“Ikani Maganizo Anu pa Zinthu Zakumwamba”
“Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko.”—AKOL. 3:2.
1, 2. (a) Kodi mumpingo wa ku Kolose munkachitika zotani? (b) Kodi abale a ku Kolose analandira malangizo othandiza ati?
MUMPINGO wa Kolose munkachitika zinthu zoopsa. Anthu ena ankalimbikitsa Akhristu anzawo kutsatira Chilamulo cha Mose ndipo zimenezi zinasokoneza mgwirizano mumpingo. Panalinso ena amene ankaphunzitsa kuti n’kulakwa kuchita zinthu zosangalatsa. Pofuna kuthandiza abale a ku Kolose kuti asatengeke ndi zimenezi, Paulo analemba kalata yowachenjeza. Iye analemba kuti: “Samalani: mwina wina angakugwireni ngati nyama, mwa nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.”—Akol. 2:8.
2 Ngati Akhristu odzozedwawo akanaika maganizo awo pa mfundo za m’dzikoli, akanataya mwayi wawo wokhala ana a Mulungu. (Akol. 2:20-23) Pofuna kuwathandiza kuteteza ubwenzi wawo wamtengo wapatali ndi Mulungu, Paulo anawalangiza kuti: “Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba, osati pa zinthu zapadziko.” (Akol. 3:2) Abale a Khristuwo anayenera kuika maganizo awo pa chiyembekezo chodzalandira moyo wosafa kumwamba.—Akol. 1:4, 5.
3. (a) Kodi Akhristu odzozedwa amaika maganizo awo pa zinthu ziti? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?
3 Masiku anonso, Akhristu odzozedwa amaika maganizo awo pa Ufumu wa Mulungu wakumwamba ndiponso mwayi wawo wodzalamulira limodzi ndi Khristu. (Aroma 8:14-17) Koma kodi a “nkhosa zina,” omwe akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, angatsatire bwanji malangizo a Paulo oti aziika maganizo awo pa “zinthu zakumwamba”? (Yoh. 10:16) Nanga tingatsanzire bwanji anthu monga Abulahamu ndi Mose omwe ankaikabe maganizo awo pa zinthu zakumwamba pokumana ndi mavuto? M’nkhaniyi tikambirana mafunso amenewa.
KODI TINGAIKE BWANJI MAGANIZO PA ZINTHU ZAKUMWAMBA?
4. Kodi a nkhosa zina angaike bwanji maganizo awo pa zinthu zakumwamba?
4 Ngakhale kuti a nkhosa zina sakuyembekezera kupita kumwamba, iwonso angaike maganizo awo pa zinthu zakumwamba. Angachite zimenezi poika patsogolo Yehova Mulungu ndiponso zinthu zokhudza Ufumu. (Luka 10:25-27) Tingachite bwino kutsatira chitsanzo cha Khristu pa nkhaniyi. (1 Pet. 2:21) M’dziko la Satanali, ifenso timakumana ndi maganizo ndiponso nzeru zotsutsana ndi Mawu a Mulungu. (Werengani 2 Akorinto 10:5.) Choncho tiyenera kutsanzira Khristu n’kumapewa zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova.
5. Kodi tingadzifunse mafunso ati kuti tidziwe zimene zili mumtima mwathu?
5 Kodi tayamba kutsatira maganizo a dzikoli pa nkhani yofunafuna chuma? Zimene timakonda kwambiri ndi zimene timaganiziranso kwambiri komanso kuchita. Yesu anati: “Kumene kuli chuma chako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:21) Ndiye tingachite bwino kumadzifufuza kuti tidziwe zimene zili mumtima mwathu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaganizira kwambiri za ndalama? Kodi ndimangokhalira kuganizira za bizinezi, kupeza chuma kapena moyo wawofuwofu? Kapena kodi ndimayesetsa kuganizira zinthu zokhudza kutumikira Yehova?’ (Mat. 6:22) Yesu anasonyeza kuti anthu amene amafuna “kudziunjikira chuma padziko lapansi” akhoza kuwononga ubwenzi wawo ndi Yehova.—Mat. 6:19, 20, 24.
6. Kodi tingatani kuti tisatengeke ndi zinthu zokopa za m’dzikoli?
6 Anthufe ndife ochimwa, choncho sitichedwa kulakwitsa zinthu. (Werengani Aroma 7:21-25.) Ngati sitikutsogoleredwa ndi mzimu woyera tikhoza kuyamba kuchita “ntchito za mdima” monga ‘maphwando aphokoso, kumwa mwauchidakwa ndi khalidwe lotayirira.’ (Aroma 13:12, 13) Kuti tisatengeke ndi “zinthu zapadziko” zomwe zingaoneke zokopa, tiyenera kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba. Koma pamafunika khama kuti tichite zimenezi. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anati: “Ndikumenya thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo.” (1 Akor. 9:27) Choncho si bwino kudzilekerera. Tiyeni tsopano tikambirane zimene anthu awiri okhulupirika anachita kuti ‘akondweretse Mulungu.’—Aheb. 11:6.
