Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ine Ndili Pamodzi ndi Inu”

“Ine Ndili Pamodzi ndi Inu”

“Ine Ndili Pamodzi ndi Inu”

“Anthu ambiri adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”—DAN. 12:4.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi anthu adziwa bwanji ‘zinthu zoona’ masiku ano?

Kodi zatheka bwanji kuti anthu odziwa choonadi akhale “ambiri”?

N’chiyani chathandiza kuti anthu padziko lonse adziwe “zinthu zambiri zoona”?

1, 2. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu akuthandiza otsatira ake masiku ano ndiponso adzawathandiza m’tsogolo? (b) Kodi ulosi wa Danieli 12:4 unanena kuti chidzachitika n’chiyani anthu akamaphunzira Malemba mosamala?

TAYEREKEZANI kuti muli m’Paradaiso. Tsiku lililonse, mukudzuka ndi mphamvu. Simukumva kupweteka paliponse. Matenda kapena mavuto alionse amene munali nawo m’thupi atha. Mukutha kuona bwinobwino, kumva zinthu bwinobwino, kumva kununkhira kwa zinthu ndiponso kukoma kwa chakudya. Mukuona kuti muli ndi mphamvu zambiri, mukugwira ntchito zosangalatsa, muli ndi anzanu ambirimbiri ndiponso nkhawa zanu zonse zatha. Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso amenewa. Khristu Yesu, amene ndi Mfumu yoikidwa ndi Mulungu, adzadalitsa anthu ndiponso kuwaphunzitsa za Yehova.

2 Yehova adzathandiza atumiki ake okhulupirika pamene akugwira ntchito yophunzitsa imeneyi. Mulungu ndi Mwana wake akhala akuthandiza anthu okhulupirika kuyambira kalekale. Yesu asanapite kumwamba, anatsimikizira ophunzira ake okhulupirika kuti adzakhala nawo. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Tsopano tiyeni tikambirane ulosi wina wochokera kwa Mulungu umene ungatithandize kukhulupirira kwambiri lonjezo limeneli. Ulosiwu unalembedwa ndi mneneri Danieli ku Babulo zaka zoposa 2,500 zapitazo. Iye analemba zokhudza “nthawi yamapeto” ino. Anati: “Anthu ambiri adzayenda uku ndi uku ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.” (Dan. 12:4) Panopa timadziwa kuti mawu achiheberi amene anawamasulira kuti ‘kuyenda uku ndi uku’ ndi ophiphiritsa ndipo amatanthauza kuphunzira chinthu mosamala. Ulosiwu unasonyeza kuti anthu amene adzaphunzire Malemba mosamala adzadalitsidwa kwambiri. Iwo adzadziwa mfundo zoona za m’Mawu a Mulungu. Unanenanso kuti ndi anthu ambiri amene adzadziwe ‘zinthu zoona’ ndipo zinthuzo zidzakhala zambiri. Zinthu zoonazo zizidzafalitsidwa kulikonse ndiponso zizidzapezeka mosavuta. Tikamakambirana za kukwaniritsidwa kwa ulosiwu, tiona kuti Yesu akuthandiza ophunzira ake masiku ano. Tionanso kuti Yehova amakwaniritsa zonse zimene walonjeza.

‘ZINTHU ZOONA’ ZINADZIWIKA

3. N’chiyani chinachitikira ‘zinthu zoona’ atumwi atamwalira?

3 Atumwi atamwalira, mpatuko unayambika pakati pa Akhristu oona ndipo unafalikira kwambiri. Zimenezi zinali zitanenedweratu. (Mac. 20:28-30; 2 Ates. 2:1-3) Kwa zaka zambirimbiri izi zitachitika, anthu osadziwa Baibulo komanso anthu amene ankati ndi Akhristu sankadziwa ‘zinthu zoona.’ Ngakhale kuti atsogoleri a matchalitchi achikhristu ankanena kuti amakhulupirira Malemba, ankaphunzitsa zinthu zabodza. Iwo ankaphunzitsa “ziphunzitso za ziwanda” zonyoza Mulungu. (1 Tim. 4:1) Anthu wamba sankaphunzitsidwa Mawu a Mulungu. Ampatuko ankaphunzitsa zinthu zabodza ngati zoti Mulungu ndi Utatu, mzimu sufa ndiponso kuti anthu ena amakazunzika kumoto kwamuyaya.

