Anadzipereka ndi Mtima Wonse ku Myanmar
ZAKA pafupifupi 2,000 zapitazo Yesu anati: “Zokolola n’zochulukadi, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokololazo kuti atumize antchito okam’kololera.” (Luka 10:2) Umu ndi mmene zilili m’dziko la Myanmar masiku ano. Tikutero chifukwa chakuti m’dzikoli muli ofalitsa pafupifupi 4,200 okha omwe akuyesetsa kulalikira anthu okwana 55 miliyoni amene amakhala m’dzikoli.
Koma ‘Mwini zokolola’ walimbikitsa abale ndi alongo ochokera m’mayiko osiyanasiyana kuti abwere kudzikoli, lomwe ndi kum’mwera chakum’mawa kwa Asia, kuti adzathandize pa ntchito yolalikira. Kodi n’chifukwa chiyani anthuwa achoka kudziko la kwawo? Nanga n’chiyani chinawathandiza kusamuka? Kodi apeza madalitso otani? Tiyeni tsopano tikambirane mafunso amenewa.
“BWERANI, TIKUFUNA APAINIYA AMBIRI KUNO”
Zaka zingapo zapitazo, mpainiya wina wa ku Japan dzina lake Kazuhiro anayamba matenda akugwa. Iye anakomoka ndipo anapita naye kuchipatala. Dokotala anamuuza kuti asayendetse galimoto kwa zaka ziwiri. Iye anadabwa ndipo anadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingapitirize bwanji utumiki umene ndimakonda kwambiri wa upainiya?’ Kazuhiro anapemphera kuchokera pansi pa mtima ndipo anachonderera Yehova kuti amuthandize kupeza njira yopitirizira upainiya.
Kazuhiro ananena kuti: “Patapita mwezi umodzi, mnzanga amene ankachita upainiya ku Myanmar anamva za vuto langa. Iye anandiimbira foni ndipo anandiuza kuti: ‘Kuno ku Myanmar anthu ambiri amakwera basi kuti apite kumene akufuna. Mukabwera kuno, simungafunike galimoto kuti muzilowa mu utumiki.’ Ndinafunsa dokotala ngati matenda anga angandilepheretse kupita ku Myanmar. Ndinadabwa chifukwa anandiuza kuti, ‘Ku Japan kuno kwabwera dokotala wa ubongo wochokera ku Myanmar. Ndikonza zoti mukumane naye ndipo ngati mungadwale ku Myanmar, akhoza kukuthandizani.’ Ndinaona kuti yankho la dokotalayu linachokera kwa Yehova.”
Nthawi yomweyo, Kazuhiro anatumiza imelo ku ofesi ya nthambi ya ku Myanmar yonena kuti iye ndi mkazi wake akufuna kuti akachite upainiya m’dzikoli. Patangopita masiku 5, abale akunthambiyi anayankha kuti, “Bwerani tikufuna apainiya ambiri kuno.” Kazuhiro ndi mkazi wake dzina lake Mari anagulitsa magalimoto awo, anapeza ziphaso zoyendera komanso anagula matikiti a ndege. Panopa akutumikira mosangalala m’kagulu ka chinenero chamanja mumzinda wa Mandalay ku Myanmar. Kazuhiro anati: “Zimene zatichitikirazi zatithandiza kukhulupirira kwambiri lonjezo la Mulungu la Salimo 37:5 lakuti: ‘Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.’”
paYEHOVA ANATSEGULA NJIRA
Mu 2014, a Mboni za Yehova ku Myanmar anali ndi mwayi wochita msonkhano wapadera m’dzikoli. Anthu ambiri ochokera kumayiko ena anapezeka pamsonkhanowu. Mlongo wina wazaka za m’ma 30 wochokera ku United States dzina lake Monique yemwe anapezekakonso anati: “Nditabwerera kwathu pambuyo pa msonkhanowu, ndinapemphera kwa Yehova zokhudza zimene ndiyenera kuchita pa moyo wanga. Ndinakambirananso ndi makolo anga pa nkhani ya zolinga zanga zauzimu. Tonsefe tinaona kuti ndingachite bwino kubwerera ku Myanmar. Koma ndinaganizira komanso kupemphera kwambiri ndisanasankhe zochita.” Monique anafotokoza chifukwa chake zinamutengera nthawi kuti asankhe zopita ku Myanmar.
