Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Odzichepetsa Ndiponso Achifundo Ngati Yesu

Khalani Odzichepetsa Ndiponso Achifundo Ngati Yesu

“Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.”1 PET. 2:21.

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutsanzira Yesu kungatithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova?

ANTHUFE timakonda kutsanzira anthu amene timawasirira. Yesu Khristu ndi woyenera kumutsanzira kuposa munthu wina aliyense. Tikutero chifukwa chakuti Yesu anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Yesu amatsanzira Atate wake kwambiri moti mukaona Mwana zili ngati mwaonanso Atatewo. Choncho tikamatsanzira Yesu timalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova, yemwe ndi wabwino kuposa wina aliyense m’chilengedwe chonse. Ndi mwayi waukulu kwambiri kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anachititsa kuti nkhani za moyo wa Yesu zilembedwe m’Baibulo? (b) Kodi Yehova amafuna kuti tizitani? (c) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi ndiponso yotsatira?

2 Koma kodi tingadziwe bwanji makhalidwe a Yesu? Tili ndi mwayi chifukwa Yehova anachititsa kuti nkhani zokhudza moyo wa Yesu zilembedwe m’Malemba Achigiriki. Iye anachita zimenezi n’cholinga choti tidziwe bwino Mwana wake n’kumamutsanzira. (Werengani 1 Petulo 2:21.) Baibulo limanena kuti tiyenera kutsatira “mapazi” a Yesu. Choncho zili ngati Yehova akufuna kuti tiziyenda kumbuyo kwa Yesu n’kumaponda pamene iye waponda. N’zoona kuti ndife ochimwa pomwe Yesu ndi wangwiro. Koma Yehova sayembekezera kuti tizitsatira mapazi a Yesu ndendende. M’malomwake, amafuna kuti tizichita zonse zimene tingakwanitse pomutsanzira.

3 Tiyeni tsopano tikambirane makhalidwe abwino a Yesu. M’nkhaniyi, tikambirana kudzichepetsa ndiponso chifundo cha Yesu ndipo m’nkhani yotsatira tikambirana za kulimba mtima ndi kuzindikira kwake. Pokambirana khalidwe lililonse tiziyankha mafunso atatu awa: Kodi munthu wakhalidweli amatani? Kodi Yesu analisonyeza bwanji? Kodi tingamutsanzire bwanji?

YESU NDI WODZICHEPETSA

4. Kodi munthu wodzichepetsa amatani?

4 Kodi munthu wodzichepetsa amatani? M’dzikoli anthu ambiri ndi onyada ndipo amaganiza kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka kapena wodzikayikira. Koma zimenezi si zoona. Munthu ayenera kukhala wolimba mtima kuti akhale wodzichepetsa. Iye amapeweratu kunyada kapena kudzikuza. Kuti tikhale odzichepetsa tiyenera kudziona moyenera. Buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limati: “Munthu wodzichepetsa amadziwa kuti iyeyo ndi wotsika kwambiri akadziyerekezera ndi Mulungu.” Kuzindikira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tizipewa kudziona ngati apamwamba tikakhala ndi anzathu. (Aroma 12:3; Afil. 2:3) Koma anthu ochimwafe kudzichepetsa kumativuta. Choncho kuti tikhaledi odzichepetsa tiyenera kukumbukira mmene tilili tikadziyerekezera ndi Mulungu n’kumayesetsa kutsanzira Mwana wake.

5, 6. (a) Kodi Mikayeli mkulu wa angelo ndi ndani? (b) Kodi Mikayeli anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa?

5 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa? Iye wakhala akusonyeza khalidweli kuyambira pamene anali mngelo wamphamvu kumwamba komanso pamene anali padzikoli. Tiyeni tikambirane mmene anasonyezera zimenezi.

