Funafunani Yehova, Amene Amayesa Mitima
Funafunani Yehova, Amene Amayesa Mitima
“Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo.”—AMOSI 5:4.
1, 2. Kodi Malemba akamati Yehova ‘amayang’ana mumtima’ amatanthauzanji?
YEHOVA MULUNGU anauza mneneri Samueli kuti: “Munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samueli 16:7) Kodi Yehova ‘amayang’ana mumtima’ mwa njira yotani?
2 M’Malemba, mtima umaimira mmene munthu alili m’kati, kutanthauza zokhumba zake, zoganiza zake, mmene akumvera, ndi zokonda zake. Choncho Baibulo likamanena kuti Mulungu amayang’ana mumtima, limatanthauza kuti iye sayang’ana maonekedwe akunja koma amayang’ana mmene munthu alili m’kati mwake.
Mulungu Ayesa Israyeli
3, 4. Malinga ndi lemba la Amosi 6:4-6, kodi zinthu zinali bwanji mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi?
3 M’nthawi ya Amosi, pamene Woyesa mitima ameneyu anayang’ana ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi, kodi anaona chiyani? Lemba la Amosi 6:4-6 limafotokoza za anthu ‘ogona pa makama aminyanga, odzithinula pa maguwa awo ogonapo.’ Anali kudya “ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng’ombe ochoka pakati pa khola.” Anthu oterowo anali ‘kungoimba kutsata maliridwe a zeze’ ndipo anali ‘kumwera vinyo m’zipanda.’
4 Poyamba, zimenezi zingaoneke ngati zinthu zosangalatsa. Pokhala m’nyumba zawo zokonzedwa bwinozo, anthu olemerawo anali ndi zakudya komanso zakumwa zabwino ndiponso anali kumvetsera nyimbo zosangalatsa zoimbidwa ndi zida zamakono zedi panthawi imeneyo. Analinso ndi “makama aminyanga.” Akatswiri okumba zinthu zakale apeza minyanga yosemedwa bwino kwambiri ku Samariya, likulu la ufumu wa Israyeli. (1 Mafumu 10:22) Mosakayikira, yambiri ya minyangayi ayenera kuti anali kuikhomera ku mipando ngakhalenso kukongoletsera makoma a nyumba zawo.
5. N’chifukwa chiyani Mulungu sanasangalale ndi Aisrayeli panthawi ya Amosi?
5 Kodi Yehova Mulungu anatsutsa Aisrayeliwo chifukwa chakuti anali kukhala moyo wabwino, kudya zakudya zokhetsa dovu, kumwa vinyo wabwino, ndi kumvetsera nyimbo zoimbidwa mochititsa kaso? Ayi. Sakanawatsutsa chifukwa ndi Mulungu yemweyo amene amapatsa anthu zinthu zabwino zoterozo kuti azisangalala nazo. (1 Timoteo 6:17) Zimene Yehova anakwiya nazo kwambiri ndi zilakolako zawo zoipa, mtima wawo woipa, khalidwe lopanda ulemu lomwe anaonetsa kwa Mulungu, ndi kusakonda kwawo Aisrayeli anzawo.
6. Kodi moyo wauzimu wa Aisrayeli unali wotani panthawi ya Amosi?
6 Anthu amene anali ‘kudzithinula pa maguwa awo ogonapo, kudya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi kuimba kutsata maliridwe a zeze’ anatsala pang’ono kudzidzimuka ndi zinthu zimene zinali kudzachitika. Anauzidwa kuti anali ‘kutalikitsa tsiku loipa.’ Iwo anayenera kukhumudwa kwambiri ndi mmene zinthu zinalili mu Israyeli, koma ‘sanagwidwe chisoni ndi kuthyoka kwa Yosefe.’ (Amosi 6:3-6) Ngakhale kuti mtundu umenewu unali wolemera, Mulungu anaona kuti moyo wauzimu wa Yosefe, kapena kuti Israyeli, unali woipa. Koma anthuwo ankangokhala n’kumachita ntchito zawo za masiku onse ngati kuti zonse zinali bwino. Masiku anonso anthu ambiri ali ndi mtima ngati umenewo. Angazindikire kuti tikukhaladi m’masiku ovuta, koma malinga ngati mavutowo sakuwakhudza, saganizira za mavuto a ena ndipo amasonyeza kuti zinthu zauzimu sizimawakhudza n’komwe.
