Kodi Dzikoli Likupita Kuti?
Kodi Dzikoli Likupita Kuti?
PALIBE amene sangakonde kuti dziko lonse likhale logwirizana, si choncho kodi? N’zoona kuti pali zinthu zambiri zimene anthu akhala akunena zokhudza mgwirizano. Nthawi zambiri, imeneyi ndiyo imakhala nkhani yaikulu m’misonkhano ya atsogoleri a mayiko. Mu August 2000, atsogoleri achipembedzo oposa 1,000 anakumana ku bungwe la United Nations ku New York, pa msonkhano wa Millennium World Peace Summit, wokambirana za mtendere wa padziko lonse. Pamsonkhanopo anakambirana za njira zothetsera nkhondo za padziko pano. Komabe, ngakhale pamsonkhanowu zokambirana zawo sizinali zamtendere ayi, chifukwa chosagwirizana pankhani zovuta za padziko pano. Katswiri wina wa malamulo a Chisilamu wa ku Jerusalem anakana kufika pamsonkhanopo chifukwa panali mphunzitsi wa Chiyuda. Anthu ena anakhumudwa chifukwa choti mtsogoleri wa chipembedzo cha Chilama sanamuitane pa masiku awiri oyambirira a msonkhanowo poopa kukhumudwitsa dziko la China.
Mu October 2003, mayiko okhala m’mphepete mwa nyanja ya Pacific anakambirana zokhazikitsa bata padziko lonse pa msonkhano wa Asia-Pacific Economic Cooperation (APEC), womwe unachitikira ku Thailand. Mayiko 21 omwe anali pamsonkhanopo analonjeza kuti ayesetsa kuthetsa magulu a zigawenga ndiponso anagwirizana zopeza njira zothandiza kuti padziko lonse pakhale bata. Komabe, pamsonkhanopo nthumwi
zambiri zinaipidwa chifukwa cha zimene nduna yaikulu ina inanena, zomwe ati zinali zosonyeza kuti ndunayo imadana ndi Ayuda.N’chifukwa Chiyani Palibe Mgwirizano?
Ngakhale kuti za mgwirizano wa padziko lonse zimakambidwa kawirikawiri, palibe chooneka chimene chikuchitikapo. Anthu ambiri achita khama kwambiri pankhaniyi, koma kodi n’chifukwa chiyani mgwirizano wotere wakhala ukuwalaka anthu kuyambira kalekale mpaka pano?
Imodzi mwa nduna zazikulu zimene zinali pamsonkhano wa APEC uja inatchula mfundo yomwe ili mbali ya yankho la funso limeneli. Iye anati, “Chinthu chimodzi ndicho mtima wokondetsetsa dziko lanu mopitirira muyeso.” Inde, anthu amadzikuza kwambiri chifukwa cha mayiko awo. Dziko ndiponso fuko lililonse la anthu limafuna kukhala ndi ufulu wochita zimene likufuna. Kudziimira kwa mayiko pamodzi ndi mzimu wa mpikisano komanso umbombo zabweretsa vuto lomwe lingathe kufika poipa kwambiri. Nthawi zambiri, zimene boma linalake likufuna n’zimene zimachitika, ngakhale ngati mayiko ena onse sakuzifuna.
Mogwirizana ndi wamasalmo, mtima wokonda dziko lanu mopitirira muyezo tinganenedi kuti ndi “mliri wosakaza.” (Salmo 91:3) Khalidweli lili ngati mliri womwe ukuvutitsa anthu mosaneneka. Limachititsa kuti anthu azidana ndi anthu a m’mayiko ena ndipo lakhalapo kwa zaka zambiri zedi. Masiku ano, khalidwe limeneli limagawanitsa anthu, ndipo atsogoleri alephera kulithetsa.