6 Maganizo ake. Yuda analemba nkhani ina yosonyeza kuti Yesu anali wodzichepetsa asanabwere padzikoli. (Werengani Yuda 9.) M’nkhaniyi Yesu amatchedwa Mikayeli mkulu wa angelo ndipo imanena kuti iye “anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose.” Pamene Mose anamwalira, Yehova anamuika m’manda koma palibe amene anadziwa malo ake. (Deut. 34:5, 6) N’kutheka kuti Satana ankafuna kuti Aisiraeli azigwiritsa ntchito thupi la Mose polambira. Kaya Satanayo amafuna kuchita zotani ndi thupilo, Mikayeli analimba mtima n’kutsutsana naye. Buku lina limanena kuti mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “anasemphana maganizo” komanso akuti “anakangana” amanenanso zimene zimachitika anthu akamatsutsana kukhoti. Choncho mawuwa angasonyeze kuti Mikayeli ankatsutsa zoti Mdyerekezi ali ndi ufulu wotenga thupi la Mose. Ngakhale kuti Mikayeli anali mkulu wa angelo, anazindikira kuti alibe udindo woweruza Mdyerekezi. M’malomwake anasiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova podziwa kuti iye ndi Woweruza Wamkulu. Apatu tingati Mikayeli anaputidwa koma sanalole kuchita zinthu zopitirira udindo wake. Kodi kudzichepetsa kumaposa apa?

7. Kodi zolankhula ndiponso zochita za Yesu zimasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa?

7 Mawu a Yesu komanso zimene anachita padzikoli zimasonyeza kuti iye ndi wodzichepetsa kwambiri. Zolankhula zake. Yesu sankafuna kuti anthu aziganizira kwambiri za iye n’kumamulemekeza. Koma ankafuna kuti ulemerero wonse uzipita kwa Atate wake. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 7:16) Iye sankalankhula kapena kuchita zinthu ndi ophunzira ake ngati bwana wawo. Koma ankawalemekeza, ankawadalira ndiponso ankayamikira zabwino zimene ankachita. (Luka 22:31, 32; Yoh. 1:47) Zochita zake. Yesu anasankha zongokhala ngati munthu wamba ndipo sanafune kukhala ndi katundu wambiri. (Mat. 8:20) Iye ankalolera kugwira ntchito zooneka ngati zonyozeka. (Yoh. 13:3-15) Yesu anasonyezanso kudzichepetsa kwambiri pomvera Mulungu. (Werengani Afilipi 2:5-8.) Anthu odzikuza safuna kumvera koma Yesu ankadzichepetsa n’kumachita zonse zimene Mulungu amafuna. Iye anakhala “womvera mpaka imfa.” Zonsezi zikungosonyeza kuti Yesu ndi munthu wodzichepetsadi.Mat. 11:29.

KHALANI ODZICHEPETSA NGATI YESU

8, 9. Kodi tingasonyeze bwanji kudzichepetsa?

8 Kodi tingatani kuti tikhale odzichepetsa ngati Yesu? Maganizo athu. Kudzichepetsa kumathandiza kuti tisachite zinthu zopitirira udindo wathu. Tikazindikira kuti tilibe udindo woweruza ena, sitingafulumire kupezera anzathu zifukwa kapena kuwakayikira. (Luka 6:37; Yak. 4:12) Ngati ndife odzichepetsa sitidzakhala ‘olungama mopitirira muyezo’ n’kumaona kuti anthu amene alibe luso kapena udindo umene tili nawo ndi otsika. (Mlal. 7:16) Mkulu wodzichepetsa saona kuti ndi wapamwamba kuposa abale ena. Koma ‘amaona ena kukhala omuposa’ ndipo amakhala ngati wamng’ono.Afil. 2:3; Luka 9:48.

9 Taganizirani za m’bale wina dzina lake W. J. Thorn. Iye anali woyang’anira dera kuyambira mu 1894. Koma atagwira ntchito imeneyi kwa nthawi yaitali, anapemphedwa kuti apite ku Beteli ku New York kuti azikaweta nkhuku. Iye anati: “Ndikayamba kuganiza kwambiri za ineyo, ndimapita penapake n’kudziuza kuti: ‘Iwetu ndiwe fumbi basi. Palibe chifukwa choti uzidziona ngati wapamwamba.’” (Werengani Yesaya 40:12-15.) Iye analidi ndi mtima wodzichepetsa.