Mtundu Wovunda wa Israyeli
7. Kodi chinali kudzachitika n’chiyani ngati anthu Aisrayeli sanamvere machenjezo a Mulungu?
7 Buku la Amosi likufotokoza za mtundu wovunda, ngakhale kuti unkaoneka ngati wabwino kunjaku. Chifukwa chosamvera machenjezo a Mulungu n’kusintha maganizo awo, Yehova anati sadzawatetezanso kwa adani awo. Asuri adzabwera n’kuwagwira, kuwachotsa pa makama awo a minyanga n’kupita nawo ku ukapolo. Moyo wawo wabwino uja udzathera pompo!
8. Kodi chinachitika n’chiyani kuti moyo wauzimu wa Israyeli uwonongeke?
8 Kodi chinachitika n’chiyani kuti Aisrayeli aipe chonchi? Zimenezi zinayamba m’chaka cha 997 Yesu Asanabwere, pamene Mfumu Solomo anamwalira n’kulowedwa m’malo ndi mwana wake Rehabiamu ndipo mafuko khumi a Israyeli anadzipatula kusiyana ndi fuko la Yuda ndi Benjamini. Mfumu yoyamba ya ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi inali Yerobiamu woyamba, 1 Mafumu 11:26) Yerobiamu ananyengerera anthu a mu ufumu wake kuti asamapitenso ku Yerusalemu kukalambira Yehova chifukwa kunali kutali. Koma iye sikuti analidi kudera nkhawa anthuwo. M’malo mwake, iye ankangofuna kuti zake zimuyendere bwino. (1 Mafumu 12:26) Yerobiamu ankachita mantha kuti Aisrayeli akapitiriza kumapita ku kachisi ku Yerusalemu kukachita madyerero apachaka olemekeza Yehova, sadzakhalanso okhulupirika kwa iye koma adzayamba kukhulupirika ku ufumu wa Yuda. Pofuna kupewa zimenezi, Yerobiamu anapanga ana a ng’ombe awiri agolidi, ndipo anaimika mmodzi ku Dani ndi wina ku Beteli. Choncho kulambira mwana wa ng’ombe kunakhala chipembedzo cha boma mu ufumu wa Israyeli.—2 Mbiri 11:13-15.
“mwana wa Nebati.” (9, 10. (a) Kodi Mfumu Yerobiamu woyamba anayambitsa madyerero achipembedzo otani? (b) Kodi Mulungu ankawaona motani madyerero amene ankachitika ku Israyeli panthawi ya Mfumu Yerobiamu wachiwiri?
9 Yerobiamu anayesetsa kuti chipembedzo chatsopanocho chizioneka cholemekezeka. Anayambitsa madyerero omwe zochitika zake zinali zosasiyana kwenikweni ndi madyerero ochitika m’Yerusalemu. Pa 1 Mafumu 12:32, timawerenga kuti: “Yerobiamu anaika madyerero mwezi wachisanu ndi chitatu, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m’Beteli.”
10 Yehova sanasangalale ndi madyerero a chipembedzo chonyenga amenewo. Iye ananena mosabisa mawu kuti sanasangalale ndi madyererowo kudzera mwa Amosi patatha zaka zopitirira 100, panthawi ya ulamuliro wa Yerobiamu wachiwiri, amene anakhala mfumu ya ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi pafupifupi m’chaka cha 844 Yesu Asanabwere. (Amosi 1:1) Malinga ndi Amosi 5:21-24, Mulungu anati: “Ndidana nawo, ndinyoza madyerero anu, sindidzakondwera nawo masonkhano anu oletsa. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng’ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine. Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva maimbidwe a zisakasa zanu. Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.”
Kufanana Kwake ndi Masiku Ano
11, 12. Kodi pali kufanana kotani pakati pa kulambira kwa Aisrayeli akale ndi kumene kumapezeka m’Matchalitchi Achikristu?