Atsogoleri ambiri odziwa bwino nkhaniyi amavomereza kuti khalidweli pamodzi ndi kudzikonda n’zimene kwenikweni zimayambitsa mavuto padziko pano. Mwachitsanzo, amene kale anali Mlembi Wamkulu wa bungwe la United Nations a U Thant anati: “Mavuto ambiri amene timakumana nawo masiku ano, amayamba chifukwa cha kukhulupirira zinthu zolakwika . . . Chimodzi mwa zinthu zoterezi ndicho mfundo yongotsatira chilichonse chimene dziko lanu likufuna, ngakhale chitakhala cholakwika bwanji.” Koma mayiko ambiri masiku ano, amaganizirabe kwambiri zofuna zawo basi, motero amalimbikira kwambiri kukhala odziimira. Mayiko amene ali ndi ufulu wotere safuna ngakhale pang’ono kuchepetsako ufuluwo. Mwachitsanzo nyuzipepala ya International Herald Tribune inafotokoza izi ponena za bungwe la European Union: “Mpaka panopo, mayiko a ku Ulaya amangokhalira kupikisana
ndipo sakhulupirirana. Mayiko ambiri a m’bungweli sasangalala kuti dziko lina la m’bungweli likule mphamvu kwambiri n’kuyamba kutsogolera mayiko anzake.”Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu, limalongosola molondola zotsatirapo za ulamuliro wa anthu. Limati: “Wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlaliki 8:9) Pogawa dzikoli kuti likhale maulamuliro awoawo osiyanasiyana, anthu enaake paokhapaokha ndiponso magulu osiyanasiyana, akumana ndi zimene Baibulo limatanthauza ponena kuti: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1.
Mlengi wathu, yemwe amadziwa bwino zimene timafunikiradi, sanafune kuti anthu azikhazikitsa maboma awo n’kumadzilamulira okha. Pochita zimenezi, anthu anyalanyaza cholinga cha Mulungu ndiponso mfundo yakuti iye ndiye mwini zonse. Lemba la Salmo 95:3-5 limati: “Yehova ndiye Mulungu wamkulu; ndi mfumu yaikulu yoposa milungu yonse. Malo ozama a dziko lapansi ali m’dzanja lake; chuma cha m’mapiri chomwe ndi chake. Nyanja ndi yake, anailenga; ndipo manja ake anaumba dziko louma.” Mulungu ndiye Woyenera kulamulira ndipo aliyense ayenera kutsatira ulamuliro wake. Pofuna kukhazikitsa maulamuliro awoawo, mayiko kwenikweni akulimbana ndi chifuno cha Mulungu.—Salmo 2:2.
Kodi Pakufunikira Chiyani Kuti Pakhale Mgwirizano?
Njira yokhayo imene idzagwirizanitse dziko ndiyo kukhala ndi ulamuliro umodzi wokha padziko lonse wochita zinthu moganizira anthu onse. Anthu ambiri oganiza bwino amaona kuti pakufunikadi ulamuliro wotere. Komabe, ambiri a iwo amakhulupirira mabungwe olakwika poganiza kuti ndiwo angakwanitse kutero. Mwachitsanzo, anthu ambiri otsata bwino nkhani zotere, kuphatikizapo atsogoleri a zipembedzo, akhala akulimbikitsa anthu kudalira bungwe la United Nations kuti ndilo lidzabweretse mgwirizano padziko lonse. Komatu, mabungwe a anthu, ngakhale atamatsatira mfundo zabwino motani, sanathetsepo n’kale lonse mavuto a padziko lonse a anthu. M’malo mwake, zochita za mabungwe ambiri oterewa zimangosonyeza kugawanika kumene kulipo pakati pa mayiko osiyanasiyana.
Potichenjeza kuti tisamakhulupirire zoti magulu okhazikitsidwa ndi anthu angathetse vutoli, Baibulo limati: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Salmo 146:3) Kodi pamenepa ndiye kuti ndibwino kuti tingoiwalako za mgwirizano wa padziko lonse? Ayi tisatero. Pali njira ina.
