Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amalalikira Uthenga Wabwino kwa Ogontha

Amalalikira Uthenga Wabwino kwa Ogontha

Amalalikira Uthenga Wabwino kwa Ogontha

“AMALIMBIKITSA munthu mwauzimu.” Umu ndi mmene posachedwapa mkulu woyang’anira nyumba ina yosamalira okalamba ku Navalcarnero, mumzinda wa Madrid, m’dziko la Spain, anafotokozera maulendo obwera ku nyumbayo a Mboni za Yehova. Kodi ananena zimenezi chifukwa chiyani?

Ambiri mwa anthu amene ali pa nyumba yosamalira okalamba ya Rosas del Camino ndi ogontha. Komabe, chifukwa choti Mboni zachita khama n’kuphunzira chinenero chamanja cha ku Spain, tsopano Mbonizo zikutha kulankhula ndi anthu a panyumbayo. Mkuluyo anayamikira Mbonizo chifukwa chogwiritsa ntchito nthawi yawo kwaulere kuphunzitsa zinthu za m’Baibulo anthu ofunika kuganiziridwa mwapadera. Iye anafotokoza mmene anthu panyumbayo apindulira ndi ntchito yowaphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu. Nawonso anthu a panyumbayo, makamaka amene amavutika kumva ndiponso kuona, amayamikira kwambiri maulendo a Mbonizo.

Eulogio, mmodzi mwa anthu okhala panyumbayo yemwe ndi wakhungu ndiponso wogontha, tsopano akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsiku lina ali m’kati mophunzira, bambo wina wachikulire anafika ndi kupatsa Mboni yomwe inali kuphunzira ndi Eulogio, ndakatulo imene anthu a panyumbayo analemba posonyeza kuyamikira kwawo. Mutu wa ndakatuloyo unali wakuti “Kukhala Mboni.” Mwa zina ndakatuloyo inati: “Amakhala moyo wabwino, wosunga mwambo, ndipo amalandira nzeru kwa Yehova zimene zimawapatsa chimwemwe. Saatha phazi pa makomo a anthu chifukwa chodalira Yehova.”

Zoonadi, kudalira Yehova kumeneku n’komwe kwachititsa Mboni zambiri padziko lonse kuphunzira chinenero chamanja cha anthu ogontha a m’dziko lawo. Mwa njira imeneyi Mbonizi zimalalikira kwa anthu amenewa uthenga wa m’Baibulo womwe ndi wolimbikitsa ndi wopatsa chiyembekezo.