Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kudziwa Mulungu Kungakuthandizeni Bwanji?

Kodi Kudziwa Mulungu Kungakuthandizeni Bwanji?

Mfundo zimene taphunzira munkhani zapitazi zatithandiza kupeza yankho la funso lakuti, Kodi Mulungu ndi ndani? Kuchokera m’Baibulo taphunzira kuti dzina lake ndi Yehova ndipo khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Taonanso zimene anachita kale komanso zimene adzachite m’tsogolo kuti athandize anthu. Koma padakali zambiri zimene mungaphunzire zokhudza Mulungu. Komabe mwina mungadzifunse kuti, Kodi kuphunzira zimenezi kundithandiza bwanji?

Yehova amatilonjeza kuti ‘tikam’funafuna, adzalola kuti tim’peze.’ (1 Mbiri 28:9) Taganizirani madalitso apadera amene tingapeze tikamufunafuna ndiponso kumudziwa Mulungu, omwe ndikukhala pa “ubwenzi wolimba ndi Yehova.” (Salimo 25:14) Kodi ubwenzi umenewu ungakuthandizeni bwanji?

Kukhala wosangalala. Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Kukhala naye pa ubwenzi ndiponso kumutsanzira kungakuthandizeni kuti muzikhala wosangalala ndipo zimenezi zingachititse kuti mukhale ndi thanzi labwino. (Salimo 33:12) Komanso mungathe kupewa makhalidwe oipa, kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhala bwino ndi ena. Kuchita zimenezi kungakuthandizeninso kuti muzikhala wosangalala. Mungayambe kukhala ndi maganizo ofanana ndi amene wolemba Masalimo wina anali nawo. Iye anati: “Kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.”​—Salimo 73:28.

Kusamaliridwa. Yehova analonjeza atumiki ake kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.” (Salimo 32:8) Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova amasamalira mtumiki wake aliyense mogwirizana ndi zimene akufunikira. (Salimo 139:1, 2) Mukayesetsa kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, mudzaona kuti nthawi zonse amakhala wokonzeka kukuthandizani.

Tsogolo labwino. Kuwonjezera pa kukuthandizani kukhala ndi moyo wosangalala panopa, Yehova Mulungu akukupatsaninso mwayi wokhala ndi tsogolo labwino. (Yesaya 48:17, 18) Baibulo limati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) Mu nthawi yovuta ino, chiyembekezo chimene Mulungu watipatsa chimakhala ngati nangula chifukwa chimatithandiza kuti tisagwedezeke.​—Aheberi 6:19.

Zimene takambiranazi ndi zifukwa zochepa chabe zotichititsa kufuna kuti timudziwe bwino Mulungu komanso tikhale naye pa ubwenzi. Kuti mudziwe zambiri, funsani wa Mboni za Yehova aliyense kapena pitani pa webusaiti yathu ya jw.org/ny.