Kusakasaka Chuma
Kusakasaka Chuma
“Ngati tili ndi mtima womangofuna chuma, sitingakhutitsidwe nacho,” linatero lipoti la Worldwatch Institute.
“KODI tikufuna chiyani? Zinthu zonse. Kodi tikuzifuna liti? Pomwe pano.” Mawu ameneŵa anali otchuka kwa ophunzira ena akukoleji m’zaka za m’ma 1960. Masiku ano, mwina sikumveka mawu ofanana ndendende ndi mawuŵa, koma mfundo ya mawu ameneŵa imamvekabe. Inde, zikuoneka kuti anthu ambiri masiku athu ano ali ndi mtima wosakasaka chuma chambiri.
Kwa anthu ambiri, kupeza chuma ndiponso zinthu zambiri ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri pamoyo wawo. Pulezidenti wakale wa dziko la America, Jimmy Carter, nthaŵi ina anati: “Anthu masiku ano sadziŵikanso ndi zimene amachita koma ndi zimene ali nazo.” Kodi zilipo zinthu zofunika kwambiri kuposa chuma? Ngati zilipo, kodi zinthu zake n’chiyani, nanga n’zopindulitsa bwanji?