Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Pemphero Limene Linakonzedwa Bwino?
“Atamande dzina lanu laulemerero.”—NEH. 9:5.
1. (a) Kodi tikambirana za msonkhano uti wa anthu a Mulungu? (b) Nanga mungadzifunse mafunso ati?
POLIMBIKITSA anthu a Mulungu kuti asonkhane n’kupemphera limodzi, Alevi ananena kuti: “Dzukani, tamandani Yehova Mulungu wanu kuyambira kalekale mpaka kalekale.” (Neh. 9:4, 5) Pemphero limeneli ndi limodzi mwa mapemphero ataliatali amene analembedwa m’Baibulo. Msonkhanowu unachitikira mu Yerusalemu m’chaka cha 455 B.C.E. Unachitika pa tsiku la 24 la mwezi wa Tishiri, womwe unali wa 7 pa kalendala yachiyuda. Pamene tikukambirana zimene zinachitika pa nthawiyi, mudzifunse kuti: ‘Kodi n’chiyani chinathandiza kuti msonkhanowu uyende bwino? Kodi ndi zinthu zina ziti zimene ndikuphunzira pa pemphero limeneli?’—Sal. 141:2.
MWEZI WAPADERA
2. Kodi Aisiraeli anatipatsa chitsanzo chotani pa msonkhano umene anachita atamaliza kumanganso mpanda wa Yerusalemu?
2 Ayuda anachita msonkhanowu patadutsa mwezi umodzi kuchokera pamene anamaliza kumanga mpanda wa Yerusalemu. (Neh. 6:15) Anthu a Mulungu anamaliza ntchitoyi pa masiku 52 okha ndipo kenako ankafuna kusonkhana kuti aphunzire za Mulungu. Choncho pa tsiku loyamba la mwezi watsopano wa Tishiri anasonkhana m’bwalo lalikulu kuti amvetsere Ezara ndiponso Alevi ena akuwerenga komanso kufotokoza Chilamulo cha Mulungu. Anthu onse m’banja omwe “akanatha kumvetsera ndi kuzindikira zimene zinali kunenedwa” anaimirira n’kumvetsera “kuyambira m’mawa mpaka masana.” Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife masiku ano amene timasonkhana m’Nyumba za Ufumu zabwino. Kodi nthawi zina muli pa misonkhano mumayamba kuganizira zinthu zina zosafunika kwenikweni? Ngati zili choncho, mungachite bwino kuganiziranso chitsanzo cha Aisiraeliwa. Iwo anamvetsera mwatcheru ndipo zimene anamvazo zinawafika pamtima moti anayamba kulira chifukwa choona kuti alephera kutsatira Chilamulo cha Mulungu.—Neh. 8:1-9.
3. Kodi Aisiraeli anamvera malangizo ati?
3 Koma imeneyi sinali nthawi yoti anthuwo aulule machimo awo. Tsikuli linali lachikondwerero, choncho inali nthawi yoti asangalale polambira Yehova. (Num. 29:1) Ndiyeno Nehemiya anauza anthuwo kuti: “Pitani mukadye zinthu zonona, kumwa zinthu zokoma ndi kugawa chakudya kwa anthu amene sanathe kudzikonzera chakudya, pakuti lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Choncho musadzimvere chisoni pakuti chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.” Chosangalatsa n’chakuti anthuwo anamvera ndipo anayamba “kukondwera kwambiri.”—Neh. 8:10-12.
4. (a) Kodi atsogoleri a mabanja anachita chiyani ndipo anazindikira chiyani? (b) Kodi chinthu chofunika kwambiri pa Chikondwerero cha Misasa chinali chiyani?
4 Tsiku lotsatira, atsogoleri a mabanja anasonkhana kuti akambirane zimene Aisiraeli angachite kuti azitsatira kwambiri Chilamulo cha Mulungu. Pophunzira Malemba anazindikira kuti pa mwezi wa 7 wa Tishiri anayenera kuchita Chikondwerero cha Misasa ndiponso msonkhano wapadera kuyambira pa 15 mpaka pa 22. Choncho anayamba kukonzekera. Chikondwererocho chinayenda bwino kwambiri kuposa Chikondwerero cha Misasa chilichonse chimene chinachitika kuchokera nthawi ya Yoswa. Ndipo panali “chisangalalo chachikulu kwambiri.” Chinthu chofunika kwambiri pa chikondwererochi n’chakuti ankawerenga Chilamulo cha Mulungu “tsiku ndi tsiku, kuchokera tsiku loyamba mpaka tsiku lomaliza.”—Neh. 8:13-18.
