Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Atate Wanu Ndi Wachifundo’

‘Atate Wanu Ndi Wachifundo’

‘Atate Wanu Ndi Wachifundo’

“Pitirizani kukhala achifundo, monga Atate wanu ali wachifundo.”​—LUKA 6:36.

1, 2. Kodi zimene Yesu anauza alembi ndi Afarisi ndiponso otsatira ake, zikusonyeza motani kuti chifundo ndi khalidwe lofunika kwambiri?

CHILAMULO chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose chinali ndi malamulo pafupifupi 600. Ngakhale kuti kutsatira Chilamulo cha Mose kunali kofunika, kuchitira ena chifundo kunalinso kofunika kwambiri. Taganizirani zimene Yesu ananena kwa Afarisi, omwe sankachitira anzawo chifundo. Iye anawadzudzula kawiri konse, n’kuwauza kuti Mulungu ananena kuti: “Ndikufuna chifundo, osati nsembe.” (Mateyo 9:10-13; 12:1-7; Hoseya 6:6) Chakumapeto kwa utumiki wake, Yesu anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma munyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.”​—Mateyo 23:23.

2 Mosakayikira, Yesu ankaona kuti chifundo n’chofunika kwambiri. Iye anauza otsatira ake kuti: “Pitirizani kukhala achifundo, monga Atate wanu ali wachifundo.” (Luka 6:36) Komabe, kuti tikhale “otsanzira Mulungu” pambali imeneyi, tikufunika kudziwa tanthauzo lenileni la chifundo. (Aefeso 5:1) Ndiponso, tikamvetsa ubwino wa chifundo zingakhale zosavuta kuti nafenso tikhale achifundo.

Kuchitira Chifundo Anthu Ovutika

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Yehova kuti tidziwe tanthauzo lenileni la chifundo?

3 Wamasalmo anaimba kuti: “Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.” (Salmo 145:8, 9) Yehova ndi “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Munthu wachifundo amakhala wokoma mtima kwa ena. Imeneyi ndi mbali yaikulu ya khalidwe la Mulungu. Ifeyo tingaphunzire tanthauzo lenileni la chifundo kudzera m’chitsanzo chake ndiponso malangizo ake.

4. Kodi lemba la Yesaya 49:15 limatiphunzitsa chiyani za chifundo?

4 Pa Yesaya 49:15, Yehova anati: “Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wom’bala iye?” Maganizo amene amapangitsa Yehova kukhala wachifundo akuyerekezedwa ndi chikondi chimene mayi woyamwitsa amakhala nacho kwa mwana wake. Ngati mwana ali ndi njala kapena akufuna chinachake, chisoni chimalimbikitsa mayiyo kupatsa mwanayo zimene akufuna. Umu ndi mmenenso Yehova amamvera ndi anthu amene amawachitira chifundo.

5. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ndi “wachifundo chochuluka” kwa Aisiraeli?

5 Kumvera ena chisoni n’kofunika koma chofunika kwambiri n’kuwathandiza pa mavuto awo. Taonani zimene Yehova anachita pamene olambira ake anali akapolo ku Iguputo zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Iye anauza Mose kuti: “Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Iguputo, ndamvanso kulira kwawo chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zawo; ndipo ndatsikira kuwalanditsa m’manja a anthu a Aiguputo, ndi kuwatulutsa m’dziko lija akwere nalowe m’dziko labwino ndi lalikulu, m’dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.” (Eksodo 3:7, 8) Patatha zaka pafupifupi 500 Aisiraeli atamasulidwa mu ukapolo ku Iguputo, Yehova anawakumbutsa kuti: “Ine ndinatulutsa Isiraeli mu Iguputo, ndipo ndinakupulumutsani m’manja a Aiguputo, ndi m’manja a maufumu onse anakusautsani.” (1 Samueli 10:18) Chifukwa chosiya kutsatira mfundo zolungama za Mulungu, Aisiraeli ankakumana ndi mavuto aakulu. Koma Yehova ankawachitira chifundo ndipo ankawapulumutsa. (Oweruza 2:11-16; 2 Mbiri 36:15) Izi zikusonyeza mmene Mulungu wachikondi amathandizira anthu ovutika, kapena amene moyo wawo uli pa ngozi. Zoonadi, Yehova ndi “wachifundo chochuluka.”​—Aefeso 2:4.

