Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera
Yehu Anamenyera Nkhondo Kulambira Koyera
YEHU anagwira ntchito yaikulu popititsa patsogolo kulambira koyera. Iye anagwira ntchito imeneyi mwakhama, mosabwerera m’mbuyo komanso molimba mtima. Yehu anaonetsa makhalidwe amene tingachite bwino kutengera.
Yehu anadzozedwa kukhala mfumu ya Isiraeli pamene dzikolo linali loipa kwambiri chifukwa cha munthu woipa Yezebeli. Pa nthawiyi, Ahabu, mwamuna wake, anali ataphedwa ndipo amene ankalamulira anali mwana wake dzina lake Yehoramu. Yezebeli ankalimbikitsa kulambira Baala m’malo molambira Yehova. Anapha aneneri a Mulungu ndiponso anasocheretsa anthu chifukwa cha “dama” lake ndi ‘zamatsenga.’ (2 Maf. 9:22; 1 Maf. 18:4, 13) Yehova analamula kuti anthu onse a m’nyumba ya Ahabu aphedwe, kuphatikizapo Yehoramu ndi Yezebeli. Mulungu anasankha Yehu kuti atsogolere ntchito imeneyi.
Malemba amatchula Yehu koyamba pamene ankakambirana ndi akuluakulu a asilikali. Pa nthawiyo n’kuti Aisiraeli akumenyana ndi Asuri ku Ramoti-giliyadi. Yehu anali ndi udindo waukulu pakati pa asilikali. N’kutheka kuti anali mtsogoleri wa asilikali a Isiraeli. Mneneri Elisa anatumiza mmodzi mwa ana a aneneri kuti akadzoze Yehu kuti akhale mfumu komanso kukamuuza kuti aphe ana onse aamuna a anthu opanduka a m’nyumba ya Ahabu.—2 Maf. 8:28; 9:1-10.
Anzake a Yehu atamufunsa za cholinga cha ulendowo, Yehu sanawauze. Koma atamukakamiza, iye anawauza zoona ndipo Yehu ndi anzakewo anayamba kumukonzera Yehoramu chiwembu. (2 Maf. 9:11-14) Zikuoneka kuti anthu ambiri sankasangalala ndi ulamuliro wa nyumba ya Ahabu ndiponso zochita za Yezebeli. Choncho Yehu anakonza mapulani abwino oti akaphere anthu opandukawo.
Mfumu Yehoramu inali itavulala ku nkhondo ndipo inali itabwerera ku Yezereeli kuti ikachire mabala ake. Yehu ankadziwa kuti, ngati akufuna kuti akwanitse kuchita zomwe anakonzazo, m’pofunika kuti anthu a ku Yezereeli asamve chilichonse za nkhaniyi. Iye anati: “Musalole aliyense kuthawa kutuluka mumzinda uno kuti akanene ku Yezereeli.” (2 Maf. 9:14, 15) Mwina Yehu ankadziwa kuti anthu ena amene anali ku mbali ya Yehoramu angadane nazo choncho sanafune kuti alimbane ndi anthu ngati amenewa.
KUYENDETSA GALETA PA LIWIRO LOOPSA
Pofuna kungodzidzimutsa Yehoramu, Yehu ananyamuka pa galeta kuchoka ku Ramoti-giliyadi kupita ku Yezereeli, ulendo wa makilomita 72. Atatsala pang’ono kufika, mlonda amene anaimirira pansanja anaona “gulu lankhondo la Yehu likubwera mwaliwiro.” (2 Maf. 9:17) N’kutheka kuti Yehu anapita ndi gulu lalikulu la nkhondo n’cholinga choti zimene anakonza zitheke basi.
Atazindikira kuti Yehu yemwe anali wolimba mtima ali m’galeta, mlonda wa pansanja uja ananena kuti: ‘Iye akuthamangitsa galeta ngati wamisala.’ (2 Maf. 9:20) Mwina Yehu ankayendetsa mothamangitsa nthawi zonse, koma ulendo uno ziyenera kuti zinafika poipa kwambiri.
Yehu anakana kuyankha chilichonse kwa anthu awiri amene Yehoramu anawatuma. Kenako Mfumu Yehoramu inanyamuka limodzi ndi mfumu ya Yuda, Ahaziya. Aliyense ananyamuka pa galeta lake kukakumana ndi Yehu. Mfumu Yehoramu inamufunsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Ndipo Yehu anamuyankha kuti: “Mtendere ungakhalepo bwanji pali dama la Yezebeli mayi ako ndi amatsenga ake ambirimbiri?” Yehoramu anachita mantha ndi yankho limeneli ndipo anayamba kuthawa. Koma mwamsangamsanga Yehu anakoka uta n’kubaya Yehoramu kumsana moti muviwo unatulukira pamtima pake. Yehoramu anagwera m’galeta lake n’kufera pompo. Ahaziya anathawa koma Yehu anamutsatira mpaka kumupeza n’kulamula kuti aphedwe.—2 Maf. 9:22-24, 27.
