Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Ngati mwana wabadwa wakufa, kodi pali chiyembekezo chakuti mwanayo adzauka?

Kwa anthu amene sanaberekepo mwana wakufa kapena kupita padera, kungakhale kovuta kudziwa chisoni chimene anthu ogweredwa tsokali amakhala nacho. Makolo ena amakhala ndi chisoni kwambiri tsoka limeneli likawachitikira. Mayi wina zinamuchitikira zimenezi maulendo asanu. Koma kenako anakhala ndi ana aamuna awiri athanzi, ndipo anaona kuti limeneli linali dalitso. Komabe, iye sanaiwale za mwana aliyense amene anamwalira. Pa nthawi yonse ya moyo wake, mayiyu ankadziwa zaka zimene ana ake amene anabadwa akufa ndi amene anapititsa padera akanakhala nazo ngati anali ndi moyo. Kodi Akhristu ngati amenewa ali ndi chifukwa choyembekezera kuti ana amene anamwalirawo adzaukitsidwa?

Yankho losavuta la funso limeneli ndi lakuti sitikudziwa. Baibulo silinena za nkhani ya kuuka kwa ana amene anabadwa akufa kapena amene anapititsidwa padera. Ngakhale zili choncho, Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zothandiza pa funso limeneli, zimene zingakhale zotonthoza.

Tiyeni tikambirane mafunso awiri okhudza nkhaniyi. Loyamba, kodi Yehova amaona kuti moyo wa munthu umayamba liti, mayi akatenga pathupi kapena mwana akabadwa? Lachiwiri, kodi Yehova amaona bwanji ana osabadwa? Kodi amawaona ngati anthu enieni kapena ngati maselo ndi minofu wamba m’mimba mwa mayi? Mfundo za m’Baibulo zimapereka mayankho omveka a mafunso awiriwa.

Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwinobwino kuti moyo wa munthu suyamba pa nthawi imene akubadwa koma umayambira patali asanabadwe. Kodi chinasonyeza bwanji zimenezi? Chilamulocho chinanena kuti munthu wopha mwana wosabadwa ayenera kuphedwa. Chinati: “Uzipereka moyo kulipa moyo.” * (Eks. 21:22, 23) Choncho, mwana wosabadwa ndi munthu wamoyo. Kumvetsa mfundo yosasintha imeneyi, kwathandiza Akhristu ambirimbiri kupewa kuchotsa mimba podziwa kuti ndi tchimo lalikulu kwa Mulungu.

Kunena zoona, mwana wosabadwa ndi munthu wamoyo. Koma kodi Yehova amaona moyo wa mwana wosabadwayo kukhala wamtengo wapatali? Lamulo talitchula pamwambali linanena kuti munthu wamkulu ayenera kuphedwa akapha mwana wosabadwa. Apa zikuonekeratu kuti Mulungu amaona moyo wa mwana wosabadwa kukhala wamtengo wapatali. Ndiponso m’Malemba muli mavesi ambiri amene amasonyeza kuti Yehova amaona kuti ana osabadwa ndi anthu. Mwachitsanzo, Mfumu Davide anauziridwa kunena za Yehova kuti: “Munandiumba ndisanabadwe ine . . . Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe.”​—Sal. 139:13-16; Yobu 31:14, 15.

Yehova amaonanso kuti ana osabadwa ali ndi makhalidwe awoawo ndiponso amadziwa zimene iwo angathe kudzachita m’tsogolo. Mwachitsanzo, pamene Rebeka mkazi wa Isake anali ndi pathupi pa mapasa, Yehova analosera za ana aamuna awiri amene ankalimbana m’mimba mwake. Izi zikusonyeza kuti iye anaoneratu makhalidwe awo ndi mmene adzakhudzire anthu ambiri m’tsogolo mwawo.​—Gen. 25:22, 23; Aroma 9:10-13.

Chitsanzo chinanso chochititsa chidwi ndi cha Yohane Mbatizi. Nkhani ya mu Uthenga Wabwino wa Luka imati: “Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linalumpha; ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera.” (Luka 1:41) Pofotokoza nkhani imeneyi, Luka yemwe anali dokotala, anagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki amene angatanthauze mwana wosabadwa kapena amene wabadwa. Iye anagwiritsanso ntchito mawu omwewa pofotokoza za Yesu wakhanda atagona modyera ziweto.​—Luka 2:12, 16; 18:15.

