Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Taonani Khamu Lalikulu!’

‘Taonani Khamu Lalikulu!’

Imani Amphumphu ndi Otsimikiza Kotheratu

‘Taonani Khamu Lalikulu!’

NKHANI ya khamu lalikulu inazunguza atumiki a Yehova kwa zaka makumi ambiri. Kwanthaŵi yaitali anayesetsa kuti apeze yankho la m’Malemba. Panali mafunso ambiri okhudza nkhaniyi. Koma potsiriza pake, yankho la m’Baibulo linapezeka ndipo linasangalatsa omvetsera omwe anali pamsonkhano waukulu ku Washington, D.C., m’chaka cha 1935.

Nkhani yomwe sanali kuimvetsa inali yakuti: Kodi chizindikiro cha “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9 n’chiyani? Kodi gulu la okhulupirira limeneli likakhala kumwamba?

Funso Lomwe Lakhalapo Kwanthaŵi Yaitali

Kuchokera m’nthaŵi ya mtumwi Yohane mpaka lero, Akristu akhala akuzunguzika pankhani ya chizindikiro cha “khamu lalikulu.” Ophunzira Baibulo ankaona kuti khamu lalikulu ndi gulu lachiŵiri la okakhala kumwamba amene akudziŵa choonadi cha m’Baibulo koma sakuchita khama kwenikweni kuchifalitsa.

Komabe, panali otsatira ena a Akristu odzozedwa amene anali akhama kwambiri pantchito yolalikira. Iwo analibe chikhumbo chopita kumwamba. Inde, chiyembekezo chawo chinali chogwirizana ndi nkhani ya anthu onse yakuti “Mamiliyoni Okhala ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse,” yokambidwa ndi anthu a Yehova kuyambira mu 1918 mpaka 1922. Anthu ameneŵa adzalandira moyo wosatha padziko lapansi.

Nsanja ya Olonda ya October 15, 1923, inalongosola fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi kuti: “Nkhosa sikuti zimaimira odzozedwa ndi mzimu koma zimaimira anthu a mitundu yonse amene amayesetsa kuchita chilungamo, kuzindikira kuti Yesu Kristu ndiye Ambuye, ndiponso kuyembekezera zinthu zabwino muulamuliro wake.”​—Mateyu 25:31-46.

Kuwala Kowonjezereka

Mu 1931, Buku Loyamba, lakuti ‘Vindication,’ polongosola Ezekieli chaputala 9 linanena kuti, anthu olembedwa chizindikiro pamphumi zawo kuti apulumutsidwe pa mapeto a dzikoli ndiwo nkhosa za m’fanizo la Yesu. Buku Lachitatu lakuti ‘Vindication’ (lofalitsidwa mu 1932), linalongosola za mtima woongoka wa munthu yemwe sanali mwiisrayeli wotchedwa Yehonadabu. Iye anakwera pa galeta wa Mfumu yodzozedwa ya Israyeli Yehu ndi kupitira naye limodzi kuti akaone changu cha Yehu pokantha olambira onyenga. (2 Mafumu 10:15-28) Bukulo linanena kuti: Yehonadabu anaimira gulu la anthu amene tsopano ali padziko lapansi koma amene sali mbali ya Satana. Iwo akuchirikiza chilungamo ndipo ndi amene Ambuye adzawapulumutse pa Armagedo ndi kuwapatsa moyo wosatha padziko lapansi. Ameneŵa ali m’gulu la ‘nkhosa.’”

Mu 1934, Nsanja ya Olonda inanena mosapita m’mbali kuti Akristu amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi ayenera kudzipatulira kwa Yehova ndiponso kubatizidwa. Ndithudi, kuwala pankhani ya gulu la padziko lapansi limeneli kunali kukuwalirawalirabe!​—Miyambo 4:18.

Kumvetsa Kochititsa Chidwi

Kumvetsa Chivumbulutso 7:9-17 kunali pafupi kuwala mochititsa chidwi. (Salmo 97:11) Nsanja ya Olonda inali itanena kuti msonkhano waukulu womwe unali kudzayamba pa May 30 mpaka June 3, 1935, ku Washington D.C., U.S.A., ukakhala wolimbikitsa ndi wopindulitsa kwambiri kwa anthu oimiridwa ndi Yehonadabu. Ndipo unaterodi!

M’nkhani yake yogwira mtima yonena za “Khamu Lalikulu” pamsonkhano waukulu womwe panali anthu pafupifupi 20,000, J. F. Rutherford anatchula umboni wa m’Malemba wakuti “nkhosa zina” zamakono ndizo “khamu lalikulu” lotchulidwa pa Chivumbulutso 7:9. (Yohane 10:16) Atafika pachimake pankhaniyo, iye anapempha omvera kuti: “Onse amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi aimirire.” Namtindi wa omvera ataimirira, Rutherford anafuula amvekere: “Taonani khamu lalikulu!” Kunangoti zii, kenako, kunalitu kululutira kwadzaoneni. Tsiku lotsatira, Mboni za Yehova zatsopano zokwana 840 zomwe zambiri zinali za khamu lalikulu zinabatizidwa.

Mphatso Yapadera

Chaka cha 1935 chisanafike, anthu omwe anali kuchulukirachulukira amene analabadira uthenga wa Baibulo ndiponso kuonetsa changu pantchito yolalikira uthenga wabwino, anasonyeza chidwi chokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi la Paradaiso. Analibe chikhumbo chopita kumwamba, chifukwa chakuti Mulungu sanawapatse chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Kudziŵa kwawo kuti anali a khamu lalikulu la nkhosa zina kunasonyeza kuti pomwe chinkafika chaka cha 1935, kuitana Akristu odzozedwa a 144,000 kunali kutatha.​—Chivumbulutso 7:4.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itaulika, Satana Mdyerekezi anayesetsa kuletsa ntchito yosonkhanitsa anthu amene anali kudzakhala khamu lalikulu. Ntchito yolalikira inaletsedwa m’mayiko ambiri. M’nthaŵi yovuta imeneyo, J. F. Rutherford atatsala pang’ono kumwalira mu January 1942, ananena kuti: “Zikuoneka ngati khamu lalikulu limeneli silikhala lalikulu n’komwe.”

Koma chifukwa cha madalitso a Mulungu zinthu zinasintha. ‘Ataima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu,’ a nkhosa zina akhala akukwaniritsa lamulo lopanga ophunzira. (Akolose 4:12; Mateyu 24:14; 28:19, 20) Pomwe chimafika chaka cha 1946, Mboni za Yehova zomwe zinali kulalikira padziko lonse zinalipo 176,456 ndipo ambiri mwa iwo anali a khamu lalikulu. M’chaka cha 2000, Mboni zopitirira 6,000,000 zikutumikira Yehova mokhulupirika m’mayiko 235​—khamu lalikuludi! Ndipo khamuli likuchulukirachulukira.