Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Anandikomera Mtima ndi Kundisamalira

Yehova Anandikomera Mtima ndi Kundisamalira

Mbiri ya Moyo Wanga

Yehova Anandikomera Mtima ndi Kundisamalira

YOSIMBIDWA NDI FAY KING

Makolo anga anali anthu okoma mtima, koma mofanana ndi anthu ena ambiri, sankakonda zachipembedzo. Mayi anga ankakonda kunena kuti: “Kuyenera kuti kuli Mulungu, chifukwa ngati kulibe, ndani anapanga maluwa ndi mitengoyi?” Koma zinkangothera pomwepo.

BAMBO anga anamwalira mu 1939 pamene ndinali ndi zaka 11, ndipo ndinkakhala ndi mayi anga m’tawuni ya Stockport, chakum’mwera kwa mzinda wa Manchester ku England. Kuyambira kale ndinakhala ndikufuna kudziŵa zambiri zokhudza Mlengi wanga ndipo ndinkalemekeza Baibulo ngakhale sindinkadziŵa kuti muli zotani. Choncho ndinaganiza zopita ku Tchalitchi cha England kuti ndikamve zimene ankaphunzitsa.

Mapemphero awo sanandigwire mtima koma pamene anaŵerenga Mauthenga Abwino, mwa njira inayake mawu a Yesu anandithandiza kukhulupirira kuti Baibulo liyenera kukhala loona. Ndikaganizira zimenezi, n’zodabwitsa kuti sindinaŵerenge Baibulo pandekha. Ngakhale patapita nthaŵi, pamene mnzanga amene banja lathu linkamudziŵa anandipatsa “Chipangano Chatsopano” m’matembenuzidwe amakono, sindinaliŵerenge.

Kuyambika kwa nkhondo ya ku Korea mu 1950 kunandichititsa kuganiza kwambiri. Kodi nkhondoyo idzafalikira ngati mmene inachitira nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse? Ngati ikanafalikira, kodi ndikanamvera bwanji lamulo la Yesu loti ndizikonda adani anga? Komabe, kodi ndikanangokhala osachitapo kanthu ndikuona anthu akuukira dziko lathu? Ngati ndikanachita zimenezo, ndikanakhala ndikuzemba udindo wanga. Ngakhale kuti maganizo anga anali osokonezeka choncho, ndinakhulupirirabe kuti mayankho a mafunso anga onse anali m’Baibulo, ngakhale kuti sindinadziŵe kuti ndingawapeze bwanji kapena ndingawapeze pati.

Kufunafuna Choonadi ku Australia

Mu 1954, ine ndi mayi anga tinaganiza zosamukira ku Australia, kumene mkulu wanga, Jean, anali kukhala. Patapita zaka zingapo, Jean anandiuza kuti anapempha Mboni za Yehova kuti zibwere kudzalankhula nane chifukwa chakuti ankadziŵa zoti ndimachita chidwi ndi Baibulo ndiponso ndimapita ku tchalitchi. Ankafuna adziŵe kuti ndimaganiza chiyani za Mboni za Yehova. Jean anandiuza kuti: “Sindikudziŵa ngati zimene amafotokoza zili zolondola kapena ayi, komabe amatha kufotokoza zinthu, zimene matchalitchi satha kuchita.”

Bill ndi Linda Schneider, amene anabwera kudzalankhula nane, anali anthu okwatirana osangalatsa kwambiri. Anali ndi zaka za m’ma 60 ndipo anali atakhala Mboni kwa zaka zambiri. Anali atagwirapo ntchito ku nyumba youlutsira mawu ya Mboni za Yehova ku Adelaide, ndipo pamene ntchito yolalikira inaletsedwa ku Australia pa nthaŵi ya nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, analembetsa kuti akhale olalikira a nthaŵi zonse. Ngakhale kuti Bill ndi Linda anandithandiza kwambiri, ndinali kufufuzabe zipembedzo zina.

Mwamuna wina amene ndinkagwira naye ntchito ananditenga kupita nane ku msonkhano wa mlaliki wotchedwa Billy Graham, ndipo pamapeto pa msonkhanowo anthu angapo mwa ife tinakumana ndi mtsogoleri wina wachipembedzo amene ananena kuti tingamufunse mafunso. Ndinam’funsa funso limene linali kundisowetsabe mtendere lakuti: “Kodi munthu ungakhale bwanji Mkristu ndi kukonda adani ako pamene ukuwapha pa nkhondo?” Gulu lonselo nthaŵi yomweyo linavomerezana nane mokweza mawu, chifukwa nawonso anali ndi funso lomwelo! Pomaliza pake, mtsogoleri wachipembedzoyo anati: “Sindikudziŵa yankho la funso limenelo. Ndikuliganizirabe.”

