Musamaone Kuti Palibe Chifukwa Chokhalira ndi Moyo
NKHANI zapitazi zafotokoza kuti nthawi zina mavuto angatichititse kuona kuti sitingathenso kupirira. Mukakumana ndi mavuto mwina inunso mungayambe kudzifunsa kuti, ‘Kodi palinso chifukwa chokhalira ndi moyo? Kodi pali aliyense amene akudziwa mmene ndikumvera?’ Musamakayikire zoti Mulungu amakuganizirani ndipo akudziwa mavuto anu. Iye amaona kuti ndinu wamtengo wapatali.
Amene analemba Salimo 86 anasonyeza kuti ankadalira Mulungu. Iye anati: “Pa tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu, ndipo inu mudzandiyankha.” (Salimo 86: 7) Koma mwina mungadabwe kuti, ‘Yehova angandiyankhe bwanji “pa tsiku la nsautso yanga”?’
Ngakhale kuti Mulungu sangathetse vuto lanulo nthawi yomweyo, Baibulo lomwe ndi Mawu ake, limanena kuti angakupatseni mtendere wamumtima kuti muthe kupirira. Limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afilipi 4:6, 7) Taonani mmene mavesi otsatirawa akusonyezera kuti Mulungu amatiganizira.
Mulungu Amakuganizirani
“Palibe ngakhale [mpheta] imodzi imene imaiwalika kwa Mulungu. . . . Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta ambiri.”—Luka 12:6, 7.
TAGANIZIRANI IZI: Ngakhale kuti anthu ambiri amaona kuti mbalame zing’onozing’ono monga mpheta ndi zosafunika kwenikweni, Mulungu amaziona kuti ndi zofunika. Iye amadziwa zokhudza mpheta iliyonse ndipo amaiona kuti ndi yofunika. Komatu Mulungu amaona kuti anthu ndi amtengo wapatali kuposa mpheta. Pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga padzikoli, anthu ndiye ofunika kwambiri ndipo analengedwa “m’chifaniziro” chake komanso angathe kusonyeza makhalidwe ake.—Genesis 1:26, 27.
“Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa. . . . Mumadziwa maganizo anga . . . Ndisanthuleni ndi kudziwa malingaliro anga amene akundisowetsa mtendere.”—Salimo 139:1, 2, 23.
TAGANIZIRANI IZI: Mulungu amakudziwani bwino. Amadziwa mmene mukumvera mumtima mwanu komanso zinthu zimene zikukudetsani nkhawa. Anthu ena sangadziwe mavuto anu komanso sangakumvetseni. Koma Mulungu amadziwa, amakuderani nkhawa ndiponso amafuna kukuthandizani. Tikaganizira zimenezi, tingaone kuti palidi chifukwa chokhalira ndi moyo.
Moyo Wanu ndi Wofunika
“Inu Yehova, imvani pemphero langa. Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo. . . . Tcherani khutu lanu kwa ine. Fulumirani kundiyankha pa tsiku limene ndikuitana. . . . Iye adzamvetsera pemphero la anthu amene alandidwa chilichonse.”—Salimo 102:1, 2, 17.
TAGANIZIRANI IZI: Tingati kuyambira pamene anthu anayamba kuvutika, Yehova wakhala akulemba m’buku lake misozi yawo yonse. (Salimo 56:8) Misozi imeneyi ikuphatikizaponso yanu. Mulungu amakumbukira mavuto ndi misozi yanu yonse chifukwa choti amaona kuti ndinu ofunika kwambiri.
“Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. . . . Ine, Yehova Mulungu wako . . . ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—Yesaya 41:10, 13.
TAGANIZIRANI IZI: Mulungu ndi wokonzeka kukuthandizani. Mukakumana ndi mavuto adzakugwirani dzanja.
M’tsogolomu Zinthu Zidzakhala Bwino
“Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
TAGANIZIRANI IZI: Mulungu amakukondani kwambiri moti analolera kupereka Mwana wake Yesu monga nsembe chifukwa cha machimo anu. Nsembe imeneyi ingakuthandizeni kuti mudzasangalale ndi moyo wosatha. *
Mwina mukukumana ndi mavuto ndipo mukuona kuti simungathenso kupirira. Ngati ndi choncho tikukulimbikitsani kuti muphunzire Baibulo ndipo muzikhulupirira zimene Mulungu walonjeza. Izi zikuthandizani kuti muzikhala wosangalala komanso muziona kuti palidi chifukwa chokhalira ndi moyo.
^ ndime 19 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene nsembe ya Yesu ingakuthandizireni, onerani vidiyo yakuti, Tizikumbukira Imfa ya Yesu pa www.ps8318.com/ny. Pitani pamene alemba kuti MABUKU > MAVIDIYO > MISONKHANO NDI UTUMIKI WATHU.