ABULAHAMU ‘ANAKHULUPIRIRA YEHOVA’
7, 8. (a) Kodi Abulahamu ndi Sara anakumana ndi mavuto ati? (b) Kodi Abulahamu ankaganizira kwambiri zinthu ziti?
7 Abulahamu atauzidwa ndi Yehova kuti asamukire ku Kanani, anamvera ndi mtima wonse. Iye analidi munthu womvera ndipo ankakhulupirira Yehova. Choncho Yehova anachita naye pangano lakuti: “Ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe. Ndidzakudalitsa.” (Gen. 12:2) Koma panapita zaka zambiri Abulahamu ndi Sara alibe mwana. Kodi mwina Abulahamu ankaganiza kuti Yehova waiwala lonjezo lake? Mzinda wa Uri, umene Abulahamu ndi banja lake ankakhala ku Mesopotamiya, unali wotukuka ndipo moyo wake unali wabwino. Koma iwo analolera kusamuka n’kuyenda ulendo wa makilomita 1,600 kupita ku Kanani. Ndiyeno moyo wa ku Kananiko unali wovuta. Ankakhala m’mahema, kuvutika ndi njala komanso kukumana ndi achifwamba. (Gen. 12:5, 10; 13:18; 14:10-16) Ngakhale zinali choncho, sankafuna kubwerera ku Uri kuti azikasangalala.—Werengani Aheberi 11:8-12, 15.
8 Abulahamu sankaika maganizo ake pa “zinthu zapadziko” koma ‘ankakhulupirira Yehova.’ (Gen. 15:6) Iye ankaganizira kwambiri zinthu zakumwamba kapena kuti zimene Mulungu anamulonjeza. Chifukwa cha zimenezi, Mulungu anaonekera kwa iye n’kumuuza kuti: “‘Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.’ Ndipo anamuuzanso kuti: ‘Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.’” (Gen. 15:5) Mawu amenewa ayenera kuti anamulimbikitsa kwambiri. Nthawi iliyonse imene Abulahamu ankayang’ana kumwamba n’kuona nyenyezi, ayenera kuti ankakumbukira zimene Yehova anamulonjeza. Ndiyeno Abulahamu anadzakhaladi ndi mwana pa nthawi imene Mulungu ankafuna.—Gen. 21:1, 2.
9. Kodi tingatsanzire bwanji Abulahamu?
9 Ifenso tikuyembekezera zimene Mulungu watilonjeza. (2 Pet. 3:13) Tikasiya kuganizira kwambiri zinthu zimenezi, tikhoza kuona kuti zikuchedwa ndipo tingayambe kuchita mphwayi potumikira Mulungu. Mwachitsanzo, kodi kale munalolera kusiya zinazake kuti muchite upainiya kapena utumiki winawake? Dziwani kuti munachita bwino kwambiri. Koma kodi panopa mukuchita chiyani? Muyenera kutsanzira Abulahamu amene ankaganizira kwambiri za “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:10) Baibulo limati: “Abulahamu anakhulupirira mwa Yehova, ndipo anaonedwa ngati wolungama.”—Aroma 4:3.
MOSE ANKAONA “WOSAONEKAYO”
10. Kodi zinthu zinali bwanji pa moyo wa Mose ali mnyamata?
10 Nayenso Mose ankaika maganizo pa zinthu zakumwamba. Iye ali mnyamata, “anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo.” Maphunziro amenewa sanali maphunziro wamba. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawiyo, ufumu wa Iguputo unali wamphamvu kwambiri ndipo Mose anali m’banja la Farao. M’pake kuti maphunzirowa anachititsa Mose kukhala “wamphamvu m’mawu ndi m’zochita zake.” (Mac. 7:22) Iye akanatha kuchita zinthu zambirimbiri koma ankafunitsitsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Choncho tingati ankaika maganizo ake pa zinthu zapamwamba kwambiri.
11, 12. (a) Kodi Mose ankaona kuti maphunziro ofunika kwambiri ndi ati? (b) Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
11 Mayi a Mose anali Yokebedi ndipo n’zosakayikitsa kuti Mose ali mwana, mayi akewo ankamuphunzitsa za Mulungu wa Aheberi. Mose ankaona kuti zimene anaphunzira zokhudza Yehova n’zofunika kwambiri kuposa chuma chilichonse. Choncho analolera kusiya zonse zimene akanapeza m’banja la Farao. (Werengani Aheberi 11:24-27.) Mose anaphunzitsidwa za Yehova ndipo ankamukhulupirira kwambiri. Izi zinamuthandiza kuti aziika maganizo ake pa zinthu zakumwamba.
12 Mose anaphunzitsidwa zinthu zapamwamba kwambiri ku Iguputo koma sanagwiritse ntchito maphunzirowo pofuna udindo, kutchuka kapena chuma. Iye “anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao, ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo.” Mose anagwiritsa ntchito zimene anaphunzira zokhudza Yehova kuti akwaniritse cholinga cha Yehovayo.
