MBIRI YA MOYO WANGA
Ndine Msilikali wa Khristu
Pamene zipolopolo zinkalakatika n’kumagwera pafupi ndi pamene ndinabisala, ndinakweza m’mwamba kampango kanga koyera. Asilikali anandiitana kuti ndituluke pamene ndinabisalapo. Ndinayenda mwamantha kupita kumene anali ndipo sindinkadziwa kuti andisiya ndi moyo kapena ayi. Dikirani ndifotokoze zomwe zinachitika kuti ndikumane ndi zimenezi.
NDINABADWA m’chaka cha 1926. M’banja mwathu tinalimo ana 8 ndipo ineyo ndi wa nambala 7. Tinkakhala m’mudzi wina waung’ono wotchedwa Karítsa m’dziko la Greece ndipo makolo anga anali olimbikira ntchito.
Mu 1925, makolo anga anakumana ndi a John Papparizos omwe anali a Mboni za Yehova. Pa nthawiyo ankatchedwa Ophunzira Baibulo. A John anali akhama komanso okonda kulankhula. Makolo anga anasangalala ndi mfundo za m’Malemba zimene a John ankawaphunzitsa ndipo anayamba kusonkhana. Mayi ankakhulupirira kwambiri Yehova ndipo ngakhale kuti sankadziwa kuwerenga, ankayesetsa kufotokozera ena zimene ankaphunzira. N’zomvetsa chisoni kuti bambo anga anasiya kusonkhana chifukwa choti ankaganizira kwambiri zimene abale ena ankalakwitsa.
Ngakhale kuti ine ndi abale anga tinkakonda kwambiri mfundo za m’Baibulo, tinatengeka ndi zimene achinyamata ambiri ankachita moti tinasiya kuphunzira Baibulo. Koma mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayamba ku Europe, panachitika zinthu zina zimene sitinkayembekezera. Wachibale wathu wina dzina lake Nicolas Psarras, yemwe anali atangobatizidwa kumene, anakakamizidwa kuti alowe usilikali. Pa nthawiyo Nicolas anali ndi zaka 20 ndipo anauza asilikaliwo molimba mtima kuti: “Sindingapite kunkhondo chifukwa ndine msilikali wa Khristu.” Khoti la asilikali linamuweruza kuti akakhale m’ndende kwa zaka 10 ndipo zimenezi zinatikhudza kwambiri.
Chakumayambiriro kwa chaka cha 1941, asilikali amene ankamenyana ndi dziko la Greece anafika ndipo izi zinachititsa kuti Nicolas atulutsidwe
m’ndende. Atabwerera ku Karítsa, mchimwene wanga wamkulu dzina lake Ilias anamufunsa mafunso ambirimbiri okhudza Baibulo. Ndinkamvetsera mwachidwi zimene ankafotokoza. Patapita nthawi, ineyo, Ilias komanso mchemwali wanga wamng’ono dzina lake Efmorfia, tinayamba kuphunzira Baibulo ndiponso kusonkhana. Chaka chotsatira, tonse tinabatizidwa. Kenako azichimwene anga awiri komanso azichemwali anga awiri nawonso anakhala a Mboni.Mu 1942, mumpingo wa Karítsa tinalimo achinyamata azaka za pakati pa 15 ndi 25 okwana 9. Tonse tinkadziwiratu kuti tikumana ndi mayesero. Choncho kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu, tinkakumana n’kumaphunzira Baibulo, kuimba nyimbo komanso kupemphera. Izi zinalimbitsadi chikhulupiriro chathu.
NKHONDO YAPACHIWENIWENI
Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatsala pang’ono kutha, anthu ena a ku Greece anaukira boma ndipo nkhondo yapachiweniweni inayambika. Anthu oukira bomawo anali ponseponse ndipo ankakakamiza anthu kuti akhale kumbali yawo. Atafika m’mudzi wathu, ananditengaineyo, Ilias ndiponso M’bale Antonio Tsoukaris. Tinawauza kuti ndife Akhristu ndipo sitimenya nkhondo koma sanatimvere. Anayenda nafe ulendo wa maola 12 kupita kuphiri la Olympus.
Titafika, msilikali wina anatiuza kuti tilowe m’gulu loukiralo. Titanena kuti ndife Akhristu ndipo sitimenya nkhondo, anakwiya kwambiri n’kutitengera kwa mkulu wawo. Titafotokoza mbali yathu kwa mkulu wawoyo, anatiuza kuti: “Ngati ndi choncho ndiye muziyenda pa bulu n’kumakatenga asilikali ovulala kupita nawo kuchipatala.”
