MAVUTO A M’DZIKOLI
1 | Muziteteza Thanzi Lanu
CHIFUKWA CHAKE ZILI ZOFUNIKA
Mavuto kapena ngozi zam’chilengedwe zikhoza kukhudza thanzi lathu m’njira zosiyanasiyana.
-
Zinthu zoipa zikachitika, anthu amakhala ndi nkhawa, ndipo amene amakhala ndi nkhawa kwa nthawi yaitali akhoza kudwala.
-
Kukabuka miliri, zipatala zimalephera kusamalira bwinobwino odwala, chifukwa amafunika kusamalira anthu ambirimbiri pa nthawi imodzi ndipo mankhwala amasowa.
-
Masoka amabweretsa mavuto azachuma ndipo zimenezi zimachititsa kuti anthu alephere kupeza zinthu zofunika monga chakudya chopatsa thanzi komanso amalephera kulipira thandizo la zachipatala.
Zimene Muyenera Kudziwa
-
Kudwala kwambiri komanso kuvutika maganizo kungasokoneze mmene mumaganizira ndipo zimenezi zingachititse kuti musamachite zinthu zosamalira thanzi lanu. Pamapeto pake matenda anu akhoza kuwonjezereka.
-
Ngati simungasamalire mavuto a thanzi omwe muli nawo, mavutowo akhoza kukula kwambiri ndipo akhoza kuwononga moyo wanu.
-
Mukakhala ndi thanzi labwino, sizingakuvuteni kusankha zinthu mwanzeru panthawi imene mwakumana ndi mavuto.
-
Kaya ndinu wolemera kapena wosauka, mukhoza kuchita zinthu zimene zingateteze thanzi lanu.
Zimene Mungachite Panopa
Munthu wanzeru amadziwiratu zoipa zimene zingachitike ngati angathe ndipo amachita zinthu mosamala kuti azipewe. Zimenezi zingagwirenso ntchito pa nkhani ya thanzi lanu. Nthawi zambiri mungapewe kutenga matenda kapena kuthandiza kuti asafalikire kwambiri pokhala aukhondo. Pajatu kupewa kumaposa kuchiza.
“Tikamayesetsa kukhala aukhondo komanso kusamalira pakhomo pathu, timakhala tikupulumutsa ndalama zimene tikanagwiritsa ntchito popitira kuchipatala komanso kugula mankhwala.”—Andreas. a
a Mayina ena asinthidwa m’magaziniyi.