11 Mwachionekere, Yehova anayesa mitima ya anthu a mu Israyeli amene ankachita madyerero, ndipo anakana madyerero awowo ndi nsembe zawo. Mofanana ndi zimenezo, Mulungu masiku ano amakana madyerero achikunja a Matchalitchi Achikristu, monga Khirisimasi ndi Isitala. Kwa anthu olambira Yehova, sipangakhale kugwirizana pakati pa chilungamo ndi chosalungama, ndipo kuunika sikungayanjane ndi mdima.—2 Akorinto 6:14-16.
12 Palinso kufanana kwina pakati pa kulambira kwa mwana wa ng’ombe kumene Aisrayeli anali kuchita ndi kulambira kwa Matchalitchi Achikristu. Ngakhale kuti anthu ena amene amanena kuti ndi Akristu amavomereza kuti Mawu a Mulungu ndi oona, anthu a m’Matchalitchi Achikristu salambira Mulungu chifukwa choti amamukonda. Akanakhala kuti amam’konda, akanalimbikitsa kulambira Yehova “mumzimu ndi m’choonadi” chifukwa iye amakondwera ndi kulambira koteroko. (Yohane 4:24) Ndiponso, Matchalitchi Achikristu salola kuti “chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.” M’malo mwake, iwo nthawi zonse amapeputsa makhalidwe abwino amene Mulungu amafuna. Matchalitchi Achikristu amalekerera chiwerewere ndi machimo ena aakulu ndipo amafika mpaka podalitsa zikwati za amuna okhaokha kapena akazi okhaokha!
‘Kondani Chokoma’
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mawu a pa Amosi 5:15?
13 Onse amene akufuna kulambira Yehova movomerezeka akuuzidwa kuti: “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma.” (Amosi 5:15) Chikondi ndi chidani ndi makhalidwe amphamvu amene amachokera mu mtima wophiphiritsira. Popeza mtima ndi wonyenga kwambiri, tifunika kuyesetsa kwambiri kuutchinjiriza. (Miyambo 4:23; Yeremiya 17:9) Ngati tilola mtima wathu kulakalaka zinthu zolakwika, tingayambe kukonda zinthu zoipa n’kumadana ndi zinthu zabwino. Ndipo ngati tikhutiritsa zilakolako zimenezo mwa kupitiriza kuchita tchimo, ngakhale tichite changu chotani, sitidzakhala ovomerezeka pamaso pa Mulungu. Choncho tiyeni tizipemphera kwa Mulungu kuti atithandize ‘kudana nacho choipa, ndi kukonda chokoma.’
14, 15. (a) Mu Israyeli, kodi anthu ena amene anali kuchita zabwino anali ndani, koma kodi ena a iwo anali kuchitiridwa zinthu zotani? (b) Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene ali mu utumiki wa nthaŵi zonse masiku ano?
14 Sikuti Aisrayeli onse anali kuchita zoipa pamaso pa Yehova. Mwachitsanzo, Hoseya ndi Amosi ‘anakonda chokoma’ ndipo anatumikira Mulungu mokhulupirika ngati aneneri. Enanso analumbira kukhala Anaziri. Ndipo panthawi imene anakhala Anaziriyo, anapewa kugwiritsa ntchito chinthu chilichonse chopangidwa ndi mpesa, makamaka vinyo. (Numeri 6:1-4) Kodi Aisrayeli enawo anawaona bwanji anthu okhulupirika odzimana amenewa? Yankho lake n’lodabwitsa kwambiri ndipo likusonyeza mmene mtunduwo unaipira. Amosi 2:12 amati: “Munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.”
15 Poona kukhulupirika kwa Anaziri ndi aneneriwo, Aisrayeliwo anafunika kuchita manyazi ndi kusintha njira zawo. M’malo mwake, iwo mopanda chikondi anayesetsa kulepheretsa anthu okhulupirika amenewo kuti asapatse Mulungu ulemerero. Nafenso tisamayese kukopa Akristu anzathu amene ali apainiya, amishonale, oyang’anira oyendayenda, kapena otumikira pa Beteli kuti asiye utumiki wawo wanthawi zonse n’kuyambiranso kukhala moyo umene anthu ambiri amati ndiye moyo weniweni. M’malo mwake, tiyeni tiziwalimbikitsa kupitiriza ntchito yawo yabwino.