Panthaŵi imeneyi phunziro langa la Baibulo ndi Bill ndi Linda linali kupitirirabe, ndipo mu September 1958 ndinabatizidwa. Ndinafuna kutsatira chitsanzo cha aphunzitsi anga, choncho pofika August chaka chotsatiracho, ndinakhala mpainiya wokhazikika, mlaliki wa nthaŵi zonse. Patatha miyezi eyiti anandipempha kuti ndikhale mpainiya wapadera. Ndinasangalala kwambiri kumva kuti mkulu wanga Jean nayenso anapita patsogolo ndi phunziro lake ndipo anabatizidwa.

Khomo la Mwayi Wotumikira Linatseguka

Ndinali mu mpingo wina wa ku Sydney ndipo ndinali kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba angapo. Tsiku lina ndinakumana ndi munthu amene kale anali mtsogoleri wa Tchalitchi cha England ndipo ndinam’funsa zimene tchalitchi chake chimanena za kutha kwa dziko. Ngakhale anandiuza kuti anali ataphunzitsa zikhulupiriro za tchalitchicho kwa zaka 50, ndinadabwa pamene anandiyankha kuti: “Ndifunika kuti ndikafufuze kaye zimenezo, chifukwa Baibulo sindilidziŵa bwino kwambiri ngati mmene zimalidziŵira Mboni za Yehova.”

Nthaŵi yochepa izi zitachitika, panali pempho loti anthu amene angafune angapite kukatumikira ku Pakistan. Ndinalemba kalata yofunsa kuti ndipite, chifukwa sindinadziŵe kuti akazi osakwatiwa sanali kuwatumizako koma amatumiza amuna osakwatira kapena mabanja. Zikuoneka kuti kalata yanga anaitumiza ku likulu lathu ku Brooklyn chifukwa pasanapite nthaŵi yaitali ndinalandira kalata yondiuza kuti ku Bombay (kumene tsopano kumatchedwa Mumbai), ku India, kunkafunika anthu, ndipo anandifunsa ngati ndingafune kupitako. M’menemo munali mu 1962. Ndinapita ndipo ndinakhala ku Bombay chaka chimodzi ndi theka ndisanasamukire ku Allahabad.

Nthaŵi yomweyo ndinayamba kuphunzira mwakhama chinenero cha Chihindi. Chinenero cha ku India chimenechi nthaŵi zambiri mawu ake sasinthasintha polemba ndi potchula, choncho sichivuta kuchiphunzira. Koma ndinkagwa ulesi eni nyumba akandiuza kuti ndizingolankhula Chingelezi m’malo molimbana n’kulankhula chinenero chawocho. Komabe m’dziko latsopano limeneli munali zinthu zofunika kuthana nazo zochititsa chidwi ndiponso zosangalatsa, ndipo ndinkachezanso ndi Mboni zina za ku Australia.

M’masiku anga oyambirira, ndinkaganiza zokwatiwa, koma pofika pa nthaŵi imene ndinabatizidwa, ndinali wotanganidwa kwambiri kutumikira Yehova moti sindinaganizirenso zimenezo. Koma panthaŵi imeneyi ndinayambanso kumva kuti ndikufunika kukhala ndi mnzanga pamoyo wanga. Sindinafune kusiya utumiki wanga wa kudziko lakunja, choncho ndinapemphera kwa Yehova za nkhaniyi kenako sindinkaiganiziranso.

Dalitso Losayembekezeka

Edwin Skinner anali kuyang’anira ntchito imene nthambi ya India inali kuchita panthaŵiyo. Anaphunzira m’kalasi la nambala eyiti la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo mu 1946 limodzi ndi abale ena ambiri okhulupirika, kuphatikizapo Harold King ndi Stanley Jones, amene anawatumiza ku China. * Mu 1958, Harold ndi Stanley anawatsekera m’ndende imene sankaonana ndi munthu wina aliyense chifukwa cha ntchito yawo yolalikira ku Shanghai. Pamene Harold anamasulidwa mu 1963, Edwin anamulembera kalata. Harold anayankha atabwereranso ku Hong Kong kuchokera ku maulendo ake a ku United States ndi Britain ndipo anatchula zoti akufuna kukwatira. Anamuuza Edwin kuti anapempherera nkhani imeneyi pamene anali m’ndende, ndipo anafunsa Edwin ngati amadziŵa Mboni imene ingakhale mkazi wabwino.

