Mmene Kudzichepetsa kwa Yehova Kumatikhudzira
Mmene Kudzichepetsa kwa Yehova Kumatikhudzira
DAVIDE anali munthu wodziŵa mavuto. Anazunzidwa ndi Mfumu Sauli, yemwe anali mpongozi wake wansanje kwambiri. Katatu konse, Sauli anafuna kupha Davide ndi mkondo ndipo kwa zaka zambiri anali kum’sakasaka, motero Davide anali kukhala mobisala. (1 Samueli 18:11; 19:10; 26:20) Komabe, Yehova anali naye Davide. Yehova anam’pulumutsa kwa Sauli komanso kwa adani ake ena. Motero, tingathe kumvetsa mmene Davide ankamvera, malingana ndi mmene analongosolera m’nyimbo, kuti: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi mpulumutsi wanga, wangadi; . . . [Yehova] munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa [“kudzichepetsa,” NW] kwanu kunandikulitsa.” (2 Samueli 22:2, 36) Davide anafika pokhala munthu wofunika kwambiri mu Israyeli. Ndiyeno, kodi zimenezi zinakhudzana motani ndi khalidwe la Yehova la kudzichepetsa?
Malemba akamanena kuti Yehova ndi wodzichepetsa, sikuti amatanthauza kuti iye ndi wopereŵera pa zinthu zina kapena kuti iye ali pansi pa ena. M’malo mwake, khalidwe labwinoli limasonyeza kuti iye amawakomera mtima kwambiri anthu amene akuyesetsa kuti aziyanjana naye ndipo amawachitira chifundo. Pa Salmo 113:6, 7, timaŵerenga kuti: ‘[Yehova] amadzichepetsa apenye zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi. Nautsa wosauka kum’chotsa kufumbi.’ ‘Kudzichepetsa’ kwakeku kukutanthauza kuti “iye amaŵerama pansi pofuna kutiona.” (Today’s English Version) Motero kumwambako, Yehova mwiniyo ‘anaŵeramira pansi,’ pofuna kuthandiza Davide, munthu wopanda ungwiro koma wofatsa, amene anali kufuna kutumikira Mulungu. Motero, Davide anatitsimikizira kuti: “Yehova ngwokwezeka, apenyanso wopepukayo.” (Salmo 138:6) Yehova anachitira chifundo, analeza, ndiponso kukomera mtima Davide, ndipo izi ziyenera kulimbikitsa onse ofuna kuchita chifuniro cha Mulungu.
Ngakhale kuti Yehova ndi Wolamulira Wamkulu motero n’ngokwezeka kwambiri m’chilengedwe chonse, iye ndi wofunitsitsa kuchita zinthu ndi aliyense wa ife. Motero sitikayikira n’komwe kuti nthaŵi iliyonse iye angatithandize ngakhale titakhala m’mavuto aakulu kwambiri. Palibe chifukwa choti tizichitira mantha kuti adzatiiŵala. Polongosola zimene Yehova Salmo 136:23.
anachitira Israyeli wakale, Baibulo limanena momveka bwino kuti anali monga ‘amene anawakumbukira popepuka [iwo]; pakuti chifundo chake n’chosatha.’—Popeza kuti ifenso tikutumikira Yehova masiku ano, tingathe kukumana ndi mavuto ngati momwe anachitira Davide. N’kutheka kuti timanyozedwa ndi anthu osadziŵa Mulungu, kapena thanzi lathu silili bwino kwenikweni mwinanso munthu amene tinali kum’konda kwambiri anamwalira. Zilibe kanthu kuti tikukumana ndi vuto lotani, koma ngati tili oona mtima, tingathe kupemphera kwa Yehova kuti atichitire chifundo. Yehova ‘adzaŵeramira pansi’ kuti amvetsere mapemphero athu. Wamasalmo analemba mouziridwa kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo.” (Salmo 34:15) Kodi khalidwe losangalatsa kwambiri limeneli la kudzichepetsa, lomwe Yehova ali nalo, silikukukhudzani mtima?
[Zithunzi patsamba 30]
Yehova anayankha mapemphero a Davide, moteronso masiku ano iye ndi wofunitsitsa kuyankha mapemphero athu