10. Kodi zolankhula ndi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa?

10 Zolankhula zathu. Ngati ndifedi odzichepetsa, mawu athu amasonyeza zimenezi. (Luka 6:45) Tikamacheza ndi ena timapewa kulankhula kwambiri zimene takwanitsa kuchita kapena udindo umene tapatsidwa. (Miy. 27:2) M’malomwake, timayesetsa kuona zabwino zimene abale ndi alongo athu achita. Komanso timawayamikira chifukwa cha makhalidwe awo abwino, luso lawo kapena zimene akwanitsa kuchita. (Miy. 15:23) Zochita zathu. Akhristu odzichepetsa safuna kukhala otchuka m’dzikoli. Koma amayesetsa kukhala moyo wosalira zambiri. Chifukwa chofuna kutumikira Yehova mwakhama, iwo amalolera kugwira ntchito zimene anthu m’dzikoli amaona kuti n’zonyozeka. (1 Tim. 6:6, 8) Koma chofunika kwambiri posonyeza kuti ndife odzichepetsa ndi kukhala omvera. Tiyenera kukhala odzichepetsa kuti ‘tizimvera amene akutsogolera’ mumpingo n’kumatsatira malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa.Aheb. 13:17.

YESU NDI WACHIFUNDO

11. Kodi munthu wachifundo amatani?

11 Chifundo n’chogwirizana ndi chikondi. Buku lina limafotokoza mtima wachifundo umene Baibulo limatilimbikitsa kukhala nawo. Limati: “Baibulo limatilimbikitsa kumvera chisoni anthu amene akuvutika. Kuwonjezera pa zimenezi, mtimawu uyenera kutilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe pothandiza anthu amene akuvutikawo.” Choncho, munthu wachifundo amayesetsa kuthandiza ena amene ali m’mavuto n’cholinga choti zinthu ziyambe kuwayendera bwino.

12. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankamvera ena chifundo? (b) Kodi mtima wake wachifundo unamulimbikitsa kuchita chiyani?

12 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi wachifundo? Maganizo ndi zochita zake. Yesu ankamvera ena chifundo kwambiri. Mwachitsanzo, iye “anagwetsa misozi” ataona Mariya ndi anthu ena akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro. (Werengani Yohane 11:32-35.) Kenako Yesu anagwidwa kwambiri chifundo moti anaukitsa Lazaro. Izi ndi zimene anachitanso pa nthawi imene anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye. (Luka 7:11-15; Yoh. 11:38-44) Mtima wachifundo wa Yesu unathandiza kuti Lazaro adzapezenso mwayi wodzakhala ndi moyo kumwamba. Pa nthawi ina m’mbuyomo, Yesu ‘anamvera chifundo’ gulu la anthu amene anasonkhana moti “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Zimene Yesu ankaphunzitsa pa nthawiyo zinathandiza kwambiri anthu amene anazitsatira. Apatu sikuti Yesu ankangomvera chisoni anthu basi n’kuwasiya koma ankawathandiza.Mat. 15:32-38; 20:29-34; Maliko 1:40-42.

13. Kodi Yesu ankalankhula bwanji ndi anthu ena? (Onani chithunzi patsamba 5.)

13 Mawu ake. Yesu ankalankhula mwachifundo, makamaka kwa anthu ovutika. Mtumwi Mateyu anasonyeza kuti Yesaya ankanena za Yesu pamene analemba kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo chingwe cha nyale chomwe chatsala pang’ono kuzima sadzachizimitsa.” (Yes. 42:3; Mat. 12:20) Yesu ankalankhula mawu olimbikitsa kwa anthu amene anali ngati bango lophwanyika kapena nyale imene yatsala pang’ono kuzima. Ankalalikira uthenga umene unkathandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo. Apa zinali ngati ‘akumanga zilonda za anthu osweka mtima.’ (Yes. 61:1) Yesu anauza anthu “ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa” kuti abwere kwa iye n’cholinga choti ‘awatsitsimutse.’ (Mat. 11:28-30) Iye anauzanso otsatira ake kuti Mulungu amamvera chifundo anthu onse amene amamulambira. Pa anthu amene Yehova amawamvera chifundo, pali ena amene Yesu anawatchula kuti ‘tiana’ chifukwa chakuti amaoneka onyozeka m’dzikoli.Mat. 8:12-14; Luka 12:6, 7.

KHALANI ACHIFUNDO NGATI YESU

14. Kodi tingatani kuti tizichitira ena chifundo?

14 Kodi tingatani kuti tikhale achifundo ngati Yesu? Mtima wathu. Anthufe sitibadwa ndi mtima wachifundo. Choncho Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukhala ndi mtima umenewu. Mkhristu aliyense ayenera kuvala umunthu watsopano ndipo chifundo ndi khalidwe lina limene timauzidwa kuti tivale. (Werengani Akolose 3:9, 10, 12.) Kodi tingatani kuti tizichitira ena chifundo? Tiyenera kusintha mtima wathu. (2 Akor. 6:11-13) Tizikhala okonzeka kumvetsera mwatcheru ngati wina akufuna kutidandaulira zinazake. (Yak. 1:19) Tizidzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikanakumana ndi vuto lakeli ndikanamva bwanji? Kodi ndikanafuna kuti ena andichitire chiyani?’1 Pet. 3:8.