6. Kodi Yesu Khristu anatsanzira bwanji Atate wake pochitira ena chifundo?

6 Ali pa dziko lapansi, Yesu Khristu anatsanzira Atate ake bwino lomwe mwa kuchitira ena chifundo. Kodi Yesu anatani amuna awiri akhungu atam’pempha kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo”? Amunawa ankapempha Yesu kuti awachiritse mozizwitsa, ndipo iye anawachiritsa. Koma Yesu sanachite chozizwitsachi mopanda chifundo. Baibulo limati: “Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anagwira maso awo, ndipo nthawi yomweyo anayamba kuona.” (Mateyo 20:30-34) Chifundo n’chimene chinapangitsa Yesu kuti achite zozizwitsa zambiri zimene zinathandiza anthu osaona, ogwidwa ndi ziwanda, akhate, ndiponso makolo a ana ovutika.​—Mateyo 9:27; 15:22; 17:15; Maliko 5:18, 19; Luka 17:12, 13.

7. Kodi chitsanzo cha Yehova Mulungu ndi Mwana wake chimatiphunzitsa chiyani za chifundo?

7 Chitsanzo cha Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu chikusonyeza kuti chifundo chili ndi mbali ziwiri. Yoyamba ndi kumvera ena chisoni, ndipo yachiwiri ndi kuwathandiza pa vuto lawo. Kuti munthu akhale wachifundo ayenera kuchita zonsezi. M’Malemba, chifundo kawirikawiri chimatanthauza kulankhula kapena kuchita zinthu zothandiza anthu ovutika. Nangano munthu angasonyeze bwanji chifundo poweruza milandu? Kodi chifundo chingalepheretse munthu kuchita zinthu zina, monga kupereka chilango?

Kuchitira Chifundo Anthu Ochimwa

8, 9. Kodi chifundo chimene Mulungu anachitira Davide atachimwa ndi Bateseba chinaphatikizapo chiyani?

8 Taganizirani zimene zinachitika mneneri Natani atadzudzula Mfumu Davide ya Isiraeli chifukwa chochita chigololo ndi Bateseba. Davide analapa n’kupemphera kuti: “Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu.”​—Salmo 51:1-4.

9 Davide anadzimvera chisoni kwambiri. Yehova anam’khululukira tchimo lakelo ndipo anachepetsa chilango chimene iye ndi Bateseba anayenera kulandira. Malinga ndi Chilamulo cha Mose, Davide ndi Bateseba anayenera kuphedwa. (Deuteronomo 22:22) Ngakhale kuti sanapewe mavuto onse amene anabwera chifukwa cha tchimo lawolo, iwo sanaphedwe. (2 Samueli 12:13) Chifundo cha Mulungu chimaphatikizapo kukhululukira ena. Komatu zimenezi sizilepheretsa Yehova kupereka chilango choyenera.

10. Ngakhale kuti Yehova amaweruza mwachifundo, n’chifukwa chiyani sitiyenera kuchimwa mwadala?

10 Popeza “uchimo unalowera m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi [Adamu],” ndipo “malipiro a uchimo ndiwo imfa,” anthu onse ndi oyenera kufa. (Aroma 5:12; 6:23) Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatiweruza mwachifundo. Komabe, tiyenera kusamala kuti tisamachimwe mwadala popeza kuti Mulungu ndi wachifundo. Lemba la Deuteronomo 32:4 limati: “Njira [za Yehova] zonse ndi chiweruzo,” kutanthauza kuti n’zolungama. Pochitira chifundo ena, Mulungu sanyalanyaza mfundo zake zolungama.

11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji chilungamo kwa Davide patchimo lake ndi Bateseba?