13, 14. (a) N’chiyani chinathandiza Mose kuti agwire bwino ntchito imene Yehova anamupatsa? (b) Kodi nafenso tiyenera kuphunzira chiyani?
13 Mose ankakonda kwambiri Yehova ndi anthu ake. Iye ali ndi zaka 40, anaganiza kuti akhoza kupulumutsa anthu a Mulungu ku ukapolo. (Mac. 7:23-25) Koma Yehova ankadziwa kuti Mose ayenera kuphunzira kaye makhalidwe monga kudzichepetsa, kuleza mtima, kufatsa ndiponso kudziletsa. (Miy. 15:33) Kuphunzira zinthu zimenezi kukanamuthandiza kuti akwanitse kupirira mavuto amene anali m’tsogolo. Zaka 40 zimene anagwira ntchito yaubusa zinamuthandiza kuti akhale ndi makhalidwe amene tatchulawa.
14 Kodi ubusawo unamuthandizadi? Ee. Paja Mawu a Mulungu amati Mose anadzakhala “munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Iye anaphunzira kukhala wodzichepetsa ndipo izi zinamuthandiza kuti azileza mtima pothandiza anthu osiyanasiyana. (Eks. 18:26) Nafenso tiyenera kuphunzira makhalidwe abwino kuti tidzadutse bwinobwino pa “chisautso chachikulu” n’kulowa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (Chiv. 7:14) Kodi timayesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse ngakhale amene timawaona kuti ndi ovuta? Tingachite bwino kwambiri kutsatira malangizo a mtumwi Petulo onena kuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani. Kondani gulu lonse la abale.”—1 Pet. 2:17.
TIZIIKA MAGANIZO ATHU PA ZINTHU ZAKUMWAMBA
15, 16. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kuika maganizo athu pa zinthu zabwino? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala ndi khalidwe labwino?
15 Panopa tikukhala m’nthawi “yovuta.” (2 Tim. 3:1) Choncho tiyenera kuika maganizo athu pa zinthu zoyenera kuti tikhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (1 Ates. 5:6-9) Tiyeni tione njira zitatu zimene tingachitire zimenezi.
16 Khalidwe Lathu: Petulo ankadziwa kuti kukhala ndi khalidwe labwino n’kofunika. Iye anati: “Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti . . . pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zochita zanu zabwino, adzatamande Mulungu m’tsiku lake loyendera.” (1 Pet. 2:12) Kaya tili kunyumba, kuntchito, kusukulu, kocheza kapena mu utumiki, zochita zathu ziyenera kulemekeza Yehova. Popeza ndife anthu ochimwa, timalakwitsa zinthu zina. (Aroma 3:23) Koma tikapitiriza kumenya “nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro,” tikhoza kugonjetsa zilakolako zoipa.—1 Tim. 6:12.
17. Kodi tingatsanzire bwanji Khristu Yesu? (Onani chithunzi patsamba 28.)
17 Maganizo athu: Kuti tikhale ndi khalidwe labwino, tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera. Mtumwi Paulo anati: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.” (Afil. 2:5) Yesu anali wodzichepetsa. Choncho ankadzipereka kwambiri mu utumiki. Iye ankaganizira kwambiri ntchito youza anthu za Ufumu wa Mulungu. (Maliko 1:38; 13:10) Yesu ankafuna kuti Mawu a Mulungu azimutsogolera pa chilichonse. (Yoh. 7:16; 8:28) Iye ankaphunzira Malemba mwakhama n’cholinga choti aziwagwiritsa ntchito, kuwaikira kumbuyo komanso kuwafotokoza. Tingakhale ndi maganizo ofanana ndi Khristu tikamayesetsa kukhala odzichepetsa ndiponso akhama mu utumiki komanso pophunzira Baibulo.
18. Kodi tingathandize bwanji pa ntchito ya Yehova?
18 Kuthandiza pa ntchito ya Yehova: Yehova akufuna kuti ‘m’dzina la Yesu, onse akumwamba ndi apadziko lapansi apinde mawondo awo.’ (Afil. 2:9-11) Ngakhale kuti Yesu ali ndi udindo wapamwamba kwambiri, amagonjera Atate wake modzichepetsa. Ifenso tiyenera kugonjera Yehova. (1 Akor. 15:28) Tingachite zimenezi pothandiza ndi mtima wonse pa ntchito imene tapatsidwa ‘yophunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mat. 28:19) Tiyeneranso kuchitira “onse zabwino,” kaya akhale abale ndi alongo kapena anthu ena.—Agal. 6:10.
19. Kodi tonsefe tiyenera kuchita chiyani?
19 Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatikumbutsa kuti tiziika maganizo athu pa zinthu zakumwamba. Choncho tiyenera ‘kuthamanga mopirira mpikisano umene atiikirawu.’ (Aheb. 12:1) Tiyeni tonsefe tizitumikira Yehova ndi ‘moyo wathu wonse.’ Tikatero adzatidalitsa kwambiri.—Akol. 3:23, 24.