4. Kodi gulu la Akhristu linayamba bwanji kufufuza ‘zinthu zoona’ m’zaka za m’ma 1870?

4 Koma m’zaka za m’ma 1870, gulu la Akhristu ochepa ku Pennsylvania m’dziko la United States linayamba kusonkhana. Iwo ankaphunzira limodzi Baibulo n’kumafufuza ‘zinthu zoona.’ Pa nthawiyi, kunali kutatsala zaka pafupifupi 40 kuti “masiku otsiriza” ayambe. (2 Tim. 3:1) Iwo ankadzitcha Ophunzira Baibulo. Sanali “anthu anzeru ndi ozindikira” omwe Yesu ananena kuti abisiridwa zinthu. (Mat. 11:25) Koma anali anthu odzichepetsa amene ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu. Iwo ankapemphera, kuwerenga Baibulo, kukambirana ndiponso kusinkhasinkha zimene awerengazo. Ankachita zimenezi mosamala kwambiri. Iwo ankayerekezera malemba osiyanasiyana ndiponso kuona zimene anthu ena alemba pambuyo pofufuza malembawo. Pang’ono ndi pang’ono, Ophunzira Baibulowo anayamba kuzindikira choonadi chimene chinabisika kwa zaka zambiri.

5. Kodi cholinga cha timapepala ta mutu wakuti Ziphunzitso Zakale za Mulungu chinali chiyani?

5 Ophunzira Baibulowo ankasangalala kwambiri kudziwa ‘zinthu zoona.’ Koma sanalole kuti izi ziwachititse kudzitukumula ndipo sankadzitamanda kuti apeza zinthu zatsopano. (1 Akor. 8:1) M’malomwake anatulutsa timapepala ta mutu wakuti, Ziphunzitso Zakale za Mulungu (mu Chingelezi). Cholinga chake chinali kuthandiza anthu kudziwa choonadi chimene chinalembedwa kale m’Baibulo. Kapepala koyamba kanali ndi “mfundo zothandiza kuphunzira Baibulo. Kanali koti kathandize anthu kusiya zikhulupiriro zonama za anthu n’kuyambanso kukhulupirira ziphunzitso zakale za Ambuye wathu [Yesu] ndiponso atumwi.”—Ziphunzitso Zakale za Mulungu, Na. 1, April 1889, tsamba 32.

6, 7. (a) Kodi tathandizidwa kudziwa mfundo ziti za choonadi kuyambira zaka za m’ma 1870? (b) Kodi inuyo mwasangalala kwambiri kudziwa mfundo ziti?

6 Pali mfundo za choonadi zamtengo wapatali kwambiri zimene zadziwika kuchokera nthawi imeneyo. * Koma sikuti ndi mfundo zovuta zimene akatswiri azipembedzo amakonda kutsutsana. Mfundozi n’zosangalatsa ndipo zimatimasula. Zimatithandiza kukhala ndi moyo wabwino, chimwemwe ndiponso chiyembekezo. Zimatithandizanso kudziwa Yehova, makhalidwe ake ndiponso zolinga zake. Zimafotokoza bwino udindo wa Yesu, chifukwa chake anabwera padziko lapansi n’kufa ndiponso zimene akuchita panopa. Zimafotokozanso chifukwa chake Mulungu amalola zoipa kuchitika, chifukwa chake timafa, mmene tingapempherere ndiponso zimene tingachite kuti tikhale osangalala.