Anthu ambiri sadziwa kuti Mulungu wakhazikitsa kale boma limene lingathe kugwirizanitsa dziko lonse. Baibulo limanena za Yehova Mulungu kuti: “Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera. Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale ako ako.” (Salmo 2:6, 8) Onani kuti lembali likunena kuti Yehova Mulungu ‘wadzoza mfumu,’ imene mu vesi 7 akuitcha kuti “Mwana wanga.” Ameneyu si wina ayi, koma ndi Mwana wamkulu kwambiri wauzimu wa Mulungu, Yesu Kristu, amene wapatsidwa mphamvu zolamulira mayiko onse.
Mmene Mgwirizano wa Padziko Lonse Udzabwerere
Anthu ambiri savomereza ulamuliro wakumwamba umenewu womwe Mulungu wakhazikitsa. Mayiko amalimbikira kakaka ufulu wodziimira umene eniakewo akuti ali nawo. Komabe, Mulungu sadzalekerera anthu okana kuvomereza ulamuliro wake ndiponso boma limene wakhazikitsa. Pa nkhani ya anthu amene amakana kuvomereza zimene wakonzazi, lemba la Salmo 2:9 limanena za Yesu Kristu, Mwanayo kuti: “Udzawathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba.” Kaya akudziwa, kaya sakudziwa, kumene mayikowa akulowera Mulungu akawaonetsako mbonaona. Buku lotsirizira la m’Baibulo limanena za “mafumu a dziko lonse” kuti adzawasonkhanitsira “ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14) Mayikowa pamodzi ndi njira zawo zogawanitsa anthu adzawonongedwa. Zimenezi zidzalambula njira kuti boma la Mulungu liyambe kuchita ntchito yake momasuka.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, kudzera mwa Mwana wake, Iye mwanzeru adzagwiritsira ntchito mphamvu zake pokonza zinthu kuti mgwirizano wa padziko lonse utheke. Boma la Mulungu lidzabweretsa Salmo 72 m’Baibulo. Umenewu ndi ulosi wosimba zimene ulamuliro wa Mwana wa Mulungu udzachitire anthu. Padziko lonse padzakhala mgwirizano weniweni, ndipo mavuto onse a anthu monga, kuponderezana, chiwawa, umphawi, ndi mavuto ena, adzatha.
mgwirizano weniweni ndipo lidzadalitsa anthu onse okonda chilungamo. Tapezani kanthawi pang’ono n’kuwerengaM’dziko logawanika lino, anthu ambiri amaganiza kuti kuyembekezera zinthu zoterezi n’kusaganiza bwino. Komatu maganizo otere n’ngolakwika kwabasi. Malonjezo a Mulungu sanalepherepo kukwaniritsidwa, ndipo sadzalepherapo mpaka kalekale. (Yesaya 55:10, 11) Kodi inuyo mungakonde kudzakhalapo zinthu zikadzasintha chonchi? N’zotheka kuti mudzakhalepo. Ndipotu, alipo kale anthu amene akukonzekera kudzakhalapo nthawi imeneyo. Anthuwa n’ngochokera m’mitundu yosiyanasiyana ya anthu, koma m’malo momalimbana, onsewa amamvera ulamuliro wa Mulungu mogwirizana. (Yesaya 2:2-4) Kodi amenewa ndani? Anthuwa amadziwika ndi dzina loti Mboni za Yehova. Musakane ayi akakuitanani kupita ku malo amene amachitira misonkhano yawo. Ndithu, mukatsitsimutsidwa pocheza ndi anthu amenewa, omwe angakuthandizeni kumvera ulamuliro wa Mulungu kuti nanunso mudzakhalepo panthawi imene padzakhale mgwirizano wosatha.
[Zithunzi patsamba 7]
Anthu ochokera m’mitundu yonse akukonzekera kudzakhala m’dziko logwirizana
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Saeed Khan/AFP/Getty Images
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
Woman grieving: Igor Dutina/AFP/Getty Images; protesters: Said Khatib/AFP/Getty Images; armored cars: Joseph Barrak/AFP/Getty Images