11 Pankhani ya Davide ndi Bateseba, chilango chawo cha imfa chisanasinthidwe, panafunika kuwakhululukira tchimo lawo. Oweruza a mu Isiraeli sanapatsidwe mphamvu yochita zimenezi. Iwo, akanaloledwa kuzenga mlandu umenewu, sakanachitira mwina koma kuwaweruza kuti aphedwe. Zimenezi n’zimene Chilamulo chinanena. Koma, poganizira pangano lake ndi Davide, Yehova ankafuna kuona ngati panali chifukwa chokhululukira tchimo lakelo. (2 Samueli 7:12-16) Choncho, Yehova Mulungu, “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” yemwe ‘amayesa mtima,’ anasankha kuzenga yekha mlanduwo. (Genesis 18:25; 1 Mbiri 29:17) Mulungu akanatha kuona zomwe zinali mu mtima mwa Davide, ndi kudziwa ngati walapa mochokera mumtima, ndiyeno n’kumukhululukira.

12. Kodi anthu ochimwa angatani kuti apindule ndi chifundo cha Mulungu?

12 Chifundo chimene Yehova amatichitira potipulumutsa ku chilango cha imfa chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, n’chogwirizana ndi chilungamo chake. Pofuna kuti azitikhululukira machimo popanda kuphwanya mfundo za chilungamo, Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Khristu, ndipo zimenezi zimasonyeza chifundo chosaneneka. (Mateyo 20:28; Aroma 6:22, 23) Kuti tipindule ndi chifundo cha Mulungu, chimene chingatiteteze ku chilango cha uchimo wobadwa nawo, tiyenera ‘kukhulupirira mwa Mwanayo.’​—Yohane 3:16, 36.

Mulungu Wachifundo ndi Wachilungamo

13, 14. Kodi chifundo cha Mulungu chimasokonezana ndi chilungamo chake? Fotokozani.

13 Popeza kuti chifundo cha Yehova sichiphwanya mfundo zake zolungama, kodi khalidweli limasintha chilungamo chake? Kodi chifundo chimachititsa kuti Mulungu afewetseko mfundo zake zolungama? Ayi, sichoncho.

14 Kudzera mwa mneneri Hoseya, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m’chilungamo, ndi m’chiweruzo, ndi m’ukoma mtima, ndi m’chifundo.” (Hoseya 2:19) Mawu amenewa akusonyezeratu kuti nthawi zonse chifundo cha Yehova chimagwirizana ndi makhalidwe ake ena, kuphatikizapo chilungamo. Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, . . . wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34:6, 7) Choncho, Yehova ndi Mulungu wachifundo ndi wachilungamo. Ponena za iye, Baibulo limati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo.” (Deuteronomo 32:4) Chilungamo cha Mulungu ndi changwiro, mofanana ndi chifundo chake. Palibe khalidwe loposa linzake, ndipo makhalidwewa sasokonezana.

15, 16. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti chilungamo cha Mulungu si chankhanza? (b) Kodi olambira a Yehova angatsimikize za chiyani iye akamadzaweruza dongosolo loipali?

15 Chilungamo cha Yehova si chankhanza. Pafupifupi nthawi zonse, chilungamo chimakhudzana ndi nkhani za malamulo, ndipo pamene munthu wolakwa akuweruzidwa amapatsidwa chilango. Koma, chilungamo cha Mulungu chimaphatikizapo kupulumutsa anthu oyenerera. Mwachitsanzo, Loti ndi ana ake awiri anapulumutsidwa pamene anthu oipa a m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora ankawonongedwa.​—Genesis 19:12-26.