16. N’chifukwa chiyani Aisrayeli anali bwino panthawi ya Mose kusiyana ndi mmene analili panthawi ya Amosi?
16 Ngakhale kuti Aisrayeli ambiri anali ndi moyo wa mwanaalirenji panthawi ya Amosi, iwo analibe “chuma cha kwa Mulungu.” (Luka 12:13-21) Makolo awo anadya mana okhaokha m’chipululu kwa zaka 40. Sanali kudya nyama ya ng’ombe zonenepa kapena kugona mwaulesi pa makama a wofuwofu opangidwa ndi minyanga. Koma Mose anawauza zoona pamene anati: “Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; . . . Zaka izi makumi anayi Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowa kanthu.” (Deuteronomo 2:7) Inde, panthawi yonse imene Aisrayeli anali m’chipululu, anali ndi zinthu zimene ankafunikiradi pa moyo wawo. Ndipo koposa zonse, Mulungu anawakonda, anawateteza, ndiponso anawadalitsa!
17. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anatsogolera Aisrayeli akale kuwapititsa ku Dziko Lolonjezedwa?
17 Yehova anakumbutsa anthu amene analipo Amosi 2:9, 10) Koma kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anatsogolera Aisrayeli akale kuchoka ku Igupto kupita ku dziko lolonjezedwalo? Kodi cholinga chake chinali choti akakhale ndi moyo wa mwanaalirenji n’kuiwala Mlengi wawo? Ayi ndithu! M’malo mwake, iye anachita zimenezo n’cholinga choti iwowo athe kumulambira monga anthu aufulu ndiponso oyera mwauzimu. Koma anthu okhala mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi sanadane nacho choipa ndi kukonda chokoma. M’malo mwake iwo tsopano anali kulemekeza mafano osema, osati Yehova Mulungu. Zinali zomvetsa chisoni kwabasi!
panthawi ya Amosi kuti Iye anabweretsa makolo awo ku Dziko Lolonjezedwa ndipo anawathandiza kugonjetsa adani onse amene anali m’dzikomo. (Yehova Anawalanga
18. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova watimasula mwauzimu?
18 Mulungu sikuti anangonyalanyaza khalidwe lochititsa manyazi la Aisrayeliwo. Iye ananena maganizo ake mosabisa pamene anati: “Ndidzakulangani chifukwa cha mphulupulu zanu zonse.” (Amosi 3:2) Mawu amenewa ayenera kutikumbutsa za kumasulidwa kwathu ku Igupto wamakono, dongosolo la zinthu loipali. Sikuti Yehova watimasula mwauzimu n’cholinga choti tizichita zinthu zongofuna kudzisangalatsa eni akefe basi. M’malo mwake, watimasula kuti tim’patse ulemerero ndi mtima wathu wonse monga anthu aufulu otsatira kulambira koyera. Ndipo aliyense wa ife adzayankha yekha malinga ndi mmene akugwiritsira ntchito ufulu umene Mulungu watipatsawu.—Aroma 14:12.
19. Malinga ndi Amosi 4:4, 5, kodi Aisrayeli ambiri anayamba kukonda chiyani?
19 N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri mu Israyeli ananyalanyaza uthenga wa Amosi wofunikawo. Pa Amosi 4:4, 5, mneneriyu anavumbula matenda auzimu amene mtima wawo unali nawo pamene ananena kuti: “Idzani ku Beteli, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, . . . pakuti ichi muchikonda, inu ana a Israyeli.” Aisrayeli sanayesetse kukonda zinthu zoyenera Iwo sanatchinjirize mitima yawo. Motero, ambiri a iwo anayamba kukonda zoipa ndi kudana ndi zabwino. Aisrayeli ouma mtimawo, amene anali kulambira mwana wa ng’ombe, sanasinthe. Yehova anali kudzawalanga ndipo anakhalabe ochimwa mpaka imfa yawo!
