Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mawu akuti kuika chizindikiro a pa 2 Atesalonika 3:14, akunena zimene mpingo uyenera kuchita, kapena zimene Mkhristu aliyense payekha ayenera kuchita?

Mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Tesalonika kuti: “Ngati wina sakumvera mawu athu amene ali mʼkalatayi, muikeni chizindikiro.” (2 Ates. 3:14) Poyamba tinkanena kuti malangizowa amapita kwa akulu. Ngati munthu wina sakutsatira mfundo za m’Baibulo pambuyo popatsidwa malangizo mobwerezabwereza, akulu ankamuika chizindikiro pokamba nkhani yochenjeza mpingo. Zikatero ofalitsa onse ankasiya kucheza naye.

Komabe pakufunika kusintha mmene tinkamvera lembali. Zikuoneka kuti malangizo a Paulowa akufotokoza zimene Mkhristu aliyense payekha ayenera kuchita mogwirizana ndi mmene zinthu zilili. Choncho palibenso chifukwa choti akulu azikambira nkhani yochenjeza mpingo. N’chifukwa chiyani pali kusintha kumeneku? Tiyeni tione zimene Paulo ankanena popereka malangizowa.

Paulo anazindikira kuti ena mumpingowo ‘ankayenda mosalongosoka.’ Iwo ankakana kutsatira mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu. Pa ulendo wake wina, Paulo anapereka malangizo akuti: “Ngati wina sakufuna kugwira ntchito, asadye.” Komabe ena sankafuna kugwira ntchito kuti azipeza zinthu zofunika pa moyo wawo ngakhale kuti akanakwanitsa kuchita zimenezo. Ndiponso iwo ankalowerera nkhani za ena. Kodi Akhristu ankafunika kuchita bwanji ndi anthu oterewa?​—2 Ates. 3:6, 10-12.

Paulo anati: “Muikeni chizindikiro.” Mawu a Chigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito palembali amanena za kuchita zinthu mosamala ndi munthuyo. Paulo anapereka malangizowa kumpingo wonse osati kwa akulu okha. (2 Ates. 1:1; 3:6) Choncho Mkhristu aliyense payekha akaona Mkhristu wina asakutsatira malangizo a m’Malemba angasankhe ‘kusiya kugwirizana’ ndi munthu wosalongosokayo.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthuyo ankaonedwa ngati wochotsedwa? Ayi, chifukwa Paulo anawonjezera kuti: “Pitirizani kumulangiza monga mʼbale.” Choncho Mkhristu aliyense ankatha kulankhula ndi munthuyo pamisonkhano komanso kulowa naye mu utumiki koma ankapewa kuchita naye zinthu zina monga zosangalatsa. N’chifukwa chiyani? Paulo anati: “Kuti [munthuyo] achite manyazi.” Kuikidwa chizindikiro kukanachititsa munthuyo kuti achite manyazi n’kusintha khalidwe lake.​—2 Ates. 3:14, 15.

Kodi Akhristu angatsatire bwanji malangizowa? Choyamba, tiyenera kutsimikiza kuti khalidwe la munthuyo ndi ‘losalongosokadi’ mogwirizana ndi zimene Paulo anafotokoza. Iye sankanena za anthu amene timasiyana nawo pa nkhani zokhudza chikumbumtima kapena zimene timakonda. Sankanenanso za anthu omwe angotikhumudwitsa. M’malomwake, Paulo ankanena za anthu amene mwadala amasankha kuti asamamvere malangizo omveka bwino opezeka m’Mawu a Mulungu.

Masiku anonso ngati taona Mkhristu wina amene akusonyeza kuti sakufuna kumvera malangizo a Mulungu, a tingasankhe kuti tisamacheze naye kapena kuchita naye zinthu zosangalatsa. Popeza kuti aliyense ayenera kusankha yekha zochita, sitiyenera kukambirana zokhudza nkhaniyi ndi aliyense yemwe si wam’banja lathu. Komanso tingapitirize kuchita naye zinthu pamisonkhano ndi mu utumiki. Akasintha khalidwe lakelo, tingayambirenso kuchita naye zinthu ngati kale.

a Mwachitsanzo, Mkhristu angakane kugwira ntchito kuti azipeza zinthu zofunika ngakhale kuti angakwanitse. Mwinanso angakakamire kuchita chibwenzi ndi wosakhulupirira kapena angamafalitse nkhani zoipa zomwe zingachititse kuti anthu asamagwirizane mwinanso miseche. (1 Akor. 7:39; 2 Akor. 6:14; 2 Ates. 3:11, 12; 1 Tim. 5:13) Anthu amene amapitiriza kuchita makhalidwe ngati amenewa, ndi ‘osalongosoka.’