Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kudalira Chisamaliro cha Yehova

Kudalira Chisamaliro cha Yehova

Mbiri ya Moyo Wanga

Kudalira Chisamaliro cha Yehova

YOSIMBIDWA NDI ANNA DENZ TURPIN

“Nthawi zonse sulephera kufunsa kuti ‘CHIFUKWA CHIYANI,’” anatero mayi anga kwinaku akumwetulira. Ndili wamng’ono makolo anga ndinkawafunsa mafunso ambirimbiri. Koma mayi ndi bambo anga sankandikalipira chifukwa cha mafunso anga achibwanawo. M’malo mwake, iwo anandiphunzitsa kuganiza mwanzeru ndiponso kudziwa pandekha zimene chikumbumtima changa chingandilole kuchita malingana ndi zimene ndinaphunzira m’Baibulo. Zimene anandiphunzitsazi zinadzandithandiza kwambiri m’tsogolo. Tsiku lina ndili ndi zaka 14, anthu a chipani cha Nazi anandilanda makolo anga, moti aka kanali komaliza kuwaona.

BAMBO anga anali a Oskar Denz ndipo mayi anga anali a Anna Maria. Makolo angawa ankakhala mumzinda wa ku Germany wotchedwa Lörrach, womwe uli kufupi ndi malire a dziko la Switzerland. Akadali achinyamata iwo ankachita zandale, ndipo anali odziwika komanso olemekezeka kwambiri m’dera lawolo. Koma m’chaka cha 1922, atangokwatirana kumene, makolo angawa anasintha maganizo awo pankhani za ndale ndiponso anasintha zolinga zawo m’moyo. Mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Ophunzira Baibulo, omwe masiku ano amatchedwa kuti Mboni za Yehova, ndipo anasangalala kwambiri kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mtendere padziko pano. Posakhalitsa bambo anayambanso kuphunzira, ndipo onse anayamba kupita kumisonkhano ya Ophunzira Baibulo. Chaka chimenecho pa Khirisimasi bambo anapatsa mayi buku lotchedwa Zeze wa Mulungu, lothandiza pophunzira Baibulo. Ineyo ndinabadwa pa March 25, 1923 ndipo mwana ndinalipo ndekha m’banja mwathu.

Panopo, nthawi zina ndimafatsa n’kumaganizira za moyo wosangalatsa wa m’banja mwathu. Panthawi ya chilimwe tinkapita kokayenda m’nkhalango yotchedwa Black Forest ndipo ndimakumbukiranso ntchito za pakhomo zimene mayi ankandiphunzitsa. M’maganizo mwangamu ndimathabe kuwaona ataima poteropo m’khitchini n’kumandiyang’anira ineyo ndikuphika, ndikadali kamtsikana kakang’ono. Chinthu chachikulu kwambiri chimene makolo anga anandiphunzitsa ndicho kukonda Yehova Mulungu ndi kumukhulupirira.

Mpingo wathu unali ndi anthu pafupifupi 40 olalikira mwakhama za Ufumu. Makolo anga anali ndi luso louza anthu za Ufumu pampata uliwonse. Chifukwa cha zinthu zina zimene ankachita kale m’deralo, iwo ankakhala omasuka ndi anthu, ndipo anthu ambiri ankawalandira bwino. Nditakwanitsa zaka zisanu ndi ziwiri, nanenso ndinkafuna kuti ndizilalikira nawo khomo ndi khomo. Nditapita tsiku loyamba, munthu amene ndinali naye anandipatsa mabuku, n’kundilozera nyumba, basi n’kungondiuza kuti, “Pita ukaone ngati akuwafuna mabukuwa.” M’chaka cha 1931, tinapita ku msonkhano waukulu wa Ophunzira Baibulo ku Basel, Switzerland. Makolo anga anabatizidwira kumeneku.

Chipwirikiti Kenako Ulamuliro Wankhanza

Panthawiyo m’dziko la Germany munali chipwirikiti chadzaoneni, ndipo magulu angapo a ndale ankamenyana koopsa m’misewu. Tsiku lina usiku, ndinadzidzimuka nditamva kukuwa kuchokera m’nyumba yoyandikana nayo. M’nyumbamo anyamata awiri a zaka zosakwana 20 anali akupha mchimwene wawo ndi chitsulo chokusira udzu changati foloko chifukwa choti anasiyana naye maganizo pa nkhani za ndale. Kudana ndi Ayuda kunakulanso kwambiri. Kusukulu kwathu kunali mtsikana wina amene ankamuuza kuti aimirire pakona chifukwa choti anali Myuda basi. Ndinkamumvera chisoni kwambiri, osadziwa kuti inenso ndiyamba kudedwa m’njira yotereyi.

