Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi mtumwi Paulo pa Aroma 12:19, anali kusonyeza kuti Akristu sayenera kukwiya pamene iye anati: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo”?
Kunena mosapita m’mbali, ayi. Mtumwi Paulo pano anali kunena za mkwiyo wa Mulungu. Komabe, sizikutanthauza kuti ngakhale Akristu atagonjera mkwiyo ndiye kuti palibe vuto ayi. Baibulo limatilangiza momveka bwino kuti sitiyenera kukwiya. Talingalirani zitsanzo zosankhidwazi za malangizo a Mulungu.
“Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) “Yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu.” (Mateyu 5:22) “Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndewu, kaduka, zopsa mtima.” (Agalatiya 5:19, 20) “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiŵaŵa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu.” (Aefeso 4:31) “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” (Yakobo 1:19) Komanso, buku la Miyambo limatilangiza mobwerezabwereza kuti sitiyenera kukwiya kapena kukhala wosachedwa kupsa mtima pa zolakwa ndi zophophonya zing’onozing’ono za anthu.—Miyambo 12:16; 14:17, 29; 15:1; 16:32; 17:14; 19:11, 19; 22:24; 25:28; 29:22.
Nkhani ya pa Aroma 12:19 ikugwirizana ndi malangizo ameneŵa. Paulo analangiza kuti chikondano chathu chiyenera kukhala chopanda chinyengo, kuti tidalitse anthu amene akutizunza, kuti tiyese kuganizira ena zabwino, kuti tisabwezere choipa ku choipa, ndikuti tiyesetse kukhala amtendere ndi anthu onse. Kenako iye analimbikitsa kuti: “Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.”—Aroma 12:9, 14, 16-19.
Inde, tisalole mkwiyo kutisonkhezera kulipsira kapena kubwezera chilango. Chidziŵitso chathu cha mikhalidwe ya zinthu ndi maganizo athu a chiweruzo n’zopanda ungwiro. Ngati tilola mkwiyo kutisonkhezera kubwezera chilango, kaŵirikaŵiri tidzalakwa. Kuteroko kudzakhala kutumikira Mdani wa Mulungu, Mdyerekezi. Paulo analembanso kuti: “Kwiyani, koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire, ndiponso musam’patse malo Mdyerekezi.”—Aefeso 4:26, 27.
Njira yabwinopo, njira ya nzeru, ndiyo kulekera Mulungu kugamula kuti ndi liti ndipo ndani yemwe ayenera kubwezeredwa chilango. Iye angachite zimenezo ndi chidziŵitso chonse cha zochitikazo, ndipo chiweruzo chilichonse chomwe adzachipereka chidzasonyeza chilungamo chake changwiro. Tingaone kuti imeneyi ndiyo mfundo yaikulu ya Paulo pa Aroma 12:19, pamene tiona mmene akuigwirizanitsira ndi Deuteronomo 32:35, 41, pamene palinso mawu aŵa akuti: “Kubwezera chilango n’kwanga, kubwezera komwe.” (Yerekezani ndi Ahebri 10:30.) Chotero, ngakhale kuti mawu akuti “ndi kwa Mulungu” sapezeka m’malemba Achigiriki, otembenuza ambiri amakono awonjezera mawuŵa pa Aroma 12:19. Zimenezi zachititsa kuti liziŵerengedwa motere “lekani Mulungu abwezere” (The Contemporary English Version); “perekani mpata ku mkwiyo wa Mulungu” (American Standard Version); “lekani Mulungu apereke chilango ngati afuna” (The New Testament in Modern English); “siyani malo a kubwezera kwa Mulungu.”—The New English Bible.
Ngakhale pamene tachitiridwa mosayenera kapena pamene tazunzidwa ndi odana ndi choonadi, tingasonyeze chikhulupiriro ku malongosoledwe a Yehova Mulungu omwe Mose anawamva akuti: ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.’—Eksodo 34:6, 7.