TSIKU LOULULA MACHIMO
5. Kodi anthu a Mulungu anachita chiyani Alevi asanapemphere kwa Yehova?
5 Patadutsa masiku awiri, inafika nthawi yoti Aisiraeli aulule machimo awo amene anachita polephera kutsatira Chilamulo cha Mulungu. Iyi sinali nthawi yosangalala ayi. M’malomwake, anthu a Mulungu anasala kudya ndipo anavala ziguduli posonyeza kuti akulira. M’mawa wa tsikuli, anthu anawawerengeranso Chilamulo cha Mulungu kwa maola atatu. Ndiyeno madzulo “anali kuulula machimo awo ndi kugwadira Yehova Mulungu wawo.” Kenako Alevi anapereka pemphero lokonzedwa bwino m’malo mwa anthu onse. —Neh. 9:1-4.
6. (a) N’chiyani chinathandiza Alevi kuti apereke pemphero lokonzedwa bwino? (b) Kodi ife tikuphunzirapo chiyani?
6 N’zosakayikitsa kuti kuwerenga Chilamulo cha Mulungu mobwerezabwereza n’kumene kunathandiza Aleviwo kuti apereke pemphero lokonzedwa bwino. Mavesi 10 oyambirira a pempheroli, akufotokoza makhalidwe a Yehova ndiponso zimene anachita. Ndiyeno mavesi otsatira akutchula mobwerezabwereza kuti Mulungu ndi ‘wachifundo chachikulu.’ Komanso akusonyeza kuti Aisiraeli sanali oyenera kuchitiridwa chifundo ngati chimenecho. (Neh. 9:19, 27, 28, 31) Kodi ife tingatani kuti tiziperekanso mapemphero okonzedwa bwino? Mofanana ndi Aleviwa, tiyenera kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Tikamatero ndiye kuti tikulola Yehova kutilankhula tisanapemphere.—Sal. 1: 1, 2.
7. Kodi Alevi anapempha chiyani kwa Mulungu ndipo tikuphunzirapo chiyani?
7 M’pempheroli Alevi anangopempha kuti Mulungu awachitire chinthu chimodzi chokha. Zimene anapempha zili kumapeto kwa vesi 32 limene limati: “Tsopano Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi wochititsa mantha, wosunga pangano ndi kusonyeza kukoma mtima kosatha, musachepetse mavuto onse amene agwera ifeyo, mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu, aneneri athu, makolo athu ndi anthu anu onse kuchokera masiku a mafumu a Asuri mpaka lero.” Apatu Aleviwa anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Nafenso tiyenera kuyamba ndi kutamanda Mulungu ndiponso kumuyamikira tisanapemphe zimene tikufuna.
ANATAMANDA DZINA LAULEMERERO LA MULUNGU
8, 9. (a) Kodi Alevi anasonyeza bwanji kudzichepetsa kumayambiriro kwa pemphero lawo? (b) Pamene Alevi anatchula makamu a kumwamba, kodi iwo ayenera kuti ankanena za magulu awiri ati?
8 N’zoona kuti pemphero la Aleviwo linali lokonzedwa bwino. Koma iwo anali odzichepetsa ndipo ankaona kuti mawu awo sanali abwino kwenikweni moti n’kutamanda Yehova mokwanira. Choncho iwo anayamba pempheroli ndi mawu opempha Mulungu kuti athandize anthu ake kumutamanda mokwanira. Anati: “Atamande dzina lanu laulemerero, lokwezeka kuposa dalitso ndi chitamando chilichonse.”—Neh. 9:5.
9 Pempheroli linapitiriza kuti: “Inu ndinu Yehova, inu nokha. Ndinu amene munapanga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba ndi makamu ake onse. Ndinu amene munapanga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo komanso nyanja ndi zonse zili momwemo. Ndinu amene mukusunga zinthu zonse kuti zikhale ndi moyo. Ndipo makamu akumwamba amakugwadirani.” (Neh. 9:6) Yehova Mulungu analenga zinthu zonse, kuphatikizapo milalang’amba yosawerengeka yokhala ndi makamu a nyenyezi. Dzikoli analilenganso modabwitsa. Lili ndi zonse zofunika kuti zamoyo zamitundumitundu zizikhala bwinobwino komanso zizichulukana. Angelo oyera nawonso amatchedwa “makamu akumwamba,” ndipo ankaona pamene Mulungu ankalenga zinthu zonsezi. (1 Maf. 22:19; Yobu 38:4, 7) Angelo amatumikira Mulungu modzichepetsa pothandiza anthu ochimwa omwe “adzalandire chipulumutso monga cholowa.” (Aheb. 1:14) Angelowatu amapereka chitsanzo chabwino kwambiri kuti nafenso tizitumikira Yehova mogwirizana ngati makamu a asilikali ophunzitsidwa bwino.—1 Akor. 14:33, 40.
10. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mulungu anachitira Abulahamu?
