Mungatani Kuti Mukhalebe Olimba Mwauzimu mu Mpingo wa Chilankhulo China?
“Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga.”—SAL. 119:11.
NYIMBO: 142, 92
1-3. (a) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, kodi tiyenera kuona kuti chofunika kwambiri n’chiyani? (b) Kodi anthu amene ali mumpingo wa chilankhulo china amakumana ndi mavuto ati, nanga tikambirana mafunso ati? (Onani chithunzi pamwambapa.)
MASIKU ano, abale ndi alongo ambiri akuthandiza pokwaniritsa ulosi woti uthenga wabwino udzalalikidwa “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.” (Chiv. 14:6) Kodi inuyo mukuphunzira chilankhulo china? Kodi ndinu mmishonale kapena mumasonkhana mumpingo wa chilankhulo china?
2 Atumiki a Yehovafe tiyenera kuzindikira kuti chofunika kwambiri n’kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso cha banja lathu. (Mat. 5:3) Nthawi zina tingatanganidwe kwambiri moti sitingapeze nthawi yophunzira patokha bwinobwino. Koma anthu amene amasonkhana mumpingo wa chilankhulo china amakhalanso ndi mavuto ena.
3 Iwo amafunika kuphunzira chilankhulo chatsopano komanso kuonetsetsa kuti mfundo zozama za m’Mawu a Mulungu zikuwafika pamtima. (1 Akor. 2:10) Kodi angachite bwanji zimenezi ngati samva bwinobwino chilankhulo cha mpingo umene akusonkhana? Nanga makolo achikhristu angathandize bwanji ana awo kuti Mawu a Mulungu aziwafika pamtima?
CHIKHULUPIRIRO CHATHU CHINGAFOOKE
4. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba? Perekani chitsanzo.
4 Munthu amene ali mumpingo wa chilankhulo china angamalephere kumvetsa bwino mfundo za m’Mawu a Mulungu ndipo izi zingapangitse kuti chikhulupiriro chake chifooke. M’zaka za m’ma 400 B.C.E. Nehemiya anada nkhawa ataona kuti ana ambiri a Ayuda amene anabwerera kuchokera ku Babulo sankadziwa Chiheberi. (Werengani Nehemiya 13:23, 24.) Apa anawa akanataya mwayi wokhala atumiki a Mulungu chifukwa sankamvetsa bwino Mawu a Mulungu.—Neh. 8:2, 8.
5, 6. Kodi makolo ena amene akusonkhana mumpingo wa chilankhulo china azindikira chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
5 Makolo ena amene amasonkhana mumpingo wa chilankhulo china amazindikira kuti chikhulupiriro cha ana awo chayamba kufooka. Chifukwa chakuti anawo samvetsa bwinobwino zonse zimene zikunenedwa pamisonkhano ya mpingo, Mawu a Mulungu sawafika pamtima. M’bale wina dzina lake Pedro, [1] amene anasamuka limodzi ndi banja lake kuchoka ku South America n’kupita ku Australia, anati: “Kuti ubwenzi wathu ndi Mulungu ukhale wolimba, pamafunika kuti Mawu a Mulungu azitifika pamtima.”—Luka 24:32.
6 Tikamawerenga nkhani m’chilankhulo china, mwina zimene tikuwerengazo sizingatifike pamtima kwenikweni. Komanso munthu akamalephera kulankhulana bwinobwino ndi anthu achilankhulo china, amafika potopa nazo komanso chikhulupiriro chimayamba kuchepa. Choncho munthu amene akufuna kusamukira mumpingo wa chilankhulo china, ayenera kuganiziranso za moyo wake wauzimu.—Mat. 4:4.
ANAYESETSA KUTI AKHALEBE NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA
7. Kodi anthu a ku Babulo anachita zotani pofuna kuti Danieli atengere chikhalidwe komanso chipembedzo chawo?
7 Pamene Danieli ndi anzake anali ku ukapolo, Ababulo anawaphunzitsa “chinenero cha Akasidi” n’cholinga choti azitsatira chikhalidwe chawo. Komanso mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina achibabulo. (Dan. 1:3-7) Dzina limene anamupatsa Danieli linkanena za mulungu wa Ababulowo dzina lake Beli. N’kutheka kuti Nebukadinezara ankafuna kuti Danieli aziganiza kuti Yehova anagonjetsedwa ndi mulungu wa Ababulo.—Dan. 4:8.
