Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tumikirani Yehova Monga Akapolo”

“Tumikirani Yehova Monga Akapolo”

“Musakhale aulesi pa ntchito yanu. . . . Tumikirani Yehova monga akapolo.”—AROMA 12:11.

1. Kodi ukapolo wotchulidwa pa Aroma 12:11 umasiyana bwanji ndi umene anthu amaudziwa?

ANTHU akamva mawu oti kapolo amaganiza za munthu amene amalamulidwa mwankhanza, kuponderezedwa ndiponso kuzunzidwa. Koma izi n’zosiyana ndi ukapolo wa Akhristu. Mawu a Mulungu amanena za akapolo amene amadzipereka kuti atumikire Yehova, yemwe ndi Ambuye wachikondi. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu oyambirira kuti: “Tumikirani Yehova monga akapolo.” (Aroma 12:11) Apa mtumwiyu ankawalimbikitsa kutumikira Mulungu chifukwa chomukonda. Kodi munthu angatani kuti atumikire Mulungu ngati kapolo? Kodi tingapewe bwanji kukhala akapolo a Satana ndi dziko lakeli? Kodi munthu amalandira mphoto yotani akamatumikira Yehova mokhulupirika ngati kapolo?

“NDIMAM’KONDA KWAMBIRI MBUYE WANGA”

2. (a) N’chiyani chinkachititsa akapolo ena ku Isiraeli kukhalabe ndi ambuye awo? (b) Kodi kuboola khutu la kapolo kunkasonyeza chiyani?

2 Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli chimatithandiza kudziwa zimene Yehova amafuna kuti tizichita pomutumikira monga akapolo. Aisiraeli ankamasula akapolo awo akawatumikira kwa zaka 7. (Eks. 21:2) Koma Yehova ankaperekanso mwayi kwa kapolo amene ankakonda kwambiri mbuye wake moti ankafunabe kumutumikira. Mbuyeyo ankafunika kupita ndi kapoloyo pachitseko kapena pafelemu n’kumuboola khutu. (Eks. 21:5, 6) Mofanana ndi Chichewa, mawu achiheberi akuti kumvera amachokeranso ku mawu otanthauza kumva ndi makutu. Pololera kubooledwa khutu, kapoloyo ankasonyeza kuti azimvera mbuye wakeyo ndi mtima wonse. Choncho pamene tinadzipereka kwa Mulungu, tinasonyeza kuti tizimumvera ndi mtima wonse chifukwa chomukonda.

3. Kodi timadzipereka kwa Mulungu chifukwa chiyani?

3 Pamene tinkabatizidwa, tinali titasankha kale kutumikira Yehova monga akapolo ake. Tinadzipereka kwa Yehova chifukwa chofuna kumumvera ndiponso kuchita zimene amafuna. Palibe amene anatikakamiza kuchita zimenezi.  N’chimodzimodzinso ndi mwana amene akubatizidwa. Iye amachita izi chifukwa choti wadzipereka kwa Mulungu osati chifukwa chofuna kusangalatsa makolo ake. Timadzipereka kwa Yehova chifukwa chomukonda monga Mbuye wathu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.”—1 Yoh. 5:3.

TAMASULIDWA KOMABE NDIFE AKAPOLO

4. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale “akapolo a chilungamo”?

4 Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa chotipatsa mwayi womutumikira monga akapolo ake. Tikamakhulupirira nsembe ya dipo ya Khristu timamasuka ku ukapolo wa uchimo. Ngakhale kuti tidakali anthu ochimwa, tadzipereka mofunitsitsa kuti Yehova ndi Yesu azitilamulira. Paulo anafotokoza zimenezi momveka bwino m’kalata ina. Iye anati: “Dzioneni ngati akufa ku uchimo koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.” Kenako anachenjeza kuti: “Kodi simukudziwa kuti ngati mudziperekabe kwa winawake monga akapolo kuti muzimumvera, mumakhala akapolo ake chifukwa chakuti mumamumvera, kaya mukhale akapolo a uchimo umene umatsogolera ku imfa, kapena mukhale akapolo a kumvera kumene kumatsogolera ku chilungamo? Koma tikuyamika Mulungu kuti ngakhale poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mtundu wa chiphunzitso chimene chinaperekedwa kwa inu. Inde, popeza munamasulidwa ku uchimo, munakhala akapolo a chilungamo.” (Aroma 6:11, 16-18) Onani kuti mtumwiyu ananena kuti: “Munamvera mochokera pansi pa mtima.” Choncho tikadzipereka kwa Yehova timakhaladi “akapolo a chilungamo.”