16 Sitingakayikire kuti Yehova akamadzaweruza dongosolo loipali, “khamu lalikulu” la olambira oona, amene “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa” lidzapulumuka. Choncho iwo ‘adzatuluka m’chisautso chachikulu.’​—Chivumbulutso 7:9-14.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Achifundo

17. Kodi chifukwa chachikulu chokhalira achifundo n’chiti?

17 N’zoonadi, chitsanzo cha Yehova ndi Yesu Khristu chimatiphunzitsa tanthauzo lenileni la chifundo. Lemba la Miyambo 19:17 limatipatsa chifukwa chachikulu chokhalira achifundo. Limati: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzam’bwezera chokoma chakecho.” Yehova amasangalala tikamachitirana chifundo chifukwa timakhala tikutsanzira iyeyo ndiponso Mwana wake. (1 Akorinto 11:1) Komanso, timalimbikitsa ena kukhala achifundo popeza kuti wochitira ena chifundo iyenso amachitiridwa chifundo.​—Luka 6:38.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala achifundo?

18 Chifundo chimaphatikizapo makhalidwe ambiri abwino, monga chisomo, chikondi, kukoma mtima ndiponso ubwino. Chisoni n’chimene chimalimbikitsa munthu kuchitira ena chifundo. Ngakhale kuti chifundo cha Mulungu sichifewetsa chilungamo chake, Yehova sakwiya msanga ndipo moleza mtima amapatsa anthu ochimwa nthawi yokwanira kuti alape. (2 Petulo 3:9, 10) Choncho, munthu wachifundo amakhalanso wodekha ndiponso woleza mtima. Popeza kuti chifundo chimaphatikizapo makhalidwe ena ambiri abwino, komanso zipatso zosiyanasiyana za mzimu wa Mulungu, khalidweli limatipatsa mwayi wosonyeza makhalidwe enawo. (Agalatiya 5:22, 23) Choncho ndi bwino kwambiri kuti tiyesetse kukhala achifundo.

“Osangalala Ali Iwo Amene Ali Achifundo”

19, 20. Kodi chifundo chimaposa bwanji chiweruzo?

19 Wophunzira Yakobe anafotokoza chifukwa chimene tiyenera kuchitira ena chifundo nthawi zonse. Iye analemba kuti: “Chifundo n’chopambana kwambiri kuposa chiweruzo.” (Yakobe 2:13b) Yakobe ankanena za chifundo chimene wolambira Yehova amachitira ena. Chifundo chimaposa kwambiri chiweruzo chifukwa chakuti nthawi ikakwana yoti munthu ‘adziyankhire yekha kwa Mulungu,’ Yehova amaganizira ngati munthuyo ali wachifundo, ndipo amam’khululukira pa maziko a nsembe ya dipo ya Mwana Wake. (Aroma 14:12) N’zosakayikitsa kuti chimodzi mwa zifukwa zimene zinachititsa Mulungu kuchitira chifundo Davide patchimo lake ndi Bateseba chinali choti Davideyo anali munthu wachifundo. (1 Samueli 24:4-7) Koma, munthu ‘wosachitira [ena] chifundo adzaweruzidwa mopanda chifundo.’ (Yakobe 2:13a) N’zosadabwitsa kuti anthu “opanda chifundo” ali m’gulu la anthu amene Mulungu amaona kuti “n’ngoyenera imfa.”​—Aroma 1:31, 32.

20 Pa ulaliki wa paphiri, Yesu anati: “Osangalala ali iwo amene ali achifundo, popeza adzachitiridwa chifundo.” (Mateyo 5:7) Mawu amenewa akusonyezeratu kuti anthu amene amafuna kuti Mulungu awachitire chifundo ayenera kukhala achifundo. Nkhani yotsatirayi ifotokoza mmene tingakhalire achifundo.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi chifundo n’chiyani?

• Kodi chifundo chimasonyezedwa motani?

• Kodi Yehova ndi Mulungu wachifundo ndiponso wachilungamo m’njira yotani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achifundo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ovutika n’zofanana ndi mmene mayi amachitira ndi mwana wake

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi zozizwitsa za Yesu zimatiphunzitsa chiyani pankhani ya chifundo?

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi Yehova anaphwanya mfundo zake za chilungamo pamene anachitira chifundo Davide?

[Chithunzi patsamba 25]

Chifundo cha Mulungu kwa anthu ochimwa n’chogwirizana ndi chilungamo chake