20. Kodi munthu angachite bwanji zinthu zogwirizana ndi Amosi 5:4?
20 Zikuoneka kuti kunali kovuta kwa munthu aliyense wokhala mu Israyeli masiku amenewo kukhalabe wokhulupirika kwa Yehova. Masiku anonso n’zovuta kuchita zosiyana ndi zimene ambiri akuchita, ndipo Akristu achinyamata ndi achikulire omwe masiku ano akudziwa bwino zimenezi. Komabe, mtima wokonda Mulungu ndi wofuna kum’kondweretsa unalimbikitsa Aisrayeli ena kutsata kulambira koona. Yehova anawaitana iwo mokondwera monga mmene mawu a pa Amosi 5:4 akunenera kuti: “Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo.” Masiku ano, Mulungu amachitanso chimodzimodzi pochitira chifundo anthu amene alapa ndi amene akumufunafuna mwa kuphunzira molondola Mawu ake kenaka n’kuchita zimene Iye akufuna. Kuchita zimenezi si kophweka, koma kumabweretsa moyo wosatha.—Yohane 17:3.
Moyo wa Mwanaalirenji Ngakhale Kuli Njala Yauzimu
21. Kodi ndi njala yotani imene imagwera anthu amene satsatira kulambira koona?
21 Kodi anthu amene sanatsate kulambira koona akanayembekezera chiyani? Njala yoipa kuposa njala zonse. Njala imeneyi inali yauzimu! Ambuye Mfumu Yehova anati: “Akudza masiku, . . . akuti ndidzatumiza njala m’dzikomo, si njala ya mkate kapena ludzu la madzi, koma njala ya kumva mawu a Yehova.” (Amosi 8:11) Matchalitchi Achikristu ali m’kati movutika ndi njala yauzimu imeneyi. Komabe anthu ena oona mtima amene ali m’Matchalitchi Achikristuwo, akutha kuona kuti anthu a Mulungu ndi olemera mwauzimu ndipo akukhamukira ku gulu la Yehova. Kusiyana kwa mmene zinthu zilili m’Matchalitchi Achikristu ndi mmene zinthu zilili pakati pa Akristu oona kunafotokozedwa bwino m’mawu a Yehova akuti: “Taonani atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala; taonani, atumiki anga adzamwa, koma inu mudzakhala ndi ludzu; taonani, atumiki anga adzasangalala, koma inu mudzakhala ndi manyazi.”—Yesaya 65:13.
22. N’chifukwa chiyani tikusangalala?
22 Ife monga atumiki a Yehova, kodi timayamikira zinthu zauzimu zimene timapatsidwa ndi madalitso amene tili nawo? Tikamaphunzira Baibulo ndi mabuku achikristu, ndi kupezeka pamisonkhano ya mpingo, yadera, ndi yachigawo, timamvadi ngati tikufuna kuimba chifukwa chosangalala mumtima. Tikusangalala chifukwa chomvetsa bwino Mawu a Mulungu, kuphatikizapo ulosi wouziridwa ndi Mulungu wa Amosi.
23. Kodi anthu amene amalemekeza Mulungu amasangalala ndi chiyani?
23 Kwa anthu onse amene amakonda Mulungu ndipo amafuna kum’patsa ulemerero, ulosi wa Amosi uli ndi uthenga wa chiyembekezo. Kaya tikhale olemera kapena osauka pakadali pano, kapena tikumane ndi mayeso otani m’dziko lamavutoli, ife amene timakonda Mulungu tikusangalala ndi madalitso a Mulungu ndi chakudya chauzimu chapamwamba zedi. (Miyambo 10:22; Mateyu 24:45-47) Choncho, ulemerero wonse upite kwa Mulungu, amene amatipatsa ife zonse mochulukira kuti tikondwere nazo. Ndipotu tiyeni tonsefe tiyesetse kumulemekeza ndi mtima wathu wonse mpaka muyaya. Tidzakhala ndi mwayi wapadera umenewo ngati tifunafuna Yehova, Amene Amayesa mitima.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi zinthu zinali bwanji mu Israyeli panthawi ya Amosi?
• Mmene zinthu zinalili mu ufumu wa Israyeli wa mafuko khumi zikufanana bwanji ndi mmene zinthu zilili masiku ano?
• Kodi masiku ano kuli njala ya mtundu wanji imene inanenedweratu, koma kodi ndani amene sanakhudzidwe nayo?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 21]
Aisrayeli ambiri anali ndi moyo wa mwanaalirenji koma sanali olemera mwauzimu
[Chithunzi patsamba 23]
Muzilimbikitsa atumiki a nthawi zonse kuti apitirize ntchito yawo yabwino
[Zithunzi pamasamba 24, 25]
Pakati pa anthu achimwemwe a Yehova palibe njala yauzimu