5. Kodi tonsefe tikulimbana ndi chiyani?

5 Komabe timakumana ndi mavuto poyesetsa kutumikira Mulungu mokhulupirika. Mavutowa amachokera mbali ziwiri. Paulo anatchula mbali yoyamba pamene analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi chilamulo cha Mulungu, koma ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:22, 23) Ifenso timavutika ndi uchimo umene tinabadwa nawo. Choncho nthawi zonse timalimbana ndi zilakolako za thupi lathu. Mtumwi Petulo ananena kuti: “Khalani mfulu, koma ufulu wanu usakhale ngati chophimbira zoipa, koma monga akapolo a Mulungu.”—1 Pet. 2:16.

6, 7. Kodi Satana amachita chiyani kuti zinthu za m’dzikoli zizioneka zabwino?

6 Mavuto ena amene timalimbana nawo amachokera m’dzikoli, lomwe likulamuliridwa ndi Satana ndi ziwanda zake. Satana amalimbana nafe n’cholinga choti tisiye kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi Yesu. Pofuna kuti tikhale akapolo ake, iye amatikopa ndi zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. (Werengani Aefeso 6:11, 12.) Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kuchititsa kuti zinthu za m’dzikoli zizioneka zosangalatsa ndiponso zabwino. Koma mtumwi Yohane anachenjeza kuti: “Ngati wina akukonda dziko, ndiye kuti sakonda Atate. Pakuti chilichonse cha m’dziko, monga chilakolako cha thupi, chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake, sizichokera kwa Atate, koma kudziko.”—1 Yoh. 2:15, 16.

7 M’dzikoli anthu ambiri amafunitsitsa kukhala ndi chuma chambiri. Satana amachititsa anthu kukhulupirira kuti angakhale osangalala pokhapokha ngati ali ndi ndalama zambiri. Masiku ano, pali mashopu akuluakulu ambiri. Ndiyeno otsatsa malonda amalimbikitsa anthu kupeza zinthu zambirimbiri ndiponso kuti azingokhalira kusangalala. Palinso makampani ambiri amene amalimbikitsa anthu kulowa mpikisano kuti awine ndalama kapena zinthu zina zapamwamba. Dzikoli limangolimbikitsa anthu kuti ayesetse n’cholinga choti anzawo aziwaona ngati apamwamba.

8, 9. Kodi tiyenera kusamala ndi chiyani ndipo n’chifukwa chiyani?

 8 Pofotokoza za Akhristu ena oyambirira amene anatengera maganizo a m’dziko, Petulo anachenjeza kuti: “Iwo amaona kuti kuchita masana zinthu zokhutiritsa chilakolako cha thupi lawo n’kosangalatsa. Anthu amenewa ali ngati mawanga ndi zilema pakati panu, ndipo amakondwera kwadzaoneni akamakuphunzitsani zinthu zonyenga pamene akudya nanu limodzi. Pakuti amalankhula mawu odzitukumula opanda pake, ndipo pogwiritsa ntchito zilakolako za thupi komanso makhalidwe otayirira, amakopa amene akungopulumuka kumene kwa anthu ochita zolakwa. Pamene akuwalonjeza ufulu, eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa. Pakuti aliyense amene wagonjetsedwa, amakhala kapolo kwa womugonjetsayo.”—2 Pet. 2:13, 18, 19.

9 Kupeza zimene maso akulakalaka sikupatsa munthu ufulu. M’malomwake, munthuyo amakhala kapolo wa Satana Mdyerekezi, yemwe ndi mbuye wa dzikoli. (1 Yoh. 5:19) Zimakhala zosavuta kuti munthu akhale kapolo wa chuma koma kuti amasuke pamakhala matatalazi.

NTCHITO YABWINO KWAMBIRI

10, 11. Kodi Satana akulimbana kwambiri ndi ndani masiku ano, nanga maphunziro a m’dzikoli amawabweretsera mavuto otani?