Ndiye tinamufunsa kuti: “Nanga asilikali a boma akatipeza, kodi sangaganize kuti ndife oukira boma?” Iye anayankha kuti: “Chabwino, ndiye muzikangoperekera chakudya kunkhondoko.” Ndiyeno tinamufunsa kuti: “Kodi asilikali akationa tili ndi bulu, sangatiuze kuti titenge zida kukapereka kwa asilikali amene akumenya nkhondo?” Titatero, mkulu wa asilikaliyo anakhala phee kwa nthawi yaitali. Kenako anati: “Ndamvetsa. Ndiye ndikupatsani ntchito yodyetsa nkhosa m’phiri mommuno.”
Tonse atatu tinaona kuti ntchito yodyetsa nkhosayi sinali yosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Chaka chotsatira, Ilias analoledwa kupita kunyumba kuti azikasamalira mayi anga chifukwa choti bambo anali atamwalira. Nayenso Antonio anauzidwa kuti azipita chifukwa choti ankadwala. Koma ine sanandilole kupita.
Kenako asilikali a boma ankakula mphamvu kwambiri moti gulu loukira lija linayamba kuthawa kudutsa m’mapiri kupita ku Albania. Pothawapo ananditenga koma kenako tinangopezeka kuti tazunguliridwa ndi asilikali a boma. Oukirawo anapanikizika kwambiri moti anathawa. Ine ndinabisala pamtengo umene unagwera penapake. Apa m’pamene panachitika zimene ndafotokoza kumayambiriro kuja.
Nditafotokozera asilikali a boma aja kuti oukirawo anachita kundigwira, ananditengera kukampu
yawo pafupi ndi mzinda wa Véroia womwe m’Baibulo umatchedwa Bereya. Kumeneko anandifunsa mafunso ambirimbiri kenako anandiuza kuti ndizikumba maenje oti asilikali azibisalamo. Nditakana, mkulu wa asilikali a bomawo ananditumiza pakachilumba kotchedwa Makrónisos.MOYO WAPACHILUMBA UNALI WOVUTA
Kachilumbaka kanali ka makilomita 13 m’litali ndi makilomita awiri ndi hafu m’lifupi. Kachilumba kameneka kanapangidwa ndi mwala wotchedwa Makrónisos ndipo kanali m’mphepete mwa nyanja pa mtunda wa makilomita 50 kuchokera ku Athens. Koma kuyambira mu 1947 kufika mu 1958, pakachilumbapa panali akaidi okwana 100,000. Ena anali oukira boma pomwe ena ankangokayikiridwa kuti anaukira boma. Koma panalinso a Mboni za Yehova okhulupirika.
Nditafika chakumayambiriro kwa 1949, akaidi anagawidwa m’makampu angapo. Ine anandiika kumbali imene kunalibe chitetezo champhamvu ndipo kunali anthu ambirimbiri. Ndinkakhala ndi anthu pafupifupi 40 mutenti yokhala anthu 10 okha. Nthawi zambiri tinkangodya mphodza ndi mabiringano ndipo madzi amene tinkamwa anali onunkha. Kunkawomba mphepo yambiri ndipo fumbi linali paliponse. Komabe tinkaona kuti bola, chifukwa anthu ambiri ankawapatsa ntchito yogubuduza miyala koma ife sanatiuze kuti tizichita zimenezo.
Tsiku lina ndikuyenda m’mphepete mwa nyanja ndinakumana ndi a Mboni a m’makampu ena ndipo tinasangalala kwambiri. Tinkasonkhana komanso tinkalalikira koma tinkachita zimenezi mosamala ndi mochenjera kwambiri. Akaidi ena amene tinawalalikira anadzakhala a Mboni. Zimene tinkachitazi komanso kupemphera zinatithandiza kuti tisafooke.
MUNG’ANJO YAMOTO
Patatha miyezi 10, amene ankatiyang’anira anandiuza kuti ndizivala yunifomu ya asilikali. Nditakana, ananditengera kwa mkulu woyang’anira kampu yathu. Ndinamupatsa mkuluyo chikalata chofotokoza kuti: “Ineyo ndikufuna kukhala msilikali wa Khristu basi.” Atandiopseza ananditumiza kwa wachiwiri wake yemwe anali bishopu wachipembedzo cha Greek Orthodox. Ndinayankha molimba mtima mafunso onse a m’Malemba omwe bishopuyu anandifunsa. Iye anakwiya n’kunena kuti: “M’chotseni munthu ameneyu pano, ndi wamakani pa nkhani yachipembedzo chake!”
