Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Alisa

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Turkey

Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Turkey

AKHRISTU oyambirira ankayesetsa kulalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” kwa anthu osiyanasiyana. (Mat. 24:14) Akhristu ena ankapita m’mayiko ena. Mwachitsanzo, pa maulendo ake aumishonale mtumwi Paulo anakalalikira kwambiri kudera limene panopa ndi dziko la Turkey. * Mu 2014, ku Turkey kunagwiridwanso ntchito yapadera yolalikira ndipo apa n’kuti patapita zaka pafupifupi 2,000 kuchokera nthawi imene Paulo analalikira kuderali. N’chifukwa chiyani kunali ntchito yapaderayi? Nanga ndani anaigwira?

“KODI CHIKUCHITIKA N’CHIYANI?”

Ku Turkey kuli ofalitsa oposa 2,800 koma dzikoli lili ndi anthu 79 miliyoni. Apa ndiye kuti wofalitsa mmodzi ayenera kulalikira anthu oposa 28,000. Chifukwa cha zimenezi anthu ambiri m’dzikoli sakhala ndi mwayi womva uthenga wabwino. Cholinga cha ntchito yapaderayi chinali choti anthu ambiri amve uthengawu pa nthawi yochepa. Abale ndi alongo pafupifupi 550 ochokera m’mayiko osiyanasiyana omwe amalankhula Chitekishi anapita ku Turkey kukalalikira limodzi ndi ofalitsa akumeneko. Kodi n’chiyani chinachitika pa ntchito yapaderayi?

Analalikira kwa anthu ambirimbiri. Mpingo wina wa ku Istanbul unalemba kuti: “Anthu atationa ankafunsa kuti: ‘Kodi pali msonkhano wapadera? Paliponse tikungoona a Mboni za Yehova.’” Mpingo wamumzinda wa Izmir unalemba kuti: “Munthu wina woyendetsa taxi anafunsa mkulu wina kuti, ‘Kodi chikuchitika n’chiyani? Ndikuona anthu ambiri akulalikira.’” Uwutu ndi umboni wakuti anthu anazindikira zoti pali ntchito yapadera.

Steffen

Anthu ochokera kumayiko ena anasangalalanso kugwira ntchitoyi. M’bale Steffen wochokera ku Denmark anati: “Tsiku lililonse ndinkalalikira kwa anthu amene sanamvepo za Yehova. Mumtimamu ndinkamva kuti ndikuthandizadi anthu kudziwa dzina la Yehova.” M’bale Jean-David wa ku France analemba kuti: “Zinali zosangalatsa kwambiri kulalikira kwa anthu ambiri amene sankadziwa za a Mboni za Yehova. Tinalalikira kunyumba za m’mbali mwa msewu umodzi wokha kwa nthawi yaitali. Pafupifupi pakhomo lililonse tinkakambirana ndi anthu, kuwaonetsa mavidiyo komanso kuwapatsa mabuku.”

Jean-David (pakati)

Pa milungu iwiri yokha, ofalitsa 550 amene anagwira ntchitoyi anagawira zinthu pafupifupi 60,000. Ntchito yapaderayi inathandiza kuti alalikire kwa anthu ambirimbiri.

Akhristu ambiri anayamba kukonda kulalikira. Ntchito yapaderayi inathandiza abale ndi alongo kuti ayambe kukonda kulalikira moti ambiri anaganiza zoyamba utumiki wa nthawi zonse. Pamene chaka chinkatha, chiwerengero cha apainiya okhazikika chinawonjezeka ndi 24 peresenti.

Şirin

Akhristu ochokera m’mayiko ena anafotokozanso mmene anamvera pambuyo pa ntchito yapaderayi. Mlongo wina wa ku Germany dzina lake Şirin analemba kuti: “Abale ndi alongo ambiri ku Turkey amamasuka kulalikira mwamwayi pomwe ine ndi wamanyazi. Koma ntchito yapaderayi, chitsanzo cha abale akumeneko komanso kupemphera zinandithandiza kuti ndichite zinthu zimene poyamba sindikanakwanitsa. Mwachitsanzo, ndinatha kulalikira komanso kugawira timapepala kwa anthu amene ndinakwera nawo sitima. Panopa manyazi anga anachepa.”

Johannes

Mlongo wina wa ku Germany dzina lake Johannes ananena kuti: “Ndaphunzira zambiri pa nkhani ya utumiki. Abale ndi alongo a ku Turkey ali ndi mtima wofuna kulalikira kwa anthu ambirimbiri. Amagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti alalikire. Nditabwerera ku Germany ndinayambanso kuchita zomwezo. Panopa ndimalalikira anthu ambiri kuposa kale.”

Zeynep

Mlongo Zeynep wa ku France ananena kuti: “Ndasintha kwambiri chifukwa cha ntchito yapaderayi. Yandithandiza kukhala wolimba mtima komanso kuti ndizidalira kwambiri Yehova.”

Abale ndi alongo anayamba kugwirizana kwambiri. Zinali zochititsa chidwi kuona abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana akugwirizana kwambiri. M’bale Jean-David amene tamutchula kale uja anati: ‘Tinazindikira kuti abale athu alidi ndi mtima wopatsa. Ankatitenga ngati anzawo apamtima ndiponso abale awo enieni ndiponso ankatiitanira kunyumba zawo. Kwa nthawi yaitali, ndinkangowerenga m’mabuku athu kuti tili pa ubale wapadziko lonse koma panopa ndaona ndi maso anga. Ndimayamikira kwambiri kukhala wa Mboni za Yehova ndipo ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri.’