10 Mofanana ndi zimene anachita mu Edeni, masiku anonso Satana amalimbana kwambiri ndi anthu amene sakudziwa zambiri, makamaka achinyamata. Sasangalala akaona achinyamata kapena wina aliyense akudzipereka kuti atumikire Yehova. Mdani wa Mulungu ameneyu akufuna kuti aliyense amene anadzipereka kwa Yehova asiye kumutumikira mokhulupirika.

11 Tiyeni tikambiranenso chitsanzo cha kapolo wololera kuti khutu lake libooledwe. Kapoloyu ayenera kuti ankamva kupweteka kwa nthawi yochepa. Koma posakhalitsa ululuwo unkatha n’kungotsala ndi chizindikiro chosonyeza kuti azitumikirabe mbuye wakeyo. Mofanana ndi zimenezi, zimakhala zovuta komanso zopweteka kwa wachinyamata amene wasankha kuchita zinthu zosiyana ndi zimene anzake akuchita. Satana amachititsa anthu kuganiza kuti angakhale osangalala ngati atapeza ntchito yapamwamba. Koma Akhristu amadziwa kuti chofunika kwambiri n’kuchita zinthu zimene zingawathandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Akhristu amene anadzipereka kwa Mulungu amachita zofuna za Mulunguyo, osati za Satana. Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulocho usana ndi usiku. (Werengani Salimo 1:1-3.) Koma maphunziro ambiri m’dzikoli sapereka mpata kwa mtumiki  wa Yehova woti aziphunzira ndi kusinkhasinkha za Yehova.

12. Kodi achinyamata ambiri masiku ano amafunika kusankha pa nkhani iti?

12 Nthawi zina, mbuye amene sankalambira Mulungu ankachititsa kuti zinthu zikhale zovuta kwa kapolo wake amene anali Mkhristu. Choncho m’kalata yoyamba imene analembera Akhristu a ku Korinto, Paulo anafunsa kuti: “Kodi unaitanidwa uli kapolo?” Kenako anapereka malangizo akuti: “Usade nazo nkhawa zimenezo, koma ngati ungathenso kumasuka, tengerapo mwayi pamenepo.” (1 Akor. 7:21) Aliyense akanakonda kumasuka kuti asakhalenso kapolo. Masiku ano, mayiko ambiri ali ndi lamulo lakuti mwana aliyense azipita kusukulu. Koma akafika kalasi inayake amakhala ndi ufulu wopitiriza kapena kusiya. Munthu amene wasankha kupitiriza maphunziro m’dzikoli kuti apeze ntchito yapamwamba, zingamuvute kuti achite utumiki wa nthawi zonse.—Werengani 1 Akorinto 7:23.

Kodi inuyo mudzatumikira mbuye uti?

KODI MUDZASANKHA MAPHUNZIRO ATI?

13. Kodi ndi maphunziro ati amene angathandize kwambiri atumiki a Yehova?

13 Paulo anachenjeza Akhristu a ku Kolose kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.” (Akol. 2:8) Anthu ambiri m’dzikoli akuyendera “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu.” Izi zili choncho chifukwa chakuti anthu ophunzira kwambiri amalimbikitsa zimenezi. Anthu amene amapita ku yunivesite amangophunzira nzeru za anthu koma nthawi zambiri saphunzira zinthu zowathandiza kugwira bwino ntchito akamaliza maphunzirowo. Koma atumiki a Yehova amasankha kuphunzira ntchito imene ingawathandize kukhala moyo wosalira zambiri kwinaku akutumikira Mulungu. Iwo amatsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa Timoteyo akuti: “Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:6, 8) M’malo molimbana ndi kupeza madigiri kapena mayina aulemu, Akhristu oona amachita khama mu utumiki n’cholinga choti athandize anthu kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.—Werengani 2 Akorinto 3:1-3.