Ku India, maukwati ambiri amakhala ochita kukufunira mkazi kapena mwamuna, ndipo nthaŵi zambiri anthu anali kufunsa Edwin kuti akonze maukwati otereŵa, koma nthaŵi zonse samavomera. Choncho anapereka kalata ya Harold kwa Ruth McKay, amene mwamuna wake Homer anali woyang’anira woyendayenda. Pomalizira pake Ruth anandilembera kalata kundiuza kuti panali m’mishonale amene anakhala m’choonadi kwa zaka zambiri amene amafuna mkazi woti amukwatire, ndipo anandifunsa ngati ndingafune kumulembera kalata. Sanandiuze kuti mbaleyo anali ndani kapena china chilichonse chokhudza iye.

Palibe amene ankadziŵa za pemphero langa lofuna mnzanga kupatulapo Yehova yekha, choncho maganizo amene anandifikira koyamba anali okana. Komabe, pamene ndinaganizira kwambiri nkhaniyo, m’pamenenso ndinazindikira kuti nthaŵi zambiri Yehova amayankha mapemphero athu m’njira zimene sitikuyembekezera. Choncho ndinamuyankha Ruth n’kumuuza kuti angathe kumulembera m’baleyo n’kumuuza kuti angalembe kalata ina pokhapokha ngati kundilembera kalatako sikukanatanthauza kuti ndavomera. Kalata yachiŵiri imene Harold King analemba inali yobwera kwa ine.

Zithunzi za Harold King ndi nkhani yake zinatuluka m’manyuzipepala ndi magazini osiyanasiyana atatuluka m’ndende ku China. Panthaŵi imeneyi anali wotchuka padziko lonse lapansi, koma chimene chinandikhudza mtima kwambiri ndi mbiri yake ya utumiki wokhulupirika kwa Mulungu. Choncho tinalemberana makalata kwa miyezi isanu, kenako ndinapita ku Hong Kong. Tinakwatirana pa October 5, 1965.

Tonsefe tinkafuna banja komanso kupitirizabe utumiki wa nthaŵi zonse, ndipo pamene tinali kukula, tinaona kuti timafunikira kwambiri kukhala ndi mnzathu m’moyo wathu. Ndinafika pom’konda Harold, ndipo mmene ndinaona njira yokoma mtima ndi yoganizira ena imene anachitira zinthu ndi anthu, ndiponso mmene anachitira ndi zovuta zimene tinakumana nazo pa utumiki wathu, ndinayamba kumulemekeza kwambiri. Kwa zaka 27 tinali ndi banja lachimwemwe kwambiri ndipo tinalandira madalitso a Yehova ochuluka.

Matchaina ndi anthu olimbikira ntchito kwambiri ndipo ndimawakonda kwambiri. Ku Hong Kong amalankhula Chikantonizi, chimene chili Chitchaina chokhala ndi mawu amene amamveka ndi kutchulidwa m’njira zosiyanasiyana kwambiri poyerekezera ndi Chimandarini, choncho n’chovuta kuchiphunzira. Ine ndi Harold tinayamba moyo wathu wa banja pa nyumba ya amishonale pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, ndipo kenaka tinatumikira m’mbali zosiyanasiyana za dzikolo. Zoonadi, tinali osangalala kwambiri, koma mu 1976 ndinakhala ndi vuto lalikulu la thanzi langa.

Kulimbana ndi Matenda

Ndinali kukha magazi kwa miyezi ingapo, ndipo magazi anga anachepa kwambiri. Panafunika kundichita opaleshoni, koma madokotala kuchipatala anandiuza kuti sangachite opaleshoniyo popanda magazi chifukwa ngati atatero ndiye kuti mwina ndikanafa chifukwa chakuti thupi langa silikanatha kugwira bwino ntchito chifukwa cha kuchepa kwa magazi. Tsiku lina madokotalawo akukambirana za matenda anga, manesi anayesera kundilankhula kuti ndisinthe maganizo anga pondiuza kuti n’kulakwa kuti ndilolere kufa mwadala popanda chifukwa. Tsiku limenelo kunali maopaleshoni 12 oti achitike, ndipo 10 a iwo anali ochotsa mimba, koma ndinaona kuti sananene chilichonse kwa azimayi oyembekezerawo chokhudza kupha ana awowo.

