Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?

Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?

“Ife tidzamutumizira abusa 7, inde atsogoleri 8 a anthu kuti akathane naye.”—MIKA 5:5.

1. N’chifukwa chiyani zimene Mfumu ya Isiraeli ndi ya Siriya ankapangana zinali zosaphula kanthu?

CHAPAKATI pa chaka cha 762 B.C.E. ndi 759 B.C.E., mfumu ya Isiraeli ndi mfumu ya Siriya anaopseza kuti amenyana ndi ufumu wa Yuda. Kodi cholinga chawo chinali chiyani? Ankafuna kugonjetsa Yerusalemu n’kuchotsa pampando Mfumu Ahazi, kenako n’kulonga ufumu munthu wina amene mwina sanali mu mzera wa Mfumu Davide. (Yes. 7:5, 6) Koma mfumu ya Isiraeli inayenera kudziwa lamulo la Yehova lakuti mbadwa za Davide zokha n’zimene zizikhala pampando wachifumu mpaka kalekale. Inayenera kudziwanso kuti zimene Mulungu wanena sizilephereka.—Yos. 23:14; 2 Sam. 7:16.

2-4. Kodi lemba la Yesaya 7:14, 16 linakwaniritsidwa bwanji (a) m’nthawi ya Yesaya? (b) m’nthawi ya Yesu?

2 Poyamba zinkaoneka ngati adaniwo zikuwayendera bwino. Pa nthawi imodzi, iwo anapha asilikali amphamvu a Ahazi okwana 120,000. “Mwana wa mfumu” dzina lake Maaseya anaphedwanso. (2 Mbiri 28:6, 7) Komatu Yehova ankaona zonsezi ndipo ankakumbukira zimene analonjeza Davide. Choncho anatumiza mneneri Yesaya kuti akapereke uthenga wolimbikitsa kwambiri.

3 Yesaya anati: “Tamverani! Mtsikana adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli. Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino, nthaka ya mafumu awiri [a Siriya ndi Isiraeli] amene ukuchita nawo mantha ofika podwala nawowo, idzakhala itasiyidwiratu.” (Yes. 7:14, 16) N’zoona kuti mbali yoyamba ya ulosiwu inakwaniritsidwa pa kubadwa kwa Mesiya. (Mat. 1:23) Komatu pa nthawi imene Mesiya ankabadwa “mafumu awiri,” a Siriya ndi Isiraeli, sankafuna kumenyana ndi ufumu  wa Yuda. Choncho ulosi wonena za Emanueli umenewu uyenera kuti unakwaniritsidwanso nthawi ya Yesaya.

4 Pasanapite nthawi kuchokera pamene Yesaya ananena zimenezi, mkazi wake anatenga pakati n’kubereka mwana dzina lake Maheri-salala-hasi-bazi. N’kutheka kuti mwana ameneyu ndi amene Yesaya anamutchula kuti Emanueli. * Kalelo, nthawi zina mwana akabadwa ankapatsidwa dzina lina pofuna kuti anthu azikumbukira zinazake koma kenako makolo ake komanso achibale ankamutchula ndi dzina lina. (2 Sam. 12:24, 25) Koma palibe umboni wosonyeza kuti Yesu ankadziwika ndi dzina loti Emanueli.—Werengani Yesaya 7:14; 8:3, 4.

5. Kodi Ahazi anasonyeza bwanji kuti anali wopusa?

5 Pamene ufumu wa Isiraeli ndi wa Siriya unkafuna kuukira Yuda, ufumu wina wokhala ndi asilikali oopsa unkalakalakanso kugonjetsa dera lonselo. Ufumu wake unali wa Asuri ndipo unadzakhala ufumu wamphamvu padziko lonse. Ulosi wa pa Yesaya 8:3, 4, unanena kuti Asuri asanaukire ufumu wa Yuda, adzanyamula kaye “chuma cha ku Damasiko” ndi “katundu wolandidwa ku Samariya.” M’malo mokhulupirira mawu a Mulungu amene Yesaya ananena, Ahazi anachita pangano ndi Asuri ndipo izi zinachititsa kuti Asuriwo azipondereza Ayuda. (2 Maf. 16:7-10) Ahazi anali m’busa wa Yuda koma apa tingati anachita zopusa kwambiri. Ifenso tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, ndimadalira Mulungu kapena anthu?’—Miy. 3:5, 6.

