Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amatiganizira?

Kodi Mulungu Amatiganizira?

Kodi Mulungu Amatiganizira?

KODI mumaona kuti mumavutika maganizo chifukwa cha mavuto a m’banja, a thanzi, a kuntchito, kapena maudindo anu ena olemetsa? Anthu ambiri akuvutika. Ndipo ndani masiku ano amene sakuvutika chifukwa chosoŵa chilungamo, upandu, ndi chiwawa? Zilidi ngati mmene Baibulo limanenera kuti: “Cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.” (Aroma 8:22) N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amafunsa kuti: ‘Kodi Mulungu amatiganizira? Kodi adzatithandiza?’

Mfumu yanzeru Solomo popemphera kwa Mulungu inati: “Inu nokha, mudziŵa mitima ya ana a anthu.” Solomo sanangokhulupirira kuti Mulungu amatidziŵa, koma anakhulupiriranso kuti amatiganizira aliyense payekha. Anatha kupempha Mulungu kuti ‘amvere kuchokera m’Mwamba’ ndi kuyankha mapemphero a munthu aliyense woopa Mulungu amene amauza Mulungu “chinthenda chake, ndi chisoni chake.”​—2 Mbiri 6:29, 30.

Masiku ano, Yehova Mulungu amatiganizirabe ndipo akutipempha kuti tizipemphera kwa iye. (Salmo 50:15) Akulonjeza kuyankha mapemphero ochokera pansi pamtima ogwirizana ndi zimene amafuna. (Salmo 55:16, 22; Luka 11:5-13; 2 Akorinto 4:7) Inde, Yehova amamvetsera “pemphero ndi pembedzero lililonse likachitika ndi munthu [wake] ali yense.” Motero, ngati tidalira Mulungu, kupempherera thandizo lake, ndiponso kuyandikira kwa iye, adzatisamalira ndiponso kutitsogolera. (Miyambo 3:5, 6) Wolemba Baibulo Yakobo akutitsimikizira kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.”​—Yakobo 4:8.