“Ufumu Wanu Udze”—Pemphero Limene Anthu Ambiri Amalikonda
Kodi nthawi ina munapempherapo kuti Ufumu wa Mulungu ubwere? Kwa zaka zambiri, anthu akhala akunena mawu oti “Ufumu wanu udze” akamapemphera. Anthu amakonda kutchula mawu amenewa chifukwa choti Yesu anauza otsatira ake kuti azipempherera Ufumu wa Mulungu.
Poyamba, otsatira a Yesu sanamvetse zinthu zonse zomwe Yesu ankaphunzitsa zokhudza Ufumuwu. Pa nthawi ina iwo anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” N’kutheka kuti anadabwa kwambiri chifukwa choti Yesu sanawauze nthawi yeniyeni yomwe Ufumuwo udzabwere. (Machitidwe 1:6, 7) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sitingadziwe kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndiponso kuti udzabwera liti? Ayi.
Nsanja ya Olondayi ikuthandizani kupeza mayankho a mafunso otsatirawa:
N’chifukwa chiyani tikufunikira Ufumu wa Mulungu?
Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi ndani?
Kodi Ufumu wa Mulungu udzayamba liti kulamulira dzikoli?
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani?
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu panopa?
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?