Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsiku Lokambirana za Zipembedzo”

“Tsiku Lokambirana za Zipembedzo”

“Tsiku Lokambirana za Zipembedzo”

MPHUNZITSI wamkulu wachikazi wa pasukulu ina ku Poland anachita chidwi atalankhulana ndi Mboni za Yehova, ndipo anasankhira sukulu yake “Tsiku Lokambirana za Zipembedzo.” Iye anakonza zoti ophunzira omwe angadzipereke​—Achikatolika, Achibuda, ndi a Mboni za Yehova​—akonzekere nkhani zifupizifupi n’cholinga chodzadziŵitsa ophunzira anzawo zomwe iwo amakhulupirira ndiponso zomwe amachita. Achinyamata atatu a Mboni za Yehova anadzipereka nthaŵi yomweyo.

Tsikulo litakwana, woyamba kulankhula anali Malwina, mtsikana wazaka 15. Mwa zina, iye anati: “Ambiri a inu munatidziŵa tisanayambe kuphunzira pa sukulu ino chifukwa choti tinabwerapo kunyumba kwanu. Mungafunse chifukwa chomwe timachitira zimenezo. N’chifukwa chakuti timatengera chitsanzo cha Yesu Kristu, Woyambitsa Chikristu. Analalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kulikonse komwe ankapeza anthu. Atumwi ndi Akristu ena oyambirira ankachita chimodzimodzi. M’madera ambiri, Mboni za Yehova zili m’mavuto aakulu okhudza chikhulupiriro chawo, koma ndife okondwa kuti pasukulu yathu ino tili pamtendere. Nonse mumalimbikitsa mtendere umenewu. Tikukuthokozani chifukwa cha zimenezi!”

Pamapeto pa nkhani yake, Malwina anati: “Pali chifukwa chinanso chomwe timabwerera kunyumba kwanu. Timakuganizirani. Baibulo limati posachedwapa anthu adzaona zinthu zoopsa zikuchitika padzikoli. Chotero, tikadzagogodanso pakhomo panu, chonde dzatimvetsereni. Tikufuna kukuuzani mmene tingadzakhalire limodzi kosatha m’paradaiso padziko lapansi.”

Kenako, Mateusz, nayenso wazaka 15, analankhulapo. Mnyamatayu, Mateusz anauza anthuwo kuti kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova zakhala zikufalitsa uthenga wabwino pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, mu 1914​—m’nyengo ya mafilimu opanda mawu​—Mboni zinkaonetsa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” kanema ya zithunzithunzi zoyenda yomwe anaijambulira pamodzi ndi mawu.

Mateusz anafotokoza mmene wailesi inagwirira ntchito pofalitsa uthenga wa Ufumu ndipo kenako anafotokoza za pulogalamu yapamwamba yopangidwa ndi Mboni za Yehova ya pakompyuta ya multilanguage electronic phototypesetting system (MEPS). Anafotokozanso mmene Mboni za Yehova zathandizira kudziŵitsa madokotala za chithandizo chamankhwala chosagwiritsa ntchito magazi. Iye anati: “Tsopano, madokotala otchuka a m’Poland muno akutiyamikira pankhaniyi ndipo amanena kaŵirikaŵiri kuti chaka ndi chaka odwala ambiri omwe si Mboni akuchitidwa opaleshoni yopanda magazi.”

Mateusz anamaliza mwa kuwauza za ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndipo anati: “Kodi mungakonde kubwera ku Nyumba yathu ya Ufumu? Kuloŵa pakhomo ndi kwaulere, ndipo sikukhala kusonkhetsa ndalama.” Pankhani ya malo a msonkhano wachigawo mu mzinda wa Sosnowiec, Mateusz anati: “Mumachiona chinyumba chachikulu ndi chopindulitsa chimenechi. N’chifukwa chiyani simupita nafe kumeneko? Tili ndi chithunzithunzi cha zochitika kumeneko, ndipo mnzathu Katarzyna akufotokozerani.”

Kenako, Katarzyna, mtsikana wazaka 15, analankhula mosangalala, kuti: “Mudzalandiridwa ndi manja aŵiri mukadzabwera ku Sosnowiec kudzakhala nawo pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova. Kudzakambidwa nkhani zomwe zikudetsa nkhaŵa achinyamata.” Katarzyna anatchulanso za mwambo waukulu kwambiri wa Akristu​—Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. Analimbikitsa anthuwo ndi mawu akuti: “Chaka chathachi, padziko lonse, anthu oposa 14 miliyoni anachita nawo mwambowu. Bwanji osadzakhala nafe pamene tikuchita mwambowu paulendo wotsatira?”

Atatha kukamba nkhani zawo, Malwina, Mateusz, ndi Katarzyna anapatsa aphunzitsiwo buku la Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom pamodzi ndi makaseti aŵiri a vidiyo ofotokoza zikhulupiriro ndi ntchito za Mboni za Yehova. * Aphunzitsiwo anayamikira kwambiri kulandira zinthu zimenezi ndipo analonjeza kuti azizigwiritsa ntchito panthaŵi ya maphunziro a zochitika zakale.

Pamapeto pa chigawocho, Martyna, wazaka 12, anaimbira onse omwe anasonkhana nyimbo yakuti “Tikuyamikani, Yehova.” Mboni zachinyamatazi ‘zinalimbika pakamwa mwa Mulungu wawo’ ndipo zinapereka umboni wabwino kwambiri. (1 Atesalonika 2:2) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa Mboni zachinyamata kulikonse komwe zingakhale!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 26]

Malwina akukonzekera nkhani yake patatsala masiku angapo kuti akaikambe kusukulu

[Chithunzi patsamba 26]

Katarzyna akusankha malemba okagwiritsa ntchito m’nkhani yake