7 Panopa tikudziwa tanthauzo la maulosi amene akukwaniritsidwa m’nthawi yamapeto ino. Maulosi amenewa akhala akusungidwa “mwachinsinsi” kwa zaka zambirimbiri. (Dan. 12:9) Maulosiwa amapezeka m’Baibulo makamaka m’Mauthenga Abwino ndiponso m’buku la Chivumbulutso. Mulungu watithandiza kudziwa chifukwa chake kuli zinthu monga nkhondo, zivomezi, miliri, njala ndiponso anthu osaopa Mulungu amene amachititsa kuti masiku ano akhale ovuta. (2 Tim. 3:1-5; Luka 21:10, 11) Yehova watithandizanso kudziwa ngakhale zinthu zina zosaoneka monga nthawi imene Yesu anayamba kulamulira, nkhondo imene inachitika kumwamba ndiponso kuponyedwa kwa Satana padziko lapansi.—Chiv. 12:7-12.

8. Kodi tiyenera kuyamikira ndani chifukwa cha zinthu zimene tikuona ndiponso kumva?

8 Panopa titha kumvetsa mawu amene Yesu anauza ophunzira ake akuti: “Anthu amene maso awo amaona zimene inu mukuonazi ndi odala. Pakuti ndikukuuzani, Aneneri ndi mafumu ambiri analakalaka kuona zimene mukuzionazi, koma sanazione. Analakalaka kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.” (Luka 10:23, 24) Timayamikira Yehova Mulungu chifukwa chotithandiza kuona ndiponso kumva zinthu zimenezi. Timayamikiranso kuti akugwiritsa ntchito mzimu woyera, womwe ndi “mthandizi,” kutsogolera otsatira a Yesu “m’choonadi chonse.” (Werengani Yohane 16:7, 13.) Tiyeni nthawi zonse tiziona kuti choonadi chimenechi ndi chamtengo wapatali ndipo tisamaumire kuuza anthu ena.

“ANTHU AMBIRI” ANAYAMBA KUDZIWA ZINTHU ZOONA

9. Kodi m’magazini ya April 1881 munali mawu ati?

9 Pasanathe zaka ziwiri kuchokera pamene Nsanja ya Olonda yoyamba inatuluka, magazini ya April 1881 inanena kuti pakufunika anthu 1,000 olalikira. Magaziniyi inati: “Nonse amene mukhoza kudzipereka n’kuwonjezera nthawi yogwira ntchito ya Ambuye . . . , tikukulimbikitsani kuti mukhale akopotala kapena alaliki. Muyesetse mmene mungathere kupita kumizinda yaikulu ndiponso yaing’ono kukafufuza anthu amene akufuna kukhala Akhristu oona. Mudzaona kuti ambiri mwa anthuwo amadzipereka potumikira Mulungu koma samudziwa. Muziyesetsa kuwathandiza kudziwa chifundo cha Atate wathu ndiponso zinthu zamtengo wapatali zopezeka m’Mawu ake.”

10. Kodi anthu anatani atamva kuti pakufunika anthu oti azilalikira nthawi zonse?

10 Mawu amenewa akusonyeza kuti Ophunzira Baibulo anazindikira kuti kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yofunika kwambiri ya Akhristu oona. Pa nthawiyo panali anthu mahandiredi ochepa okha amene ankafika pa misonkhano ya Ophunzira Baibulo. Choncho zikanaoneka ngati n’zosatheka kuti papezeke akopotala, kapena kuti alaliki a nthawi zonse, okwana 1,000. Koma anthu ambiri atangowerenga kapepala kapena magazini, anadziwa kuti apeza choonadi ndipo anayamba ukopotala nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, mu 1882, munthu wina wa ku London ku England anawerenga Nsanja ya Olonda ndiponso kabuku kofalitsidwa ndi Ophunzira Baibulo. Atatero, analemba kuti: “Ndiuzeni mfundo zoti ndilalikire ndiponso mmene ndingalalikirire kuti ndigwire ntchito ya Mulungu yodalitsikayi.”

