Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MBIRI YA MOYO WANGA

Ndilibe Manja Koma Ndinatha Kulandira Choonadi cha M’Baibulo

Ndilibe Manja Koma Ndinatha Kulandira Choonadi cha M’Baibulo

Anthu akafuna kugwa amakonda kugwiritsitsa chinthu chinachake koma ine sindingathe kuchita zimenezi chifukwa ndilibe manja ndi mikono. Ndili ndi zaka 7 madokotala anandidula mikono kuti apulumutse moyo wanga.

Ndinabadwa mu 1960 pamene mayi anga anali ndi zaka 17. Bambo anga anachoka pakhomo ndisanabadwe. Choncho ine ndi mayi tinkakhala ndi agogo ku Burg, yomwe ndi tauni yaing’ono imene ili m’dziko lomwe linkatchulidwa kuti East Germany. Mofanana ndi anthu ambiri a m’dzikoli, banja lathu silinkakhulupirira kuti kuli Mulungu. Sitinkaganizira za Mulungu ngakhale pang’ono.

Ndili mwana ndinkasangalala chifukwa agogo aamuna ankakonda kucheza nane. Ankandiphunzitsa ntchito zambiri, kuphatikizapo kukwera m’mitengo n’kumasadza nthambi. Izi zinkandisangalatsa ndipo ndinkaona kuti moyo ndi wabwino kwambiri.

MOYO WANGA UNASINTHIRATU NDITACHITA NGOZI

Ndili ndi zaka 7 ndinachita ngozi yoopsa kwambiri. Pa nthawiyi n’kuti nditangoyamba kumene sitandade 2. Tsiku lina ndikupita kunyumba, ndinakwera pholo la magetsi. Nditakwera m’mwamba kufika mamita 8 ndinagwidwa shoko n’kukomoka. Ndinatsitsimukira kuchipatala ndipo mikono yanga inali itafa. Mikono yanga inali itapsa modetsa nkhawa moti madokotala anaona kuti ayenera kungoidula. Popeza kuti ndinali mwana sindinkadziwa kuti zimenezi zingakhudze bwanji moyo wanga. Koma mayi ndi agogo anga ankadziwa ndipo zinawamvetsa chisoni kwambiri.

Nditatuluka m’chipatala ndinayambiranso sukulu. Koma ana anzanga ankandiseka, kundikankha ndiponso kundigenda ndi zinthu chifukwa choona kuti sindingathe kubwezera. Ndinkavutika kwambiri mumtima chifukwa cha zimene ankandinena. Kenako ndinatumizidwa kusukulu ya ana olumala yomwe inali yogonera komweko. Popeza kuti sukuluyi inali kutali, mayi ndi agogo sankakwanitsa kukandiona moti ndinkaonana nawo paholide pokha. Choncho kwa zaka 10 ndinkangoonana nawo mwa apo ndi apo.

NDINAZOLOWERA KUCHITA ZINTHU POPANDA MANJA

Ndinaphunzira kuchita zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mapazi. Tangoganizirani mmene zingakhalire kudya ndi foloko kapena sipuni pogwiritsa ntchito zala zakuphazi. Komabe ndinakwanitsa kuphunzira kuchita zimenezi. Ndinaphunziranso kutsuka m’kamwa ndiponso kupesa pogwiritsa ntchito mapazi. Ndinayambanso kugwiritsa ntchito mapazi polankhula kapena kuloza zinthu ngati mmene munthu amachitira ndi manja.

Ndili mnyamata ndinkakonda kwambiri kuwerenga nkhani zopeka zokhudza zinthu zimene asayansi adzatulukire. Nthawi zina ndinkayerekezera mmene zingakhalire nditakhala ndi manja oyendera magetsi oti azitha kuchita chilichonse chomwe ndikufuna. Ndili ndi zaka 14, ndinayamba kusuta fodya. Ndinkaona kuti kusuta kunkandipangitsa kuti ndisamadziderere komanso ndizidziona kuti ndine wofanana ndi aliyense. Mumtima ndinkadziuza kuti: ‘Nanenso ndikhoza kukwanitsa zimenezi. Kaya ndili ndi manja kapena ayi, ngati ndikusuta ndiye kuti ndine wamkulu.’