10 Kenako Alevi anatchula zimene Mulungu anachitira Abulamu. Pamene Abulamu ankafika zaka 99, mkazi wake Sarai anali asanabereke mwana. Ndiyeno Yehova anasintha dzina lake kukhala Abulahamu, lomwe limatanthauza “tate wa mitundu yambiri.” (Gen. 17:1-6, 15, 16) Mulungu analonjezanso Abulahamu kuti mbewu yake idzakhala m’dziko la Kanani. Nthawi zambiri, anthu amaiwala malonjezo awo, koma Yehova saiwala. Pemphero la Alevi limatsimikizira zimenezi. Iwo anati: “Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu ndi kum’tulutsa ku Uri wa Akasidi ndipo munamutcha dzina lakuti Abulahamu. Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika pamaso panu. Chotero munachita naye pangano kuti mudzam’patsa dziko la Akanani . . . kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbewu yake, ndipo munachitadi zimene munanena chifukwa ndinu wolungama.” (Neh. 9:7, 8) Tiyeni nafenso tizitsanzira Mulungu wathu wolungama poyesetsa kukhala okhulupirika tikalonjeza zinthu.—Mat. 5:37.
ANATCHULA ZINTHU ZIMENE YEHOVA ANACHITA
11, 12. (a) Kodi dzina lakuti Yehova limatanthauza chiyani? (b) Kodi zimene Yehova anachitira mbadwa za Abulahamu zikugwirizana bwanji ndi tanthauzoli?
11 Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.” Izi zikutanthauza kuti nthawi zonse Mulungu amachita zinthu pokwaniritsa malonjezo ake. Tingaone zimenezi tikaganizira zimene Mulungu anachitira Aisiraeli, omwe anali mbadwa za Abulahamu, pamene anali mu ukapolo ku Iguputo. Pa nthawiyo zinkaoneka kuti n’zosatheka kuti mtundu wonsewo umasulidwe n’kukakhala m’Dziko Lolonjezedwa. Koma Mulungu ankachita zinthu zosiyanasiyana pokwaniritsa lonjezo lake. Izi zinasonyeza kuti iye yekha ndiye woyenera kukhala ndi dzina lapadera lakuti Yehova.
12 Ponena za Yehova, pemphero limene Nehemiya analemba limati: “Munaona nsautso ya makolo athu ku Iguputo ndipo munamvanso kulira kwawo pa Nyanja Yofiira. Ndiyeno munaonetsa Farao zizindikiro ndi zozizwitsa zomukhaulitsa pamodzi ndi atumiki ake onse ndi anthu onse okhala m’dziko lake. Munatero chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza kwa makolo athu. Pamenepo munadzipangira dzina kufikira lero. Munagawa nyanja pamaso pawo ndipo iwo anadutsa panthaka youma pakati pa nyanja. Anthu amene anali kuwathamangitsa munawaponya m’nyanja yozama ngati mwala woponyedwa m’madzi amphamvu.” Ndiyeno anapitiriza pempheroli pofotokoza zinanso zimene Yehova anachitira anthu ake. Anati: “Munagonjetsa anthu okhala m’dzikolo, Akanani.” Kenako anati anthu a Mulungu “analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Analandanso nthaka yachonde, nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino, zitsime, minda ya mpesa ndi ya maolivi ndi mitengo ya zipatso yochuluka. Atatero, anayamba kudya, kukhuta, kunenepa ndi kukondwera ndi ubwino wanu waukulu.”—Neh. 9:9-11, 24, 25.
13. Kodi Yehova anathandiza bwanji Aisiraeli kuti apitirize kukhala naye pa ubwenzi wabwino, koma iwo anatani?
13 Mulungu anachita zinthu zina zambiri pokwaniritsa cholinga chake. Mwachitsanzo, Aisiraeli atangochoka ku Iguputo, Yehova anawapatsa zinthu zowathandiza kuti apitirize kukhala naye pa ubwenzi wabwino. Mu pempheroli, Aleviwo ananena kuti: “Munatsikira paphiri la Sinai ndi kulankhula nawo muli kumwamba. Munawapatsa zigamulo zowongoka ndi malamulo a choonadi, mfundo zabwino ndi malangizo abwino.” (Neh. 9:13) Yehova ankaphunzitsa anthu ake, omwe ankayembekezera kukalowa m’Dziko Lolonjezedwa, kuti azichita zinthu mogwirizana ndi dzina lake loyera. Koma iwo anasiya kutsatira zinthu zabwino zimene anawaphunzitsazo.—Werengani Nehemiya 9:16-18.
AISIRAELI ANAFUNIKA KULANGIDWA
14, 15. (a) Kodi Yehova anasamalira bwanji anthu ake mwachifundo ngakhale kuti ankachimwa? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Mulungu ankachita ndi anthu ake osankhidwa?