M’BUSA WATSOPANO ANASINTHA ZINTHU

6. Kodi ulamuliro wa Ahazi unasiyana bwanji ndi wa Hezekiya?

6 Ahazi anafa mu 746 B.C.E. ndipo mwana wake dzina lake Hezekiya ndi amene analowa ufumu. Pa nthawiyo, zinthu sizinali kuyenda bwino mu ufumu wa Yuda pa nkhani ya zachuma komanso ya kulambira. Kodi Hezekiya atalowa ufumuwo anaona kuti chinthu chofunika kwambiri kuchita n’chiyani? Kodi anaganiza zoyamba kukonza mavuto azachuma? Ayi. Hezekiya anali munthu wokonda Mulungu choncho tingati anali m’busa woyenerera wa anthu ake. Chinthu choyamba chimene anachita chinali kubwezeretsa kulambira koyera ndiponso kuthandiza Ayuda kukonza ubwenzi wawo ndi Yehova. Hezekiya atangodziwa zimene Mulungu ankafuna kuti achite, anachita nthawi yomweyo. Apatu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.—2 Mbiri 29:1-19.

7. N’chifukwa chiyani Alevi anayenera kutsimikiziridwa ndi Hezekiya kuti awathandiza?

7 Alevi ndi amene anayenera kuthandiza kwambiri kubwezeretsa kulambira koyera. Choncho Hezekiya anasonkhanitsa Aleviwo n’kuwatsimikizira zoti awathandiza. Taganizirani mmene zinalili pa msonkhanowu. Mwina Alevi okhulupirika amene analipo anali kugwetsa misozi chifukwa chosangalala kumva mfumu yawo ikunena kuti: “Inu ndi amene Yehova wakusankhani kuti muziima pamaso pake ndi kum’tumikira.” (2 Mbiri 29:11) Choncho Alevi anali ndi udindo waukulu kuti abwezeretse kulambira koona.

8. Kodi Hezekiya anachita zinthu ziti kuti abwezeretse kulambira koyera ndipo zotsatira zake zinali zotani?

8 Hezekiya anaitana Ayuda ndiponso Aisiraeli onse kudzachita chikondwerero chachikulu cha Pasika komanso Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa cha masiku 7. Anthuwo anasangalala kwambiri pa chikondwererocho moti anawonjezera masiku ena 7. Baibulo limati: “Chotero munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira m’masiku a Solomo mwana wa Davide mfumu ya Isiraeli, kunali kusanachitike chikondwerero ngati chimenechi ku Yerusalemu.”  (2 Mbiri 30:25, 26) Chikondwerero chimenechi chinalimbikitsa kwambiri anthu onse. Lemba la 2 Mbiri 31:1 limati: “Atangomaliza kuchita zonsezi, . . . anapita kumizinda ya Yuda n’kukaphwanya zipilala zopatulika, kukadula mizati yopatulika ndi kukagwetsa malo okwezeka ndi maguwa ansembe.” Ayuda anayambadi kubwerera kwa Yehova. Kubwezeretsa kulambira koyera kumeneku kunali kofunika kwambiri chifukwa cha zimene zinali zitatsala pang’ono kuchitika.

MFUMU INADALIRA YEHOVA

9. (a) Kodi cholinga cha ufumu wa Isiraeli chinalephereka bwanji? (b) Kodi Senakeribu anachita zotani ku Yuda?

