Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Nowa analowetsa nyama zingati zodyedwa m’chingalawa? Kodi analowetsa nyama 7 zamtundu uliwonse kapena nyama 14?

Nowa atamaliza kumanga chingalawa, Yehova anamuuza kuti: “Talowani, iwe ndi a ku nyumba ako onse m’chingalawamo; chifukwa ndakuona iwe kuti uli wolungama pamaso panga m’mbadwo uno. Nyama zonse zodyedwa udzitengereko wekha zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri, yamphongo ndi yaikazi yake; ndi nyama zosadyedwa ziwiriziwiri yamphongo ndi yaikazi yake.” (Genesis 7:1, 2) Mabaibulo ena monga The New English Bible, The New Jerusalem Bible, ndi Tanakh​—The Holy Scriptures, amamasulira mawu achiheberi oyambirira onena za chiwerengero cha nyama zodyedwa zimenezi kukhala “14.”

Koma mu Chiheberi mawu oti “zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri” sikuti nthawi zonse amatanthauza kuti ayenera kuphatikizidwa kupanga 14. (Genesis 7:2) Mwachitsanzo, pa 2 Samueli 21:20 pakufotokoza za “munthu wa msinkhu waukulu” amene anali ndi “zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi paphazi lonse zala zisanu ndi chimodzi.” Mu Chiheberi, chiwerengero choti “zisanu ndi chimodzi” chinalembedwa kawiri. Zimenezi sizikutanthauza kuti chimphonacho chinali ndi zala 12 kudzanja lililonse kapena kuphazi lililonse. Kulemba chiwerengero kawiri kukungotsindika kuti dzanja lililonse ndi phazi lililonse linali ndi zala 6. 

Choncho mawu a pa Genesis 7:2 akuti “zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri” sayenera kuphatikizidwa kuti akhale 14, ngati mmene kulemba “ziwiri” kawiri pa Genesis 7:9, 15 sikutanthauza nyama zinayi. Chotero, Nowa analowetsa nyama “zisanu ndi ziwiri” zamtundu uliwonse wa nyama zodyedwa, ndipo analowetsa “ziwiri” zamtundu uliwonse wa nyama zosadyedwa.

Nangano bwanji za mawu akuti “yamphongo ndi yaikazi yake” amene akutsatira mawu akuti “zisanu ndi ziwiri, zisanu ndi ziwiri” pa Genesis 7:2? Chifukwa cha mawu amenewa, ena amaganiza kuti Nowa anauzidwa kulowetsa nyama 14 zamtundu uliwonse wodyedwa, zamphongo 7 ndi zazikazi 7. Komabe, nyama zodyedwa sizinangosungidwa ndi cholinga chobereka chokha. Lemba la Genesis 8:20 limatiuza kuti Nowa atatuluka m’chingalawa, “anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.” Popeza anasunga nyama 7 zamtundu uliwonse wodyedwa, Nowa anali ndi nyama imodzi yopanda inzake yoti apereke nsembe. Zimenezi zinachititsa kuti pakhale nyama magulu atatu zamtundu uliwonse wa nyama zodyedwa, yamphongo ndi yaikazi yake, kuti ziziberekana.