11, 12. (a) Kodi cholinga cha akopotala komanso cha ifeyo n’chiyani? (b) Kodi akopotala ankayambitsa bwanji makalasi kapena kuti mipingo?

11 Pofika mu 1885, Ophunzira Baibulo okwana pafupifupi 300 anali kuchita ukopotala. Cholinga cha anthu amenewa chinali chofanana ndi cholinga chathu masiku ano. Iwo ankafuna kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu Khristu. Koma njira zimene ankagwiritsa ntchito zinali zosiyana ndi zathu. Masiku ano, timakonda kuphunzira Baibulo ndi munthu mmodzi pa nthawi imodzi kuti timuthandize moyenerera. Kenako timamulimbikitsa kuti azisonkhana nafe mu mpingo. Koma kalelo, akopotala ankagawira mabuku kenako n’kusonkhanitsa anthu kuti aziphunzira limodzi Malemba. M’malo mophunzira ndi munthu mmodzi ankangoyambitsa mipingo, yomwe ankati makalasi.

12 Mwachitsanzo, mu 1907, gulu lina la akopotala linayendayenda mumzinda wina kuti lipeze anthu amene anali ndi mabuku a Ophunzira Baibulo. Nsanja ya Olonda inati: “Anthu amenewa anasonkhanitsidwa pamodzi m’nyumba ina. Mkopotala wina anakambirana nawo Lamlungu lonse nkhani yokhudza cholinga cha Mulungu. Kenako Lamlungu lotsatira anawauza kuti azisonkhana mlungu uliwonse.” Koma zinthu zinasintha mu 1911. Abale 58 anasankhidwa kuti azikamba nkhani za onse m’malo osiyanasiyana ku United States ndi ku Canada. Abalewa ankalemba mayina a anthu ofuna kuphunzira amene anabwera kudzamvetsera nkhanizo ndipo ankawaika m’magulu kuti apange makalasi atsopano. Pofika mu 1914, kunali mipingo ya Ophunzira Baibulo yokwana 1,200 padziko lapansi.

13. N’chiyani chimakuchititsani chidwi mukaganizira mmene anthu akudziwira ‘zinthu zoona’ masiku ano?

13 Masiku ano, pali mipingo pafupifupi 109,400 padziko lonse ndipo abale ndi alongo okwana 895,800 akuchita upainiya. Anthu pafupifupi 8 miliyoni aphunzira ‘zinthu zoona’ ndipo akuzitsatira pa moyo wawo. (Werengani Yesaya 60:22.) * Zimenezi n’zochititsa chidwi kwambiri chifukwa chakuti Yesu ananena kuti “anthu onse adzadana” ndi ophunzira ake chifukwa cha dzina lake. Ananenanso kuti otsatira ake adzazunzidwa, kumangidwa mwinanso kuphedwa kumene. (Luka 21:12-17) Anthu a Yehova amatsutsidwa ndi Satana, ziwanda komanso anthu ena. Ngakhale zili choncho, amagwirabe ntchito yophunzitsa anthu ndipo akuthandiza anthu ambiri kukhala ophunzira a Yesu. Masiku ano, akulalikira “padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” Amafika m’madera otentha kwambiri, ozizira kwambiri, m’mapiri, m’zipululu, m’mizinda ndiponso m’midzi yakutali. (Mat. 24:14) Zimenezi sizikanatheka popanda thandizo la Mulungu.