Sindinkafuna kuti ndizingokhala, choncho ndinalowa timagulu tosiyanasiyana. Ndinalowa bungwe lina la achinyamata limene linkayang’aniridwa ndi boma ndipo anandisankha kukhala mlembi. Udindowu unapangitsa kuti anzanga azindipatsa ulemu. Ndinalowanso gulu loimba komanso la ndakatulo. Kuwonjezera pa zimenezi, ndinkachita nawo masewera a anthu olumala. Nditamaliza sukulu, ndinayamba kugwira ntchito pa kampani ina ya m’dera lathu. Nditakula ndinkakonda kuvala mikono yochita kupanga kuti ndizifanana ndi anthu ena.

NDINAYAMBA KUPHUNZIRA BAIBULO

Tsiku lina ndikudikira sitima imene ndinkakwera popita kuntchito, munthu wina anabwera n’kundifunsa ngati ndimaona kuti Mulungu angathe kundipatsanso mikono. Funso limeneli linandidabwitsa. Ngakhale kuti ndinkafunitsitsa nditakhalanso ndi manja, ndinkaona kuti zimene ananenazi n’zosatheka chifukwa sindinkakhulupirira kuti kuli Mulungu. Kuyambira nthawi imeneyo, ndinayamba kumuzemba munthuyo.

Patapita nthawi, munthu wina amene ndinkagwira naye ntchito anandiitanira kunyumba kwawo. Tikumwa khofi, makolo ake anayambitsa nkhani yonena za Yehova Mulungu. Kameneka kanali koyamba kumva kuti Mulungu ali ndi dzina. (Salimo 83:18) Komabe mumtima ndinkanena kuti: ‘Kaya anene kuti dzina lake ndi ndani, nkhani ndi yoti kulibe Mulungu. Anthuwa akufunika kuwathandiza kudziwa zimenezi.’ Kuti ndipeze mwayi wotsutsa mfundo zawo, ndinavomera kuti ndiziphunzira nawo Baibulo. Koma ndinalephera kufotokoza umboni wosonyeza kuti kulibe Mulungu.

Titayamba kuphunzira maulosi a m’Baibulo, ndinayamba kusintha maganizo anga aja, oti kulibe Mulungu. Maulosi ambiri anakwaniritsidwa, ngakhale kuti analembedwa kudakali zaka zambirimbiri kuti zinthuzo zichitike. Tsiku lina, tinkayerekezera zinthu zimene zikuchitika masiku ano ndi maulosi opezeka mu chaputala 24 cha Mateyu, chaputala 21 cha Luka ndi chaputala 3 cha 2 Timoteyo. Mofanana ndi mmene zizindikiro zosiyanasiyana zimathandizira dokotala kudziwa matenda amene munthu akudwala, zinthu zimene zinafotokozedwa m’maulosiwa zinandithandiza kuzindikira kuti tikukhala mu nthawi imene Baibulo limanena kuti ndi “masiku otsiriza.” * Zinandichititsa chidwi kwambiri kuona kuti maulosi amenewa akukwaniritsidwa m’nthawi yathu.

Ndinazindikira kuti zimene ndimaphunzirazo ndi zoona. Ndinayamba kupemphera kwa Yehova Mulungu ndipo ndinasiya kusuta, ngakhale kuti kwa zaka zoposa 10 ndinkasuta kwambiri. Ndinapitirizabe kuphunzira Baibulo kwa pafupifupi chaka chimodzi. Pa 27 April 1986, ndinabatizidwa mobisa kubafa, chifukwa nthawi imeneyo ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku East Germany.

NDIMAYESETSA KUTHANDIZA ENA

Popeza ntchito yathu inali yoletsedwa, tinkasonkhana m’magulu ang’onoang’ono m’nyumba za anthu moti a Mboni ambiri sindinkawadziwa. Mwamwayi, boma linandilola kupita ku West Germany, komwe ntchito yathu sinali yoletsedwa. Kumeneko ndinakhala ndi mwayi wopezeka pa misonkhano yathu ikuluikulu komwe ndinakumana ndi a Mboni anzanga ambirimbiri. Zinali zosangalatsa kwambiri kukumana ndi abale ndi alongo anga ambiri chonchi.

