Musataye Mtima Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Wamwalira
BAIBULO limanena momveka bwino kuti mwamuna ‘azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.’ Iwo ayenera kumachita zinthu ngati “thupi limodzi.” (Aef. 5:33; Gen. 2:23, 24) Anthu okwatirana akakhala limodzi kwa nthawi yaitali amayamba kugwirizana komanso kukondana kwambiri. Amayamba kuona zinthu mofanana, ndipo amakhala ngati mizu ya mitengo iwiri imene ili pamalo amodzi yomwe yalukanalukana.
Koma kodi chimachitika n’chiyani ngati mmodzi wamwalira? Ubwenzi wolimba kwambiriwu umathera pomwepo. Wotsalayo amapwetekedwa mtima, kusowa wocheza naye, ndipo nthawi zina amakwiya kapena kudziimba mlandu. Daniella anakhala m’banja kwa zaka 58. * Pa zaka zonsezi ankaona anthu ambiri akuferedwa amuna kapena akazi awo. Koma mwamuna wake atamwalira, iye anati: “Poyamba sindinkadziwa mmene anthuwa ankamvera. Munthu sangamvetse zimenezi mpaka zitamuchitikira.”
CHISONI CHAKE CHIMAKHALA NGATI SICHIDZATHA
Anthu ena atafufuza anaona kuti palibe chinthu chovutitsa maganizo kwambiri kuposa imfa ya mwamuna kapena mkazi wanu. Anthu ambiri amene anaferedwa amavomereza zimenezi. Mwachitsanzo, Millie amene mwamuna wake anamwalira zaka zambiri zapitazo anati, “Ndimaona ngati ndalumala.” Apa ankafotokoza mmene amamvera chifukwa cha imfa ya mwamuna wake amene anakhala naye zaka 25.
Susan ankaganiza kuti akazi amene ankadandaulabe kwa zaka zambiri mwamuna wawo atamwalira, ankakokomeza. Kenako mwamuna wake amene anakhala naye kwa zaka 38 anamwalira. Panopa padutsa zaka 20, koma iye anati, “Ndimamuganizira tsiku lililonse.” Nthawi zambiri amalira chifukwa choti akumusowa kwambiri.
Baibulo limanena kuti n’zopweteka kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu akamwalira ndipo chisoni chake sichitha msanga. Sara atamwalira, mwamuna wake Abulahamu “analowa muhema kukamulira.” (Gen. 23:1, 2) Abulahamu anamva chisoni kwambiri ngakhale kuti ankakhulupirira zoti akufa adzauka. (Aheb. 11:17-19) Yakobo sanaiwalenso msanga mkazi wake Rakele atamwalira ndipo ankauza ana ake za iyeyo.—Gen. 44:27; 48:7.
Kodi tikuphunzira chiyani kwa Abulahamu ndi Yakobo? Anthu amakhala achisoni kwa zaka zambiri mwamuna kapena mkazi wawo akamwalira. Choncho akamalira kapena kumva chisoni, tiziwamvetsa ndipo tisamawaone ngati opepera. Angafunike kulimbikitsidwa kwa nthawi yaitali.
MUSADERE NKHAWA ZA MAWA
Munthu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira amavutika kuzolowera moyo wokhala yekha. Mwamuna akakhala m’banja zaka zambiri, amadziwa zimene angachite kuti alimbikitse mkazi wake pamene ali ndi nkhawa. Iye akamwalira ndiye kuti zonsezi zimathera pomwepo. Nayenso mkazi amaphunzira zimene angachite kuti azisangalatsa komanso kusamalira mwamuna wake. Iye akhoza kumusisita ndiponso kumulankhula mawu olimbikitsa. Amaganiziranso zofuna zake kuposa wina aliyense. Mwamuna akhoza kuvutika kwambiri mkazi wake akamwalira. Choncho anthu ena amene mwamuna kapena mkazi wawo wamwalira amadera nkhawa za tsogolo lawo. Kodi ndi mfundo iti ya m’Baibulo imene ingawakhazike mtima pansi?
Mfundo yake ndi yakuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.” (Mat. 6:34) Mawu a Yesu amenewa akunena makamaka za kudera nkhawa zinthu zofunika pa moyo, komabe athandiza anthu ambiri amene aferedwa. Mwachitsanzo, miyezi ingapo mkazi wake atamwalira, Charles analemba kuti: “Monique ndimamusowabe kwambiri ndipo ndikuona ngati chisoni changa chikungokulirakulira. Koma ndikudziwa kuti zimenezi si zachilendo ndipo ziyamba kuchepa pakapita nthawi.”
Charles anayenera kupirira mpaka chisonicho chitayamba kuchepa. Kodi anatha bwanji kupirira? Iye anati: “Yehova ankandithandiza tsiku lililonse kuti ndisamadere nkhawa za mawa.” Choncho Charles sanataye mtima. N’zoona kuti sanasiye msanga kumva chisoni koma sankangokhalira kuganizira zimenezi. Ngati mwamuna kapena mkazi wanu wamwalira musamadere nkhawa za mawa. Simukudziwa zinthu zabwino kapena zolimbikitsa zimene zingachitike mawalo.
Cholinga cha Yehova sichinali choti anthu azifa. Koma imfa ndi imodzi mwa “ntchito za Mdyerekezi.” (1 Yoh. 3:8; Aroma 6:23) Satana amagwiritsa ntchito imfa ndiponso kuopa imfayo kuti anthu azikhala ngati akapolo komanso kuti akhale opanda chiyembekezo. (Aheb. 2:14, 15) Satana amasangalala akaona anthu akukayikira zoti zinthu zingawayendere bwino m’dzikoli kapena m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. Choncho nkhawa imene namfedwa amakhala nayo imabwera chifukwa cha uchimo wa Adamu komanso ziwembu za Satana. (Aroma 5:12) Yehova adzathetseratu imfa ndiponso mavuto onse amene Satana wayambitsa. Ngati mwaferedwa, dziwani kuti inuyo ndiponso anthu ambiri amene anaferedwa simudzavutikanso kapena kuopa chilichonse.