15. Kodi tingathandize bwanji anthu okhala ngati bango lophwanyika kapena nyale imene yatsala pang’ono kuzima?

15 Zochita zathu. Munthu wachifundo amayesetsa kuthandiza anthu n’cholinga choti zinthu ziyambe kuwayendera bwino. Amachita zimenezi makamaka kwa anthu ooneka ngati bango lophwanyika kapena nyale imene yatsala pang’ono kuzima. Ndiyeno kodi tingathandize bwanji anthu oterewa? Lemba la Aroma 12:15 limanena kuti: “Lirani ndi anthu amene akulira.” Anthu amene ali ndi nkhawa kapena chisoni amafuna kuti tiziwalimbikitsa osati kumangowauza zochita. Izi n’zimene mlongo wina ananena pamene mwana wake anamwalira. Iye anati: “Anzanga atabwera anangoyamba kulira nane basi. Izi zinandilimbikitsa kwambiri.” Kuchitira anthu ena zinthu zabwino ndi njira inanso yosonyezera chifundo. Mwachitsanzo, tingathandize mlongo wamasiye kukonza nyumba yake. Kapena mwina tingathandize wachikulire kuti akafike ku misonkhano, kuchipatala kapena kuti alowe mu utumiki. Nthawi zina zinthu zochepa zimatha kuthandiza kwambiri munthu amene akuvutika. (1 Yoh. 3:17, 18) Koma kulalikira mwakhama ndi njira yaikulu yosonyezera chifundo. Tikutero chifukwa chakuti uthenga wabwino umasintha kwambiri moyo wa anthu amtima wabwino.

Kodi mumakonda kwambiri Akhristu anzanu? (Onani ndime 15)

16. Kodi tingalimbikitse bwanji anthu amene ali ndi chisoni kapena nkhawa?

16 Zolankhula zathu. Mtima wachifundo umatithandizanso kulankhula “molimbikitsa kwa amtima wachisoni.” (1 Ates. 5:14) Kodi tingalimbikitse bwanji anthu oterewa? Tingawalimbikitse powauza mawu osonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso kuwaganizira. Mwachitsanzo, tingathe kuwayamikira kwambiri pa zinthu zimene amachita bwino. Izi zingawathandize kuzindikira kuti iwo ndi anthu ofunika. Tingachite bwinonso kuwakumbutsa kuti Yehova anawakokera kwa Mwana wake chifukwa choona kuti iwo ndi amtengo wapatali. (Yoh. 6:44) Tingawatsimikizirenso kuti Yehova amakonda kwambiri atumiki ake amene ali ndi “mtima wosweka” ndiponso amene ‘akudzimvera chisoni.’ (Sal. 34:18) Tikamalankhula mwachifundo kwa anthu achisoni timawalimbikitsa kwambiri.Miy. 16:24.

17, 18. (a) Kodi Yehova amafuna kuti akulu azisamalira bwanji nkhosa zake? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

17 Yehova amafuna kuti akulu azisamalira nkhosa zake mwachikondi. (Mac. 20:28, 29) Akulu apatsidwa udindo wodyetsa ndiponso kulimbikitsa nkhosa. (Yes. 32:1, 2; 1 Pet. 5:2-4) Mkulu wachifundo salamulira nkhosa. Ngati munthu akuchita zonse zimene angathe, samuchititsa kudziimba mlandu kapena kuganiza kuti sakuchita zokwanira. M’malomwake amawathandiza kukhala osangalala. Amakhulupirira kuti iwo azichita zonse zimene angathe chifukwa chokonda Yehova.Mat. 22:37.

18 Tikaganizira za kudzichepetsa kwa Yesu komanso chifundo chake, timafunitsitsa kumutsanzira. M’nkhani yotsatira tidzakambirana makhalidwe ena abwino a Yesu. Tidzakambirana za kulimba mtima ndiponso kuzindikira.