Iye anati: “Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti ‘awerengere ndalama zimene adzawononge.’ Choncho ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndingakwanitse kusamuka? Nanga ndidzatha kupeza ndalama zokwanira popanda kugwira ntchito kwambiri?’” Monique ananena kuti: “Ndinazindikira kuti ndinalibe ndalama zokwanira moti n’kusamukira kudziko lakutali kwambiri.” Choncho funso n’kumati, Kodi anakwanitsa bwanji kusamuka?—Luka 14:28.
Monique anafotokoza kuti: “Tsiku lina bwana anga anandiitana. Ndinkachita mantha poganiza kuti mwina akufuna kundiuza kuti ntchito yatha. Koma m’malomwake anandithokoza chifukwa chogwira ntchito mwakhama. Kenako anandiuza kuti akonza zoti ndilandire bonasi. Ndalama zake zinali zingokwanira kuti ndilipire ngongole zanga.”
Monique wakhala akutumikira ku Myanmar kuyambira mu December 2014. Kodi iye amaona bwanji utumiki wake? Iye anati: “Ndimasangalala kwambiri kutumikira kuno. Ndili ndi maphunziro a Baibulo atatu. Mzimayi wina amene ndimaphunzira naye ali ndi zaka 67. Nthawi zonse akamandilandira amandihaga n’kumamwetulira kwambiri. Pamene anaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova analira. Iye anati: ‘Pa moyo wanga wonse, aka ndi koyamba kumva dzina la Mulungu lakuti Yehova. Ndiwe wamng’ono kwambiri kwa ine koma wandiphunzitsa chinthu chofunika kwambiri pa moyo.’ N’zosachita kufunsa kuti nanenso ndinalira. Nkhani ngati zimenezi n’zimene zimachititsa kuti kutumikira kudziko lina kukhale kosangalatsa kwambiri.” Posachedwapa, Monique anali ndi mwayi wopita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.
Chinthu china chimene chinalimbikitsa anthu kuti asamukire ku Myanmar chinali nkhani yokhudza dzikoli limene linapezeka mu Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2013. Mlongo wina wazaka za m’ma 30 dzina lake Li ankakhala kudziko lina la kum’mwera chakum’mawa kwa Asia. Iye anali pa ntchito yolembedwa koma nkhani ya mu Buku Lapachaka linamulimbikitsa kuti aganize zokatumikira ku Myanmar. Iye ananena kuti: “Mu 2014 ndinapita kumsonkhano wapadera wa ku Yangon ndipo ndinakumana ndi banja lina lomwe linkatumikira m’gawo lachitchainizi ku Myanmar. Popeza ndimalankhula Chitchainizi, ndinasankha zosamukira ku Myanmar kuti ndikathandize kagulu kachitchainizi. Ndinagwirizana ndi Monique ndipo tinasamukira mumzinda wa Mandalay. Yehova anatithandiza kupeza ntchito yauphunzitsi ya maola ochepa kusukulu imodzi. Tinapezanso nyumba yapafupi ndi sukuluyi. Ngakhale kuti kuno kumatentha kwambiri komanso timakumana ndi mavuto ena, ndimasangalala kwambiri kutumikira kuno. Anthu a ku Myanmar kuno amakhala moyo wosalira zambiri, ndi aulemu ndipo amakonda kumvetsera uthenga wabwino. Ndimasangalala kwambiri kuona mmene Yehova akudalitsira ntchito yolalikira kuno. Ndimakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yehova amafuna kuti ndizitumikira kuno ku Mandalay.”
