Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mufunikira Chikumbumtima Chophunzitsidwa Bwino

Mufunikira Chikumbumtima Chophunzitsidwa Bwino

Mufunikira Chikumbumtima Chophunzitsidwa Bwino

Apaulendo ndi oyendetsa ndege ya Air New Zealand Flight 901 kupita ku Antarctica anayembekeza kuyamba tsiku losaiŵalika paulendo wawowo. Anakonzekeretsa makamera awo, ndipo m’ndegemo aliyense anali ndi chimwemwe chokhachokha pamene ndege ya mtundu wa DC-10 inayandikira derali ndi kuyamba kuuluka cham’munsi kuti onse aone dziko lokongolalo.

MKULU wa oyendetsa ndegeyo anali atagwira nchitoyo zaka 15. Pa zaka zonsezo maola onse amene anathera ali pa ntchito yakeyo anaposa 11,000. Asananyamuke, iye mosamala analoŵetsa ndondomeko ya ulendowo m’kompyuta ya m’ndegemo asakudziŵa kuti ndondomeko yomwe anam’patsayo inali yolakwika. Mmene ndegeyo imauluka m’mitambo pamtunda pafupifupi mamita 600 m’mwamba, inawomba phiri la Erebus ndipo anthu onse m’ndegemo, okwana 257, anafa.

Masiku ano ndege zimadalira makompyuta kuti ziuluke. Anthunso ali ndi chikumbumtima chowatsogolera pa moyo. Ndipo tsoka lomwe ndege ya Flight 901 inaona lingatiphunzitse zinthu zothandiza kwambiri zokhudza chikumbumtima chathu. Mwachitsanzo, chitetezo cha ndege chimadalira makina ake ogwira ntchito bwino oonera kaulukidwe kake komanso malangizo olondola. Momwemonso moyo wathu, uzimu wathu ndi khalidwe lathu zimadalira chikumbumtima chimene chimalabadira malangizo olondola a khalidwe labwino omwe amachitsogolera.

M’dzikoli masiku ano nkhani yomvetsa chisoni ndi yakuti malangizo ngati amenewo akutha mofulumira mwinanso anthu akuwanyalanyaza. Mphunzitsi wa ku America anati: “Masiku ano timamva zambiri za mwana wa sukulu kuno ku United States amene satha kuŵerenga, kulemba ndipo sathanso kupeza dziko la France pamapu. Komanso mwanayo zimam’vuta kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Ndipo pa mavuto ake ena ambiri a maphunziro, tiikeponso nkhani yochititsa chisoni ya kusokonezeka kwake pa nkhani ya makhalidwe abwino kuwonjezera pa kusadziŵa kwake kuŵerenga ndi masamu.” Mayiyu anatinso “achinyamata amakono saidziŵa bwinobwino nkhani ya makhalidwe. Tangofunsani mmodzi wa iwo kuti anene ngati ilipo ‘miyezo ya chabwino ndi choipa’ ndipo mudzadabwa kuona mmene asokonezekere, kusoŵa chonena, kupanikizika ndi kuchita mantha. . . . Akapita ku koleji, n’kumene amakasokonezekeratu kuposa kale.”

Mwa zina zochititsa zimenezi ndi maganizo akuti nkhani ya makhalidwe imadalira mmene munthu payekha amaganizira, kuti miyezo ya makhalidwe ndi yosiyana malinga ndi zimene munthu amakonda kapena zimene pafuko lawo amafuna. Taganizani zimene zikanachitika ngati oyendetsa ndege akanati aziyendera zizindikiro zimene zimasunthasuntha mosadziŵika bwino ngakhale kusoŵa kumene, m’malo motsata malangizo odalirika! Mosakayika, ngozi ngati imene inachitika kuphiri la Erebus zikanachuluka kwambiri. Chimodzimodzinso ndi dzikoli. Posafuna kutsata miyezo yodalirika ya makhalidwe abwino, likututa mavuto okhaokha adzaoneni, chisoni ndi imfa pamene mabanja akutha chifukwa chosakhulupirika komanso anthu ambirimbiri akuzunzika ndi matenda a AIDS kapena matenda ena opatsirana mwa kugonana.

Maganizo oti nkhani ya makhalidwe imadalira mmene munthu payekha amaganizira amamveka ngati anzeru. Koma kunena zoona, onse owatsata ali ngati Anineve akale amene sankadziŵa ‘kusiyanitsa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.’ Otsata maganizo ameneŵa afanana ndi Aisrayeli ampatuko amene anati ‘zoipa ndi zabwino, ndi zabwino zoipa.’​—Yona 4:11; Yesaya 5:20.

Nangano ndi kuti kumene tingapeze malamulo ndi mfundo za chikhalidwe zomveka bwino komanso zosasokoneza zimene tingaphunzitsire chikumbumtima chathu kuti chikhale mtsogoleri wathu wodalirika? Ambiri apeza kuti Baibulo limathandiza kwambiri pamenepa. Kuyambira nkhani ya makhalidwe ndi kufunika kwa ntchito, kuphunzitsa ana ndi kulambira Mulungu, palibe mfundo iliyonse yofunika imene Baibulo limasiyako. (2 Timoteo 3:16) Lakhala lodalirika zaka mazana ambiri. Popeza amene anakhazikitsa miyezo ya makhalidwe abwino amene ali m’Baibulo ndi Mlengi wathu, amenenso ali ndi ulamuliro woposa, miyezo yakeyo n’njofunika kwambiri kwa anthu onse. Choncho, palibe chifukwa choti tizingokhala m’chimbulimbuli osadziŵa makhalidwe abwino.

Koma masiku anowo, pali zambiri zowononga chikumbumtima chanu kuposa kale. Zikutheka bwanji zimenezi? Ndipo mungatani kuti muchiteteze? Njira yabwino ndi kudziŵa amene akufuna kuwononga chikumbumtima chanucho ndi machenjera ake. Tikambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.