Pa January 30, 1933, Adolf Hitler anayamba kulamulira dziko la Germany. Chapafupi ndi nyumba yathu tinaona anthu a chipani cha Nazi akusangalala kuti apambana ndipo anali kuimika mbendera yawo pa maofesi a akuluakulu oyang’anira mzindawo. Aphunzitsi athu kusukulu anatengeka nazo kwambiri ndipo anatiphunzitsa kuti polonjerana tizinena kuti “Heil Hitler!” Tsiku lomwelo ndinawauza bambo anga za nkhaniyi. Zimenezi zinawasokoneza maganizo kwabasi. Iwo anati: “Mawu amenewo si abwino ayi. Mawu akuti “Heil” amatanthauza kuti chipulumutso. Motero ifeyo titati tizinena kuti ‘Heil Hitler’ ndiye kuti tikunena kuti iyeyo, osati Yehova ndiye angatipatse chipulumutso. Ineyo sindikuona kuti ndi bwino kutero, koma iweyo uganize wekha zoyenerera kuchita.”

Anzanga a kusukulu anayamba kundithawa chifukwa chakuti ndinasiya kuchita nawo sawatcha ya Hitler. Mpaka anyamata ena ankandimenya aphunzitsi akakhala kuti sakuona. Patapita nthawi anasiya kundivutitsa, koma ngakhale anzanga apamtima anandiuza kuti abambo awo anawaletsa kusewera nane, akuti chifukwa choti ndingawaike m’mavuto aakulu.

Patatha miyezi iwiri anthu a chipani cha Nazi atatenga boma ku Germany, iwo analetsa gulu la Mboni za Yehova akuti chifukwa choti linali losokoneza boma. Gulu lankhanza la asilikali a chipani cha Nazi linatseka ofesi ya nthambi ku Magdeburg ndipo linaletsa misonkhano yathu. Koma poti tinkakhala kufupi ndi malire, Bambo anapeza zilolezo zoti tiziwoloka malirewo n’kupita ku Basel, kumene tinkakachita misonkhano ya Lamlungu. Nthawi zambiri iwo ankanena kuti ankalakalaka abale athu a ku Germany atamalandira chakudya chauzimu chotere kuti chiwathandize kulimba mtima akamaganizira mavuto amene akumane nawo.

Maulendo Oopsa Kwambiri

Atatseka ofesi ya ku Magdeburg, munthu wina yemwe kale ankagwira ntchito ku ofesiyo, dzina lake Julius Riffel, anabwerera ku Lörrach, komwe kunali kwawo, kuti alinganize ntchito yolalikira yomwe panthawiyi inkachitika mobisa. Nthawi yomweyo bambo ananena kuti amuthandiza. Iwo anakhala nane pansi pamodzi ndi mayi anga n’kutilongosolera kuti avomera kuthandizapo pantchito yotenga mabuku ofotokoza Baibulo ku Switzerland n’kupita nawo ku Germany. Bambowo ananena kuti ntchitoyi n’njoopsa kwambiri moti angathe kumangidwa nthawi ina iliyonse. Sankafuna kuti ifeyo tione ngati kuti sitingachitire mwina koma kuchita nawo ntchitoyi basi. Anatero chifukwa ankadziwa kuti ntchitoyi ndi yoikanso moyo wathu pachiswe. Koma nthawi yomweyo mayi ananena kuti, “Ineyo ndithandizana nanu.” Kenaka onse awiri anandiyang’ana ndipo nanenso ndinanena kuti, “Nanenso ndithandizana nanu.”

Mayi analuka kachikwama kakakulu ngati magazini ya Nsanja ya Olonda. Magaziniwo ankawalowetsera pambali pa kachikwamako kenaka ankakatseka mochita kukaluka. Anasokereranso matumba obisika m’zovala za bambo ndipo anasoka zovala ziwiri zam’kati zoti ineyo ndi amayiwo tizibisamo zinthu monga timapepala ndiponso timabuku tina ting’onoting’ono tothandiza kuphunzira Baibulo. Nthawi iliyonse tikafikitsa mwachinsinsi kunyumba chuma chamtengo wapatalichi, mitima inkakhala pansi ndipo tinkathokoza Yehova. Tinkabisa mabukuwa m’chipinda chapamwamba cha nyumba yathu.