9 Mawu a Yesaya anakwaniritsidwadi. Asuri anagonjetsa ufumu wa Isiraeli n’kutenga anthu ake kupita nawo ku ukapolo. Izi zinalepheretsa cholinga chawo chofuna kuchotsa pampando mfumu ya mu mzera wa Davide. Kodi cholinga cha Asuriwo chinali chiyani? Iwo ankafuna kugonjetsanso ufumu wa Yuda. Baibulo limati: “M’chaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri anabwera kudzachita nkhondo ndi mizinda yonse ya Ayuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.” Zikuoneka kuti Senakeribu anagonjetsa mizinda 46 ya mu Yudeya. Kodi inuyo mukanakhala ku Yerusalemu pa nthawiyo n’kumva kuti mizinda yonseyo ikuwonongedwa ndi asilikali a Asuri mukanamva bwanji?—2 Maf. 18:13.

10. N’chifukwa chiyani mawu a pa Mika 5:5, 6 ayenera kuti analimbikitsa Hezekiya?

10 Hezekiya anamva zimene zinkachitikazi ndipo anadziwa kuti sizili bwino. Koma mosiyana ndi bambo ake, iye sanakapemphe thandizo ku mitundu yosalambira Mulungu. M’malomwake, anadalira Yehova. (2 Mbiri 28:20, 21) N’kutheka kuti ankakumbukira mawu amene mneneri wa pa nthawiyo dzina lake Mika ananena zokhudza Asuri. Iye anati: “Msuri . . . tidzamutumizira abusa 7, inde atsogoleri 8 a anthu kuti akathane naye. Atsogoleriwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.” (Mika 5:5, 6) Hezekiya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu ochokera kwa Mulungu amenewa. Mawuwa anasonyeza kuti asilikali odabwitsa adzatumizidwa kudzamenyana ndi Asuri ndipo adzawagonjetsa.

11. Kodi ulosi wonena za abusa 7 ndi atsogoleri 8 udzakwaniritsidwa m’njira yaikulu pa nthawi iti?

11 Yesu ndi amene Mika anamutchula mu  ulosi wake kuti ‘wolamulira mu Isiraeli, amene wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira.’ Koma ulosi wonena za abusa 7 ndi atsogoleri 8 (Baibulo lina limati “akalonga 8”) unali woti udzakwaniritsidwa m’njira yaikulu patapita zaka zambiri Yesu atabadwa. (Werengani Mika 5:1, 2.) Udzakwaniritsidwa pa nthawi imene atumiki a Yehova adzaopsezedwa kwambiri ndi “Msuri” wamakono. Yehova adzagwiritsa ntchito Mwana wake polimbana ndi adani oopsawa. Koma kodi adzagwiritsanso ntchito ndani pomenya nkhondoyi? Tiona m’nkhaniyi, koma choyamba, tiyeni tikambirane zimene Hezekiya anachita ataopsezedwa ndi asilikali a Asuri.

HEZEKIYA ANACHITA ZIMENE AKANATHA

12. Kodi Hezekiya ndi anzake anachita chiyani poteteza anthu a Mulungu?

12 Yehova ndi wofunitsitsa kutithandiza kwambiri koma amayembekezera kuti nafenso tichite mbali yathu. Hezekiya “anagwirizana ndi akalonga ake ndi amuna ake amphamvu kuti atseke akasupe a madzi amene anali kunja kwa mzindawo . . . Kuwonjezera apo, [Hezekiya] analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka. Anamanga nsanja pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina . . . ndipo anapanga zida zambiri ndi zishango.” (2 Mbiri 32:3-5) Kuti ateteze ndiponso kutsogolera anthu ake, Yehova anagwiritsa ntchito amuna amphamvu ambiri monga Hezekiya, akalonga ake komanso aneneri okhulupirika.

