Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene Mulungu anatipatsa ndipo lidzathandiza kuti tikhale ndi moyo wosatha

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MPHATSO YAMTENGO WAPATALI KWAMBIRI NDI ITI?

Kodi Mphatso Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse Ndi Iti?

Kodi Mphatso Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse Ndi Iti?

Baibulo limati: “Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo.” (Yakobo 1:17) Vesi limeneli likunena za kuwolowa manja kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Koma pa mphatso zonse zimene Yehova watipatsa, pali mphatso ina imene ndi yaikulu kuposa zonse. Kodi mphatso imeneyi ndi iti? Yankho la funsoli likupezeka m’mawu odziwika bwino a Yesu omwe ali pa Yohane 3:16. Lembali limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”

Choncho mphatso yaikulu kwambiri imene Yehova anatipatsa anthufe, ndi Mwana wake wobadwa yekha. Tikutero chifukwa mphatsoyi ingatithandize kuti timasuke ku ukapolo wa uchimo, ukalamba komanso imfa. (Salimo 51:5; Yohane 8:34) Palibe chimene anthufe tingachite kuti timasuke ku ukapolo wa uchimo, tisamakalambe komanso kuti tisamafe. Koma chifukwa choti Mulungu amatikonda kwambiri, anatipatsa mphatso yapadera. Iye anapereka Mwana wake Yesu Khristu monga dipo n’cholinga choti anthu omvera akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Koma kodi dipo ndi chiyani? N’chifukwa chiyani pankafunika kupereka dipo? Nanga tingatani kuti tipindule ndi dipo limene Yehova anapereka?

Dipo lingatanthauze ndalama kapena katundu amene amaperekedwa n’cholinga choti zinthu zimene zatengedwa zibwezedwe, kapenanso kuti munthu amene wagwidwa amasulidwe. Baibulo limati makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anali angwiro ndipo iwo ndi ana awo amene akanabereka, akanakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. (Genesis 1:26-28) N’zomvetsa chisoni kuti iwo anasankha kusamvera Mulungu ndipo anataya madalitso onsewa moti anakhala ochimwa. Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani? Baibulo limati: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ (Aroma 5:12) Choncho Adamu sanapatsire ana ake moyo wangwiro, koma anawapatsira uchimo komanso zotsatira za uchimowo, zomwe ndi imfa.

Dipo limayenera kukhala lofanana ndendende ndi zinthu zomwe zawonongedwazo. Pamene Adamu anasankha kusamvera Mulungu, anachimwa ndipo zotsatira zake zinali zakuti anataya moyo wake wangwiro. Baibulo limati zimenezi zinachititsa kuti ana ake akhale akapolo a uchimo ndi imfa. Choncho panafunika kuti munthu wina wangwiro apereke moyo wake kuti awombole anthu ku ukapolo umenewu. Munthu ameneyu anali Yesu. (Aroma 5:19; Aefeso 1:7) Mulungu wathu wachikondi analipira dipoli ndipo izi zathandiza kuti anthu akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha umene Adamu anataya. Njira yokhayi ndi imene ingathandize kuti anthu amasuke ku uchimo ndi imfa.​—Chivumbulutso 21:3-5.

Mphatso ya dipo imene Mulungu anatipatsa, ndi mphatso yamtengo wapatali kuposa zonse. Tikutero chifukwa monga taonera, dipo lidzathandiza kuti anthu akhale ndi moyo wosatha. Tsopano tiyeni tione umboni wosonyeza kuti pamene Mulungu ankapereka mphatso imeneyi, anaganizira mfundo 4 zimene takambirana m’nkhani yapita ija. Zimenezi zitithandiza kumvetsa mfundo yoti dipo ndi ‘mphatso yabwino’ kwambiri kuposa zonse.

Imatithandiza kuti tidzapeze zimene timalakalaka. Mwachibadwa anthufe sitifuna kufa koma timalakalaka kuti tikhalabe ndi moyo. (Mlaliki 3:11) Patokha sitingathe kukwaniritsa zimenezi, koma zidzatheka chifukwa cha dipo la Yesu. Baibulo limati: “Malipiro a uchimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”​—Aroma 6:23.

Inathandiza kuti tipeze zimene tikufunikira. Palibe munthu aliyense amene akanatha kutiperekera dipo. Baibulo limati: “Malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali, moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale.” (Salimo 49:8) Choncho tinali ngati anthu osowa mtengo wogwira ndipo Mulungu yekha ndi amene akanatha kutiwombola ku uchimo ndi imfa. Mulungu anachitadi zimenezi ndipo ‘anatimasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.’​—Aroma 3:23, 24.

Anaipereka pa nthawi yoyenera. Baibulo limati: “Pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.” (Aroma 5:8) Popeza Mulungu anapereka dipo “pamene tinali ochimwa,” umenewu ndi umboni wakuti amatikonda kwambiri ngakhale kuti ndife ochimwa. Chifukwa cha dipo, tikuyembekezera zinthu zabwino, ngakhale kuti panopa timakumanabe ndi zotsatira za uchimo.

Anali ndi zolinga zoyenera. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu anapereka Mwana wake monga dipo chifukwa cha chikondi. Limati: “Mulungu anatisonyeza ife chikondi chake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzera mwa iye. Chikondi chimenechi chikutanthauza kuti ife sitinakonde Mulungu, koma iye ndi amene anatikonda.”​—1 Yohane 4:9, 10.

Ndiye kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira mphatso yoposa zonse imene Mulungu anatipatsayi? Kumbukirani kuti mawu a Yesu a pa Yohane 3:16 aja amati “wokhulupirira iye” ndi amene adzapulumuke. Baibulo limati chikhulupiriro ndi “chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Aheberi 11:1) Kuti tikhale ndi chikhulupiriro chimenechi, timafunika kudziwa zolondola. Choncho tikukupemphani kuti mupeze nthawi yophunzira za Yehova Mulungu, amene anatipatsa ‘mphatso yabwino’ kwambiri ya dipo. Mungachitenso bwino kuphunzira kuti mudziwe zimene mungachite kuti mudzakhale ndi moyo wosatha umene udzatheke chifukwa cha dipo la Yesu.

Mungachite zimenezi powerenga komanso kuphunzira mfundo za m’Malemba zomwe zimapezeka pawebusaiti yathu ya www.ps8318.com/ny. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukuthandizani. Tikukhulupirira kuti mukaphunzira zokhudza mphatso yaikulu imene Mulungu anatipatsayi n’kuyamba kupindula nayo, mudzathokoza Mulungu amene “kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu,” anakonza njira yotipulumutsira.​—Aroma 7:25.