Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amamva Kulira kwa Anthu Amtima Wachisoni

Yehova Amamva Kulira kwa Anthu Amtima Wachisoni

Yehova Amamva Kulira kwa Anthu Amtima Wachisoni

MAWU amene mfumu yanzeru Solomo, ya Isiraeli inanena ndi oona. Mfumuyi inati: “Tsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera [tonsefe].” (Mlal. 9:11) Tsoka kapena mayesero ovuta akhoza kusokoneza kwambiri moyo wathu. Mwachitsanzo, imfa yadzidzidzi ya wachibale wathu ikhoza kutisokoneza kwambiri maganizo. M’milungu ndi miyezi yotsatira, tikhoza kuvutika kwambiri ndi chisoni komanso kumva ngati kuti sitingapirire. Maganizo a munthu akhoza kusokonezeka kwabasi moti angadzione kuti si woyeneranso kupemphera kwa Yehova.

Izi zikachitika munthu amafunika kulimbikitsidwa, kuganiziridwa ndiponso kusonyezedwa chikondi. Mawu amene wamasalimo Davide anaimba ndi okhazika mtima pansi. Iye anati: “Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.” (Sal. 145:14) Baibulo limatiuza kuti: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Iye ‘amakhala ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzichepetsa, kuti atsitsimutse mtima wa anthu onyozeka ndiponso kuti atsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.’ (Yes. 57:15) Kodi Yehova amathandiza ndiponso kulimbikitsa bwanji munthu wopsinjika ndi wachisoni?

“Mawu Onenedwa pa Nthawi Yoyenera”

Njira imodzi imene Yehova amaperekera thandizo pa nthawi yoyenera ndi kudzera mwa Akhristu anzathu. Akhristu amalimbikitsidwa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wachisoni.’ (1 Ates. 5:14) Mawu okoma mtima ndiponso achikondi, amene Akhristu anzathu amalankhula amathandiza kuti maganizo a munthu amene ali pa chisoni akhale m’malo. Mawu olimbikitsa amene munthu anganene pokambirana ngakhale mwachidule ndi munthu amene wawerama chifukwa cha masautso amatsitsimula kwambiri. Nthawi zina, amene anganene mawu oterewa amakhala munthu amene anakumanapo ndi vuto lofanana ndi lathulo. Apo ayi, munthu wina wozindikira ndiponso amene akudziwa zambiri akhoza kulankhula mawu amenewa. Yehova akhoza kutsitsimula munthu amene ali pa chisoni pogwiritsa ntchito njira zimenezi.

Taganizirani za Mkhristu wina dzina lake Alex yemwe ndi mkulu. Mkazi wake anali ndi matenda osachiritsika ndipo anamwalira mwadzidzidzi atangokhala m’banja nthawi yochepa. Woyang’anira dera wina wokoma mtima anakonza zocheza ndi Alex pofuna kumulimbikitsa. Mkazi wa woyang’anira derayu anali atamwalira ndipo pa nthawiyi iye anali atakwatira mkazi wina. Woyang’anira derayu anafotokoza mmene anavutikira maganizo zimenezi zitamuchitikira. Iye ankasangalala akakhala ndi abale mu utumiki ndiponso pa misonkhano ya mpingo. Koma akalowa m’nyumba n’kutseka chitseko, ankasungulumwa kwambiri. Alex anati: “Ndinalimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti vuto limene ndinali nalo silinali lachilendo ndipo enanso akhala akumva choncho.” N’zoona kuti “mawu onenedwa pa nthawi yoyenera” amalimbikitsa kwambiri pa nthawi yachisoni.​—Miy. 15:23.

Mkulu wina wachikhristu amene ankadziwana ndi athu ambiri amene amuna kapena akazi awo anamwalira analimbikitsanso Alex. Mokoma mtima ndiponso mwachikondi, iye anamuuza kuti Yehova amadziwa mmene tikumvera mu mtima mwathu ndiponso zimene zingatithandize. M’baleyu anati: “Ngati miyezi kapena zaka zikubwerazi ungafune kukwatiranso ukhoza kutero chifukwa Yehova amavomereza dongosolo limeneli.” Koma n’zoona kuti amasiye ena amene pakapita nthawi amafuna kukwatira kapena kukwatiwanso sangatero pa zifukwa zina. Ataganiziranso mawu a m’baleyu, Alex anati, “Kukumbutsidwa kuti Yehova amavomereza zimenezi kumalimbikitsa kwambiri chifukwa munthu sudziimba mlandu kwambiri poganiza kuti ngati ungakwatirenso ukhala wosakhulupirika kwa mnzakoyo kapena ku dongosolo la Yehova la ukwati.”​—1 Akor. 7:8, 9, 39.

Wamasalimo Davide amene anakumana ndi mayesero ndiponso mavuto ambirimbiri anati: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.” (Sal. 34:15) N’zosakayikitsa kuti Yehova amamva kulira kwa anthu achisoni ndipo pa nthawi yoyenera amawathandiza kudzera m’mawu anzeru ndiponso abwino amene Akhristu ena achifundo komanso okhwima mwauzimu anganene. Thandizo limeneli ndi lamtengo wapatali ndiponso labwino kwambiri.