Poyamba, anthu a chipani cha Nazi sankatikayikira m’njira ina iliyonse. Sankatifunsa chilichonse kapenanso kubwera kunyumba kwathu kudzafufuza zinthu. Komabe tinali ndi nambala yachinsinsi yoti tizigwiritsira ntchito ngati zinthu zitavuta ndipo nambala yake inali 4711. Nambalayi inali dzina la mafuta enaake otchuka onunkhiritsa thupi. Cholinga chake chinali chakuti tizichenjezera abale tikaona kuti kunyumba kwathu kwaopsa ndipo sayenera kufikako. Bambo anawauzanso abalewo kuti aziyang’ana kaye mawindo a pabalaza pathu asanalowe m’nyumbamo. Akaona kuti windo la kumanzere n’lotsegula, ndiye kuti chinachake sichili bwino ndipo asafikeko.

M’chaka cha 1936 ndi 1937, apolisi achinsinsi a chipani cha Nazi otchedwa Gestapo anamanga anthu ambirimbiri ndipo a Mboni ochuluka anawaponya m’ndende zosiyanasiyana kuphatikizapo ndende zozunzirako anthu. Kumeneko ankawazunza mosaneneka. Ofesi ya nthambi ku Bern, m’dziko la Switzerland, inayamba kusonkhanitsa malipoti a zimene zinali kuchitika m’malo oterewa, kuphatikizaponso malipoti ena amene anachita kuwazembetsa kuchokera ku ndende zozunzirako anthu. Malipotiwa ankafuna kuti akawaike m’buku lakuti Kreuzzug gegen das Christentum (Nkhondo Yolimbana ndi Chikristu), lomwe linaulula nkhanza zonse zimene a chipani cha Nazi anali kuchita. Ifeyo tinayamba kuchita ntchito yoopsayi, yotenga malipotiwa n’kuwoloka nawo malire mpaka kukafika nawo ku Basel. Anthu a chipani cha Nazi akanati atigwire nawo mapepala oletsedwawa, tikanamangidwa nthawi yomweyo. Ndinalira powerenga za mmene abale athu anali kuzunzidwira. Koma zimenezi sizinandichititse mantha ayi. Sindinkakayika kuti Yehova ndiponso makolo anga, omwe anali anzanga apamtima, andisamalira.

Ndinamaliza sukulu ndili ndi zaka 14 ndipo ndinayamba ntchito ya ukalaliki mu sitolo inayake yogulitsa zipangizo zosiyanasiyana. Nthawi zambiri, tinkayenda maulendo athuwa Loweruka madzulo kapena Lamlungu, poti masiku amenewa bambo sankagwira ntchito. Tinkayenda maulendowa pafupifupi milungu iwiri iliyonse. Tinkaoneka ngati mmene ankaonekera mabanja ena aliwonse amene ankapita kokayenda Loweruka ndi Lamlungu. Ndipo kwa zaka pafupifupi zinayi asilikali a pamalirewo sanatiimitsepo kapena kuyesa kutisecha, mpaka tsiku linalake m’mwezi wa February mu 1938.

Anatitulukira!

Sindidzaiwala nkhope ya nkhawa imene bambo anga anali nayo pamene tinafika pa malo amene tinkalandirira mabuku pafupi ndi Basel n’kuona chimulu chachikulu cha mabuku oti titenge. Popeza kuti banja lina lotenga mabuku linali litamangidwa, tinayenera kutenga mabuku ambiri ndithu. Titafika pa malirepo mkulu wina waboma anatiyang’ana motikayikira ndipo analamulira kuti atiseche. Atatipeza ndi mabuku aja, anatigwira mfuti yake ili m’manja, n’kutipititsa ku magalimoto apolisi amene anali kudikirira poteropo. Tili m’galimoto yapolisi ija, bambo anandigwira dzanja n’kundiuza monong’ona kuti: “Osapereka abale ako. Osaulula dzina la mbale aliyense!” Ndiye ndinayankha kuti “Ayi, sindingaulule aliyense.” Titafikanso ku Lörrach, bambo anga okondedwa anawatenga. Nthawi yomaliza kuwaona inali pamene anali kutseka zitseko za ndendeyo.