Poganizira zonsezi, kodi tingati Baibulo limasiyanitsa mwana amene ali m’mimba ndi mwana amene wabadwa? Sizikuoneka choncho. Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi zimene asayansi amakono apeza. Mwachitsanzo, akatswiriwa apeza kuti mwana amene ali m’mimba amatha kumva ndi kulabadira zimene zikuchitika kunja kuno. Choncho, n’zosadabwitsa kuti mayi woyembekezera ndi mwana wosabadwayo amayamba kukondana kwambiri.

Kubadwa kwa ana kumakhala kosiyanasiyana. Mwachitsanzo, zingachitike kuti mayi wina wabereka mwana wamoyo wosakwana miyezi, koma patapita masiku ochepa mwanayo n’kumwalira. Mayi winanso wakwanitsa miyezi yoti abereke mwana koma mwanayo akumwalira atasala pang’ono kubadwa. Kodi mayi woyambayu angakhale ndi chiyembekezo chakuti mwana wake adzauka chabe chifukwa chakuti mwana wakeyo anabadwa wamoyo ngakhale kuti anali wosakwana miyezi, ndipo mayi wachiwiriyu angakhale alibe chiyembekezo chimenecho chifukwa chakuti anabereka mwana wakufa?

Choncho kunena mwachidule, Baibulo limaphunzitsa kuti moyo umayamba pamene mayi atenga pathupi, ndipo Yehova amaona kuti mwana wosabadwayo ndi munthu ndiponso ndi wamtengo wapatali. Chifukwa cha mfundo za choonadi cha m’Malemba zimenezi, ena angaganize kuti kunena kuti palibe chiyembekezo chakuti ana amene amafa asanabadwe adzauka, n’kutsutsana ndi Malemba. Ndithudi, iwo angaganize kuti kunena zimenezo kumatsutsana ndi chiphunzitso chathu cha m’Malemba choletsa kuchotsa mimba, chimenenso chazikidwa pa mfundo za choonadi zimene tafotokoza pamwambapa.

M’mbuyomo, magazini ino inafunsapo mafunso omveka ndithu amene akusonyeza kuti n’zokayikitsa ngati ana amene anamwalira asanabadwe adzauka. Mwachitsanzo, kodi m’Paradaiso Mulungu adzabwezeretsa mluza m’mimba mwa mayi amene anapita padera? Koma chifukwa cha kuwerenga, kusinkhasinkha ndi kupemphera kwambiri, Bungwe Lolamulira laona kuti mafunso ngati amenewa si oyenera pa nkhani yonena za chiyembekezo cha kuuka kwa akufa. Yesu anati: “Zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.” (Maliko 10:27) Zimene zinamuchitikira Yesu, zimasonyeza kuti mawu amenewa ndi oona. Moyo wake unasamutsidwa kuchoka kumwamba n’kuikidwa m’mimba mwa namwali. Kwa ife anthu zimenezi ndi zosatheka ngakhale pang’ono.

Kodi ndiye kuti zonsezi zikutanthauza kuti Baibulo limaphunzitsa kuti ana amene anamwalira asanabadwe adzaukitsidwa? Kunena motsindika, Baibulo siliyankha funso limeneli, choncho palibe chifukwa chakuti tizilimbikira kunena kuti anawo adzauka. Nkhani imeneyi ingayambitse mafunso ambirimbiri osatha. Choncho ndi bwino kupewa kunena zinthu zongoganizira. Zimene tikudziwa ndi izi: Nkhani imeneyi ili m’manja mwa Yehova Mulungu, amene ndi wokoma mtima ndiponso wachifundo chochuluka. (Sal. 86:15) Mosakayikira, ndi kufuna kwake kuthetsa imfa mwa kuukitsa akufa. (Yobu 14:14, 15) Tili ndi chikhulupiriro chonse chakuti iye nthawi zonse amachita zinthu zolungama. Iye adzathetsa zopweteka zonse zimene timakumana nazo m’dongosolo lino loipa la zinthu, pamene mwachikondi adzalamula Mwana wake “kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”​—1 Yoh. 3:8.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mabaibulo ena amamasulira lembali mosonyeza kuti munthu angalandire chilango cha imfa chifukwa cha imfa ya mayi yokha. Komabe, m’Chiheberi choyambirira lembali limasonyeza kuti lamuloli linkanena za imfa ya mayi kapena ya mwana wake wosabadwa.

[Chithunzi patsamba 13]

Yehova adzathetsa zopweteka zonse