8. N’chiyani chinathandiza Danieli kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba pamene anali kudziko lina?
8 Ngakhale kuti Danieli anapatsidwa mwayi woti azidya zakudya za mfumu, “anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa.” (Dan. 1:8) Komanso iye anapitirizabe kuphunzira “mabuku” a chilankhulo chake. (Dan. 9:2) Izi zinamuthandiza kuti akhalebe ndi chikhulupiriro cholimba. Choncho patatha zaka 70 kuchokera pamene anafika ku Babulo, ankadziwikabe ndi dzina lake lachiheberi.—Dan. 5:13.
9. Kodi Salimo 119 likusonyeza kuti Mawu a Mulungu anathandiza bwanji amene analemba Salimoli?
9 Munthu amene analemba Salimo 119 ankaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama. Izi zinamuthandiza kuti asamachite zinthu zoipa zimene ena ankachita. Zinamuthandizanso kuti apirire zoipa zimene anthu ena a m’banja lachifumu ankamuchitira. (Sal. 119:23, 61) Iye ankayesetsanso kuti Mawu a Mulungu azimufika kwambiri pamtima.—Werengani Salimo 119:11, 46.
YESETSANI KUTI MUKHALEBE NDI CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA
10, 11. (a) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu, kodi cholinga chathu chizikhala chiyani? (b) Kodi tingatani kuti zimenezi zitheke? Perekani chitsanzo.
10 Ngakhale kuti timatanganidwa kwambiri ndi zinthu zokhudza kulambira komanso zinthu zina, tonsefe tiyenera kuyesetsa kuti tizipeza nthawi yophunzira patokha ndiponso yochita kulambira kwa pabanja. (Aef. 5:15, 16) Cholinga chathu chisamakhale choti timalize masamba ambiri kapena tingopeza zoti tikayankhe pamisonkhano. Koma tiziyesetsa kuti Mawu a Mulungu azitifika pamtima ndiponso azitithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu.
11 Kuti zimenezi zitheke, tisamangoganizira zimene tingachite kuti tithandize ena. Tiyenera kuganiziranso zoyenera kuchita kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova. (Afil. 1:9, 10) Tizidziwa kuti tikamakonzekera utumiki, misonkhano kapena nkhani, nthawi zambiri timangoganizira mmene mfundozo zingathandizire anthu ena osati ifeyo. Mwachitsanzo, munthu amene amaphika, amalawa zakudyazo asanazipereke kwa anthu ena. Koma sikuti iyeyo amangodalira zimene amalawazo. Kuti thupi lake lisafooke, amayenera kudya chakudya chopatsa thanzi. Ifenso tiziyesetsa kuphunzira Mawu a Mulungu m’njira yoti azitifika pamtima n’cholinga choti tilimbitse chikhulupiriro chathu.
12, 13. N’chifukwa chiyani anthu ambiri amene ali m’gawo la chilankhulo china amaona kuti ndi bwino kuti aziphunziranso Mawu a Mulungu m’chilankhulo chawo?
12 Anthu ambiri amene ali m’gawo la chilankhulo china, amaphunzira Baibulo ‘m’chilankhulo chimene anabadwa nacho’ ndipo amaona kuti zimenezi zimawathandiza. (Mac 2:8) Nawonso amishonale amapewa kungodalira mfundo zochepa zimene amamva pamisonkhano chifukwa izi zingapangitse kuti asakhalenso olimba mwauzimu.
13 Alain amene waphunzira Chiperisiya kwa zaka 8 anati: “Ndikamakonzekera misonkhano m’Chiperisiya, ndimangoganizira za mawu oyenera kugwiritsa ntchito. Popeza ndimangoganizira zimene ndingachite kuti ndichidziwe bwino chilankhulocho, zimene ndikuwerengazo sizindifika kwenikweni pamtima. N’chifukwa chake ndimayesetsa kuti ndizipezanso nthawi yophunzira Baibulo ndi mabuku a m’chilankhulo changa.”
KODI MAWU A MULUNGU AMAWAFIKA PAMTIMA ANA ANU?
14. Kodi makolo ayenera kuyesetsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
14 Makolo achikhristu ayenera kuonetsetsa kuti Mawu a Mulungu akuwafika pamtima ana awo. Chitsanzo ndi m’bale wina dzina lake Serge ndi mkazi wake Muriel, omwe chilankhulo chawo ndi Chifulenchi. Iwo anakhala kugawo la chilankhulo china kwa zaka zoposa zitatu. Kenako anazindikira kuti mwana wawo wa zaka 17 sankasangalala kwenikweni ndi zinthu zokhudza kulambira. A Muriel anati: “Tinaona kuti sankakonda kukalalikira m’chilankhulo china pomwe poyamba ankasangalala kwambiri kulalikira m’Chifulenchi.” A Serge anafotokoza kuti: “Titazindikira za vutoli, tinaganiza zobwerera kumpingo wathu wakale.”
15. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse makolo kusankha zobwerera kumpingo wa chilankhulo chimene ana awo amamva? (b) Kodi pa Deuteronomo 6:5-7 pali malangizo otani opita kwa makolo?
15 Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse makolo kuganiza zobwerera kumpingo wachilankhulo chimene ana awo amadziwa? Choyamba, ngati sakutha kupeza nthawi yokwanira komanso zinthu zimene zingawathandize pophunzitsa ana awo kukonda Yehova kwinaku akuwaphunzitsanso chilankhulo china. Chachiwiri, ngati akuona kuti anawo sakukonda kulalikira m’gawo la chilankhulo china kapena sakusangalala ndi zinthu zokhudza kulambira. Zikatere, kubwerera kumpingo wachilankhulo chimene anawo amachidziwa bwino mpaka atalimba mwauzimu kungathandize kwambiri.—Werengani Deuteronomo 6:5-7.
16, 17. Kodi makolo ena amene ali m’gawo la chilankhulo china amathandiza bwanji ana awo?
16 Koma palinso makolo ena omwe amatha kuphunzitsa ana awo m’chilankhulo chawo ngakhale kuti amasonkhana ndi mpingo kapena kagulu ka chilankhulo china. Chitsanzo ndi M’bale Charles amene ali ndi ana aakazi atatu. Wamng’ono ali ndi zaka 9 ndipo wamkulu ali ndi zaka 13. Banjali limasonkhana m’kagulu kolankhula Chilingala. A Charles anati: “Tinasankha kuti tiziphunzira komanso kuchita kulambira kwa pabanja m’chilankhulo chathu. Koma nthawi zina timayeserera ulaliki komanso kuchita masewera m’Chilingala n’cholinga choti anawo aziphunzira chilankhulochi.”
17 M’bale wina dzina lake Kevin, ali ndi ana aakazi awiri, wazaka 5 ndi wazaka 8 ndipo amasonkhana mumpingo wachilankhulo china. Popeza m’baleyu amadziwa kuti banja lake silipindula kwambiri ndi misonkhano, amayesetsa kuchita zinthu zina ndi banja lakelo m’chilankhulo chawo. A Kevin anati: “Ine ndi mkazi wanga timaphunzira ndi ana athu m’Chifulenchi chomwe ndi chilankhulo chathu. Tinakonzanso zoti tizikasonkhana kumpingo wachifulenchi kamodzi pa mwezi. Komanso pa nthawi ya tchuthi timapita kumsonkhano wachigawo wachilankhulo chathu.”
18. (a) Kodi mfundo ya pa Aroma 15:1, 2 ingathandize bwanji makolo? (b) Kodi makolo ena anatchula mfundo zothandiza ziti? (Onani mawu akumapeto.)
18 Ndi udindo wa banja lililonse kusankha zimene angachite kuti ana awo akhale ndi chikhulupiriro cholimba. [2] (Agal. 6:5) A Muriel, amene tawatchula kale aja anafotokoza kuti iwo ndi amuna awo analolera kusamuka mumpingo umene anali n’cholinga choti athandize mwana wawo. (Werengani Aroma 15:1, 2.) A Serge akaganizira zimene anachita, amaona kuti anasankha bwino. Iwo anati: “Kuchokera pamene tinabwerera kumpingo wa Chifulenchi, mwana wathu wapita patsogolo mwauzimu ndipo anabatizidwa. Panopa akuchita upainiya wokhazikika ndipo akuganiza zobwereranso kugawo la chilankhulo china kuja.”
MAWU A MULUNGU AZIKUFIKANI PAMTIMA
19, 20. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mawu a Mulungu?
19 Yehova ndi wachikondi kwambiri ndipo akuonetsetsa kuti Mawu ake azipezeka m’zilankhulo zambiri. Paja cholinga chake n’chakuti ‘anthu, kaya akhale a mtundu wotani adziwe choonadi molondola.’ (1 Tim. 2:4) Iye amadziwa kuti mfundo za m’Baibulo zimamufika kwambiri munthu pamtima ngati wazimva m’chilankhulo chake.
20 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, tiyeni tiziyesetsa kudya chakudya chotafuna. Tikamaphunzira Malemba nthawi zonse m’chilankhulo chathu, timakhalabe olimba mwauzimu limodzi ndi banja lathu. Timasonyezanso kuti Mawu a Mulungu ndi ofunika kwambiri pa moyo wathu.—Sal. 119:11.
^ [1] (ndime 5) Mayina a m’nkhaniyi tawasintha.
^ [2] (ndime 18) Kuti mudziwe mfundo za m’Baibulo zimene zingathandize banja lanu, onani nkhani yakuti, “Kulera Ana M’dziko Lachilendo—Mavuto ndi Mphoto Zake” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2002.