Zinthu zambiri zidzasintha anthu akadzaukitsidwa padzikoli. Mwachitsanzo, anthu okalamba komanso makolo athu akale akadzauka adzayamba kusintha n’kukhala angwiro limodzi ndi ana awo komanso zidzukulu zawo. Mavuto onse a ukalamba adzatheratu. Mwina anthu adzasintha mmene amaonera makolo awo kapena azigogo awo. Zimenezitu zidzachititsa kuti anthu azigwirizana kwambiri.
Anthu akaganizira za oukitsidwa amakhala ndi mafunso ambiri mwina okhudza anthu amene anaferedwa amuna kapena akazi angapo. Asaduki anafunsanso funso lomweli. Anafuna kudziwa kuti mkazi amene waferedwa amuna angapo adzakhala mkazi wa ndani onsewo akadzaukitsidwa. (Luka 20:27-33) Panopa sitikudziwa kuti zidzakhala bwanji ndipo palibe chifukwa chodzivutitsira kuganizira zimene zidzachitike. Chofunika panopa n’kukhulupirira Mulungu basi. Chinthu chimodzi chimene sitiyenera kukayikira n’chakuti, zimene Yehova adzachite m’tsogolo ndi zabwino zokhazokha ndipo sipadzakhala chilichonse chodetsa nkhawa.
CHIYEMBEKEZO CHAKUTI AKUFA ADZAUKA N’CHOLIMBIKITSA
Mawu a Mulungu amanena momveka bwino kwambiri kuti anthu amene anamwalira adzauka. M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anaukitsidwa ndipo zimenezi zimatsimikizira kuti anthu onse amene “ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Pa nthawiyo anthu adzasangalala kwambiri kulandira anthu oukitsidwawo. Ndipo n’zodziwikiratu kuti nawonso oukitsidwawo adzasangalala kwadzaoneni.
Anthu mabiliyoni ambiri akadzaukitsidwa, onse padzikoli adzasangalala kwambiri kuposa kale lonse. (Maliko 5:39-42; Chiv. 20:13) Kuganizira zimenezi n’kolimbikitsa kwambiri kwa onse amene anaferedwa.
Kodi padzakhala chilichonse chomvetsa chisoni anthu akadzayamba kuukitsidwa? Baibulo limayankha kuti ayi. Lemba la Yesaya 25:8 limanena kuti Yehova “adzameza imfa kwamuyaya.” Izi zikutanthauza kuti Mulungu adzachotseratu mavuto onse obwera chifukwa cha imfa. Paja ulosiwu ukupitiriza kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.” Ngati panopa muli ndi chisoni chifukwa choti mwamuna kapena mkazi wanu anamwalira, chisonicho chidzatheratu anthu akadzaukitsidwa.
Palibe munthu amene amamvetsa zonse zimene Mulungu adzachite m’dziko latsopano. Yehova akuti: “Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njira zanga n’zapamwamba kuposa njira zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.” (Yes. 55:9) Tikamakhulupirira zimene Yesu analonjeza zokhudza kuuka kwa akufa timasonyeza kuti timakhulupiriranso kwambiri Yehova ngati mmene Abulahamu anachitira. Chofunika kwambiri kwa Akhristu panopa n’kumvera Mulungu. Tikatero tidzakhala oyenerera kudzakhala ndi moyo limodzi ndi anthu amene adzaukitsidwe.—Luka 20:35.
KHULUPIRIRANI MALONJEZO A YEHOVA
Tiyeni tizikhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu ndipo tisadere nkhawa zam’tsogolo. Anthu ambiri amaganiza kuti zinthu sizidzayenda bwino m’tsogolo. Koma Yehova watilonjeza zinthu zabwino kwambiri. Sitikudziwa zonse zimene adzachite pokwaniritsa zokhumba zathu koma tisakayikire kuti adzakwaniritsadi zokhumba zathuzo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chimene chikuyembekezedwa chikaoneka sichikhalanso choyembekezedwa, chifukwa munthu akaona chinthu chimene anali kuchiyembekezera, kodi amachiyembekezanso? Koma ngati tikuyembekezera chimene sitikuchiona, timachidikirabe mopirira.” (Aroma 8:24, 25) Kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu kungakuthandizeni kupirira. Ngati mupirirabe mudzaona Yehova akukupatsani ‘zokhumba za mtima wanu.’ Paja Malemba amati iye adzakhutiritsa “zokhumba za chamoyo chilichonse.”—Sal. 37:4; 145:16; Luka 21:19.
Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, ophunzira ake ankada nkhawa kwambiri. Koma iye anawalimbikitsa ndi mawu akuti: “Mitima yanu isavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupiriraninso ine.” Ananenanso kuti: “Sindikusiyani ngati ana amasiye. Ndidzabwera kwa inu.” (Yoh. 14:1-4, 18, 27) Kwa zaka zambiri, mawu amenewa akhala akuthandiza odzozedwa kuti apirire komanso akhale ndi chiyembekezo. Ngati mwaferedwa, simuyeneranso kutaya mtima. Yehova ndi Yesu sadzakusiyani ngati amasiye. Musamakayikire zimenezi ngakhale pang’ono chifukwa posachedwapa mudzaona anzanuwo ataukitsidwa.
^ ndime 3 Mayina asinthidwa.