YEHOVA AMAMVA MAPEMPHERO
Anthu ambiri amene anasamukira kudera lina amaona Yehova akuyankha mapemphero awo. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Jumpei ndi mkazi wake Nao. Banjali ndi lazaka za m’ma 30 ndipo linkatumikira mumpingo wa chinenero
chamanja ku Japan. Ndiye n’chifukwa chiyani linasamukira ku Myanmar? Jumpei anati: “Ine ndi mkazi wanga tinali ndi cholinga chokatumikira kudziko lina. Ndiye m’bale wina amene tinkatumikira naye mumpingo wa chinenero chamanja anasamukira ku Myanmar. Ngakhale kuti tinali ndi ndalama zochepa, nafenso tinasamuka mu May 2010. Abale ndi alongo a ku Myanmar anatilandira bwino kwambiri.” Ndiye kodi m’baleyu amamva bwanji kutumikira m’gawo la chinenero chamanja ku Myanmar? Iye anati: “Kunoko anthu ambiri amafuna kuphunzira Baibulo. Anthu okhala ndi vuto losamva amasangalala kwambiri tikawaonetsa mavidiyo a chinenero chamanja. Tinachita bwino kwambiri kubwera kudzatumikira Yehova kuno.”Kodi Jumpei ndi Nao amapeza bwanji zofunika pa moyo wawo? Jumpei anati: “Titakhala zaka zitatu, ndalama zimene tinasungira zinatithera moti tinalibe yolipirira lendi chaka chotsatira. Ine ndi mkazi wanga tinkapemphera kwa Yehova mochonderera. Kenako tinalandira kalata yochokera ku ofesi ya nthambi yotiuza kuti tikhala apainiya apadera akanthawi. Tinkakhulupirira kwambiri Yehova ndipo tinkadziwa kuti sangatisiye chifukwa wakhala akutithandiza pa vuto lililonse.” Chaposachedwapa, Jumpei ndi mkazi wake anapita ku Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.
YEHOVA AKUPATSA ANTHU AMBIRI MTIMA WOFUNA KUTUMIKIRA
M’bale wina wa ku Italy dzina lake Simone ndi mkazi wake Anna wa ku New Zealand anasamukiranso ku Myanmar. M’baleyu ali ndi zaka za m’ma 40 pomwe mlongoyu ali ndi zaka za m’ma 30. Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti asamuke? Anna anati: “Titawerenga za ku Myanmar mu Buku Lapachaka la 2013 tinayamba kufunitsitsa kupitako.” Simone anati: “Timaona kuti ndi mwayi waukulu kutumikira ku Myanmar. Kunoko moyo wake ndi wosalira zambiri ndipo nthawi yambiri timaigwiritsa ntchito potumikira Yehova. N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti Yehova akutisamalira pamene tikutumikira kunoko.” (Sal. 121:5) Anna anati: “Panopa ndikusangalala kwambiri kuposa m’mbuyo monsemu. Moyo wathu ndi wosalira zambiri. Nthawi zambiri ndimakhala ndili limodzi ndi mwamuna wanga ndipo timagwirizana kwambiri. Tapezanso anzathu atsopano ambiri. Anthu akuno sadana ndi Mboni moti utumiki umasangalatsa kwambiri.” Kodi pali zitsanzo zosonyeza kuti utumiki umayenda bwino?
Anna anati: “Tsiku lina kumsika, ndinakumana ndi mtsikana wina, yemwe ankaphunzira pa yunivesite inayake, ndipo tinagwirizana zoti tidzakumanenso. Nditapitako ndinapeza kuti waitana mnzake. Ulendo wotsatira ndinapeza kuti waitananso anzake ena . Ulendo wina anaitana anzake enanso. Panopa ndikuphunzira ndi anthu 5 kumeneko.” Simone anati: “Anthu amene timawalalikira ndi ochezeka komanso okonda kuphunzira Baibulo. Ifeyo ndi amene timalephera kuti tibwerere bwinobwino kwa anthu onse.”