13. Kodi Hezekiya anachita chinthu chofunika kwambiri chiti kuti alimbitse mtima anthu ake? Fotokozani.

13 Kenako Hezekiya anachita chinthu chofunika kwambiri kuposa kutseka akasupe a madzi kapena kumanga makoma onse a mpanda. Iye anali m’busa woganizira kwambiri anthu ake ndipo anawasonkhanitsa ndi kuwalimbikitsa ndi mawu akuti: “Musaope kapena kuchita mantha ndi mfumu ya Asuri . . . , chifukwa ife tili ndi ambiri kuposa amene ali ndi mfumuyo. Iyo ikudalira mphamvu za anthu, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.” Mawuwa anali olimbikitsa kwambiri ndipo anakumbutsa anthuwo kuti Yehova adzawamenyera nkhondoyo. Ayuda atamva zimenezi “anayamba kulimba mtima chifukwa cha mawu a Hezekiya mfumu ya Yuda.” Onani kuti “mawu a Hezekiya” ndi amene anathandiza anthu kuti alimbe mtima. Mfumuyo, akalonga ake, amuna ake amphamvu ndiponso mneneri Mika ndi Yesaya analidi abusa abwino ngati amene Yehova analosera kudzera mwa mneneri wake.—2 Mbiri 32:7, 8; werengani Mika 5:5, 6.

Mawu a Hezekiya anathandiza anthu kukhala olimba mtima (Onani ndime 12 ndi 13)

14. Kodi Rabisake anachita zotani ndipo Ayuda anatani?

14 Mfumu ya Asuri inamanga misasa ku Lakisi kum’mwera chakumadzulo kwa Yerusalemu. Ndiyeno inatumiza nthumwi zitatu kukauza anthu kuti angololera kuti agonja. Amene ankalankhula anali ndi dzina laudindo lakuti Rabisake ndipo anayesa kuopseza Ayuda m’njira zosiyanasiyana. Iye analankhula mu Chiheberi ndipo analimbikitsa anthu kuti asiye kutsatira mfumu yawo n’kugonjera Asuri. Anawanamiza kuti adzapita nawo kudziko lina kumene akasangalala kwambiri. (Werengani 2 Mafumu 18:31, 32.) Kenako Rabisake ananena kuti Yehova sadzatha kupulumutsa Ayuda kwa Asuri chifukwa milungu ina inalephera kuteteza anthu awo. Ayudawo anachita mwanzeru ndipo sanayankhe mabodzawo. Izi ndi zimene atumiki a Yehova masiku ano amachitanso nthawi zambiri.—Werengani 2 Mafumu 18:35, 36.

15. (a) Kodi anthu okhala mu Yerusalemu anayenera kuchita chiyani? (b) Kodi Yehova anapulumutsa bwanji Ayuda?

15 Izi zinadetsa nkhawa Hezekiya koma sanapemphe thandizo kwa mafumu ena. M’malomwake, anapempha mneneri Yesaya kuti  abwere. Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “[Senakeribu] sadzalowa mumzinda uno, kapena kuponyamo muvi.” (2 Maf. 19:32) Anthu okhala mu Yerusalemu anayenera kungolimba mtima osagonja chifukwa Yehova ndi amene ankawamenyera nkhondoyo. “Usiku umenewo, mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri n’kukapha asilikali 185,000.” (2 Maf. 19:35) Ayuda anapulumuka chifukwa chothandizidwa ndi Yehova osati chifukwa chakuti Hezekiya anatseka akasupe a madzi kapena kumanga makoma a mpanda.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO

16. Kodi anthu awa akuimira ndani masiku ano: (a) Ayuda amene anali ku Yerusalemu (b) “Msuri” (c) abusa 7 ndi atsogoleri 8?