Kwa maola okwana anayi, amuna anayi a gulu la Gestapo anali kundifunsa mafunso, n’kumanena kuti ndiwauze mayina ndiponso malo amene kukukhala a Mboni ena. Nditakana, mkulu winayo anapsa mtima n’kundiopseza kuti, “Ngati sukufuna kuulula mwaulemu, uona!” Komabe sindinaulule chilichonse. Kenaka ineyo ndi mayi anabwerera nafe kunyumba, ndipo kwa nthawi yoyamba anasecha nyumbayo. Mayi anga anawagwira ndipo ineyo ananditumiza kwa mayi anga aakulu n’kuwauza kuti azindilera. Sankadziwa kuti mayi anga aakuluwo analinso a Mboni. Ngakhale kuti ankandilola kupita kuntchito, amuna anayi a gulu la Gestapo anaimitsa galimoto kutsogolo kwa nyumba yathu kuti aziona chilichonse chimene ndikuchita komanso panali wapolisi amene anali kuyang’anira msewu woyenda anthu apansi.

Tsiku lina masana, patapita masiku angapo, ndinatuluka m’nyumba n’kuona mlongo wina wamng’ono atakwera njinga n’kumayendetsa monditsata. Atandiyandikira ndinaona kuti akufuna kundiponyera kapepala. Ndinawakha kapepalako, n’kutembenuka nthawi yomweyo kuti ndione ngati a Gestapo aja andiona. Ndinadabwa kuona kuti panthawi imeneyi iwo anali atayang’ana kwina, akuseka mwachikhakhali.

Kakalata kamene mlongoyu anandibweretsera kanali kondiuza kuti ndipite kunyumba kwa makolo ake dzuwa likafika pamutu. Komano poti a Gestapo anali kundilonda, kodi n’kanatani kuti ndisawaike pamavuto makolo akewo? Ndinayang’ana anthu anayi a Gestapo omwe anali m’galimoto aja kenaka n’kuyang’ananso wapolisi amene anali kuyendayenda mumsewu uja. Ndinasowa chochita ndipo ndinapemphera kwa Yehova ndi mtima wonse kuti andithandize. Mosadziwika bwino wapolisi uja anangopita pa galimoto ya Gestapo ija n’kuwauza anzake aja zinazake. Kenaka iye analowa m’galimotomo, basi onsewo n’kunyamuka.

Nthawi yomweyo mayi anga aakulu anatulukira. Apa n’kuti dzuwa litadutsa kale pamutu. Iwo anawerenga kapepalako ndipo anaona kuti ndibwino kuti tipite kunyumba kwa abalewo monga mmene kapepalako kananenera. Anadziwa kuti mwina abalewo ayenera kuti akonza zondipititsa ku Switzerland. Titafika, banjalo linandisonyeza munthu wotchedwa Heinrich Reiff kuti ndidziwane naye. Iye anandiuza kuti wasangalala kuti ndafika bwinobwino ndiponso kuti wabwera kudzanditenga kuti ndithawire ku Switzerland. Anandiuza kuti pakatha theka la ola tikakumane pa tchire linalake.

Nditathawira Kunja

Mmene ndinkakumana ndi mbale Reiff uja misozi inali chuchuchu chifukwa chowawidwa mtima poganizira kuti ndasiya makolo anga. Sindinkakhulupirira kuti zimenezi zikuchitikadi. Kenaka patatha nthawi, mitima ili m’mwamba chifukwa cha mantha, tinaphatikizana ndi chigulu china cha anthu ochokera kunja kudzaona malo ndipo tinawoloka malire a dziko la Switzerland popanda chovuta.

Nditafika pa ofesi ya nthambi ku Bern, ndinauzidwa kuti abale a kunthambiwo ndiwo anakonza zondithawitsa. Iwo anandipatsa malo oti ndizikhala. Ndinkagwira ntchito m’khitchini, ndipo ndinkaikonda kwambiri ntchitoyi. Koma kukhala kunja kunkandipweteka kwambiri, chifukwa sindinkadziwa kuti chiwachitikire n’chiyani makolo anga, amene anali atawalamula kuti akhale m’ndende zaka ziwiri. Nthawi zina, ndinkakhala ndi chisoni ndiponso nkhawa yaikulu, ndipo zikatero ndinkadzitsekera m’chimbudzi n’kuyamba kulira. Koma nthawi zonse ndinkalemberana nawo makalata makolo angawo, ndipo ankandilimbikitsa kuti ndipitirizebe kukhala wokhulupirika.