14. Malinga ndi Afilipi 3:8, kodi Paulo ankaona bwanji mwayi wake wotumikira Mulungu ndi Khristu?

14 Taganizirani za mtumwi Paulo. Iye anaphunzitsidwa ndi Myuda wina dzina lake Gamaliyeli, yemwe anali katswiri pophunzitsa  Chilamulo. Masiku ano, maphunziro a Paulo tingawayerekezere ndi maphunziro a ku yunivesite. Koma kodi Paulo ankawaona bwanji maphunzirowo akawayerekezera ndi mwayi wotumikira Mulungu ndi Khristu? Iye analemba kuti: “Ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.” Ndiye anapitiriza kuti: “Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu.” (Afil. 3:8) Zimene Paulo ananenazi ziyenera kuthandiza achinyamata komanso makolo awo oopa Mulungu kuti azisankha zochita mwanzeru pa nkhani ya maphunziro. (Onani zithunzi.)

MAPHUNZIRO AMENE ANGAKUTHANDIZENI KWAMBIRI

15, 16. Kodi gulu la Yehova limapereka maphunziro otani, ndipo cholinga chake n’chiyani?

15 Kodi m’mayunivesite ambiri m’dzikoli mumachitika zotani? Nthawi zambiri kumachitika mikangano ndi zipolowe zokhudza ndale ndiponso zinthu zina. (Aef. 2:2) Koma gulu la Yehova limapereka maphunziro apamwamba kwambiri mumpingo wachikhristu, womwe ndi malo abata. Mwachitsanzo, tonsefe tingapindule ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imene imachitika mlungu uliwonse. Abale osakwatira omwe akuchita upainiya ali ndi mwayi wolandira maphunziro apadera ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira. Nawonso Akhristu apabanja amene akuchita upainiya akhoza kupita ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja. Maphunziro onsewa amatithandiza kuti tizimvera Ambuye wathu wakumwamba, Yehova.

16 Kuwonjezera pamenepo, timafufuza chuma chauzimu pogwiritsa ntchito mabuku athu kapena mlozera nkhani amene amapezeka m’magazini a December chaka chilichonse. * Cholinga cha maphunziro onsewa n’kutithandiza kutumikira bwino Yehova. Timaphunzira mmene tingathandizire ena kuti agwirizanenso ndi Mulungu. (2 Akor. 5:20) Zimenezi zingawathandize kuti nawonso aphunzitse ena.—2 Tim. 2:2.

MADALITSO OMWE KAPOLO AMALANDIRA

17. Kodi munthu amapeza madalitso otani akasankha maphunziro ochokera kwa Mulungu?

17 M’fanizo la Yesu la matalente, akapolo awiri okhulupirika anayamikiridwa ndipo anasangalala ndi mbuye wawo n’kupatsidwa ntchito yambiri. (Werengani Mateyu 25:21, 23.) Tikasankha maphunziro ochokera kwa Mulungu timasangalala ndiponso kudalitsidwa. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Michael. Iye anakhoza bwino kusukulu moti aphunzitsi ake anamuitana kuti akakambirane naye zimene angachite kuti apite kuyunivesite. Koma aphunzitsiwo anadabwa kumva kuti iye akufuna kungophunzira ntchito inayake kuti azipeza kangachepe kwinaku akuchita upainiya wokhazikika. Kodi iye amanong’oneza bondo ndi zimene anasankhazi? Iye anati: “Zimene ndaphunzira monga mpainiya komanso mkulu n’zapamwamba kwambiri. Madalitso amene ndapeza komanso mwayi wa utumiki umene ndili nawo n’zofunika kwambiri kuposa ndalama zilizonse zimene ndikanapeza. Ndinachita bwino kwambiri kukana maphunziro a kuyunivesite.”

18. N’chiyani chimakulimbikitsani kusankha maphunziro ochokera kwa Mulungu?

18 Maphunziro amene takambiranawa amatithandiza kudziwa zimene Yehova Mulungu amafuna ndiponso kumutumikira monga akapolo. Amatithandiza kuti tikhale ndi chiyembekezo ‘chodzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda n’kudzakhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:21) Chofunika kwambiri n’chakuti maphunzirowa amatithandiza kudziwa mmene tingasonyezere kuti timakonda kwambiri Yehova, yemwe ndi Mbuye wathu wakumwamba.—Eks. 21:5.

^ ndime 16 Mungagwiritsenso ntchito Watch Tower Publications Index kapena Watchtower Library ya pakompyuta.