16 Ulosi wonena za abusa 7 ndi atsogoleri 8 ukwaniritsidwa m’njira yaikulu masiku ano. Ayuda amene anali ku Yerusalemu anaukiridwa ndi Asuri. Koma posachedwapa, anthu a Yehova, amene azidzaoneka ngati osatetezeka, adzaukiridwa ndi “Msuri” wamakono. Iye adzafuna kuwonongeratu anthu a Yehovawo. Baibulo limafotokozanso za kuukira kwa ‘Gogi wa ku Magogi,’ “mfumu yakumpoto” ndiponso “mafumu a dziko lapansi.” (Ezek. 38:2, 10-13; Dan. 11:40, 44, 45; Chiv. 17:14; 19:19) Kodi onsewa adzaukira pa nthawi imodzi kapena zosiyana? N’kutheka kuti Baibulo likungofotokoza za kuukira kumodzi pogwiritsa ntchito mayina osiyanasiyana. Ndiyeno kodi ulosi wa Mika unanena kuti Yehova adzagwiritsa ntchito chiyani pomenya nkhondo ndi “Msuri” wamakonoyo, yemwe ndi woopsa kwambiri? Tingati iye adzagwiritsa ntchito asilikali amene anthu sakuganizira. Adzagwiritsa ntchito ‘abusa 7 ndi atsogoleri 8.’ (Mika 5:5) Abusa ndi atsogoleri (kapena kuti akalonga) amenewa akuimira akulu mumpingo. (1 Pet. 5:2) Masiku ano, Yehova wapereka akulu ambirimbiri mumpingo kuti aziweta nkhosa zake zamtengo wapatali ndiponso kuti azizilimbikitsa pokonzekera kuukira kwa “Msuri” wamakono. * Ulosi wa Mika umanena kuti iwo “adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga.” (Mika 5:6) Pa ‘zida za nkhondo yawo’ pali “lupanga la mzimu” lomwe ndi Mawu a Mulungu.—2 Akor. 10:4; Aef. 6:17.

17. Kodi akulu ayenera kuphunzira mfundo 4 ziti pa nkhani imene takambiranayi?

17 Pa nkhani imene takambiranayi, akulu ayenera kuphunzirapo mfundo izi: (1) Chinthu chofunika kwambiri pokonzekera kuukira kwa “Msuri” n’kuyesetsa kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu komanso kuthandiza abale athu kuchita zimenezi. (2) ‘Msuriyo’ akayamba kuukira, akulu asadzakayikire ngakhale pang’ono zoti Yehova atipulumutsa. (3) Pa nthawiyo, malangizo ena amene gulu la Yehova lingatipatse angaoneke ngati osathandiza. Koma tonsefe tiyenera kukhala okonzeka kutsatira malangizo alionse amene tingalandire ngakhale amene ifeyo kapena anthu ena angaone ngati ndi osathandiza. (4) Ino ndi nthawi yoti aliyense amene akudalira maphunziro apamwamba, chuma, mabungwe kapena maboma asinthiretu. Akulu ayenera kukhala okonzeka kuthandiza aliyense amene akuoneka kuti chikhulupiriro chake chikuchepa.

18. Kodi kukumbukira nkhani imene taphunzirayi kudzatithandiza bwanji m’tsogolomu?

18 Nthawi idzafika pamene atumiki a Yehova adzaoneka ngati osatetezeka mofanana ndi Ayuda amene anali mu Yerusalemu nthawi ya Hezekiya. Pa nthawiyo, tonsefe tiyenera kudzalimba mtima pokumbukira mawu a Hezekiya onena kuti adani athu ‘akudalira mphamvu za anthu koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kuti atithandize ndi kutimenyera nkhondo zathu.’—2 Mbiri 32:8.

^ ndime 4 Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “mtsikana” pa Yesaya 7:14 angatanthauze mkazi wokwatiwa komanso namwali. Choncho mawuwa akhoza kugwiritsidwa ntchito ponena za mkazi wa Yesaya komanso Mariya, pa nthawi imene anali namwali.

^ ndime 16 Nthawi zambiri, Baibulo limagwiritsa ntchito nambala ya 7 potanthauza chiwerengero chokwanira. Ndiyeno likawonjezera 1 n’kufika pa nambala ya 8, nthawi zina zimatanthauza kuchuluka.