Poona chitsanzo chabwino cha makolo anga cha kukhala wokhulupirika, ndinapatulira moyo wanga kwa Yehova n’kubatizidwa pa July 25, 1938. Nditatumikira pa Beteli kwa chaka chathunthu, ndinapita kukagwira ntchito pa Chanélaz, yomwe inali famu imene nthambi ya Switzerland inagula kuti azilimapo chakudya cha banja la Beteli ndiponso kuti kuzikhala abale othawa chizunzo.

Makolo anga atamaliza chilango chimene anapatsidwa mu 1940, achipani cha Nazi anawauza kuti awamasula akanena kuti asiya chipembedzo chawo. Iwo anakana motero anatumizidwa ku ndende zozunzirako anthu. Bambo anawatumiza ku Dachau ndipo mayi anawatumiza ku Ravensbrück. M’nyengo ya dzinja, chaka cha 1941, mayi anga ndi akazi ena a Mboni mu ndendeyo anakana kugwira ntchito yothandiza asilikali. Powalanga, anawauza kuti akhale choimirira panja kukuzizira kwa masiku atatu, masana ndi usiku womwe, ndipo atatero anawatsekera m’zipinda zamdima komanso kwa masiku 40 ankawapatsa chakudya chosakwanira. Kenaka anayamba kuwakwapula. Mayi anga anamwalira pa January 31, 1942, patatha milungu itatu atamenyedwa koopsa.

Bambo anga anawachotsa ku Dachau n’kuwapititsa ku Mauthausen ku Austria. M’ndende imeneyi anthu a chipani cha Nazi ankapheramo akaidi powamana chakudya ndiponso powagwiritsa ntchito yadzaoneni. Koma patatha miyezi isanu ndi umodzi mayi anga atamwalira, anthu a chipani cha Nazi anapha bambo anga m’njira ina. Njira yake inali yowagwiritsira ntchito poyeserera zachipatala. Madokotala a pandendepo ankawapatsira dala akaidi matenda a chifuwa chachikulu cha TB. Kenaka, akaidiwo ankawabaya mumtima ndi jakisoni wakupha. M’chikalata chosonyeza matenda amene bambo anafa nawo anangolembamo kuti “mnofu wa mumtima unafooka.” Bambo panthawiyi anali ndi zaka 43. Ndinadziwa patatha miyezi ingapo za kuphedwa kwa nkhanza kwa makolo angaku. Ngakhale panopa ndikamakumbukira makolo anga okondedwawa ndimatuluka misozi. Komabe chinkandilimbitsa mtima panthawiyo ngakhalenso panopo n’chakuti ndimadziwa kuti mayi ndiponso bambo anga, omwe anali ndi chiyembekezo cha moyo wokakhala kumwamba, onse ali bwinobwino m’manja mwa Yehova.

Nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itatha, ndinali ndi mwayi wochita nawo kalasi la nambala 11 la Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo ku New York. Ndinali wosangalala kwambiri kuphunzira Malemba mwakhama kwa miyezi isanu. Nditamaliza sukuluyi mu 1948, ndinatumizidwa ku Switzerland kukachita ntchito ya umishonale. Posakhalitsa, ndinakumana ndi James L. Turpin, mbale wokhulupirika amene anachita nawo kalasi lachisanu la Gileadi. Ofesi ya nthambi yoyamba itakhazikitsidwa ku Turkey, iyeyu anali woyang’anira. Tinakwatirana m’mwezi wa March 1951 ndipo posakhalitsa tinazindikira kuti ndili ndi pakati. Tinasamukira ku United States ndipo mwana wathu wamkazi, Marlene anabadwa m’mwezi wa December chaka chimenecho.

Kwa zaka zonsezi, ineyo ndi mwamuna wanga Jim takhala tikusangalala kwambiri pochita utumiki wa Ufumu. Panali mtsikana wina wochokera ku China dzina lake Penny amene ndinkaphunzira naye Baibulo, ndipo sindimuiwala. Iyeyu ankakonda kwambiri kuphunzira Baibulo. Anabatizidwa ndipo kenaka anadzakwatirana ndi Guy Pierce, amene tsopano amatumikira m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Chifukwa cha anthu okondedwa oterewa ululu wakuti makolo anga anandisiya sindiumva kwambiri.