ANTHU ANAYAMBA KUDZIWA “ZINTHU ZAMBIRI ZOONA”

14. Kodi mabuku ndi magazini athandiza bwanji kuti anthu padziko lonse adziwe “zinthu zambiri zoona”?

14 Akhristu amene akulalikira uthenga wabwino athandiza anthu kudziwa “zinthu zambiri zoona.” Nawonso mabuku ndi magazini athandiza anthu kudziwa zambiri. Mu July 1879, Ophunzira Baibulo anatulutsa Nsanja ya Olonda yoyamba m’Chingelezi. Kampani inayake inapemphedwa kuti isindikize magaziniyi ndipo inasindikiza makope 6,000. Charles Taze Russell, yemwe anali ndi zaka 27, anali mkonzi wake ndipo abale ena asanu odziwa bwino choonadi ankathandizana naye. Panopa Nsanja ya Olonda imafalitsidwa m’zinenero 195. Pa magazini onse padziko lapansi, Nsanja ya Olonda ndi imene imafalitsidwa kwambiri. Pamakhala makope 42,182,000 pa magazini iliyonse. Pa nambala 2 pali Galamukani! imene imafalitsidwa makope 41,042,000 m’zinenero 84. Komanso mabuku ndi mabaibulo pafupifupi 100 miliyoni amasindikizidwa chaka chilichonse.

15. Kodi ndalama zothandiza pa ntchito yathu zimachokera kuti?

15 Ndalama zonse zimene zimathandiza pa ntchito yaikuluyi zimachokera kwa anthu amene amapereka mwaufulu. (Werengani Mateyu 10:8.) Zimenezi zimadabwitsa anthu odziwa ntchito yofalitsa mabuku komanso mtengo wa zinthu ngati makina osindikizira, mapepala ndiponso inki. M’bale wina amene amathandiza kugula zinthu za gulu anati: “Anthu ochokera m’makampani ena amadabwa akaona ntchito yathu yosindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina amakono otha kusindikiza zinthu zambiri pa nthawi yochepa. Zimawavuta kukhulupirira kuti zopereka zaufulu n’zimene zimathandiza kuti ntchitoyi itheke. Amachitanso chidwi kwambiri kuona kuti anthu ogwira ntchito ku Beteli ndi achinyamata osangalala.”

DZIKO LAPANSI LIDZADZAZA NDI ANTHU ODZIWA MULUNGU

16. Kodi cholinga cha Mulungu podziwitsa anthu ‘zinthu zoona’ n’chiyani?

16 N’chifukwa chiyani Mulungu akuthandiza anthu padziko lonse kudziwa “zinthu zambiri zoona”? Cholinga chake n’choti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Tim. 2:3, 4) Yehova amafuna kuti anthu adziwe choonadi, azimulambira moyenera ndiponso alandire madalitso. Chifukwa chodziwitsa anthu ‘zinthu zoona,’ Yehova wasonkhanitsa Akhristu odzozedwa otsalira. Iye akusonkhanitsanso anthu a “khamu lalikulu” amene adzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Iwo akuchokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”—Chiv. 7:9.

17. Kodi kuwonjezeka kwa Akhristu oona ndi umboni wa chiyani?

17 Chiwerengero cha Akhristu oona chakhala chikuwonjezeka padziko lonse lapansi pa zaka 130 zapitazi. Umenewu ndi umboni woti Mulungu ndiponso Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu yosankhidwa ndi Yehova, akhala akuthandiza Akhristuwo. Iwo akhalanso akuwatsogolera, kuwateteza ndiponso kuwaphunzitsa. Ndi umboninso wakuti malonjezo onse a Yehova adzakwaniritsidwa. “Dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.” (Yes. 11:9) Pali madalitso ambiri amene anthu adzakhala nawo nthawi imeneyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mungapindule mutaonera ma DVD akuti Jehovah’s Witnesses—Faith in Action, Part 1: Out of Darkness ndiponso Jehovah’s Witnesses—Faith in Action, Part 2: Let the Light Shine.

^ ndime 13 Onani buku lakuti Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 2, tsamba 320.

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 6]

Ophunzira Baibulo anali odzichepetsa ndipo ankafunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 7]

Yehova amayamikira kwambiri zimene mumachita pothandiza anthu ambiri kudziwa ‘zinthu zoona’