawu a mayi awo. Anawo ankamva mawu a mayi awo mmene akanawamvera zikanakhala kuti adakali m’mimba. Choncho anapeza kuti, “Mayi akamayankhula ndi mwana wake, yemwe wabadwa masiku asanakwane, amakula bwino kwambiri.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ine ndadzitonthoza ndipo ndakhazika mtima wanga pansi. Ndakhala ngati mwana amene wangosiya kumene kuyamwa, amene ali m’manja mwa mayi ake.” —Salimo 131:2.

Ana Odzikonda

Kafukufuku wina yemwe anachitika pa ana 565 ku Netherlands, anasonyeza kuti ana amene makolo awo ankakonda kuwasasatitsa komanso kuwauza mawu osonyeza kuti ndi ofunika kuposa anthu ena onse, amakhala odzikonda kwambiri. Anapezanso kuti anawa akamakula samamva za ena. Munthu wina yemwe analemba zotsatira za kafukufukuyu anati: “Ana amakhulupirira zimene makolo awo amanena. Ndiye ngati makolo amawauza kuti ndi ofunika kwambiri, akadzakula amadzakhala ovuta ndipo amavutika kukhala ndi anthu ena.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino.”—Aroma 12:3.

Anthu a Zaka Zoposa 100

Kafukufuku wina yemwe anachitika payunivesite ya Heidelberg ku Germany, anasonyeza kuti anthu ambiri a zaka zoposa 100 amafunabe kumakhala ngati anyamata. Zimenezi ndi zodabwitsa chifukwa munthu akamakalamba amadwaladwala komanso amakhala wofooka. Koma okalamba ambiri omwe ali ndi zaka zoposa 100 amafunabe atakhala ndi moyo zaka zambiri ndipo amafuna kuchita zinthu zikuluzikulu. Pa kafukufukuyu anapeza kuti anthuwa amakwaniritsa zolinga zawo, amafuna kuti zinthu ziziwayendera bwino komanso amachitabe zinthu zina monga kupemphera ndi kutsatira chikhalidwe chawo.

ZOTI MUGANIZIRE: Lemba la Mlaliki 3:11 limanena kuti anthufe tinalengedwa ndi mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Ngati zili choncho, n’chifukwa chiyani timafa?