14 Mu pempheroli, Alevi ananena za machimo awiri amene Aisiraeli anachita atangolonjeza paphiri la Sinai kuti azisunga Chilamulo cha Mulungu. Chifukwa cha machimowa, Mulungu anayenera kungowasiya Aisiraeliwo kuti azifa. Koma Aleviwo anatamanda Yehova kuti: “Inuyo simunawasiye m’chipululu chifukwa cha chifundo chanu chachikulu. . . . Kwa zaka 40 munawapatsa chakudya . . . Iwo sanasowe kanthu. Zovala zawo sizinathe ndipo mapazi awo sanatupe.” (Neh. 9:19, 21) Masiku anonso, Yehova amatipatsa zonse zofunika kuti tizimutumikira mokhulupirika. Choncho tisakhale ngati Aisiraeli amene anafera m’chipululu chifukwa chosamvera Mulungu komanso kusowa chikhulupiriro. Zimene zinachitikira Aisiraeli “zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.”—1 Akor. 10:1-11.
15 N’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli atalowa m’Dziko Lolonjezedwa, anayamba kulambira milungu ya Akanani. Polambira milungu imeneyi ankachita zinthu zachiwerewere ndiponso kupha anthu. Choncho Yehova analola kuti mitundu yowazungulira iziwapondereza. Aisiraeliwo akalapa, Yehova ankawachitira chifundo n’kuwakhululukira ndipo ankawalanditsa kwa adani awo. Zimenezi zinkachitika “mobwerezabwereza.” (Werengani Nehemiya 9:26-28, 31.) Alevi anati: “Munaleza nawo mtima kwa zaka zambiri ndipo munapitirizabe kuwachenjeza mwa mzimu wanu potumiza aneneri anu, koma iwo sanamvere. Pamapeto pake munawapereka m’manja mwa mitundu ya anthu ya m’dzikolo.”—Neh. 9:30.
16, 17. (a) Kodi n’chiyani chinachitika Aisiraeli atayambanso kuchita zosemphana ndi Chilamulo cha Yehova? (b) Kodi Aisiraeli anavomereza chiyani ndipo analonjeza kuchita chiyani?
16 Ngakhale atamasulidwa ku ukapolo, Aisiraeli anayambanso kuchita zosemphana ndi Chilamulo cha Yehova. Ndiyeno n’chiyani chinawachitikira? Alevi anafotokoza m’pemphero lawo kuti: “Onani, lero ife ndife akapolo. Ndife akapolo m’dziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino. Zokolola za m’dzikoli zachulukira mafumu amene mwatiikira chifukwa cha machimo athu . . . ndipo tili pamavuto aakulu.”—Neh. 9:36, 37.
17 Kodi Alevi ankatanthauza kuti Mulungu sanachite chilungamo polola kuti Aisiraeli avutike? Ayi. Iwo anavomereza machimo awo ponena kuti: “Inu ndinu wolungama pa zinthu zonse zimene zatichitikira, pakuti inu mwachita zinthu mokhulupirika koma ife tachita zinthu zoipa.” (Neh. 9:33) Iwo anamaliza pempheroli polonjeza kuti Aisiraeli ayamba nthawi yomweyo kumvera Chilamulo cha Mulungu. (Werengani Nehemiya 9:38; 10:29) Aleviwo analemba lonjezolo ndipo atsogoleri 84 analisainira.—Neh. 10:1-27.
18, 19. (a) Kodi timafunikira chiyani kuti tidzalowe m’dziko latsopano la Mulungu? (b) Kodi sitiyenera kusiya kupempherera chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?
18 Anthufe timafunikira kulangizidwa ndi Yehova kuti tikhale oyenerera kulowa m’dziko latsopano. Paja mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Ndi mwana wanji amene bambo ake samulanga?” (Aheb. 12:7) Timasonyeza kuti timafuna kulangizidwa ndi Mulungu tikamatumikirabe mokhulupirika ndiponso kulola kuti mzimu wake uzitiumba. Tikachita tchimo lalikulu, Yehova adzatikhululukira ngati talapa moona mtima ndiponso kulandira chilango modzichepetsa.
19 Posachedwapa, Yehova adzachititsa kuti anthu alemekeze dzina lake kuposa mmene anachitira populumutsa Aisiraeli ku Iguputo. (Ezek. 38:23) Mofanana ndi anthu ake akale amene analandira Dziko Lolonjezedwa, Akhristu onse okhulupirika adzalandira moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (2 Pet. 3:13) Popeza kuti tikuyembekeza zinthu zabwino zimenezi, tiyeni tisasiye kupemphera kuti dzina laulemerero la Mulungu liyeretsedwe. M’nkhani yotsatira, tidzakambirana pemphero lina. Tidzaonanso kuti ngati tichita zinthu mogwirizana ndi pemphero limenelo, Mulungu azitidalitsa panopa mpaka muyaya.