Tsiku lotsatira asilikali anandiuzanso kuti ndivale yunifomu. Nditakana anandimenya ndi zibagera komanso ndodo. Kenako ananditengera kukachipatala ka pakampupo kuti akaone ngati sindinathyoke mafupa. Atatero anakandisiya mutenti imene ndinkakhala. Ankandichita zimenezi tsiku lililonse kwa miyezi iwiri.
Popeza sindinkalola kusiya zimene ndimakhulupirira, asilikaliwo anakwiya kwambiri ndipo anaganiza zoyesa njira ina. Anandimanga manja kumbuyo n’kumandimenya m’mapazi ndi zingwe. Ndikumva ululu wosaneneka, ndinakumbukira mawu a Yesu akuti: “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani. . . . Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:11, 12) Anachita izi kwa nthawi yaitali kwambiri mpaka ndinakomoka.
Ndinatsitsimukira muselo ina yozizira kwambiri ndipo munalibe chakudya, madzi komanso chofunda. Ngakhale zinali choncho, sindinkada nkhawa kwambiri ndipo mtima wanga unali m’malo. Monga mmene Baibulo limalonjezera, “mtendere wa Mulungu” unateteza ‘mtima wanga ndi maganizo anga.’ (Afil. 4:7) Tsiku lotsatira msilikali wina wokoma mtima anandipatsa chakudya, madzi ndi jasi. Kenako msilikali winanso anandipatsa chakudya chake. Apa ndinaonanso kuti Yehova akundisamalira.
Akuluakulu a boma ankandiona ngati chigawenga choukira. Choncho ananditumiza ku Athens kuti ndikaweruzidwe ndi khothi la asilikali. Kumeneko anandigamula kuti ndikakhale m’ndende yapachilumba cha Gyaros kwa zaka zitatu. Chilumbachi chinali pa mtunda wa makilomita 50 chakum’mawa kwa Makrónisos.
“SI INU OKAYIKITSA”
Ndendeyi inali mumpanda wa njerwa ndipo munali akaidi oposa 5,000 omwe anamangidwa pa zifukwa za ndale. Munalinso a Mboni za Yehova 7 amene anamangidwa chifukwa chokana kumenya nkhondo. Ankatiletsa kusonkhana koma tinkayesetsa kusonkhana mobisa. Anthu ena ankatibweretsera magazini
a Nsanja ya Olonda ndipo tinkawakopera pamanja kuti tizigwiritsa ntchito pophunzira.Tsiku lina tikusonkhana, msilikali woyang’anira ndende anatulukira n’kutilanda zimene tinkagwiritsa ntchito pophunzira. Kenako anatitengera ku ofesi ya wachiwiri kwa mkulu wa asilikaliwo. Tinkaganiza kuti awonjezera zaka za ukaidi wathu. Koma wachiwiri kwa mkulu wa asilikaliyo anati: “Timakudziwani bwinobwino. Ndipo timalemekeza maganizo anu. Tikudziwa kuti si inu okayikitsa. Pitani muzikagwira ntchito.” Iye anachepetsanso ntchito zimene enafe tinkagwira ndipo tinasangalala kwabasi. Kukhalabe okhulupirika kundendeku kunathandiza kuti Yehova atamandike.
Pali zinthu zinanso zabwino zimene zinachitika chifukwa choti tinakhalabe okhulupirika. Mwachitsanzo, mkaidi wina, yemwe anali mphunzitsi wamkulu wa masamu, ataona kuti tili ndi khalidwe labwino anayamba kutifunsa mafunso. Titamasulidwa chakumayambiriro kwa 1951, nayenso anamasulidwa. Patapita nthawi anabatizidwa ndipo anakhala mpainiya wokhazikika.
NDIDAKALI MSILIKALI
Nditamasulidwa ndinabwerera kwathu ku Karítsa. Patapita nthawi, ineyo ndi achibale anga tinasamukira mumzinda wa Melbourne ku Australia. Kumeneku ndinakumana ndi mlongo wina wabwino kwambiri dzina lake Janette ndipo tinakwatirana. Tili ndi ana 4, aakazi atatu ndi wamwamuna ndipo onse ndi obatizidwa.
Panopa ndili ndi zaka zoposa 90 koma ndikutumikirabe monga mkulu. Nthawi zina ndikayenda kupita kolalikira, thupi ndi mapazi zimandipweteka chifukwa cha kumenyedwa kuja. Komabe ndidakali “msilikali wa Khristu” ndipo sindidzasiya.—2 Tim. 2:3.