Claire (pakati)

Mlongo Claire wa ku France anati: “Tinali anthu a m’mayiko osiyanasiyana monga Denmark, France, Germany komanso Turkey koma tinkakhala ngati a banja limodzi. Zinali ngati Mulungu watenga chilabala chachikulu n’kufufuta malire a mayiko.”

Stéphanie (pakati)

Mlongo Stéphanie wa ku France ananena kuti: “Ntchito yapaderayi inatithandiza kudziwa kuti Akhristufe timagwirizana chifukwa choti tonse timakonda Yehova osati chifukwa cha chikhalidwe kapena chilankhulo.”

AKUTHANDIZA KWAMBIRI

Abale ndi alongo ochokera m’mayiko ena amene anagwira nawo ntchitoyi anaganiza zongosamukira ku Turkey kuti akathandize pa ntchito yaikulu imene idakalipo. Panopa, ena anasamukirako ndipo akuthandiza anthu kwambiri.

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi kagulu kena kamene kanali ndi ofalitsa 25. Kwa zaka zambiri kunali mkulu mmodzi yekha. Koma mu 2015 anthu 6 ochokera ku Germany ndi ku Netherlands anasamukirako kuti akathandize.

TIMAKHALA PATSOGOLO PA NTCHITO YOLALIKIRA

Kodi abale ndi alongo amene anasamukira ku Turkey amati bwanji? N’zoona kuti nthawi zina amakumana ndi mavuto ena koma moyo wake ndi wosangalatsa kwambiri. Taonani zimene ena ananena:

Federico

M’bale wina wa ku Spain yemwe anasamukira kudzikoli, dzina lake Federico, ndipo ali ndi zaka za m’ma 40 komanso ali pa banja, ananena kuti: “Panopa ndilibe zinthu zambiri ndipo zimenezi zimandipatsa mpata woganizira zinthu zofunika kwambiri.” Kodi iye amalimbikitsa ena kusamukira kudziko lina? M’baleyu anayankha kuti: “Ee kwambiri. Ukasamukira kudziko lina kuti ukathandize anthu kudziwa za Yehova zimakhala ngati wadzipereka m’manja mwake kuti azikusamalira. Umaona Yehova akukuthandiza kuposa kale.”

Rudy

M’bale wina wochokera ku Netherlands dzina lake Rudy, yemwe ali ndi zaka za m’ma 50 ndiponso ali pa banja, ananena kuti: “Timasangalala kwambiri chifukwa timatsogolera pa ntchito yolalikira ndipo timaphunzitsa choonadi anthu ambiri amene sanamvepo za Yehova. Timamva bwino tikaona anthu akusangalala kwambiri chifukwa chophunzira choonadi.”

Sascha

M’bale wina wa ku Germany dzina lake Sascha yemwe ali ndi zaka za m’ma 40 ndipo alinso pa banja anati: “Nthawi iliyonse ndikalowa mu utumiki ndimakumana ndi anthu amene sanamvepo choonadi. Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza anthu ngati amenewa kuti adziwe za Yehova.”

Atsuko

Mlongo wina wa ku Japan dzina lake Atsuko, yemwe ali ndi zaka za m’ma 30 ndipo ali pa banja, anati: “M’mbuyomu ndinkafuna kuti Aramagedo ibwere mwamsanga. Koma nditasamukira ku Turkey ndinayamba kuona kuti Yehova akuchita bwino kuleza mtima. Ndikaona mmene Yehova akuchitira zinthu ndimafunitsitsa kulimbitsa kwambiri ubwenzi wanga ndi iye.”

Mlongo wina wa ku Russia dzina lake Alisa, yemwe ali ndi zaka za m’ma 30, ananena kuti: “Kuchita utumiki umenewu kwandithandiza kudziwa kuti Yehova ndi wabwinodi.” (Sal. 34:8) Iye ananenanso kuti: “Yehova ndi Atate wanga komanso Mnzanga wapamtima ndipo zinthu zosiyanasiyana zimene ndimakumana nazo zimathandiza kuti ubwenziwu uzilimba. Masiku ano moyo wanga ndi wosangalatsa ndipo ndimaona kuti Yehova amandidalitsa m’njira zosiyanasiyana.”

“MUONE M’MINDAMO”

Ntchito yapadera yolalikira ku Turkey inathandiza kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino. Koma padakali madera ambiri amene sanalalikidwe. Tsiku lililonse, abale ndi alongo amene anasamukira ku Turkey amakumana ndi anthu amene sanamvepo za Yehova. Kodi inuyo mungakonde kulalikira kudera langati limeneli? Ngati ndi choncho tikukulimbikitsani kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Mwina mungasamukire kudera kapena dziko limene lili ngati ‘munda woti wayera kale ndipo ukufunika kukolola.’ Kuti zimenezi zitheke, mungachite bwino kuyamba kukonzekera panopa. Chomwe muyenera kudziwa n’chakuti kuwonjezera nthawi imene mumalalikira uthenga wabwino “mpaka kumalekezero a dziko lapansi” kudzathandiza kuti mudalitsidwe kwambiri.​—Mac. 1:8.

^ ndime 2 Onani kabuku kakuti “Onani Dziko Lokoma,” tsamba 32 ndi 33.