Koma kodi ndi zinthu ziti zimene abale ndi alongo anachita kuti asamukire ku Myanmar? Mlongo wina wa ku Japan dzina lake Mizuho anati: “Ine ndi mwamuna wanga Sachio tinkafunitsitsa kusamukira kudziko
limene kukufunika ofalitsa ambiri. Koma sitinkadziwa kuti tingasamukire kuti. Titangowerenga nkhani ya ku Myanmar mu Buku Lapachaka la 2013, tinakhudzidwa kwambiri moti tinayamba kuganiza zoti tisamukire kumeneko ngati n’zotheka.” Sachio anati: “Tinagwirizana kuti tipite kukayendayenda mumzinda wa Yangon, ku Myanmar, kuti tikaone mmene zinthu zilili kumeneko. Ulendowu unali wa mlungu umodzi ndipo unatithandiza kuti titsimikize zosamukira kumeneko.”KODI NANUNSO MUNGASAMUKE?
M’bale Rodney ndi mkazi wake Jane anasamuka ku Australia kupita ku Myanmar mu 2010 ndipo akutumikirabe komweko. Banjali ndi lazaka za m’ma 50 ndipo anapita limodzi ndi mwana wawo wamwamuna dzina lake Jordan komanso ndi mwana wawo wamkazi dzina lake Danica. Rodney anati: “Zinatikhudza kwambiri kuona kuti anthu akuno ali ndi njala yauzimu. Mabanja ena amene angakwanitse kusamuka angachite bwino kupita kumadera ngati amenewa.” Pofotokoza chifukwa chake, anati: “Kusamukira kunoko kwathandiza kwambiri banja lathu mwauzimu. Achinyamata ambiri amatanganidwa ndi mafoni, magalimoto, ntchito komanso zinthu zina. Koma ana athu amatanganidwa n’kuphunzira mawu oti azigwiritsa ntchito mu utumiki. Amaphunzira zimene angachite pokambirana ndi anthu amene akufuna kuphunzira Baibulo komanso mmene angayankhire pamisonkhano. Amatanganidwanso ndi zinthu zambiri zosangalatsa zokhudza kulambira.”
Oliver, yemwe ndi m’bale wazaka za m’ma 30 wa ku United States, anafotokoza ubwino wokatumikira kudziko lina. Iye anati: “Kutumikira Yehova m’dziko lachilendo kunandithandiza kwambiri. Kwandichititsa kuti ndizidalira kwambiri Yehova komanso kukhulupirira kuti angandithandize kulikonse kumene ndingakhale. Kutumikira ndi abale amene poyamba sindinkawadziwa koma timakhulupirira zofanana, kwandithandiza kuzindikira kuti palibenso chinthu china chofunika kwambiri padzikoli kuposa Ufumu wa Mulungu.” Panopa, Oliver ndi mkazi wake dzina lake Anna akutumikirabe mwakhama m’gawo la anthu olankhula Chitchainizi.
Trazel, yemwe ndi mlongo wazaka za m’ma 50 wa ku Australia, wakhala akutumikira ku Myanmar kuyambira mu 2004. Iye ananena kuti: “Ndikulimbikitsa amene angakwanitse kusamuka kuti apite kumene kukufunika antchito ambiri. Ndazindikira kuti munthu ukakhala ndi mtima wofunitsitsa kutumikira, Yehova amakuthandiza kuti ukwanitse kumutumikira. Sindinaganizirepo kuti ndingakhale ndi mwayi wotumikira chonchi. Koma ndimasangalala kwambiri kuti ndakwanitsa kugwiritsa ntchito moyo wanga kutumikira Yehova.”
Tikukhulupirira kuti mfundo zolimbikitsa zimene anthu amene anapita kukatumikira ku Myanmar anenazi zikuthandizani kufunitsitsa kuthandiza anthu a m’madera amene salalikiridwa. Abale ndi alongo amene akutumikira ku Myanmar akukuitanani kuti, “Chonde bwerani mudzatithandize kuno.”