Mayiko a East ndi West Germany atayambiranso kugwirizana, ntchito ya Mboni za Yehova sinakhalenso yoletsedwa. Apano tinali ndi mwayi wolambira Yehova Mulungu mwaufulu. Ndinkafunitsitsa nditawonjezera zomwe ndinkachita pa ntchito yolalikira. Komabe ndinkachita mantha kulankhula ndi anthu osawadziwa. Ndinkadzikayikira chifukwa chakuti ndine wolumala komanso chifukwa choti ndinakulira kumalo osamalira ana olumala. Koma mu 1992, ndinayesetsa kuti mwezi winawake ndilalikire kwa maola 60. Ndinakwanitsa kuchita zimenezi ndipo ndinasangalala kwambiri. Kenako ndinakonza zoti ndizichita zimenezi mwezi uliwonse ndipo ndinapitiriza kwa zaka zitatu.

Nthawi zonse ndimakumbukira mawu a m’Baibulo akuti: “Ndani ali wofooka, ine osakhalanso wofooka?” (2 Akorinto 11:29) Ngakhale kuti ndilibe manja, ndimatha kuganiza bwinobwino komanso kulankhula. Choncho ndimagwiritsa ntchito zimenezi kuti ndizithandiza anthu ena. Komanso ndimamvetsa bwino mavuto a anthu enanso olumala. Ndimayesetsa kulimbikitsa anthu oterewa chifukwa ndimadziwa mmene zimakhalira ukamalakalaka kuchita zinazake koma sungakwanitse. Kuchita zimenezi kumandithandiza kukhala wosangalala.

Kuuza anthu ena uthenga wabwino kumandithandiza kukhala wosangalala

YEHOVA AMANDITHANDIZA TSIKU LILILONSE

Komabe nthawi zina ndimadandaula chifukwa ndimafunitsitsa nditakhala ndi manja ndi mikono ngati mmene anthu ena alili. Ndimatha kuchita zinthu zatsiku ndi tsiku koma pamafunika mphamvu zambiri komanso zimanditengera nthawi yaitali kuti ndimalize. Mfundo imene ndimayendera ndi yakuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.” (Afilipi 4:13) Yehova amandipatsa mphamvu kuti ndikwanitse kuchita zimene ndiyenera kuchita tsiku lililonse. Popeza Yehova sanasiye kundithandiza, inenso sindifuna kusiya kumutumikira.

Yehova wandidalitsa moti panopa ndili ndi banja losangalala. Ndinapeza mkazi wabwino dzina lake Elke, yemwe amandikonda komanso kundisamalira. Komanso a Mboni anzanga padziko lonse ndimawatenga ngati achimwene ndiponso achemwali anga enieni.

Ine ndi mkazi wanga wokondedwa, Elke

Ndimalimbikitsidwanso ndi zimene Mulungu analonjeza zoti m’dziko latsopano adzapanga zinthu zonse kukhala ‘zatsopano,’ kuphatikizapo manja anga. (Chivumbulutso 21:5) Sindikayikira zimenezi ndikaganizira zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Iye ankachiritsa anthu olumala mosavutikira ndipo nthawi ina anabwezeretsa khutu la munthu winawake litadulidwa. (Mateyu 12:13; Luka 22:50, 51) Zimene Yehova analonjeza komanso zomwe Yesu anachita zimanditsimikizira kuti posachedwapa ndikhalanso ndi manja ndiponso mikono.

Koma dalitso lalikulu limene ndapeza ndi kumudziwa bwino Yehova Mulungu. Iye ndi bambo anga komanso mnzanga chifukwa amandilimbikitsa ndiponso kundipatsa mphamvu. Ndili ndi maganizo ofanana ndi Mfumu Davide, yomwe inalemba kuti: “Yehova ndiye mphamvu yanga . . . Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.” (Salimo 28:7) Mfundo imeneyi sindifuna kuiiwala moyo wanga wonse.

^ ndime 17 Kuti mumve zambiri zokhudza zizindikiro za masiku otsiriza, onani mutu 9 wakuti, “Kodi Dzikoli Lithadi Posachedwa?” m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli likupezekanso pawebusaiti ya www.ps8318.com/ny.