Kumayambiriro kwa chaka cha 2004, abale a ku Lörrach, komwe kuli kumudzi kwa makolo anga, anamanga Nyumba ya Ufumu yatsopano m’mphepete mwa msewu wotchedwa Stich. Pokumbukira zimene Mboni za Yehova zinachita, ofesi yoyang’anira mzindawo inaganiza zosintha dzina la msewuwo n’kuupatsa dzina la makolo anga, moti anautcha kuti Denzstraße (Msewu wa Denz). Nyuzipepala ya kumeneku, yotchedwa Badische Zeitung, inali ndi nkhani ya mutu wakuti “Msewu Ausintha Dzina Pokumbukira Banja la a Denz Limene Linaphedwa.” M’nkhaniyi analongosolamo kuti makolo anga “anaphedwa ku ndende ina yozunzirako anthu muulamuliro wa chipani cha Nazi, chifukwa cha chikhulupiriro chawo.” Zimene ofesi yoyang’anira mzindawo inachita sindinkaziyembekezera koma zinandilimbikitsa kwambiri.

Bambo ankakonda kunena kuti tizikonzekera zam’tsogolo ngati kuti nkhondo ya Armagedo siidzafika ifeyo tidakali moyo, komano tsiku lililonse tizichita zinthu ngati kuti Armagedo ikubwera mawa. Ndimayesetsabe kutsatira malangizo amtengo wapatali amenewa. Inde, nthawi zina zimandivuta kuchita zinthu moleza mtima kwinakunso n’kumachita zinthu mosonyeza chiyembekezo champhamvu. Zimandivuta kutero makamaka chifukwanso chakuti ukalamba wandichititsa kuti ndizingokhala panyumba. Komabe, sindinayambe ndakayikapo kuti zimene Yehova analonjeza kwa atumiki ake okhulupirika n’zoona. Iye anati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse . . . Um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”​—Miyambo 3:5, 6.

[Bokosi/​Zithunzi patsamba 29]

MAKALATA AKALE AMTENGO WAPATALI KWAMBIRI

Mayi wina wochokera kumudzi winawake wakutali ndithu anafika ku Lörrach m’ma 1980. Panthawiyo, anthu am’tauniyo ankatenga katundu amene sakumufuna n’kukamuika pa malo enaake amene aliyense ankasankhapo zimene angakonde kuti atenge. Mayiyu anatengapo bokosi lokhala ndi zipangizo zosokera zovala ndipo anapita nalo kunyumba kwake. Kenaka, anapeza kuti m’bokosimo pansi pake panali zithunzi za kamtsikana ndiponso makalata olembedwa pa mapepala a ku ndende zozunzirako anthu. Mayiyu anachita chidwi kwambiri ndi makalatawo ndipo ankafuna kudziwa kamwana katsitsi lomangako.

Ndiyeno tsiku lina m’chaka cha 2000, mayiyo anaona nkhani ina ya m’nyuzipepala yonena za chionetsero cha ku Lörrach chokhudza mbiri yakale. Nkhaniyo inalongosola za mbiri ya Mboni za Yehova, komanso ya banja lathu, panthawi ya ulamuliro wa chipani cha Nazi. Nkhaniyo inali ndi chithunzithunzi cha ineyo ndili mtsikana. Poona kuti kamtsikana ka pa zithunzipo kanali kofanana ndi kamtsikana ka pa zithunzi zina zija, mayiyu anaimbira foni mtolankhani amene analemba nkhaniyi n’kumuuza za makalata aja, amene analipo 42. Patatha milungu ingapo ineyo ndinalandira makalatawo. Anali makalata olembedwa pamanja ndi makolo anga ndipo anali ofunsa mayi anga aakulu za moyo wanga. Makolo angawo sanasiye kudera nkhawa za moyo wanga. N’zodabwitsa kwambiri kuti makalata amenewa sanawonongeke ndipo anapezeka patatha zaka 60.

[Zithunzi patsamba 25]

Banja lathu, lomwe linali losangalala, linapasuka Hitler atayamba kulamulira

[Mawu a Chithunzi]

Hitler: U.S. Army photo

[Zithunzi patsamba 26]

1. Ofesi ya ku Magdeburg

2. Gulu la Gestapo linamanga Mboni zambirimbiri

[Chithunzi patsamba 28]

Ineyo ndi Jim takhala osangalala kwambiri pochita utumiki wa Ufumu