Munthu wina wa m’nyumba ya Ahabu amene anafunika kuphedwa anali Mfumukazi Yezebeli yomwe inali yoipa kwambiri. Yehu ananena kuti iye anali ‘munthu wotembereredwa.’ Yehu atafika ku Yezereeli anaona Yezebeli ataima pawindo la nyumba yachifumu n’kumayang’ana kunja. Nthawi yomweyo Yehu anauza nduna zina kuti zimuponye pansi kudzera pawindo. Zitamuponya, Yehu anam’pondaponda ndi mahatchi ake munthu amene anaipitsa Isiraeliyu. Kenako Yehu anapitiriza kuwononga anthu ena a m’banja la Ahabu.—2 Maf. 9:30-34; 10:1-14.
Ngakhale kuti kupha anthu si kosangalatsa, tiyenera kukumbukira kuti pa nthawiyo, Yehova ankagwiritsa ntchito atumiki ake kuti apereke chiweruzo chake. Malemba amati: “Mulungu ndi amene anachititsa kuti Ahaziya awonongeke mwa kupita kwa Yehoramu. Atafika kumeneko, anatengana ndi Yehoramu n’kupita kukakumana ndi Yehu mdzukulu wa Nimusi, yemwe Yehova anam’dzoza kuti aphe a m’nyumba ya Ahabu.” (2 Mbiri 22:7) Pamene ankaponya mtembo wa Yehoramu m’munda wa Naboti, Yehu anazindikira kuti zochita zake zikukwaniritsa zimene Mulungu analonjeza. Mulungu analonjeza kuti adzabwezera chiwembu chimene Ahabu anachitira Naboti. Ndipotu Yehu analamulidwa kuti ‘abwezere magazi a atumiki a Mulungu’ amene anaphedwa ndi Yezebeli.—2 Maf. 9:7, 25, 26; 1 Maf. 21:17-19.
Masiku ano, atumiki a Yehova samenyana ndi anthu amene amadana ndi kulambira koyera. Mulungu ananena kuti: “Kubwezera ndi kwanga.” (Aheb. 10:30) Koma pofuna kuti anthu ena asaipitse mpingo, Akulu achikhristu angafunike kuchita zinthu molimba mtima ngati Yehu. (1 Akor. 5:9-13) Ndipo ngati munthu wina wachotsedwa, anthu onse mu mpingo ayenera kupeweratu kucheza naye.—2 Yoh. 9-11.
YEHU SANALEKERERE ANTHU OPIKISANA NDI YEHOVA
Mawu amene Yehu anauza munthu wokhulupirika Yehonadabu angatithandize kuzindikira cholinga chake pogwira ntchito imene anapatsidwa. Iye anati: “Tiye tipitire limodzi ukaone kuti sindilekerera zoti anthu azipikisana ndi Yehova.” Yehonadabu anavomera ndipo anakwera m’galeta la Yehu n’kupita naye limodzi ku Samariya. Atafika kumeneko, Yehu “anawapusitsa n’cholinga choti awononge anthu olambira Baala.”—2 Maf. 10:15-17, 19.
Yehu anauza anthu kuti akufuna kupereka “nsembe yaikulu” kwa Baala. (2 Maf. 10:18, 19) Katswiri wina wa zamaphunziro ananena kuti: “Apa Yehu anagwiritsa ntchito mawu mochenjera kwambiri.” Mawu akuti “nsembe” amene anawagwiritsa ntchito pa lembali angagwiritsidwenso ntchito kutanthauza ‘kupha’ moti pogwiritsa ntchito mawu amenewa iye ankatanthauza kuti apha anthu ampatuko. Popeza Yehu ankafuna kuti munthu aliyense wolambira Baala apezekepo, iye anawasonkhanitsa m’nyumba ya Baala n’kuwauza kuti avale zovala zawo zapadera. ‘Yehu atangomaliza kupereka nsembe yopsereza,’ anauza asilikali ake okwana 80 onyamula malupanga kuti aphe anthu onse olambira Baala. Kenako anagumula nyumba ya Baala ndipo malowo anawasandutsa zimbudzi kuti asakhalenso malo olambirirapo.—2 Maf. 10:20-27.
N’zoona kuti Yehu anapha anthu ambiri. Koma Malemba amanena kuti iye anali munthu wolimba mtima amene anamasula Aisiraeli mu ulamuliro wopondereza wa Yezebeli ndi banja lake. Kuti wolamulira wa Isiraeli akwanitse kuchita zimenezi, anayenera kukhala munthu wolimba mtima, wakhama ndiponso wosabwerera m’mbuyo. Buku lina lofotokoza Baibulo limati iye anagwira ntchito ‘yovuta ndipo sanalekerere aliyense. Mwina akanachita zinthu mwachifatse sakanakwanitsa kuthetsa kulambira Baala mu Isiraeli.’
