Anthu Amene Amamvera Mulungu Amalandira Madalitso
Mneneri Mose ananena kuti tikamamvera malamulo a Mulungu, iye adzatidalitsa. (Deuteronomo 10:13; 11:27) Tizimvera Mulungu chifukwa chomukonda osati chifukwa choopa chilango. Makhalidwe abwino a Mulungu amatichititsa kuti tizimumvera ndi kuyesetsa kupewa zimene zingamukhumudwitse. Zili choncho “chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yohane 5:3.
Kodi Mulungu amatidalitsa bwanji tikamamumvera? Taganizirani njira ziwiri izi.
1. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA ANZERU
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, . . . ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”—YESAYA 48:17.
Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu, amatidziwa bwino ndipo amatipatsa malangizo amene angatithandize. Kuti zimene tikuphunzira zitithandize kusankha zinthu mwanzeru, tiyenera kuphunzira zimene Mulungu amafuna m’Malemba Opatulika komanso kuchita zimene tikuphunzirazo.
2. TIKAMAMVERA MULUNGU TIMAKHALA OSANGALALA
“Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—LUKA 11:28.
Masiku ano anthu mamiliyoni ambiri amene amamvera Mawu a Mulungu amakhala ndi moyo wosangalala. Mwachitsanzo, taganizirani bambo wina wa ku Spain amene sankachedwa kupsa mtima ndipo ankachitira nkhanza anthu ena kuphatikizapo mkazi wake. Tsiku lina anawerenga zimene mneneri Mose analemba zokhudza Yosefe, mwana wa Yakobo, yemwe anali wougwira mtima. Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo komanso anaikidwa m’ndende ngakhale kuti sanalakwe. Komabe iye anakhalabe wougwira mtima, ankachita zinthu mwamtendere komanso ankakhululukira ena. (Genesis, machaputala 37-45) Bambo wa ku Spain uja anati: “Kuganizira chitsanzo cha Yosefe kunandithandiza kuti nanenso ndikhale wougwira mtima, ndizichita zinthu mokoma mtima ndi ena komanso ndikhale wodziletsa. Zimenezi zathandiza kuti panopa ndizikhala moyo wosangalala.”
M’Malemba Opatulika muli malangizo enanso okhudza mmene tingamachitire zinthu ndi anthu ena. Tiyeni tione mfundo zina m’nkhani yotsatirayi.