Pamapeto pake Harold analembera kalata achipatalawo yonena kuti madokotala sadzakhala ndi mlandu uliwonse ngati nditafa, ndipo madokotalawo anavomera kuchita opaleshoniyo. Anandipititsa ku chipinda chochitirako opaleshoni ndipo anakonzekera kundipatsa mankhwala oti ndisamve ululu. Koma atangotsala pang’ono kuti achite zimenezo, wopereka mankhwala oletsa ululuyo anakana kupitiriza, ndipo achipatalawo ananditulutsa m’chipatala.

Kenako tinakaonana ndi dokotala wa matenda a akazi amene sankagwira ntchito pachipatalapo. Ataona kuti matenda anga anali aakulu, anavomera kuchita opaleshoniyo pa mtengo wotsika, pokhapokha ngati sitikanauza anthu ena ndalama zimene anatiuza kuti tilipire. Anachita opaleshoniyo ndipo inayenda bwino, popanda kugwiritsa ntchito magazi alionse. Panthaŵi imeneyi, ine ndi Harold tinaonadi kuti Yehova anatikomera mtima ndi kutisamalira.

Mu 1992 Harold anadwala matenda amene sanachire nawo. Tinasamukira ku ofesi ya nthambi ndipo anatisamalira bwino kwambiri. Mwamuna wanga wokondedwa anamaliza moyo wake wapadziko lapansi mu 1993 ali ndi zaka 81.

Kubwerera ku England

Ndinali wosangalala kukhala nawo m’banja la Beteli la ku Hong Kong, koma ndinkavutika kwambiri chifukwa cha kutentha. Kenaka ndinalandira kalata mwadzidzidzi kuchokera ku likulu ku Brooklyn yondifunsa ngati ndikanakonda kusamukira ku nthambi imene inali ndi zinthu zambiri zothandizira pa matenda chifukwa cha thanzi langa lofooka. Choncho m’chaka cha 2000, ndinabwerera ku England n’kukakhala nawo m’banja la Beteli la ku London. Zaoneka kuti chinali chikondi chachikulu pondichitira zimenezi. Anandilandira bwino kwambiri, ndipo ndimasangalala kugwira ntchito zosiyanasiyana, kuphatikizapo kusamalira laibulale ya banja la Beteli yomwe ili ndi mabuku 2,000.

Ndimasonkhananso mu mpingo wa anthu olankhula Chitchaina umene umakumana ku London, koma kunoko zinthu zasintha tsopano. Masiku ano, anthu ochepa okha ndi amene amabwera kuchokera ku Hong Kong. Ambiri amachokera ku China. Amalankhula Chimandarini, ndipo zimenezo zimachititsa kuti pakhale zovuta zina tikamachita ntchito yolalikira. M’dziko lonse lino timamva za anthu amene akuchititsa maphunziro a Baibulo osangalatsa ndi anthu amene akuphunzira maphunziro apamwamba ochokera ku China. Ndi anthu akhama ndipo amayamikira choonadi cha m’Baibulo chimene akuphunzira. N’zosangalatsa kuwathandiza anthu ameneŵa.

Ndikakhala m’chipinda changa chatsopano cha phe, nthaŵi zambiri ndimaganizira za moyo wanga wosangalala ndipo ndimachitabe chidwi ndi kukoma mtima kwa Yehova. Kumakhudza zinthu zonse zogwirizana ndi cholinga chake, ndipo n’zoonekeratu kuti amasamalira atumiki ake, aliyense payekha. Ndili ndi zifukwa zonse zoyamikira mmene wandisamalirira mwachikondi.​—1 Petro 5:6, 7.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Mbiri za moyo wa amishonale aŵiri ameneŵa zinalembedwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya July 15, 1963, masamba 437-442, ndi ya December 15, 1965, masamba 756-767.

[Chithunzi patsamba 24]

Kutumikira ku India

[Zithunzi patsamba 25]

Harold King mu 1963 ndiponso akutumikira ku China m’ma 1950

[Zithunzi patsamba 26]

Tsiku la ukwati wathu ku Hong Kong, pa October 5, 1965

[Chithunzi patsamba 26]

Tili ndi a pa banja la Beteli ku Hong Kong, banja la a Liang pakati ndi banja la a Gannaway kumanja