Timalimbikitsidwa pa Misonkhano Yachikhristu

N’zosavuta kuti munthu amene ali pa chisoni aziganiza zinthu zolakwika ndipo izi zimam’chititsa kuti asamakonde kukhala ndi anthu ena. Koma lemba la Miyambo 18:1 limachenjeza kuti: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amachita zosemphana ndi nzeru zonse zopindulitsa.” Alex anavomereza mfundoyi kuti: “Mwamuna kapena mkazi wako akamwalira ukhoza kumaganiza zinthu zambiri zolakwika.” Nthawi zina iye ankadzifunsa kuti: “‘Kodi mwina pali zina zimene ndikanachita? Kodi mwina ndikanasonyeza kumuganizira ndiponso kumumvetsa kwambiri mwanjira ina yake?’ Sindinkafuna kukhala ndekha. Sindinkafuna kukhala wosakwatira. N’zovuta kwambiri kuchotsa maganizo amenewa chifukwa tsiku lililonse munthu umakumbukira kuti ulibe mnzako.”

Nthawi imene munthu uli pa chisoni ndi pamene umafunika kwambiri anthu abwino ocheza nawo. Nthawi zonse anthu ocheza nawo amapezeka pa misonkhano yampingo. Pa misonkhano imeneyi timaphunzira mawu a Mulungu omwe ndi olimbikitsa ndiponso otonthoza.

Misonkhano yachikhristu imatithandiza kuona zinthu zimene tikukumana nazo m’njira yoyenera. Tikamamvetsera ndiponso kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo, maganizo athu amakhala pa zinthu zofunika kwambiri zomwe ndi kutsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuyeretsedwa kwa dzina lake osati mavuto athu okha. Pa nthawi imeneyi, timalandira malangizo auzimu ndipo timalimbikitsidwa kudziwa kuti ngakhale kuti ena sangadziwe mavuto amene tikukumana nawo ndiponso mmene tikumvera mumtima mwathu, Yehova amadziwa zonsezi. Iye amadziwa kuti “chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.” (Miy. 15:13) Mulungu woona amafuna kutithandiza ndipo zimenezi zimatilimbikitsa ndi kutithandiza kuti tipeze mphamvu zoti tipirire.​—Sal. 27:14.

Mfumu Davide atapanikizika ndi adani, anapemphera kwa Mulungu kuti: “Mtima wanga walefuka, ndipo wachita dzanzi.” (Sal. 143:4) Mavuto amachititsa munthu kulefuka ndiponso kusokonezeka maganizo moti zingakhale ngati mtima wake wachita dzanzi. Mwina tingamazunzike chifukwa cha matenda kapena vuto lina losatherapo. Tisakayike zoti Yehova adzatithandiza kupirira. (Sal. 41:1-3) Masiku ano Mulungu sachiritsa anthu mozizwitsa koma amapereka nzeru ndi mphamvu kuti munthu apirire vutolo. Kumbukirani kuti Davide atapanikizika ndi mayesero anayang’ana kwa Yehova. Iye anaimba kuti: “Ndakumbukira masiku akale. Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse, ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.”​—Sal. 143:5.

Kulembedwa kwa mawu amenewa m’Baibulo ndi umboni wakuti Yehova amadziwa mmene tikumvera mumtima mwathu. Mawu amenewa amasonyeza kuti iye amamva mapembedzero athu. Tikalola kuti Yehova atithandize ‘iye adzatichirikiza.’​—Sal. 55:22.

“Muzipemphera Mosalekeza”

Lemba la Yakobe 4:8 limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” Pemphero ndi njira imodzi imene tingayandikirire kwa Mulungu. Mtumwi Paulo anatilangiza kuti ‘tizipemphera mosalekeza.’ (1 Ates. 5:17) Ngakhale pamene tikuvutika kufotokoza maganizo athu m’pemphero, “mzimu umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza.” (Aroma 8:26, 27) Yehova amamvetsa bwino mmene tikumvera mumtima mwathu.

Mlongo wina dzina lake Monika, ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Iye anati: “Panopa ndikuona kuti Yehova ndi bwenzi langa lapamtima. Zimenezi zatheka chifukwa cha pemphero, kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo pandekha. Panopa ndikum’dziwa bwino kwambiri Yehova moti nthawi zonse ndimaona kuti akundithandiza. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti ngakhale pamene ndikulephera kufotokoza bwino mmene ndikumvera, iye amandimvetsa. Ndikudziwa kuti kukoma mtima kwake ndi madalitso ake ndi osatha.”

Choncho, tiyeni tizilandira mawu achikondi ndi otonthoza amene abale athu amatiuza. Tizitsatiranso malangizo okoma mtima ndiponso olimbitsa chikhulupiriro amene timalandira pa misonkhano yachikhristu. Tizipempheranso kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima. Zonsezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa posonyeza kuti amatidera nkhawa. Chifukwa cha zimene zinamuchitikira, Alex anati, “Tikamayesetsa kugwiritsa ntchito zinthu zimene Yehova Mulungu watipatsa potithandiza kuti tikhale olimba mwauzimu, tidzapeza ‘mphamvu yoposa yachibadwa’ imene ingatithandize kupirira mayesero alionse amene tingakumane nawo.”​—2 Akor. 4:7.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 18]

Kulimbikitsa Anthu Achisoni

M’buku la Masalimo muli mawu ambiri ofotokoza mmene anthu amamvera mumtima komanso otsimikizira kuti Yehova amamva kulira kwa anthu achisoni amene asokonezeka maganizo. Taonani mawu otsatirawa:

Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova, ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake. Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.”​—Sal. 18:6.

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—Sal. 34:18.

“Iye [Yehova] amachiritsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.”​—Sal. 147:3.

[Chithunzi patsamba 17]

“Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera” amalimbikitsa kwambiri munthu akakhala pa chisoni