Apa tsopano mutha kuona kuti zinthu zina zimene Akhristu amakumana nazo masiku ano zimafuna kuti iwo asonyeze makhalidwe amene Yehu anali nawo. Mwachitsanzo, kodi tiyenera kutani ngati tikuyesedwa kuti tichite zinthu zimene Yehova amadana nazo? Tiyenera kukana mwamsanga, molimba mtima ndiponso mosanyengerera. Sitiyenera kulekerera zinthu pa nkhani zokhudza kudzipereka kwathu kwa Yehova.
YESETSANI KUYENDA MOTSATIRA MALAMULO A YEHOVA
Zimene zili kumapeto kwa nkhaniyi ndi chenjezo kwa ife. Baibulo limasonyeza kuti Yehu anayamba kulambira mafano. Limanena kuti: ‘Sanasiye kutsatira ana a ng’ombe agolide amene anali ku Beteli ndi ku Dani.’ (2 Maf. 10:29) Kodi zinatheka bwanji kuti munthu amene ankakonda kulambira koyera ayambe kulambira mafano?
N’kutheka kuti Yehu ankaganiza kuti popeza ufumu wa Isiraeli unali utagawikana ndi wa Yuda, ndiye kuti pafunika kuti asiyanenso pa nkhani ya kulambira. Ndiyeno mofanana ndi mafumu ena a Isiraeli, iye analimbikitsa kulambira ana a ng’ombe pofuna kuti akhalebe osiyana ndi ufumu wa Yuda. Apatu anasonyeza kuti sankakhulupirira kwambiri Yehova, amene anamudzoza kuti akhale mfumu.
Yehova anayamikira Yehu chifukwa chakuti ‘anachita zoyenera pamaso pake.’ Komabe, Yehu “sanayesetse kuyenda motsatira malamulo a Yehova Mulungu wa Isiraeli ndi mtima wake wonse.” (2 Maf. 10:30, 31) Mukaganizira zimene anadzachita pamapeto ake poyerekezera ndi zonse zimene Yehu anachita kumbuyoku, mukhoza kudabwa ndiponso kumva chisoni. Koma zimene iye anachitazi zikutipatsa phunziro. Ubwenzi wathu ndi Yehova sitiyenera kuuona mwachibwanabwana. Tsiku lililonse tiyenera kuyesetsa kukhala okhulupirika kwa Mulungu. Kuphunzira Baibulo, kusinkhasinkha zimene taphunzira ndiponso kupemphera ndi mtima wonse kwa Atate wathu wakumwamba kungatithandize kuchita zimenezi. Choncho tiyeni tiyesetse kwambiri kutsatira malamulo a Yehova ndi mtima wathu wonse.—1 Akor. 10:12.
[Bokosi patsamba 4]
Zimene Anthu Ena Akale Analemba Zokhudza Yehu
Anthu ena amakayikira zoti anthu amene amatchulidwa m’Malemba anali anthu enieni. Ndiyeno kodi pali umboni wosonyeza kuti Yehu anali munthu weniweni?
Pali zolembedwa zitatu zonena za ufumu wa Asuri zimene zimatchula dzina la mfumu ya Isiraeli imeneyi. Chimodzi mwa zinthu zimenezi ndi chipilala chojambulidwa munthu amene akuti ndi Yehu kapena munthu wina woimira mfumu. Munthuyo akugwadira mfumu ya Asuri, Salimanesere Wachitatu, komanso akupereka msonkho. Pachipilalachi pali mawu oti: “Msonkho wa Yehu (Ia-ú-a), mwana wa Omuri (Hu-um-ri). Ndinalandira kuchokera kwa Yehu siliva, golide, mbale yagolide yotchedwa sapulu, mtsuko wagolide wosongoka kunsi kwake, matambula agolide, mabaketi agolide, zitsulo za tini, ndodo ya mfumu ndi chinthu china chathabwa.” Yehu sanali mwana weniweni wa Omuri koma mawuwa akusonyeza kuti anali mu mzera wa mafumu a Isiraeli. N’kutheka kuti Omuri anatchuka chifukwa choti anamanga likulu la Isiraeli lomwe ndi Samariya.
Palibe umboni wotsimikizira kuti Yehu anaperekadi msonkho umenewu kwa mfumu ya Asuri. Ngakhale zili choncho, mfumu ya Asuriyi inatchula Yehu katatu. Koyamba pachipilala, kachiwiri chiboliboli cha Salimanesere ndiponso mu mbiri ya mafumu a Asuri. Zonsezi zikusonyeza kunalidi munthu wotchedwa Yehu.